Chipulumutso Chiri Pafupi kwa Anthu Odzipereka Mwaumulungu!
“Yehova amadziŵa kulanditsa anthu odzipereka mwaumulungu ku chiyeso, koma kuwasunga anthu osalungama kaamba ka tsiku la chiweruzo kuti akadulidwe.”—2 PETRO 2:9, “NW.”
1. (a) Kodi ndi mikhalidwe yovutitsa yotani imene mtundu wa anthu ukuyang’anizana nayo m’tsiku lathu? (b) Polingalira zimenezi, kodi ndi mafunso otani amene tidzalingalira?
MAVUTO a moyo akuwonjezereka ku mtundu wonse wa anthu. Zimenezi nzowona kaya wina amakhala kumene zinthu zakuthupi nzambiri kapena kumene ziri zochepa. Kupanda chisungiko kulipo konsekonse. Ngati kuti mikhalidwe yosakhazikika ya zachuma siyokwanira kuda nayo nkhaŵa, mavuto owopsya a malo otizinga akusakaza pulaneti Dziko Lapansi, kuwopsyeza zamoyo zonse zokhalapo. Matenda ali ofala. Matenda opatsirana, nthenda za mtima, ndi mliri wa kansa zimatenga chiŵerengero chachikulu. Mkhalidwe wachisembwere wasakaza maganizo a anthu ndi moyo wa banja. Pambali pa zonsezi, dziko ladzazidwa ndi chiwawa. Polingalira za zimene chitaganya cha anthu chikuyang’anizana nazo, mozindikira tikufunsa kuti: Kodi pali maziko abwino oyembekezerera chipulumutso chamwamsanga? Ngati ndi tero, kodi chidzabwera motani, ndipo kaamba ka yani?—Yerekezerani ndi Habakuku 1:2; 2:1-3.
2, 3. (a) Kodi nchifukwa ninji lerolino tikupeza zimene zanenedwa pa 2 Petro 2:9 kukhala zolimbikitsa? (b) Kodi ndi machitidwe achipulumutso achindunji otani amene Baibulo limasonyako monga maziko a chilimbikitso?
2 Zimene zikuchitika m’tsiku lathu zimatikumbutsa za nthaŵi zina zotchuka m’mbiri ya munthu. Mtumwi Petro akukokera chisamaliro chathu ku machitidwe a chipulumutso amene Mulungu anachita pa zochitika zimenezo ndipo akufika ku mapeto otsimikizira awa: “Yehova amadziŵa kulanditsa anthu odzipereka mwaumulungu ku chiyeso.” (2 Petro 2:9, NW) Onani mawu ozungulira lemba a ndemanga imeneyo, pa 2 Petro 2:4-10 (NW):
3 “Ndithudi ngati Mulungu sanaleka kulanga angelo amene anachimwa, koma, mwa kumawaponya iwo mu Dzenje, anawapereka iwo ku maenje a mdima waukulu kuti akasungidwe kaamba ka chiweruzo; ndipo iye sanaleka kulanga dziko lakale, koma anamsunga Nowa, mlaliki wa chilungamo, bwino lomwe limodzi ndi ena asanu ndi aŵiri pamene iye anadzetsa chigumula pa dziko la anthu opanda umulungu; ndipo mwa kumaisandutsa mizinda ya Sodomu ndi Gomora kukhala phulusa iye anaitsutsa iyo, akumapereka chitsanzo kaamba ka anthu opanda umulungu a zinthu zirinkudza; ndipo iye anamlanditsa Loti wolungamayo, amene anasautsidwa kwakukulu ndi kumwerekera kwa anthu onyoza lamulo mu mkhalidwe wachisembwere—pakuti munthu wolungama ameneyo mwa zimene iye anaziwona ndi kuzimva pamene anali kukhala pakati pawo tsiku ndi tsiku zinali kumauzunza moyo wake wolungama chifukwa cha zochita zawo zosaweruzika—Yehova amadziŵa kulanditsa anthu odzipereka mwaumulungu ku chiyeso, koma kuwasunga anthu osalungama kaamba ka tsiku la chiweruzo kuti akadulidwe, komabe, makamaka, awo amene amatsatira thupi limodzi ndi chikhumbo chakuliipitsa ndi amene amanyozetsa umbuye.” Monga mmene malemba amenewo akusonyezera, zimene zinachitika m’tsiku la Nowa ndi m’nthaŵi ya Loti ziri ndi tanthauzo kwa ife.
Mzimu Wofalikira m’Tsiku la Nowa
4. M’tsiku la Nowa, kodi nchifukwa ninji Mulungu anawona dziko lapansi kukhala lovunda? (Salmo 11:5)
4 Cholembedwa cha mbiri mu Genesis mutu 6 chimatiuza kuti m’tsiku la Nowa dziko lapansi linavunda pamaso pa Mulungu. Chifukwa ninji? Chifukwa cha chiwawa. Iyo sinali nkhani ya upandu wachiwawa cha apa ndi apo. Genesis 6:11 akusimba kuti “dziko lapansi . . . linadzala ndi chiwawa.”
5. (a) Kodi ndi mkhalidwe wotani kumbali ya anthu umene unathandizira ku chiwawa cha tsiku la Nowa? (b) Kodi Enoke adali atachenjezanji ponena za kupanda umulungu?
5 Kodi nchiyani chimene chinali chochititsa? Lemba logwidwa mawu pa 2 Petro likulozera kwa anthu opanda umulungu. Inde, mzimu wa kupanda umulungu unaipitsa machitachita a anthu. Zimenezi zinaloŵetsamo osati kokha kusasamala malamulo aumulungu kwachisawawa koma mkhalidwe wamwano kulinga kwa Mulungu iyemwini.a Ndipo pamene anthu ali amwano kulinga kwa Mulungu, kodi zingayembekezeredwe motani kuti iwo akachitira mwachifundo anthu anzawo? Kalekale Nowa asanabadwe, kupanda umulungu kumeneku kunali kochuluka kotero kuti Yehova anapangitsa Enoke kulosera ponena za zotulukapo zake. (Yuda 14, 15) Kuchitira kwawo Mulungu mwano kunali kotsimikiza kuwabweretsera chiweruzo chaumulungu.
6, 7. Kodi ndi mkhalidwe wotani woloŵetsamo angelo umene unali chochititsa chenicheni cha mikhalidwe imene inachitika Chigumula chisanadze?
6 Padalinso chisonkhezero china chimene chinathandizira ku chiwawa cha masiku amenewo. Genesis 6:1, 2 akulunjikitsako chisamaliro pamene akunena kuti: “Ndipo panali pamene anthu anayamba kuchuluka padziko, ndi ana aakazi anawabadwira iwo, kuti ana aamuna a Mulungu anayang’ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.” Kodi ana aamuna a Mulungu ameneŵa anali yani? Osati anthu wamba. Amuna kwa zaka mazana ambiri anakhala akuwona akazi okongola ndi kumawakwatira. Ana aamuna a Mulungu ameneŵa anali angelo amene anavala matupi. Pa Yuda 6, iwo akulongosoledwa kukhala “angelonso amene sanasunga chikhalidwe chawo choyamba.”—Yerekezerani ndi 1 Petro 3:19, 20.
7 Pamene zolengedwa zosakhala zaumunthu zimenezi zimene zinavala matupi aumunthu zinakhala ndi unansi wakugonana ndi ana aakazi a anthu, kodi nchiyani chimene chinatulukapo? “Pa dziko lapansi panali anthu akulukulu masiku omwewo ndiponso pambuyo pake, ana aamuna a Mulungu atalowa kwa ana aakazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka.” Inde, mbadwa za kugonana kosakhala kwachibadwa kumeneko zinali Anefili, amphamvu amene anagwiritsira ntchito mphamvu zawo zazikulu kuvutitsa ena.—Genesis 6:4.
8. Kodi Yehova anachitapo kanthu motani ku mikhalidwe yoipa ya padziko lapansi?
8 Kodi mkhalidwewo unali woipa motani? Unafika ku mlingo wakuti “anawona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu pa dziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha.” Kodi Mulungu anachitanji ku zimenezi? “Yehova anamva chisoni chifukwa anapanga munthu pa dziko lapansi, ndipo anavutika m’mtima mwake.” Izi sizikutanthauza kuti Mulungu anadzimva kuti anaphophonya pamene analenga mtundu wa anthu. Koma, anamva chisoni kuti pambuyo popanga anthu, mkhalidwe wawo unakhala woipa kotero kuti anakakamizika kuwawononga.—Genesis 6:5-7.
Njira Imene Inatsogolera ku Chipulumutso
9. (a) Kodi Mulungu anachitiranji mwachiyanjo kulinga kwa Nowa? (b) Kodi ndi chenjezo la pasadakhale lotani limene Mulungu anampatsa Nowa?
9 Koma Nowa, iye “anapeza ufulu pamaso pa Yehova. . . . Nowa anali munthu wolungama ndi wangwiro m’mibadwo yake; Nowa anayendabe ndi Mulungu.” (Genesis 6:8, 9) Chotero Yehova anampatsa Nowa chenjezo la pasadakhale kuti Iye akabweretsa chigumula cha dziko lonse ndi kumlangiza kumanga chingalawa. Mtundu wonse wa anthu, kupatulapo Nowa ndi banja lake, akasesedwa pa nkhope ya dziko lapansi. Ngakhale zolengedwa za nyama zikawonongedwa, kupatulapo zoŵerengeka za mtundu uliwonse zimene Nowa akaziloŵetsa m’chingalawa.—Genesis 6:13, 14, 17.
10. (a) Kodi ndi kukonzekera kotani kumene kunayenera kuchitidwa polingalira za kupulumutsidwa, ndipo kodi ntchitoyo inali yaikulu motani? (b) Kodi nchiyani chimene chiri chosangalatsa ponena za mkhalidwe umene Nowa anasamalirira ntchito yake?
10 Chidziŵitso chapasadakhale chimenechi chinaika thayo lalikulu pa Nowa. Chingalawa chiyenera kumangidwa. Chinayenera kupangidwa ngati bokosi lalikulu, la ukulu wamkati wa mamita macubic 40,000. Nowa anayenera kuchidzaza ndi zakudya ndipo kenaka kusonkhanitsa zinyama ndi mbalame, “mtundu uliwonse wa chamoyo,” (NW) kuti upulumutsidwe. Inali projekiti imene ikaloŵetsamo zaka za ntchito. Kodi Nowa anavomereza motani? Iye “anachita . . . monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anachita.”—Genesis 6:14-16, 19-22; Ahebri 11:7.
11. Ponena za banja lake, kodi ndi thayo lofunika koposa lotani limene linali pa Nowa?
11 Pamene ankachita ntchito imeneyo, Nowa anayeneranso kupereka nthaŵi ya kumangirira uzimu wa banja lake. Iwo anafunikira kuchinjirizidwa kusatengera njira zachiwawa ndi mkhalidwe wamwano wa anthu owazinga. Chinali chofunika kuti iwo asakhale oloŵerera mopambanitsa m’zochitika za moyo za tsiku ndi tsiku. Mulungu anali ndi ntchito yoti iwo aichite, ndipo chinali chofunika koposa kuti miyoyo yawo izikidwe pa iyo. Tikudziŵa kuti banja la Nowa linalandira malangizo ake ndipo linali ndi chikhulupiriro chake chifukwa chakuti Nowa, mkazi wake, ana awo aamuna atatu, ndi akazi a ana awo—onse pamodzi anthu asanu ndi atatu—akulankhulidwa mwachiyanjo m’Malemba.—Genesis 6:18; 1 Petro 3:20.
12. Monga momwe kwasonyezedwera pa 2 Petro 2:5, kodi ndi thayo lotani limene Nowa anakwaniritsa mokhulupirika?
12 Nowa analinso ndi thayo lina—kuchenjeza za kudza kwa Chigumula ndi kudziŵikitsa chifukwa chimene chinkadzera. Nchachiwonekere kuti iye anachita thayo limenelo mokhulupirika, popeza kuti akulozeredwako m’Mawu a Mulungu kukhala “mlaliki wa chilungamo.”—2 Petro 2:5.
13. Kodi ndi mikhalidwe yotani imene inayang’anizana ndi Nowa pamene anali kusamalira ntchito yake yopatsidwa ndi Mulungu?
13 Tsopano tangolingalirani za mikhalidwe mu imene Nowa anachitira ntchito imeneyo. Dziikeni m’malo ake. Ngati mudali Nowa kapena chiŵalo cha banja lake, mukanazingidwa ndi chiwawa chimene chinakulitsidwa ndi Anefili ndi anthu opanda umulungu. Mukanayang’anizana mwachindunji ndi chisonkhezero cha angelo opanduka. Pamene munkagwira ntchito pa chingalawa, mukanakhala chandamale cha kusekedwa. Ndipo chaka ndi chaka pamene munkachenjeza anthu za Chigumula chomadzacho, mukanapeza kuti anthu anali otanganitsidwa koposa ndi zochita za tsiku ndi tsiku za moyo kotero kuti “sanadziŵa”—uko ndiko kuti, “kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse.”—Mateyu 24:39; Luka 17:26, 27.
Kodi Zokumana Nazo za Nowa Zimatanthauzanji kwa Inu?
14. Kodi nchifukwa ninji ife lerolino sitichipeza kukhala chovuta kumvetsetsa mkhalidwe umene Nowa ndi banja lake anayang’anizana nawo?
14 Mkhalidwe woterowo siwovuta kwa aŵerengi athu ambiri kuulingalira. Chifukwa ninji ayi? Chifukwa chakuti mikhalidwe m’tsiku lathu njofanana kwambiri ndi ija imene inafalikira m’masiku a Nowa. Yesu Kristu anati ichi chinayenera kuyembekezeredwa. Mu ulosi wake waukulu wonena za nthaŵi ya kukhalapo kwake mkati mwa mathedwe a dongosolo iri la zinthu, Yesu ananeneratu kuti: “Monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu.”—Mateyu 24:37.
15, 16. (a) Kodi ndizowona motani kuti, mofanana ndi m’tsiku la Nowa, dziko lapansi lerolino ladzala ndi chiwawa? (b) Kodi ndi chiwawa chiti mwapadera chimene atumiki a Yehova akuchitiridwa?
15 Kodi zachitika motero? Kodi dziko lerolino ladzazidwa ndi chiwawa? Inde! Anthu oposa miliyoni zana limodzi afa m’nkhondo m’zaka za zana lino. Ena a aŵerengi athu azimva mwachindunji ziyambukiro za zimenezi. Owonjezereka awopsyezedwa ndi apandu ofunitsitsa kutenga ndalama zawo kapena zinthu zina za mtengo. Ndipo achichepere awunikiridwa ku chiwawa ku sukulu.
16 Komabe, atumiki a Yehova akumana ndi zoposa kusakaza kwa nkhondo ndi upandu wachiwawa wosasankha. Iwo akuchitiridwanso chiwawa chifukwa chosakhala mbali ya dziko koma kuyesetsa kukhala anthu odzipereka mwaumulungu. (2 Timoteo 3:10-12) Nthaŵi zina chiwawa choterocho chimangokhala kukankhidwa kapena kuwombedwa mbama; nthaŵi zina chimaloŵetsamo kuwonongedwa kwa katundu, kumenya kwankhalwe, ndipo mwina kupha kwenikweni.—Mateyu 24:9.
17. Kodi kupanda umulungu nkochuluka lerolino? Longosolani.
17 Pamene akudziloŵetsa m’chiwawa choterocho, anthu opanda umulungu akhoza, nthaŵi zina, kulengeza mwapoyera kunyoza kwawo Mulungu. M’dera lina mu Africa, apolisi analengeza kuti: “Boma ndi lathu. Inu pitani kwa Mulungu, ngati aliko, ndi kumpempha kuti abwere adzakuthandizeni.” M’ndende ndi misasa yachibalo, Mboni za Yehova zayang’anizana ndi amuna onga ngati Baranowsky, mu Sachsenhausen, Germany, amene ananyoza kuti: “Ndayamba kumenyana ndi Yehova. Tidzawona amene ali wamphamvu, ine kapena Yehova.” Mwamsanga pambuyo pake, Baranowsky anadwala namwalira; koma ena akupitirizabe kusonyeza mkhalidwe wofananawo. Nduna zodziloŵetsa m’nkhondo ya mtanda yozunza siziri zokha zimene zimachitira Mulungu mwano. Kuzungulira dziko, atumiki a Mulungu amamva ndi kuwona zinthu zimene zimapereka umboni wakuti awo amene amadziloŵetsa mu izo sawopa Mulungu m’mitima yawo.
18. Kodi mizimu yoipa ikuthandizira motani ku mkhalidwe wovutitsa wa mtundu wa anthu?
18 M’masiku ano amene ali ofanana kwambiri ndi nthaŵi ya Nowa, tikuchitiranso umboni kusokoneza kochitidwa ndi mizimu yoipa. (Chibvumbulutso 12:7-9) Ziŵanda zimenezi ziri angelo amodzimodziwo amene anavala matupi aumunthu ndi kukwatira akazi m’masiku a Nowa. Pamene Chigumula chinadza, akazi awo ndi ana anawonongedwa, koma angelo osamverawo anakakamizika kubwerera ku m’bwalo la mizimu. Iwo analibenso malo m’gulu loyera la Yehova koma anatumizidwa ku Dzenje, mkhalidwe wa mdima woti bii, wopanda kuunika kwaumulungu. (2 Petro 2:4, 5) Pogwira ntchito pansi pa chitsogozo cha Satana, iwo apitirizabe kugwirizana mwathithithi ndi anthu ndipo, ngakhale kuti sali okhoza kuvalanso matupi, ayesera kulamulira amuna, akazi, ndiponso ana. Zina za izi zikuchitika kupyolera m’machitachita a kuwombeza. Iwo amasonkhezeranso anthu kuti awonongane m’njira zimene zimaipitsa kulingalira kwa anthu. Komatu sizokhazo.
19. (a) Kodi nkwayani makamaka kumene ziŵandazo zimalunjikitsa chidani chawo? (b) Kodi ziŵanda zikuyesera kutikakamiza kuchita chiyani?
19 Baibulo likuvumbula kuti ziŵanda zikumenya nkhondo yolimbana ndi awo “amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nawo umboni wa Yesu.” (Chibvumbulutso 12:12, 17) Mizimu yoipa imeneyo ndiyo oyambitsa enieni a chizunzo cha atumiki a Yehova. (Aefeso 6:10-13) Iyo imagwiritsira ntchito njira iriyonse yachinyengo kunyengerera kapena kukopa anthu okhulupirika kuti aswe umphumphu kwa Yehova ndi kuleka kulengeza Ufumu wa Yehova ndi Yesu monga Mfumu Yaumesiya.
20. Kodi ndimotani mmene ziŵanda zimayesera kulepheretsa anthu kumasuka ku ulamuliro wawo? (Yakobo 4:7)
20 Ziŵanda zimayesera kuletsa anthu amene amafuna kumasuka ku chisonkhezero chawo chopondereza. Yemwe kale anali wamizimu wa ku Brazil akusimba kuti pamene Mboni zinafikira pa nyumba yake, mawu a chiŵanda anamulamula kusatsegula chitseko; koma anatsegula, ndipo anaphunzira chowonadi. M’madera ambiri ziŵanda zimagwiritsira ntchito ochita ufiti kuyesera kuimitsa ntchito ya Mboni za Yehova. Mwachitsanzo, m’mudzi wina mu Suriname, otsutsa Mboni za Yehova anafunsira wamizimu amene anali wotchuka chifukwa chokhala wokhoza kupangitsa imfa ya anthu ya mwadzidzidzi mongowaloza ndi ndodo yake yamatsenga. Ndi makamu ake a ovina ndi oimba ng’oma, wamizimuyo, wogwidwa ndi chiŵanda, anayang’anizana ndi Mboni za Yehova. Analankhula mawu ake amatsenga ndi kuziloza ndi ndodo yake yamatsenga. Anthu a m’mudziwo anayembekezera kuti Mbonizo zidzagwa pansi zakufa, koma anali wamizimuyo amene anakomoka ndipo anayenera kuchotsedwa ndi achilikizi ake omvetsedwa manyazi.
21. Mofanana ndi m’tsiku la Nowa, kodi ndimotani mmene unyinji wa anthu umachitira ku kulalikira kwathu, ndipo kodi nchifukwa ninji?
21 Ngakhale m’malo mmene ufiti ndi kupenduza sizimachitika mwapoyera, Mboni iriyonse ya Yehova yakumana ndi mmene ziriri kuyesera kulalikira kwa anthu amene ali otanganitsidwa koposa ndi zochitika za tsiku ndi tsiku za moyo kotero kuti samafuna kuvutitsidwa. Monga momwe zinaliri m’tsiku la Nowa, unyinji waukulu ‘sumadziŵa.’ (Mateyu 24:37-39) Ena angamakhumbire kugwirizana kwathu ndi zipambano. Koma ntchito yathu yomanga yauzimu—yoloŵetsamo maola a phunziro laumwini, kupezeka pa misonkhano mokhazikika, ndi utumiki wakumunda—zonsezo ziri kupusa kwa iwo. Iwo amaseka chidaliro chathu m’malonjezo a Mawu a Mulungu chifukwa chakuti miyoyo yawo yazikidwa pa chuma chakuthupi ndi zosangalatsa zotsitsimula zimene iwo angakhale nazo tsopano.
22, 23. Kodi ndimotani mmene zochitika za m’tsiku la Nowa zimaperekera chitsimikizo chabwino chakuti Yehova adzapulumutsa anthu odzipereka mwaumulungu ku chiyeso?
22 Kodi atumiki okhulupirika a Yehova adzachitiridwa moipa kosatha ndi awo amene sakonda Mulungu? Kutalitali! Kodi nchiyani chimene chinachitika m’tsiku la Nowa? Motsogozedwa ndi Mulungu, Nowa ndi banja lake analoŵa m’chingalawa chotsirizidwacho. Kenaka, pa nthaŵi yoikidwiratu mwaumulungu, “akasupe onse a madzi aakulu anasefukira, ndi mazenera a kumwamba anatseguka.” Chigumulacho chinapitiriza kufikira mapiri anamizidwa. (Genesis 7:11, 17-20) Angelo amene anasiya malo awo anakakamizika kuvula matupi awo aumunthu ndi kubwerera ku bwalo la mizimu. Anefili ndi dziko lonselo la mtundu wa anthu opanda umulungu, kuphatikizapo awo amene sanafune kugonjera ku chenjezo la Nowa, anawonongedwa. Kumbali ina, Nowa ndi mkazi wake ndi ana awo aamuna atatu ndi akazi a anawo anapulumutsidwa. Chotero, Yehova anapulumutsa Nowa ndi banja lake ku chiyeso chimene iwo anapirira mokhulupirika kwa zaka zambiri.
23 Kodi Yehova adzachita zofananazo kwa anthu odzipereka mwaumulungu lerolino? Palibiretu chikaikiro ponena za chimenecho. Iye walonjeza zimenezo, ndipo sanganame.—Tito 1:2; 2 Petro 3:5-7.
[Mawu a M’munsi]
a “Anomia kuli kunyalanyaza, kapena kuchitira mwano, malamulo a Mulungu; asebeia [mpangidwe wa nauni wa liwu lotembenuzidwa ‘anthu opanda umulungu’] uli mkhalidwe umodzimodziwo kulinga ku Munthu wa Mulungu.”—Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words, Volyumu 4, tsamba 170.
Kodi Mumakumbukira?
◻ Kodi ndimotani mmene Petro anasonyezera kuti Yehova amadziŵa kupulumutsa anthu odzipereka mwaumulungu ku chiyeso?
◻ Kodi ndi nsonga zotani zimene zinathandizira ku chiwawa cha m’tsiku la Nowa?
◻ Polingalira za Chigumula cha dziko lonse chimene chinkadza, kodi ndi thayo lotani limene Nowa anali nalo?
◻ Kodi ndi zofanana zotani ndi tsiku la Nowa zimene tikuwona m’nthaŵi yathu?
[Chithunzi patsamba 12]
Kumanga chingalawa kunaloŵetsamo zaka za ntchito yakalavula gaga
[Chithunzi patsamba 13]
Nowa anapereka nthaŵi yokulitsa uzimu wa banja lake