Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 7/1 tsamba 8-9
  • Chakudya Chamadzulo cha Chikumbutso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chakudya Chamadzulo cha Chikumbutso
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Nkhani Yofanana
  • Mgonero Wachikumbutso
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Chakudya Chamadzulo Cha Ambuye
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Khristu Anaperekedwa Kenako Anamangidwa
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kuperekedwa ndi Kugwidwa
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 7/1 tsamba 8-9

Moyo ndi Uminisitala za Yesu

Chakudya Chamadzulo cha Chikumbutso

PAMBUYO pakusambitsa kwa Yesu mapazi a atumwi ake, iye agwira mawu a lemba la Salmo 41:9, ndikuti: ‘Iye wakudya mkate wanga anatsalimira pa Ine chidendene chake.’ Pamenepo, atavutitsidwa maganizo, analongosola kuti: “Mmodzi wa inu adzandipereka Ine.”

Atumwiwo ayamba kumva chisoni nayamba kunena kwa Yesu mmodzi ndi mmodzi kuti: “Ndine kodi?” Ngakhale Yudase Isikariote aphatikana nawo m’kufunsako. Yohane, amene ali pafupi ndi Yesu pagomepo, atsamira pachifuwa cha Yesu nafunsa kuti: “Ambuye, ndiye yani?”

“Mmodzi wa khumi ndi awiriwo, ndiye wakusunsa pamodzi ndi Ine m’mbale,” ayankha Yesu. “Pakuti Mwana wa munthu amukadi, monga kwalembedwa za Iye; koma tsoka munthuyo amene apereka Mwana wa munthu! Kukadakhala bwino kwa munthu ameneyo ngati sakadabadwa iye.” Pambuyo pake, Satana analowanso mwa Yudase, akumatenga mwaŵi wa chikhoterero cha mtima wake, chomwe chakhala choipa. Pambuyo pake usiku umenewo, Yesu akutcha Yudase molondola kukhala ‘mwana wa chiwonongeko.’

Pambuyo pake Yesu auza Yudase kuti: ‘Chimene uchita, chita msanga.’ Palibe ndi mmodzi yense wa atumwiwo akuzindikira chimene Yesu akutanthauza. Ena akulingalira kuti popeza kuti Yudase akusunga thumba, Yesu akumuuza kuti: “Gula zimene zitisowa paphwando,” kapena kuti akayenera kupita ndikukapatsa kanthu kwa aumphawi.

Pamene Yudase achokapo, Yesu ayamba phwando latsopano kotheratu, kapena chikumbukiro, ndi atumwi ake okhulupirika. Iye atenga mkate, nayamika, nau- nyema, ndi- kuwapatsa, ndikuti: “Te- ngani, idyani.” Iye alongosola kuti: ‘Ichi ndi thupi langa lopatsidwa chifukwa cha inu; chitani ichi chikumbukiro changa.’

Pamene aliyense wamaliza kudya mkate, Yesu atenga chikho cha vinyo, mwachiwonekere chikho chachinayi chogwiritsiridwa ntchito pa utumiki wa Paskha. Ayamikanso, nawapatsa, nawapempha kumwa, ndikuti: ‘Chikho ichi ndi pangano latsopano m’mwazi wanga wothiridwa chifukwa cha inu.’

Chotero ichi, kwenikweni, n’chikumbutso cha imfa ya Yesu. Chaka chirichonse pa Nisani 14 chiyenera kubwerezedwa, monga mmene Yesu ananenera, kumkumbukira. Chidzakumbutsa okondwererawo chimene Yesu ndi Atate wake wakumwamba achita kupereka populumukira pa anthu kuchoka ku chiweruzo cha imfa. Kwa Ayuda amene akhala atsatiri a Kristu, phwandolo lidzalowa mmalo Paskha.

Pangano latsopano, lomwe limagwira ntchito chifukwa cha mwazi wokhetsedwa wa Yesu, limalowa mmalo pangano lakale la Chilamulo. Ilo lakhalidwa nkhoswe ndi Yesu Kristu pakati pa magulu aŵiri​—ku gulu iri, kuli Yehova Mulungu, ndipo ku linalo, kuli Akristu obadwa ndi mzimu a 144,000. Kuwonjezera pa kupereka chikhululukiro cha machimo, panganolo limalola kupangidwa kwa mtundu wa kumwamba wa mafumu ndi ansembe. Mateyu 26:21-29; Marko 14:18-25; Luka 22:19-23; Yohane 13:18-30; 17:12; 1 Akorinto 5:7.

◆ Kodi ndiulosi wa Baibulo uti umene Yesu akugwira mawu ponena za ubwenzi, ndipo kodi iye akuugwiritsira ntchito motani?

◆ Kodi nchifukwa ninji atumwiwo akumva chisoni chachikulu, ndipo kodi aliyense akufunsanji?

◆ Kodi Yesu akuuza Yudase kuchitanji, koma kodi ophunzira enawo akumasulira malangizowa motani?

◆ Kodi ndi phwando lotani limene Yesu akuyambitsa pamene Yudase achokapo, ndipo kodi likutumikira chifuno chotani?

◆ Kodi ndani omwe akupanga magulu a pangano latsopano, ndipo kodi panganolo likukwaniritsanji?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena