Ripoti la Olengeza Ufumu
◻ MTUMWI Yohane ananena kuti: “Tisakonde ndi mawu, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m’chowonadi.” (1 Yohane 3:18) Yesu anati ‘tiyenera kukonda mnansi wathu monga ife eni.’ (Mateyu 22:39) Kusonyeza chikondi kumatsimikiziradi chowonadi, monga mmene chokumana nacho chotsatirachi cha ku Britain chikusonyezera.
Pamene Pauline anachezera amayi ake, omwe anali ndi matenda a multiple sclerosis, sankapezako wina aliyense kumeneko. Koma panthaŵiyi, pamene analoŵa m’nyumba, iye anamva kulira kwa makina ochapira ndi winawake m’chipinda chapamwamba akusesa ndi vacuum cleaner. “Kodi nchiyani chikuchitika, ndani ali muno?” iye anawafunsa amayi ake. Amayi ake analongosola kuti Mboni za Yehova zinabwera pa khomo lawo, zinawona vuto lawo, ndi kuima kuti zipereke thandizo. Zitachita ntchito ya m’nyumba ndi kukonza chakudya, zinakhala pansi nizifunsa kuti: “Kodi mwakonzekera?” “Kukonzekera chiyani?” anafunsa tero Pauline. Amayi ake analongosola kuti anali atavomera kuphunzira Baibulo. Pauline anazengereza zakuti akhale, koma popeza anachokera kutali, anafunsa ngati zikakhala bwino kuti nayenso akhalepo pa phunzirolo. Iye anasangalala nalo kwambiri kotero kuti anapanga makonzedwe kubwera tsiku limodzimodzilo mlungu uliwonse kuti adzipezekapo mokhazikika. M’kupita kwa nthaŵi, bwenzi linatsagana naye, ndipo tsopano onse aŵiri ngobatizidwa. Monga chotulukapo cha phunziro loyambirira limeneli, ziŵalo khumi zabanja limodzimodzilo ziri Mboni za Yehova tsopano! Inde, thandizo “m’kuchita”!
Pasitala mu New Guinea Alandira Chowonadi
◻ M’tsiku la Yesu ansembe ena analandira chiphunzitso cha Yesu. Atsogoleri achipembedzo owona mtima lerolino akuchitanso tero, monga zasonyezedwa ndi chokumana nacho cha ku New Guinea, chosimbidwa ndi woyang’anira wadera. Iye akufotokoza kuti: “Mwamuna wachichepere wophunzira bwino, pasitala wa Pentekosite, ankamanga tchalitchi chaching’ono pafupi ndi Nyumba Yaufumu. Mbale wina wa mpingowo anachitira umboni kwa iye, ndipo anawoneka kukhala waubwenzi. Mwamsanga pambuyo pa izi, ndinachezera mpingowo ndipo ndinakhala kwa mbaleyo kamtunda pang’ono kuyenda ndi msewu kuchokera pa nyumba ya pasitalayo. Madzulo oyamba nditafika, mwamuna wachichepereyu anabwera pa khomo pathu ndi Baibulo lake, limodzi ndi gulu lalikulu lochokera ku mpingo wake. Onsewo anafuna kumva uthenga wa Ufumu. Iye anafunsa mafunso ambiri, ndipo kukambitsiranako kunafika mpaka usiku. Madzulo aliwonse a kuchezetsa kwanga, iye ndi ena okondwerera anabwera kuti mafunso awo ayankhidwe. Ndinamuitanira ku msonkhano wadera mlungu wotsatira, ndipo anapezekapo atatsagana ndi mbale amene anachitira umboni kwa iye nthaŵi yoyamba. Mwamunayu anapitiriza ndi phunziro lake la Baibulo, waleka Tchalitchi cha Pentekosite, ndipo tsopano ali wofalitsa wokhazikika wa mbiri yabwino.”
Nzowonadi, chiri chifuniro cha Mulungu kuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira chowonadi.”—1 Timoteo 2:4.