“Achimwemwe Ngamtendere”
MU 1901 Mphotho ya Mtendere ya Nobel, yoperekedwa kwanthaŵi yoyamba, inagawanidwa ndi Jean-Henri Dunant, muyambitsi wa Red Cross, ndi katswiri wachuma Frédéric Passy. Chiyambire pamenepo iyo yaperekedwa nthaŵi 69, nthaŵi 55 kwa anthu 71 osiyanasiyana, mmodzi ndi mmodzi kapena aŵiri aŵiri, ndipo nthaŵi 14 kwa magulu 16. Magulu ena aipata kuposa kamodzi, monga ngati Komiti ya International Red Cross (1917, 1944, ndi 1963) ndipo Ofesi ya United Nations High Commissioner for Refugees (1954 ndi 1981). Mwachionekere kaamba ka kusoŵeka kwa wolandira woyenerera, komiti yopereka mphotho ya Nobel inakana kuipereka kwa nthaŵi 19.
Monga mmene wina angalingalire, opata mphotho ambiri akhala akulu akulu, akazembe, kapena anthu omwe angogwirizana ndi ndale zadziko. Koma amtola nkhani, oweruza, akatswiri a mayanjano, akatswiri achuma, ndi okonzanso mayanjano ailandiranso iyo. Ngakhale asayansi, pakati pa awa Linus Pauling mu 1962 ndi Andrey Sakharov mu 1975, awa alemekezedwa, monga mmene achitira atsogoleri antchito, monga Lech Wałesa mu 1983. Ndipo mu 1970 mphothoyi inaperekedwa kwa katswiri wa zamalimidwe Norman E. Borlaug.
Munthu woyamba wachipembedzo kupatsidwa mphothoyi anali akibishopu wa ku Sweden wa Lutheran, Nathan Söderblom, wosankhidwa mu 1930. Mu 1946 munthu wamba wa Methodist ndi mlengezi, John R. Mott anagawana mphothoyo, kutsatiridwa mu 1952 ndi katswiri wa maphunziro a zaumulungu ndi wanthanthi, Albert Schweitzer ndipo mu 1958 ndi kalaliki wa ku Belgium, Dominique Georges Pire. Mu 1964 wosankhidwa anali mtsogoleri wa malamulo a kuyenera kwa anthu ndi minisitala wa Baptist, Martin Luther King, Jr.
Koma m’zaka zaposachedwapa, chipembedzo chakhala chikuchita mbali yaikulu m’kulondola mtendere kwadziko. Potsatira chikhotererochi, anthu atatu a asanu ndi anayi omalizira kupatsidwa Mphotho ya Mtendere ya Nobel akhala anthu achipembedzo: Virigo Wachikatolika Mayi Teresa wa ku Calcutta mu 1979, bishopu wa Anglican, Desmond Tutu wa ku South Africa mu 1984, ndipo chaka chatha, “mfumu ndi mulungu” Wachibuda woikidwa m’ndende wa ku Tibet, Dalai Lama.
Nzowona kuti Yesu Kristu anati: “Odala ngodzetsa mtendere.” (Mateyu 5:9, King James Version) Koma kodi kuyesayesa kwachipembedzo—kaya Akatolika, Aprotesitanti, Abuda, kapena ena ake—kutumikira monga odzetsa mtendere m’dziko kuyenera kuvekedwa ndi chipambano?
Baibulo limatisimbira kuti dziko loipa lamakonoli lotalikana ndi Mulungu silidzakumanapo ndi mtendere wosatha, chenicheni chakuti chipembedzo chimadziphatikiza m’ntchito yothandiza dziko, mayanjano, ndi machitachita a ndale zadziko sichingasinthe. Mwa kuloŵa m’malo maboma amakonowa ndi Ufumu wake wokhala pansi pa Kristu Yesu, ‘Kalonga wa Mtendere,’ Mlengi iyemwini mofulumira adzadalitsa anthu okhulupirika ndi mtendere.—Yesaya 9:6, 7; 57:21; Salmo 46:9; Danieli 2:44.
Anthu amtendere adzazindikira chowonadi ichi ndipo ogwirizanitsa miyoyo yawo mofananamo adzakhaladi achimwemwe. Monga mmene New World Translation imanenera mawu a Yesu motere: “Achimwemwe ngamtendere.”