Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 5/15 tsamba 27-29
  • Kumbukirani Mlengi Wanu Wamkulu Muunyamata Wanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kumbukirani Mlengi Wanu Wamkulu Muunyamata Wanu
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Talikiranani ndi Zokopa Zadziko
  • Kupereka Malangizo Achindunji
  • Khalani ndi Chifuno m’Moyo
  • Achinyamata, Kodi Mukukonzekera Tsogolo?
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Kodi Mwana “Wosakaza” Mungamuthandize Bwanji?
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Achichepere—Kodi Mukulondola Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 5/15 tsamba 27-29

Kumbukirani Mlengi Wanu Wamkulu Muunyamata Wanu

“WACHICHICHEPERE Wosakhutiritsidwa: Mfundo Yotsimikizirika ya m’Mitundu Yonse.” Unatero mutu wina m’nkhani ya mu The Star ya ku Johannesburg, South Africa. Mawu olongosola nkhaniyo adalembedwa motere: “Pokhala ndi chiŵerengero chachikulu cha achichepere omwe tsopano akukhala ndi mwaŵi wokhala ndi polekezera umene ukuchepetsedwa ngakhale mosalekeza ndi kutsika kwa zachuma padziko lonse, kusakhutiritsidwa kwa achichepere m’mizinda yodzala anthu kwakhala chochitika chofala m’maiko amitundu yonse. M’chiukiro cha ku Miami, m’San Salvador, Managua, m’Teheran ndi m’Cape Town munali chinthu chimodzi chofanana​—m’chochitika chirichonse woyamba kupha ndi kuphedwa anali wachichepere.”

Imeneyo inafalitsidwa zaka zokwanira khumi zapitazo, ndipo mikhalidwe yaipiraipo kwambiri chiyambire nthaŵiyo. Kodi nchifukwa ninji pali kusakhutiritsidwa kotero pakati pa achichepere padziko lonse? Kukulakula kwa kusakhazikika kwa dongosolo iri lazinthu ndiko kumene kulidi nakatande. Ulova wafikira pa chiŵerengero chachikulu. Ndipo pokhala pali kunyonyosoka kofulumira kwambiri kwa moyo wa banja, kodi ndichisungiko chotani chimene achichepere ali nacho? Mposadabwitsa kuti ena a iwo amabwezera pamene asowa chochita. Kodi ichi sichifukwa chakuti alibe chiyembekezo chotsimikizirika pa chimene angasumike miyoyo yawo?

Munthu angayembekezere zipembedzo zadziko kupereka chiyembekezo choterocho. Komabe, wachichepere wina analemba kuti: “Ndiri wosokonezeka maganizo kwenikweni. . . . ndiri nawo mabwenzi ambiri, a zipembedzo zambiri zosiyanasiyana, ndipo ngofananadi ndi ine. Ndiridi wosokonezeka maganizo kotero kuti sindidziŵa chomwe ndingakhulupirire. Chonde, kodi mungandipatse uphungu?” Kodi ndi uphungu wotani umene mungapatse wachichepere wotereyu?

Achichepere omwe amamamatira mwathithithi ku Mawu a Mulungu ndi mpingo wowona Wachikristu samaphatikizidwa m’kusokonezeka maganizo ndi kuŵaŵidwa mtima koteroko. Pamene kuli kwakuti achichepere ambiri alibe chiyembekezo chotsimikizirika cha mtsogolo, achichepere Achikristu amakhulupirira Yehova Mulungu ndi Mawu ake otsimikizirika achowonadi. Motero, iwo ali ndi chiyembekezo cha kupulumuka mapeto a dongosolo iri lazinthu ndi kuyembekezera moyo wosatha. Pambuyo pake, padziko lapansi lopanda chisalungamo ndi kuipa, iwo adzapanga mbali ya maziko a “dziko latsopano” mmene “mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:13; Yohane 17:3) Kuti ziyembekezo zaulemerero zoterozo zikwaniritsidwe, achicheperewo akulangizidwa ‘kukumbukira Mlengi wawo Wamkulu.’ (Mlaliki 12:1) Ndipo uphungu wabwino koposa umene ungaperekedwe ngwakuti iwo akhale mbali yaikulu ya mpingo Wachikristu osasiya. Kodi nchifukwa ninji ziri motero?

Ambiri a achicheperenu amene muli mumpingo Wachikristu muli ndi makolo okhulupirira omwe amakukondani ndi kukusamalirani. Mpingo uliwonse uli ndi akulu ake oikidwa, omwe ali okondwerera kwambiri mumkhalidwe wanu wauzimu. Thandizo loterolo ndi chisamaliro siziyenera kunyalanyazidwa. Chowonadi chochokera m’Mawu a Mulungu, limodzi ndi chitsogozo cha teokratiki, zidzakupatsani chisungiko, ufulu kukugwiritsidwa mwala, ndi chiyembekezo chotsimikizirika cha mtsogolo. Zonsezi zidzakuthandizani ‘kukhala ndi chikhulupiriro ndi chikumbumtima chabwino’ ndi kumamatira ku chiyembekezo chomwe chiri chofanana ndi nangula wotetezera ngalaŵa kuti isaswedwe ndi namondwe wanyanja yoŵinduka.​—1 Timoteo 1:18, 19; yerekezerani ndi Ahebri 6:19.

Talikiranani ndi Zokopa Zadziko

Mosasamala kanthu ndi kuchuluka kwa madalitso auzimu amene achicheperenu mungasangalale nawo mumpingo Wachikristu, chikhoterero cha ena ndicho kulondola njira zadziko. Kuli ngati kuti amaganiza kuti akuphonya kanthu kena ka mtengo wapatali kamene kangapezedwe kokha kudziko lokhala kunja kwa mpingo Wachikristu. Koma kodi dziko liridi ndi chirichonse cha mtengo wapatali chimene lingapereke?

Atathera zaka zoposa 40 muuminisitala wa nthaŵi zonse, mmodzi wa atumiki a Mulungu ananena nkhaniyo mwanjira iyi: “Mbali yokha ya moyo wanga imene ndimamvera chisoni ndiyo mbali imene ndinali ndi moyo ndisanaloŵe m’chowonadi. Panthaŵiyo ndinali mbali yadziko. Ndinakhalira moyo kokha dziko. Pamene ndinafika pamsinkhu wa zaka 18 ndikuyang’ana mmbuyo m’moyo wanga, ndinazindikira kuti unali wachabechabe. Munalibe cholinga, munalibe chifuno, m’moyo wanga. Zokondweretsa zadziko zomwe ndinaganiza kuti ndinasangalala nazo kwambiri zinadzetsadi kugwiritsidwa mwala ndi chisoni zokha. Ndinayamba kufunafuna chowonadi. Ndinachipeza ndipo chaka chimodzi pambuyo pake ndinayamba utumiki wa nthaŵi zonse. Ndinalibe ndalama, ndinali n’chaka chimodzi chokha cha kudziŵa chowonadi ndi chikhulupiriro chakuti Yehova akandichilikiza. Tsopano pamene ndikuyang’ana mmbuyo m’moyo wanga, mbali ziŵiri mwa zitatu zomwe ndathera muutumiki wa nthaŵi zonse, ndiridi wachimwemwe koposa. Sindidzafuna konse kusinthanitsa zimene ndapeza m’kutumikira Yehova ndi chirichonse chimene dziko lingapereke.” Ndithudi, izi zimabwereza malingaliro a zikwi zambiri za Mboni za Yehova.

Motero kodi nchifukwa ninji mungalakalake zinthu zimene Akristu ena azisiya? Kodi nchifukwa ninji kukhumba zinthu zadziko zomwe zikupita ku chiwonongeko? (1 Yohane 2:15-17) Monga wachichepere, mwinamwake inu mukulingalira kuti kutumikira Yehova kuli ndi ziletso zambiri ndipo kudzakupangitsani kuphonya zisangalalo zomwe dziko limapereka. Koma kodi nkwanzeru kulingalira makolo anu ndi akulu kukhala oletsa kwambiri pamene akufuna kukuthandizani kukondweretsa Yehova ndi kupeza moyo wosatha?

Ngati nakubala amene akutumiza mwana wake kusitolo ya kwawoko amkumbutsa kuima kaye ndi kuyang’ana mbali zonse ziŵiri asanadutse khwalala, kodi mukanalingalira kukhala woletsa mopambanitsa? Mmalo mwake, kodi iye mwachikondi sakuyesa kutetezera mwana wake? Bwanji ngati mwanayo ananyalanyaza chenjezolo naagundidwa ndi galimoto ndi kuphedwa? Kodi mungalingalirebe kuti nakubalayo anali woletsa kwambiri? Eya, inu mungaganize kuti kukanakhala bwino nakubalayo akanawonjezera ziletso kutetezera moyo wa mwana wake! Mofananamo, zokumbutsa zochokera m’Mawu a Mulungu ndi gulu lake zimaperekedwa mwachikondi, osati monga ziletso koma kaamba ka chititetezo chathu.

Kukulira m’banja Lachikristu nkosakwanira kukupangitsani kulaka zitsenderezo zadziko iri. Inu mufunikiranso kukhutiritsidwa nokha za chowonadi cha Mawu a Mulungu. Chikhutiro chaumwini chimenechi ndi chikondi cha pa Mlengi zimapanga maziko a kupatulira moyo wanu kwa Mulungu. Kukhutiritsidwa kwaumwini kumeneku kulinso koyenerera kwa inu kuti mukhoze kutetezera chikhulupiriro chanu pamaso pa ena (1 Petro 3:15) Kutsogozedwa ndi Mawu a Mulungu ndiko maziko a moyo wachipambano. (Yoswa 1:8; Salmo 119:9) Koma kuti mukhale ndi chipambano m’moyo, inu mufunikiranso malangizo abwino.

Kupereka Malangizo Achindunji

Zowonadi, makolo Achikristunu mungakondwere kuwona ana anu akutenga kaimidwe ka nji kaamba ka chowonadi ndi kukhalabe ogwirizana nanu m’kulambira kowona. Liri kwakukulukulu thayo la atate kulera ana “m’maleredwe ndi m’chilangizo cha Yehova.” (Aefeso 6:4) Koma kodi mungawone mbali zimene mufunikira kuwongolera powalangiza? Kodi mukuthera nthaŵi yokwanira ndi ana anu ? Kodi mumachita zinthu monga banja? Ndipo kodi mumasangalalira pamodzi zosangulutsa zabwino?

Musaiŵale kuti kukhazikitsa kwanu chitsanzo chabwino kuli ndi chiyambukiro champhamvu pa ana anu. Ngati mufuna kuti iwo awone chowonadi mwamphamvu, pamenepo imeneyo ndiyo njira imene inuyo muyenera kuwonera. (3 Yohane 2-4) Ndipo ngati mukufuna kuti akulitse ulemu wakuya kaamba ka gulu la Yehova ndi akulu, pamenepo inu mwininu nthaŵi zonse muyenera kukhala ndi mkhalidwe wabwino woterowo.

Ngakhale kuti kwakukulukulu kulangiza ana ndithayo lamakolo, akulu alinso ndi thayo kulinga kwa achichepere mumpingo. Posamalira gulu la Mulungu, oyang’anira afunikiranso kuŵeta ana ankhosa. (1 Petro 5:1-3) Ha, nchitsanzo chabwino chotani nanga chimene Yehova wakhazikitsa kusamalira ngakhale achicheperewo mwachifundo! (Yesaya 40:11) Polabadira ku chitsanzo chake, abusa aang’ono Achikristu adzafunanso kusonyeza chikondwerero chachifundo, chachikondi mwa achichepere ndi kuwachititsa kulingalira kukhala mbali ya mpingo. Achichepere ena asonyeza chikhumbo chawo kuti akulu adzilankhula nawo kaŵirikaŵiri ndi kuwathandiza muuminisitala wakumunda.

Kuphunzitsa wachichepere kumatanthauza zambiri kuposa kungompatsa chidziŵitso cha mmutu cha Malemba. Kuchokera pansi pamtima wake, iye ayenera kuda zimene Mulungu amada ndi kukonda zimene Mulungu amakonda. (Amose 5:14, 15) Ngati ati akumbukire Mlengi wake muunyamata, iye afunikira kulangizidwa mwa Malemba m’kuyenda m’njira ya Yehova yachilungamo. (Miyambo 22:6; 2 Timoteo 3:16) Makolo sayenera kuleka kupereka chilango chofunikira. Makolo ena omwe amafuna kusunga unansi ndi mwana wawo pamlingo uliwonse amakhoterera pakunyalanyaza zolakwa, akumapondereza kuwopsa kwake. Iwo amayambukiridwa ndi njira yolekerera yadziko. Koma kholo lachikondi ndilo latcheru pomva malipoti akuti mwana wake wakhala asakudzisungira bwino ndipo limapereka chilango choyenerera pamene chifunika. (Miyambo 13:24) Ndithudi, kodi ndi kholo liti Lachikristu limene lingafune kusunga unansi wozikidwa panjira yolekerera komano ndikutaikiridwa ndi mwana wakeyo chifukwa chosoŵa chilango choyenerera?​—Miyambo 22:15.

Khalani ndi Chifuno m’Moyo

Yehova Mulungu anatipanga kotero kuti tipeze chimwemwe chathu chachikulu ndi chikhutiro m’kumtumikira. Tangoganizirani za munda waukulu umene achicheperenu mungasamalire. Pafupifupi theka la chiŵerengero cha anthu chadziko nchamsinkhu wa zaka 20 ndi kucheperapo. Achichepere amenewa akudzandiradzandira m’nyanja ya mtundu wa anthu. Pamene kuli kwakuti anthu alibe chiyembekezo, achichepere Achikristunu muli ndi chiyembekezo chotsimikizirika ndi chinthu chamtengo wapatali chakugaŵana nawo. Kupyolera mwa mkhalidwe wanu Wachikristu ndi changu chanu kaamba ka utumiki wa Yehova, inu mungakopere ambiri a iwo kuchowonadi. Motero mungawathandize kukhala panjira yakumoyo.

Kodi nchonulirapo chamtengo wapatali chiti chimene mungakhale nacho kuposa kupereka moyo wanu ku utumiki wa Yehova Mulungu? Kodi mwaganiza za kutenga ntchito yolalikira yopulumutsa moyo pamlingo wanthaŵi zonse? Mwinamwake mungakhale ndi phande m’kufalitsa mbiri yabwino monga mpainiya, kapena mungatumikire pa imodzi ya maofesi a nthambi a Watch Tower Society kumene mabuku olongosola Baibulo amafalitsidwa. Ngakhale ngati simungathe kutero, kodi simungapange kulambira Yehova kukhala chinthu chachikulu m’moyo wanu, motero kukumbukira Mlengi wanu Wamkulu? Inu muli ndi ntchito yoyenera yakuichita. Chotero, kufikira mapeto a dongosolo iri la zinthu, khalani wotsimikiza kukhala ndi ‘zambiri zochita m’ntchito ya Ambuye.’​—1 Akorinto 15:58

Motero pitani patsogolo achichepere Achikristunu. Kumbukirani Mlengi wanu Wamkulu tsopano, ndipo adzakupulumutsani pamene adzabweretsa mapeto a dziko losapembedza. Inde, Yehova adzakutetezerani panthaŵi imeneyo ndi kukudalitsani ndi mtsogolo mosatha, mwaulemerero.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena