Chisungiko Chapadziko Lonse—Motani?
TANGOLINGALIRANI kukhala padziko lapansi lopanda ngozi ndikuda nkhaŵa. Chimenecho nchimene chisungiko chapadziko lonse chimatanthauza. Kodi chiri loto lokha?
Ayi. Talingalirani masiku a Mfumu Solomo yakalekale. Ponena za kulamulira kwake kwanzeru, Baibulo limanena izi: ‘Ndipo Ayuda ndi Aisrayeli anakhala [mwachisungiko, NW], munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake, . . . masiku onse a Solomo.’—1 Mafumu 4:25.
Phunziro m’Kulamulira kwa Solomo
Malemba a Baibulo odabwitsa, monga liri pamwambalo, amanyalanyazidwa ndi osuliza kukhala kukuza mawu ndi mkamwa. Motero, munthu angafunse kuti: ‘Kodi ndingatsimikizire motani kuti kulamulira kwa Solomo sikuli nthano yokha?’ Umboni wosakhala wachindunji wofukulidwa pansi waperekedwa pambuyo pankhaniyi. Ndithudi, umboni wabwino kwambiri wa kulamulira kwenikweni kwa Solomo ngwakuti iko kwasimbidwa m’Mawu osalakwika a Mulungu wamoyo, Yehova.—Yohane 17:17; 1 Petro 1:24, 25.
Chinsinsi cha chisungiko chosangalalidwa pansi pa kulamulira kwa Solomo nchozikidwa pakugwiritsira ntchito malamulo olungama a Yehova. Aisrayeli asanaloŵe m’Dziko Lolonjezedwa, Mulungu adanena kuti: ‘Mukamayenda m’malemba anga, ndi kusunga malamulo anga, minda idzabala zipatso zake. Ndipo mudzakhala m’dziko mwanu [mwachisungiko]. Ndipo ndidzapatsa mtendere m’dzikomo, ndipo mudzagona pansi, popanda wina wakukuopsyani.’—Levitiko 26:3-6.
Mwachisoni, pambuyo pa imfa ya Solomo Aisrayeli analeka kumvera Yehova; iwo anatembenukira ku kulambira mafano ndi kulambira kugonana konyansa. Monga chotulukapo, iwo anataikiridwa chisungiko chawo, ndipo dzikolo linaloŵereredwa ndi Farao Sisaki wa ku Igupto. (1 Mafumu 14:21-26) ‘Inu mwandisiya Ine, chifukwa chake Inenso ndasiya inu m’dzanja la Sisaki,’ analongosola tero Yehova ku msonkhano wa olamulira m’Yerusalemu.—2 Mbiri 12:5.
Winawake Wamkulu Kuposa Solomo
Yesu Kristu anatsimikizira zenizeni za m’mbiri ponena za Solomo ndi ‘ulemerero wake wonse.’ (Mateyu 6:29) Koma polozera kwa iyemwini, Yesu anati: “Ndipo onani, wakuposa Solomo ali pano.” (Mateyu 12:42) Kodi anatanthauzanji? Chisungiko chosangalalidwa pansi pa kulamulira kwa Solomo chinali ndi polekezera. Mfumu yaumunthu imeneyo sikawonjola nzika zake ku matenda, uchimo, ndi imfa. Komabe, Yesu anaphunzitsa anthu ochimwa mmene angapezere moyo wangwiro m’chisungiko chosatha.—Yohane 10:10; 13:34, 35; 17:3.
Maziko opezera chisungiko chokwanira choterocho anakhazikitsidwa ndi imfa ndi chiukiriro cha Yesu. (Yohane 3:16; 1 Akorinto 15:20) Kudzanja lamanja la Mulungu m’mwamba, iye posachedwapa adzabweretsa chisungiko chapadziko lonse kwa onse ogonjera ku kulamulira kwake. Mfumu Davide wakale anauziridwa kulemba ponena za ichi m’ndakatulo ya Salmo la 72. Mawu ameneŵa anakwaniritsidwa pang’ono mkati mwa kulamulira kwa mwana wamwamuna wa Davide, nchifukwa chake pali mawu akuti, “Salmo la kwa Solomo.” Komabe, kukwaniritsidwa kwakukulu kukuphatikiza kulamulira kwa Ufumu wa Solomo Wamkulu, Yesu Kristu.
Mogwirizana ndi Salmo 72:7, 8, chisungiko chodzasangalalidwa pansi pa kulamulira kwa Kristu chidzakhala cha ponse paŵiri padziko lonse ndi chosatha. ‘Masiku ake wolungama adzakhazikika; ndi mtendere wochuluka kufikira sipadzakhala mwezi. Ndipo adzachita ufumu kuchokera kunyanja kufikira kunyanja, ndi kuchokera ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko lapansi.’—Yerekezerani ndi Zekariya 9:9, 10.
Nzika za kulamulira kwa Kristu zidzasangalalanso ndi ufulu wa kusada nkhaŵa, popeza kuti Salmo 72:16 likutitsimikizira motere: ‘M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa.’ Mwachibadwa, padzakhalanso kuwonjoledwa ku kusankhana, kutsenderezedwa, ndi chiwawa. ‘Pakuti adzapulumutsa waumphawi wopfuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzaombola moyo wao ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wa mtengo pamaso pake.’—Salmo 72:12, 14.
Monga m’nthaŵi ya Mfumu Solomo, maziko a chisungiko chapadziko lonse choterocho adzakhala kugwiritsiridwa ntchito kwanzeru kwa malamulo a chilengedwe chonse a Yehova. Uku kudzakhala kuyankha pempho la ulosi la Davide iri: “Patsani mfumu maweruzo anu, Mulungu, . . . Adzaweruza ozunzika a mwa anthu, adzapulumutsa ana aumphawi, nadzaphwanya wosautsa.”—Salmo 72:1, 4.
Kodi Bwanji Ponena za Zosoŵa Zathu za Lerolino?
‘Zimenezo nzabwino kwambiri,’ munthu wina angatero, ‘komatu ine ndikufuna chisungiko chakuthupi tsopano lino.’ Zowona, Akristu adakali owunikiridwabe ku mikhalidwe yopanda chisungiko yokantha anthu—upandu, matenda, masoka achilengedwe, ukalamba, ndi imfa. Komabe, zokumana nazo padziko lonse zasonyeza kuti, ndi chidziŵitso cha Baibulo, iwo ngokhoza kuchita nazo. (Miyambo 15:1; 22:3) Ndiponso, iwo ali ndi chikhutiritso cha chiyembekezo chotsimikizirika. Wophunzira watsopano wa Baibulo wokhala m’dera lodzala ndi upandu la Johannesburg, South Africa, analongosola njira imodzi mmene Malemba anamthandizira: “Tsopano ndimadziŵa kuti upandu ngosakhalitsa; ngwapakanthaŵi kochepa.”
Eya, palidi chiyembekezo kwa omwe anafa monga minkhole ya chiwawa chaupandu. “Ine ndine kuuka ndi moyo,” Yesu analonjeza tero, ndipo pambuyo pake anawonjezera izi: “Wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo.”—Yohane 11:25.
Kuti musangalale nkudzimva wachisungiko motero, inu mufunikira chikhulupiriro cholimba, chimene chimachokera m’kuphunzira Mawu a Yehova. Mwakuika pambali tsiku ndi tsiku nthaŵi yakuphunzira Baibulo, inu mungakumane ndi kukwaniritsidwa kwa lonjezo labwino kwambiri iri: “Wondimvera ine adzakhala [ndi chisungiko, NW], Nadzakhala phe osaopa zoipa.”—Miyambo 1:33; 2:21, 22.
[Bokosi patsamba 6]
“Pansi pa Solomo, chuma chakuthupi cha Israyeli chinapita patsogolo kwambiri m’zaka makumi atatu kuposa mmene chinachitira m’zaka mazana aŵiri za kumbuyoko. M’zinthu zakalekale za Solomo timapezamo zotsala za zizindikiro za nyumba, mizinda yaikulu yokhala ndi malinga aakulu, kuchuluka kwa nyumba zogonamo anthu zokhala ndi nyumba zomangidwa mokongola zokhalamo anthu olemera, kupita patsogolo kwakukulu m’chipambano cha zopangapanga za kuumba mbiya ndi njira zake zopangira. Timapezanso zotsala za zinthu zopangidwa ndi manja zozindikiritsa zinthu zopangidwa m’malo akutali, zizindikiro zamphamvu za kugula ndi kugulitsa malonda m’mitundu yonse.”—The House of David, lolembedwa ndi Jerry M. Landay.
[Mawu a Chithunzi patsamba 5]
NASA photo