Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 7/1 tsamba 10-13
  • Madalitso a Yehova Andilemeretsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Madalitso a Yehova Andilemeretsa
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuyang’anizana ndi Chitokoso cha Chiletso
  • Kukwaniritsa Chonulirapo Chathu
  • Kutsegula Gawo Latsopano
  • Mofanana ndi Kumadzulo Kowopsya
  • Zitokoso​—Koma Wolemerabe
  • Anapatsa Agalu Anga Mabisiketi
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Yehova Anandiphunzitsa Kuchita Chifuniro Chake
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Chifukwa Chimene Ndimasangalalira Kupanga Ophunzira
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kusumika Maso ndi Mtima Pamphoto
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 7/1 tsamba 10-13

Madalitso a Yehova Andilemeretsa

Monga momwe yasimbidwira ndi Elsie Meynberg

‘MADALITSO a Yehova alemeretsa, saonjezerapo chisoni.’ (Miyambo 10:22) Ndachiwona mwaumwini chowonadi cha mwambi wa Baibulo umenewu. Ndiloleni ndikusimbireni.

Pamene ndinali wa zaka zisanu ndi chimodzi zokha, ndinamvetsera kukambirana kwa amayi wanga ndi mphunzitsi wa Baibulo yemwe anatichezera, ndipo ndinawona mmene amayi anakhalira kakasi ndi zimene ankaphunzira. Usiku wina m’nyengo yachisanu yozizira, ndinatsikira ku chipinda cha kunsi kukamwa madzi ndipo ndinapeza Amayi akuŵerenga chapafupi ndi khomo la chitofu lotseguka. Mmalo mondizazira monga momwe ndinayembekezera, iwo anandikumbata ndikulongosola kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. Kufewa kwa liwu lawo kunandifotokozera kuti zimene anaziŵerenga zinali zofunika kwa iwo.

Pambuyo pa kukambirana kungapo ndi mphunzitsi wa Baibulo, Amayi ananyamuka pansi kunka kukagawana mbiri yabwino imene anaiphunzira ndi anansi. Komabe, iwo kaŵirikaŵiri sankalonjeredwa bwino. Tinkakhala m’dziko lapafupi ndi Beatty, Saskatchewan, Canada, ndipo ambiri a anansi athu anali achibale athu, Alutheran okangalika kapena Aevangelist. Komabe, Amayi anapitirizabe kuwachezera.

Ndinkapenyerera pa zenera yowoneka mwachizimezime pamene Amayi ankavutikira kutulutsa akavalo m’khola, podziŵa kuti sanali wozoloŵera kuwabusa. Nthaŵi zina iwo ankapita ku misonkhano kapena ku utumiki wakumunda mosasamala kanthu za madandaulo a Atate. Iwo sanavomerezane ndi chikhulupiriro chatsopano cha Amayi, koma iwo anali otsimikiza nacho. Nthaŵi zonse ankabwerera odzala ndi chimwemwe chomwe chidawonekera kwa onse. “Madalitso a Yehova alemeretsa,” iwo ankatero. Ndinkadabwa kuti kodi anatanthauzanji mwakutero. Ngakhale kuti ndinali wa zaka zisanu ndi chimodzi zokha, nanenso ndinafuna kutumikira Yehova.

Tsiku lina ndinakwera padenga ndi bambo wanga, pomwe ankakonza malata. Amayi ndi m’chemwali wanga Eileen ankapita paulendo m’gulu ndi galimoto ya Mtundu wa T Ford kukakhala ndi phande “m’kuguba ndi chidziŵitso.” Iwo ankapita kukazungulira mzindawo ndi zikwangwani zolengeza nkhani ya Baibulo.

“Iwe sudzakhala wopusa motero, kodi sitero?” Anandifunsa tero Atate. Koma ngakhale kuti ndinali mtsikana amene anakonda zokwera zinthu, ndidakhumba kwenikweni kukhala m’kugubira chidziŵitsoko kuposa kukwera pa denga. Komabe, iwo anati ndinali wamfupi kwambiri osakhoza kunyamula zikwangwanizo.

Kuyang’anizana ndi Chitokoso cha Chiletso

Pomalizira, mwaŵi wanga woyamba kukhalamo ndi phande m’kulalikira Ufumu unabwera mu November 1940. Chinali chosangalatsa chotani nanga! Popeza kuti ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova inaletsedwa mu Canada panthaŵiyo, ife tinatulukira pakati pausiku ndikusiya kabuku kakuti End of Nazism pakhomo pa nyumba iriyonse.

Pamene ndinali wa zaka zisanu ndi zinayi, ndinatsimikizira kupereka moyo wanga kwa Yehova ndi kubatizidwa. Chifukwa cha chizunzo, sitinauzidwe kokasonkhanira, koma tinatsogozedwa ku malo m’nkhalango kumene gulu lalikulu la Mboni linkasangalala ndi “phwando.” Konko m’chemwali wanga wamkulu Eleanor ndi ine tinali pakati pa ambiri omwe anabatizidwa m’madzi ozizira a nyanja yapafupipo.

Maphunziro a kusukulu m’masiku amenewo ankayambidwa ndi kuchitira sawatcha mbendera kwa kalasi ndikuimba nyimbo yaufuko. Mosasamala kanthu za kuyang’ana kotineneza kochokera kwa anzathu a m’kalasi, tidakhoza kukana mwaulemu kukhalamo ndi phande chifukwa cha chiphunzitso cha Baibulo pa kulambira mafano. (Danieli, mutu 3) Msuwani wanga Elaine Young, yemwe analinso Mboni, ankayenda mtunda wa makilomita asanu ndi limodzi kunka ku sukulu, koma tsiku lirilonse akapitikitsidwa chifukwa cha kusachitira sawatcha ku mbendera. Pambuyo pake ankabwereranso pamtunda wonsewo kunka kunyumba. Ichi anachichita kwa theka la chaka cha sukulu kotero kuti asalembedwe kuti ngophonyaphonya nkulephera mayeso.

Pamene ndinamaliza sukulu, ndinagwira ntchito m’banki. Koma chiyeso chinadza pamene anandikanira pempho langa la kukapezeka ku msonkhano wa mitundu yonse wa Mboni za Yehova mu New York mu 1950. Ndidali ndi ndalama ndipo ndinasankhapo kuleka ntchitoyo ndi kuyamba utumiki wa nthaŵi zonse. Chotero Elaine ndi ine tinasamukira ku mzinda wa Regina. “Mlekeni adzabweranso kuno kudzapemphapempha m’nyengo ya ngululu,” ananyoza tero ena. Komabe, ndinali wokhoza kudzidyetsa mwa kugwirira ena ntchito ya panyumba yaganyu. Madalitso olemerera a Yehova andisungabe ine muutumiki wake wa nthaŵi zonse chiyambire nthaŵiyo.

Kukwaniritsa Chonulirapo Chathu

Mu 1955 Elaine ndi ine tinakondwera kuitanidwa ku kalasi ya 26 ya Gileadi ndipo pambuyo pake tinagawiridwa ku Bolivia, South America. Kunali pafupipafupi Mboni 160 zokha m’dziko lonselo panthaŵiyo. Pambuyo pake, tinanka ku Tarija kukaphatikana ndi amishonale ena aŵiri m’gawo lathu loyambirira.

Tarija inali tauni yokongola. Kunali kokondweretsa kwenikweni kuwona akazi ovala mwamwambo wa kwawoko atasenza katundu pa mitu yawo. Anthuwo anali osangalatsa ndipo sanatiuzepo kuti anali osakondweretsedwa. Iwo mwachiwonekere analingalira kuti kunali ulemu kwenikweni kutiuza kuti tikabwerenso panthaŵi ina imene anadziŵa kuti sadzakhala panyumba. Kunatenga nthaŵi kuti tizoloŵerane ndi izi.

Tsiku lina tinkalankhula ndi mwamuna wina panyumba pake pamene galimoto yotchedwa jeep inadzaima ndipo munatuluka wansembe wokwiya, atakwinya nkhwidzi pamaso. “Ngati sudzaleka kulankhula ndi atsikanawa, udzachotsedwa mu tchalitchi!” anamfuulira tero mwamunayo. Atatembenukira kwa ife, anatiwopsyeza kuti: “Inu mulibe lamulo la kulalikira muno. Ngati simudzaleka, ndidzapita nazo patali.” Panthaŵiyi oyandikana nawo ambiri anali atadza kudzapenyerera. Chotero tinangopitirizabe ndi ntchito yathu, tikumagawira mabuku ndi Mabaibulo ambiri kwa openyerera modabwitsidwawo.

Pokhala titathera zaka ziŵiri m’chigwa chokongolachi kumene mapichesi, mtedza, ndi mpesa nzambiri, poyamba sitinakondwere kusinthidwa gawo kunka ku Potosí, mzinda wa migodi wozizira kwabasi wokhala pamtunda wa mamita 4,000. Tinazoloŵerana ndi kuzizira kwa nyengo yachisanu ya ku Canada, koma kusiyana kwake kunali kwakuti mu Potosí kaŵirikaŵiri nyumba zinalibe zofunditsa. Komabe, mu Potosí munali mayanjano abwino a mpingo Wachikristu, pamene mu Tarija munalibe mpingo wokhazikitsidwa.

Kutsegula Gawo Latsopano

Chotsatira, Elaine ndi ine tinagawiridwa ku Villamontes kukatsegula ntchito yolalikira kumeneko. Galimoto yomwe tinanka nayo inali yodzala ndi shuga woletsedwa, chotero kuti apewe mavuto ndi apolisi pa nyumba ya misonkho, woyendetsa galimotoyo sananyamuke kufikira usiku. Tinalakalaka chotani nanga kuti tinakanyamula tochi, popeza kuti mwadzidzidzi chinachake chinatakata pambali pathu pansi pa chilona! Anali wothandiza wa woyendetsa galimotoyo.

Panthaŵi ya 5 koloko mmawa, tinaima. Tinatuluka panja, odwala ndi utsi wa galimotoyo ndi otuwa ndi fumbi. Thanthwe linagwera m’njira ndikulitseka. Pomalizira, pambuyo pa maola anayi a ntchito ya kalavulagaga, mwiniwakeyo analamulira athandizi ake kupititsira galimotoyo pa kamsewu kopapatiza komwe kanatsegulidwa. Mwiniwakeyo sanatsegule maso pamene galimotoyo inkadutsa pang’onopang’ono limodzi la magudumu ake okhala aŵiri likuzungulira m’malele pamwamba pa dzenje lakuya kwabasi kumbali kwa msewuwo. Elaine ndi ine tinadutsa pansi. Pamene tinapitirizabe kunka ku Villamontes m’galimotoyo, makona a msewuwo m’mapiri anali opapatiza kwenikweni kwakuti woyendetsayo anakakamizidwa mobwerezabwereza kubwerera m’mbuyo ndi kukhotetsa galimoto bwino. Pomalizira pake, pambuyo pa maola 35 otopetsa, tinafika.

Kukhala tokha kunali chokumana nacho chatsopano kwa Elaine ndi ine. Chatsopanonso kwa ife tinali tizilombo ta mmalo otentha. Anankafumbwe aakulu ankatigwera pambuyo pogunda m’gulobo la m’nyumba. Zinkhamba zinkatiluma mowawa, zikumapangitsa zithupsya zamadzi zoyabwa. Usiku woyamba m’nyumba yathu yatsopanoyo, ndinatulukira panja kukagwiritsira ntchito chimbudzi chakunja. Koma pamene ndinayatsa tochi yanga, pansi ponse panadzala ndi mphemvu. Abuluzi anathawa, ndipo achule aakulu anandituzulira maso m’ngondya zanyumba. Ndinasankhapo za kuyembekezera kufikira mmawa.

Pambuyo pake, tinapita kumbali kwa mtsinje ndipo tinalingalira za kupuma pa chipinjiri chomwe tinawona kumeneko. Komabe, tinasankhapo za kupanga ulendo wobwereza chapafupipo choyamba. Pamene tinabwerera, chipinjiricho panalibe. Odutsa njira achimwemwe anatiuza kuti panali njoka yaikulu pajapo. Ndiri wokondwa kuti sitinayesere kukhala pa “chipinjiri” chimenechija!

Chomwe tinasangalala nacho kwambiri mu Villamontes chinali kuchezera anthu m’madzulo. Tinkawapeza ali khale pamipando yosalimba m’mbali mwanjira, akumamwa thobwa lotchedwa maté. Tinathera maola ambiri osangalatsa tikulongosola malonjezo Aufumu mmalo oterowo. Koma nthaŵi zovuta kwenikweni zinadza pamene Elaine anakwatiwa ndipo ndinagawiridwanso ku Vallegrande ndi mnzanga watsopano.

Mofanana ndi Kumadzulo Kowopsya

Kufika ku Vallegrande, ulendo wina wotopetsa wa masiku atatu unafunikira, ndipo panthaŵiyi ndinali ndekha. Misewu yaing’ono yafumbi inawoneka ngati inkalunjika kuchipululu nthaŵi zonse. Pomalizira ndinafika pamene dzuŵa linkalowa. Basiyo inasokoneza bata la m’tauni kumene akavalo anali ofala kwambiri kuposa magalimoto. Anthu ankayang’ana ali kunsi kwa mataya a m’mbali mwa misewu ndipo anachilikizidwa ndi mizati. Anthu ena amene anatsamira mizatiyo anavala malamba odzala ndi zipolopolo ndi makalifafala. Pafupifupi aliyense anawonedwa wovala zakuda. Ndinalingali kuti: ‘Eya kuno nkofanana ndi Kumadzulo koopsya kuja!’

Kwenikweni, kunalidi tero. Mikangano inkathetsedwa ndi mfuti. Ngakhale kuti inali tauni ya anthu zikwi khumi, mbanda ndi chiwawa zinali zofala panthaŵiyo. Nzikazo zinalamulidwa ndi gulu lomwe linalanda nyumba ya misonkho poloŵera tauniyo. Ziŵalo za gululo zinkapeza zakudya mwakuimitsa mabasi ndikubera anthu. Alimi nawonso ankaberedwa pobweretsa dzinthu zawo m’tauni. Atsikana achichepere anagwiriridwa chigololo mwa kulozeredwa mfuti pamaso pa makolo awo. Anakubala sanaloledi ana awo akazi kupita okha kungondya kukagula.

Talingalirani zimene tinaganiza pamene tsiku lina mtsogoleri wa gululo analoŵa m’Nyumba Yaufumu. Iye anali woledzera. Woyang’anira wadera, yemwe ankapereka nkhani, ananjenjema. “Ndikhulupirira!” anafuula tero mtsogoleri wa gululo pamene anamenya benchi mwamphamvu kwakuti inathyoka. Kenaka anagwira woyang’anira waderayo. Koma mwadzidzidzi anachita bata, ndipo yemwe kale anali mnzake kusukulu m’gululo anatha kumtulutsa.

Pomalizira, mkulu wa ankhondo anatokosa mtsogoleri wa gululo ndi zida. Mkuluyo anapachika galu wakufa m’bwalo lamaseŵera ndikuikapo chizindikiro chakuti: “Choka m’tauni ino, ukapanda kutero chofafanachi chidzakuchitikira.” Ngwazi ya guluyi inathawa, ndipo mkhalidwe unawongokera mu Vallegrande.

Nthaŵi zina tinayenda kwa maola 12 titakwera akavalo kukalalikira m’midzi yakutali. Mphunzitsi wa pasukulu pamudzi wina anatilandira mowolowa manja ndipo pambuyo pake anakhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Nthaŵi ina ndinabwereka bulu kunka nayo kumeneko, koma nthaŵi iriyonse pamene anadutsa panyumba ya mmodzi wa ambuye ake akale, analunjika kunka kumeneko, ndipo anafunikira kutibwezanso kunjira.

Zitokoso​—Koma Wolemerabe

Mofanana ndi amishonale ena ambiri, ine ndazindikira kuti chitokoso chachikulu sichingakhale kutentha kapena tizilombo, kuzizira kapena mtunda, kapena ngakhale matenda ndi kusauka. Mmalo mwake, kungakhale kusiyana maganizo. ‘Kodi nchifukwa ninji mavuto awa amabuka m’gulu la Yehova?’ Ndinadabwa, ndipo ndinayambadi kukaikira kuti Yehova ankandilemeretsa ndi madalitso. Pamenepo ndinakumbukira lemba lonena za madalitso a Yehova pa Miyambo 10:22. Mbali yachiŵiri ya vesilo imati, ‘Sawonjezerapo chisoni.’ Chotero sitiyenera kuika liŵongo pa Yehova kaamba ka mavutowa. Ndinadzazindikira kuti ali mbali ya zimene Adamu anatipatsira ndipo ngophatikizidwa m’zimene Paulo akufotokoza pa Aroma 8:22: ‘Cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zowawa pamodzi.’

Ndinkalemberana makalata ndi Walter Meynberg wa ku Beteli ya ku Canada, ndipo pamene ndinali patchuthi mu Canada mu 1966, tinakwatirana ndipo tinagawiridwa ku La Paz, mzinda waukulu wa Bolivia. Kwakhala dalitso lotani nanga kuwona mipingo ikuwonjezeka kuno kuchokera pa umodzi wokha pamene ndinafika mu Bolivia kufika pa 24, m’mbali iriyonse ya mzinda. Kwakhala kofanana m’mizinda ina ya dzikoli. Ndithudi, gulu la pafupifupi ofalitsa 160 omwe ankalalikira mbiri yabwino mu Bolivia pamene ndinafikako choyamba mu 1955 lakula kukhala 7,000!

Chitsanzo cha amayi wanga chotsimikizirika chimene anakhazikitsa kalekale chatulukapo kulowa mu utumiki wa nthaŵi zonse kwa ziŵalo za m’banja langa zoposa khumi. Ndiri wachimwemwe kunena kuti atate wanga anakhala Mboni yodzipereka, ndipo anthu oposa 30 omwe ndinali ndi mwaŵi wa kuphunzira nawo Baibulo abatizidwa. Kodi awa sichuma? Inde, ndikhulupirira tero. Ndithudi, ‘madalitso a Yehova ngomwe andilemeretsa ine.’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena