Achichepere Omwe Amatumikira Mulungu
KODI mumachipeza kukhala chachilendo kuti achichepere angapereke nthaŵi yawo, popanda kulipiridwa, kubwera kukhomo lanu kudzalankhula ponena za Mulungu? Kodi chimaonekera chodabwitsa, m’mbadwo wa kusakhulupirira komakulakula, kuti ana akugwirizana ndi makolo awo m’kulankhula kwa ena ponena za malonjezo odabwitsa a Baibulo a mtsogolo mwachimwemwe?a
M’mipingo 60,000 ndi yambiri yowonjezereka ya Mboni za Yehova padziko lonse lapansi, inu mudzapeza achichepere ambiri. Iwo samapita kusukulu ya Sande ya mlungu ndi mlungu kapena ku makalasi akatekisimu. M’malomwake, achicheperewa amapindula ndi kugawanamo m’misonkhano ya mpingo. Achichepere angathirire ndemanga zokhweka. Achichepere kwenikweni amagawana m’Sukulu ya Utumiki wa Teokratiki. Achichepere ambiri amathera matchuthi a kusukulu akuthandiza anansi kuphunzira ponena za Mulungu ndi malonjezo ake odabwitsa a mtsogolo.
Palibedi chatsopano ponena za ntchito ya achichepereyi. Baibulo limasimba za anyamata ndi asungwana okhulupirika, limodzinso ndi achichepere ndi ana aang’ono, omwe anakhazikitsa zitsanzo zapadera m’kutumikira Mulungu.
Bukhu la Baibulo la Masalmo linaneneratu za “khamu la anyamata,” otsitsimula ndi ochuluka ngati “mame,” mu utumiki wa Mulungu. Ilo linasimbanso za “anyamata” ndi “anamwali” akutamanda dzina la Mulungu. (Salmo 110:3, NW; 148:12, 13) Mwachidziŵikire, achichepere ena anali pakati pa omwe analipo pamene mzimu woyera wa Mulungu unatsanuliridwa pa akhulupiriri pa Pentekoste wa 33 C.E. Patsikulo pafupifupi 3,000 anakupatira Mawu ndipo anabatizidwa. Mtumwi Petro ananena kuti chochitika chochititsa nthumazichi chinali kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yoweli uwu: ‘Ana anu aamuna, ndi aakazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzaona masomphenya, ndi akulu anu adzalota maloto.’—Machitidwe 2:4-8, 16, 17, 41.
Zitsanzo zina Zabaibulo za anthu omwe anatumikira Yehova Mulungu mu uchichepere wawo zimaphatikizapo Samueli, Mfumu yolungama Davide, aneneri otchuka a m’Baibulo Yeremiya ndi Danieli, limodzi ndi Timoteo wokhulupirika. Kope lino liri ndi nkhani zitatu zochita ndi zina zazitsanzo Zabaibulozi. Inu mudzaona kuchokera m’nkhanizi chifukwa chimene achichepere, limodzi ndi anthu omwe ali achikulire, amatenga kutumikira Mulungu mosamalitsa ndi chifukwa chake amathera nthaŵi yaikulu akuthandiza anansi awo kuchita zofananazo.
[Mawu a M’munsi]
a Kufufuza kosonkhanitsidwa kwa mu 1985 kunapeza kuti anthu a ku Amereka 12 peresenti okha omwe anabadwa chiyambire 1946 anati anali ndi “chikhulupiriro chachikulu” pamsinkhu wazaka 16.