Kutumikira Yehova M’nyengo Yabwino ndi m’Nyengo Yovuta
Monga yasimbidwa ndi Hal Bentley
MAKONZEDWE anapangidwa kaamba ka msonkhano wadera wa Mboni za Yehova m’mudzi waung’ono wa Nyasaland (tsopano Malaŵi). Oyang’anira adera ndi achigawo ankapanga kufufuza kwawo komalizira kwa pulatifomu yaudzu ndi nsungwi ndi misasa yaudzu yogonamo. Mwadzidzidzi, anazingidwa ndi gulu la anthu limene lidabisala m’thengo chapafupi. Gululo linayatsa misasayo ndi pulatifomu ndi kukakamiza abale aŵiriwo kupita kunyumba zimene ankakhalako.
Mkazi wa woyang’anira wachigawo, Joyce Bentley, anathamangira kudzawona zimene zinkachitika. Nayenso anabwezedwa mwankhanza. Mtsogoleri wa gululo anafuula kuti mzungu anayenera kuchoka nthaŵi yomweyo. Gululo silinatilole kutenga katundu wathu ndipo linatikankhira mu Land-Rover yanthu. Iwo anazinga galimotoyo—amuna, akazi, ndi ana—akumafuula kuti “Pitani mzungu” ndikuti “Kwacha.” Tinaganiza kuti akatigubuduzira Land-Rover, motero tinapemphera mwakachetechete kwa Yehova. Koma gululo linachepa, ndipo tinanyamuka kupita ku polisi yapafupipo, ku Mzimba, pamtunda wa makilomita 50.
Pambuyo pake tinabwerera, tiri ndi ofisala wapolisi mmodzi. Chifukwa cha mavuto m’malo ena, anali mmodzi yekhayu yemwe akatumizidwa. Pofika pamalo omwe tinazingidwa, tinapezapo mbendera ya Malaŵi Congress Party iri kupakupa pabwalo ndi zilembo zakuti M.C.P. zozokotedwa pa chipupa chomatidwa. Komabe, wapolisiyo atalankhula kwa anthu akumaloko, anatilola kulonga katundu wathu mu Land-Rover.
Tinapezanso woyang’anira wadera, Rightwell Moses, limodzinso ndi mkazi wake. Mkazi wakeyo anali anathaŵira mthengo pamene gululo linawaukira. Koma Rightwell anatsala nenene kumizidwa mumtsinje wapafupi. Gululo linafunkhanso zakudya zonse zamsonkhano. Pambuyo pake analamulira abalewo kuyendera m’njira limodzi ndipo alongo ndi ana kuloŵera njira inanso kwa makilomita angapo kufikira gululo lidatopa ndikuwasiya.
Chochitika chimenechi chinali chimodzi cha zambiri zimene zinathera m’kuletsedwa kwa ntchitoyo m’Malaŵi, kumene kunatsogolera ku chizunzo chowopsya cha Mboni za Yehova, kuphatikizapo kupha, kumenyedwa kwankhanza, kugwiriridwa chigololo kwa akazi, ndi kuponyedwa m’ndende.
Kodi Nchifukwa Ninji Tinali m’Malaŵi?
Pa June 28, 1916, ndinabadwa mu mzinda wa Leeds, mu Yorkshire, England, wachichepere m’banja la ana asanu. Sitinali banja lopembedza ndipo sitinkapita ku tchalitchi.
Pofika 1939, pamene Nkhondo Yadziko ya II inaulika, makolo anga onse anali atamwalira. Mu June 1940, pamene ndinali ndi zaka 24 zokha, ndinakhala msilikali, ndipo kwa zaka zisanu zotsatira, ndinatumikira m’magawo osiyanasiyana a ntchito za makina. M’zakazo, ndinkakhala m’malo a mfuti zamzinga pa gombe lakumpoto kwa kum’mawa kwa England ndikuyang’ana kumwamba ku thambo lodzala ndi nyenyezi, kaŵirikaŵiri ndinkakhala ndi nthaŵi yolingalira za Mulungu ndi kuzizwa chifukwa chake Mpangi wa kukongola kodabwitsa uku akalola chiwawa choterocho, kukhetsa mwazi, ndi kuvutika kwa anthu. Sizinachitike kufikira nditachotsedwa m’gulu lankhondo mpamene ndinapeza mayankho ku mafunso ambiri amene anandithetsa nzeru kwanthaŵi yaitali.
Madzulo ena m’nyengo yachisanu yozizira chaka chimenecho, winawake anagogoda pakhomo panga. Pamene ndinatsegula ndinapeza mwamuna wachikulire amene anayamba kulankhula za Baibulo. Zimenezi zinatsogolera ku phunziro Labaibulo ndipo mwamsanga ku ubatizo wanga mu April 1946. Mu 1949 ndinaleka ntchito yanga ndikukhala mtumiki wachipainiya wa Mboni za Yehova.
Kenaka ndinatumikira pa Beteli ya ku London kwa zaka zoposa zitatu, ndipo mu 1953 ndinaitanidwa kukapezeka pa kalasi ya 23 ya Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower mu South Lansing, New York, kukaphunzitsidwa monga mishonale. Pomalizira pake, ndinayamba ntchito yaumishonale m’dziko limene panthaŵiyo linali Nyasaland. Pambuyo pake ndinatumizidwa m’ntchito yachigawo. Kwa zaka zisanu ndinayenda uku ndi uku m’dziko lokongolalo monga mwamuna wachichepere wosakwatira. Ndinawakonda anthuwo, omwe anali achimwemwe kwambiri ndi ochereza ngakhale kuti ambiri anali ndi chuma chochepa chakuthupi kusiyapo minda yawo yachimanga yokha, nkhuku zoŵerengeka, ndi mbuzi kapena nkhumba. Ena anali asodzi ansomba. Ndinakhala nawo m’nyumba zodekha zomatidwa ndi dothi ndikuyenda nawo m’ntchito yolalikira ya kumudzi ndi mudzi. Ndinasangalalanso ndi kusonkhana nawo pa misonkhano yawo ya m’mipanda, mmene ankakhala ndi mabanja awo akumatchera khutu mosamalitsa kwa alankhuli, ngakhale kuti nthaŵi zina mvula inkagwa!
Nditakhala m’mudzimo, aliyense, wamkulu ndi wamng’ono, ankabwera mmodzi ndi mmodzi kudzandipatsa moni, namati: “Moni, muli bwanji?” Ngakhale pamene ndinayenda kumudzi ndi mudzi, anthu ankaleka kulima minda yawo ndi kundipatsa moni mofuula.
Mpingo uliwonse umene ndinachezera limodzi ndi woyang’anira wadera ukandimangira nyumba yanga yanga. Nthaŵi zina inkakhala yolimba yomangidwa ndi mitengo ndi denga lofoleredwa ndi udzu, chomwe ndinayamikira kwambiri. Koma ndinadzapeza kuti pamapita nthaŵi kuti denga lofoleredwa udzu chatsopano lileke kudontha!
Nthaŵi ina abalewo anandimangira nyumba ya nsenjere zokha zokha. Inali yambali zitatu, Land-Rover ikumakhala mbali yachitatu. Umu munali m’chigwa cha Mtsinje wa Shire, kumene kumakhala kotentha nyengo zonse, ndipo udzudzu umagwira ntchito m’mashifiti, kunena kwake titero, kupangitsa munthu kusapuma usana kapena usiku! Popanda ukonde waudzudzu ndi mankhwala ophera, kunali kosatheka kuchita nazo.
Mnzanga Wammoyo Agwirizana Nane
Mu 1960 ndinaphatikana ndi mkazi, Joyce Shaw, amene ankatumikira monga mishonale mu Ecuador. Inde, pambuyo posangalala ndi mphatso yaumbeta kwa zaka zingapo, ndinadalitsidwa ndi mphatso ina—ukwati—umene ndidakayamikirabe kwambiri pambuyo pa zaka 30. Joyce ndi ine tadalitsidwa ndi zokumana nazo zambiri zosangalatsa.
Pa chochitika china, akumagwiritsira ntchito mitengo ndi udzu, abale anamanga ulalo modutsa mfuleni. Ichi chinachitidwa kotero kuti ndiwolokere ku mudzi umene anafuna kuti ndikawonetseko filimu ya Sosaite yakuti “The New World Society in Action.” (Sosaite ya Dziko Latsopano Pantchito).” Koma ngolo ya Land-Rover inakodwa ku mtengo paulalopo. Molimbika, abalewo anakhumula ngoloyo, kunditheketsa kuyendetsa galimotoyo kuchoka paulalopo, kenaka anakankha ngoloyo naiwolotsera kutsidya. Tinawonetsa filimuyo bwino kwambiri.
Nthaŵi zina mitsinje inali yaikulu kwambiri mosakhoza kuikidwa ulalo. Pamenepo abalewo ankachotsa zonse mu Land-Rover—jenereta yonyamulidwa, projekitala, mafilimu, kama—ndi kuwoloka nazo mtsinje, pamene ine ndinkanyamulidwa pa mapewa amphamvu a mmodzi wa abalewo. Alongo aŵiri ankanyamula Joyce ndikumuwolotsa. Mitsinje ina inali yakuya kwambiri. Iyi tinaiwoloka ndi choombo chopangidwa ndi pulatifomu ya matabwa oyalidwa pa madalamu aakulu asanu ndi atatu kufika ku khumi. Amuna aŵiri owolotsa ankatikokera kutsidya ndi chingwe.
Abale a ku Malaŵi anali othandiza ndi achifundo kwenikweni ndipo anatichitira mwaulemu waukulu. Pamalo ena anthu akumaloko anawopsyeza kutentha nyumba imene tinkakhalamo, chotero abalewo analonda usiku wonse kutsimikizira chisungiko chathu. Ngakhale pamene chiletso chisanaikidwe pa Mboni za Yehova mu 1967, panali zochitika zowopsya, kuphatikizapo chomwe chalongosoledwa kuchiyambi kwa nkhani ino. Abale ndi alongo ambiri a ku Malaŵi akanapereka miyoyo yawo chifukwa cha ife.
Pa nthaŵi ina ndinagwira ntchito ya kunyumba ndi nyumba ndi mbale wina amene anali ndi chotupa chachikulu pamphumi pake. Iye anali atamenyedwa mowopsya masiku oŵerengeka kumbuyoko. Pa nyumba ina iye mwaulemu anapereka umboni wabwino kwa mwininyumba. Titachoka, mbaleyo anati: “Mwamuna uja ndiye amene adandipanda moipa chotere!” Ndinakumbukira mawu awa a mtumwi Paulo: ‘Musabwezere munthu ali yense choipa chosinthana ndi choipa . . . Ndi chabwino gonjetsani choipa.’—Aroma 12:17-21.
Kufutukula Utumiki Wathu
Tidakali m’Malaŵi, Joyce ndi ine tinapanga maulendo obwerezabwereza ku Mozambique yokhala pafupi. Kudziŵa kwake Chispanya, chimene anaphunzira pamene ankatumikira mu Ecuador, kunatithandiza, popeza kuti Apwitikizi ankamumva. M’kupita kwanthaŵi tonsefe tinakhoza kulankuzana m’Chipwitikizi. Tinapitirizabe kuchezera Mozambique kuchokera ku gawo lathu lotsatira, Zimbabwe. Tchalitchi Chachikatolika chinali chinatsutsa ntchito yolalikirayo mowopsya ndipo chinayambitsa mavuto. Koma m’zaka khumi zotsatira, kaŵirikaŵiri tinakhala ndi chisamaliro chachikondi cha Yehova ndi chitetezo pamene tinafufuza onga nkhosa kumeneko.
Mkati mwa kuchezera kwathu kwina ku Mozambique, ndinachezera dona wina wokondwerera kumpoto kwa doko la Beira. Mlongo wake wokhala m’Portugal anali atamulembera ndi kufotokoza zina za zinthu zodabwitsa zimene anadziŵa mwakuphunzira ndi Mboni za Yehova. Donayo anali atazifufuza m’Baibulo lake ndipo anayamba kuzisimba kwa anansi ake. Komabe, keyala yokha imene tinali nayo inali dzina la garaji kumene mwamuna wake ankagwira ntchito.
Pamene tinafika pakhomo pa garajiyo, mwamuna wina anatifunsa ngati tinafunikira thandizo. Tinapempha kuwonana ndi mwamuna wa donayo. Iye analoza kwa makanika yemwe ankakonza galimoto ndi kuchokapo mwamsanga. Tinadzidziŵikitsa kwa makanikayo ndikuti tinafuna kuchezera mkazi wake. Iye anali wamantha kwambiri. Pamene ankatiperekeza kunyumba yake, anafotokoza kuti mwamuna uja tinalankhula naye poyamba anapita kukaulula za kucheza kwathu kwa mkulu wapolisi wa P.I.D.E. (polisi yamseri). Tinaloŵa mumsampha! Iye analongosolanso kuti mkazi wake, chifukwa cha ntchito yake yolalikira, anali pansi pa chiyang’aniro cha apolisi kwa kanthaŵi ndikuti anagwira kalata yomudziŵitsa kuti tinkabwera kudzamchezera. Iwo anamlanda Baibulo lake, koma mwanzeru anabisa Baibulo lina! Iwo anabweretsanso bishopu Wachikatolika kuyesera kumukopa kuti aleke kulankhula za Yehova ndi Ufumuwo!
Pamene tinakumana ndi dona wokondwererayo, anasangalala kwenikweni nakupatira Joyce. Anachonderera kwa mwamuna wake kuti atilole kukhala nawo, koma iye anakana ndikubwerera ku ntchito. Tinachita zimene tinakhoza m’kucheza kwachiduleko, kumpatsa chilimbikitso kuchokera m’Baibulo ndikumuyamikira kaamba ka kutenga kaimidwe kolimba koteroko. Kuti tipeŵe kumdzetsera mavuto ena, tinabwerera nthaŵi yomweyo koma tinalonjeza kubwereranso nthaŵi ina mkhalidwe utawongokera. Pamene tinanyamuka panyumbapo ndipo kudzaza petulo mu tanki pa garaji, tinazindikira kuti tinkazondedwa, koma sitinagwidwe. Pamenepo tinapita ku Beira ndi kuchezera mpingo waung’ono kumeneko tisanabwerere ku Zimbabwe. Miyezi ingapo pambuyo pake tinabwerera ndipo tinakhoza kusangalala ndi chakudya ndi dona wokondwerera uja limodzi ndi mwamuna wake ndi mwana wake wamkazi. M’kupita kwanthaŵi donayo anabatizidwa pamene anakacheza ku Portugal ndipo anakhala mlaliki wa Ufumu wachangu.
Chakumpoto tinapanga maulendo obwerezabwereza ku malo onga Quelimane, Nampula, ndi Nacala, doko laling’ono. Ku Nacala kaŵirikaŵiri tinachezera banja la Soares. Bambo Soares chowonadi anachimverera choyamba mu Portugal. Koma pamene anasamukira ku Mozambique, abale mu Lourenço Marques (tsopano Maputo), likulu la Mozambique, anaphunzira naye ndi banja lake. Iwo anayamikira kwambiri kuti tinali okonzekera kuyenda makilomita mazanamazana kukachezera banja lakutalilo. Iwo anapanga kupita patsogolo kwabwino. Pambuyo pake anasamukira ku South Africa, kumene mwana wamkaziyo, Manuela, akutumikira pa Beteli monga mtembenuzi wa Chipwitikizi.
Tinachezera mpingo ku Lourenço Marques nthaŵi zambiri. Ichi chinatanthauza maulendo a makilomita oposa 1,100 kuchokera ku Blantyre mu njira zoipa. Tinali ndi mavuto aakulu agalimoto kaŵiri ndipo tinafunikira kukokedwa mpaka kukafika ku Salisbury (tsopano Harare). Chikhalirechobe, chinali chosangalatsa kwambiri kuwona gulu laling’ono mu Lourenço Marques likukula kukhala mpingo wabwino mosasamala kanthu za kugwira ntchito kwawo pansi pa chiletso. Misonkhano yadera yaing’ono inachitidwa mokhazikika. Koma inafunikira kuchitidwira mthengo monga ngati kuti abalewo anali chabe gulu lalikulu likusangalala ndi phwando. Pa zochitika zambiri msonkhano unakonzedwa kutsidya la malire ku Nelspruit mu South Africa. Ichi chinathandiza abale a ku Maputo kuyamikira gulu la Yehova ndi kukula mwauzimu.
Mpingo wa ku Beira nawonso unalimba. Chifukwa cha chipwirikiti cha ndale zadziko mu Mozambique, abale ochokera m’dzikolo tsopano ngomwazikana mu Portugal, South Africa, Canada, Brazil, United States, ndi malo ena. Chiyamikiro chonse chikunka kwa Yehova, amene ‘anakulitsa mbewuzo.’ (1 Akorinto 3:6, 7) Inde, kwa zaka khumi tinali ndi mwaŵi wakuthandiza abale mu Mozambique pansi pa ulamuliro wa Apwitikizi. Titayang’ana kumbuyo, timazizwa ndi njira imene Yehova anatitsegulira yochitira ichi.
Pa chochitika china, pamene tinkachezera Nampula chakumpoto, tinamangidwa ndi chiŵalo cha P.I.D.E. Mabuku athu onse, kuphatikizapo Mabaibulo, anafunkhidwa, ndipo tinawuzidwa kuti sitikaloledwanso kubwerera mu Mozambique. Mosasamala kanthu za chimenecho, ndi thandizo la Yehova tinakhoza kupanga maulendo ena ambiri m’dzikolo. Nthaŵi zonse pamene tinafika pamalire, tinkapempha thandizo lake ndi chitsogozo kotero kuti tikakhoze kukwaniritsa chifuniro chake ndi kupereka chilimbikitso chofunika kwenikwenicho ndi kuphunzitsa abale athu m’dziko limenelo.
Mu 1979 tinasamutsidwira ku Botswana. Ilo liri ndi malo aakulu, chifupifupi theka la South Africa. Popeza kuti malo aakulu ngachipululu, chotchedwa Kalahari, muli nzika zochepera pa miliyoni imodzi. Munomu takhala ndi mwaŵi wothandiza kumanga Nyumba Yaufumu ndi nyumba ya amishonale mu Gaborone, likulu. Mwaŵi wina wakhala wothandiza othaŵa kwawo olankhula Chipwitikizi ochokera ku Angola ndi kuphunzira nawo Baibulo.
Tinalinso okhoza kuthandiza achichepere angapo a ku Zimbabwe. Zikuwoneka ngati kuti m’dziko lopanga nalo malireli, Mboni za Yehova, mwamakonzedwe apadera, zinaloledwa kuphunzitsa Malemba m’sukulu zina. Ichi chinadzutsa chikondwerero mwa achichepere ameneŵa. Pamene anasamukira ku Botswana, tinakumana nawo, ndipo anapempha phunziro Labaibulo. Komabe, makolo awo anali otsutsa, chotero anafunikira kubwera kunyumba yaumishonale kudzaphunzira. Anapanga kupita patsogolo kwabwino nakhala Mboni zobatizidwa.
Nditayang’ana kumbuyo m’zaka 41 za utumiki wanthaŵi zonse m’maiko asanu ndi atatu, ndimayamikiradi Yehova kaamba ka madalitso ambiri amene ndasangalala nawo. Sichinakhale chosavuta, koma chakhala chosangalatsa kwa Joyce ndi ine kuthandiza ambiri kutenga kaimidwe kolimba ka Ufumu ndi kuwona kupita patsogolo kwabwino mosasamala kanthu za mavuto ambiri ndi chitsutso cholimba. Yakhaladi nkhani ya ‘kulalikira mawu, ndi kuchita nawo m’nyengo yabwino ndi m’nyengo yovuta.’ Inde, utumiki wanthaŵi zonse uli chokumana nacho cholemeretsa ndi mwaŵi waukulu umene tikuvomereza ndi mtima wonse kwa omwe angasinthe miyoyo yawo kusangalala nawo.—2 Timoteo 4:2.
[Mapu patsamba 21]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
ANGOLA
ZAMBIA
MALAWI
Mzimba
Blantyre
MOZAMBIQUE
Nacala
Beira
Maputo
ZIMBABWE
Harare
NAMIBIA
BOTSWANA
Gabarone
SOUTH AFRICA
INDIAN OCEAN
600 km
400 mi
[Chithunzi pamasamba 24, 25]
Pamene mitsinje inali yakuya kwambiri, amuna aŵiri owolotsa ankatikokera kutsidya ndi chingwe