Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kusangalala ndi Unansi Wathithithi
PAMBUYO pa chakudya cha chikumbutso, Yesu wakhala akulimbikitsa atumwi ake ndi nkhani ya mwamwaŵi yokhudza mtima. Mwinamwake pakati pa usiku papita kale. Chotero Yesu akufulumiza kuti: ‘Nyamukani, tizimuka kuchokera kuno.’ Komabe, asananyamuke, Yesu, posonkhezeredwa ndi chikondi kwa iwo, akupitiriza kulankhula, kupereka fanizo lodzutsa maganizo.
“Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye wam’munda,” iye akuyamba. Wolima Wamkulu, Yehova Mulungu, anadzala mpesa wophiphiritsira umenewu pamene anamudzoza Yesu ndi mzimu woyera pa ubatizo wake m’chilimwe cha 29 C.E. Koma Yesu akupitiriza kusonyeza kuti mpesawo ukuphiphiritsira zinanso osati iye yekha, akumalongosola kuti:
‘Nthambi iriyonse ya mwa ine yosabala chipatso, aichotsa; ndi iriyonse yakubala chipatso, aisadza, kuti ikabale chipatso chochuluka. . . . Monga nthambi siingathe kubala chipatso pa yokha, ngati siikhala mwampesa; motere mulibe inunso ngati simukhala mwa ine. Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zake.’
Pa Pentekoste, masiku 51 pambuyo pake, atumwiwo ndi ena akukhala nthambi za mpesa pamene mzimu woyera watsanuliridwa pa iwo. Potsirizira pake, anthu 144,000 akukhala nthambi zophiphiritsira za mtengo wa mpesa. Limodzi ndi tsinde la mpesawo, Yesu Kristu, iwo akupanga mpesa wophiphiritsira umene ukubala zipatso za Ufumu wa Mulungu.
Yesu akulongosola mfungulo yobalira zipatso: ‘Wakukhala mwa ine, ndi ine mwa iye, ameneyo abala chipatso chambiri; pakuti kopanda ine simungathe kuchita kanthu.’ Komabe, ngati munthu alephera kubala chipatso, Yesu akuti, “watayika kunja monga nthambi, nafota; ndipo azisonkhanitsa nazitaya kumoto, nazitentha.” Kumbali ina, Yesu akulonjeza kuti: ‘Ngati mukhala mwa ine, ndi mawu anga akhala mwa inu, pemphani chimene chirichonse muchifuna ndipo chidzachitika kwa inu.’
Yesu akupitiriza kusonyeza atumwi ake chimene chimalemekeza Atate, ndiko kuti, ‘kuti mubale chipatso chambiri; ndipo mudzakhala akuphunzira anga.’ Chipatso chimene Mulungu amafuna kuchokera ku nthambi ndicho kusonyeza kwawo mikhalidwe yonga ya Kristu, makamaka chikondi. Kuwonjezerapo, popeza kuti Kristu anali wolengeza wa Ufumu wa Mulungu, chipatso chofunidwacho chikuphatikizaponso ntchito yawo yopanga ophunzira monga mmene iye anachitira.
‘Khalani m’chikondi changa,’ akufulumiza tero Yesu tsopano. Komabe, kodi atumwi ake angatero motani? ‘Ngati musunga malamulo anga,’ iye akutero, ‘mudzakhala m’chikondi changa.’ Popitiriza kulongosola, Yesu akuti: ‘Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mnzake, monga ndakonda inu. Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.’
M’maola oŵerengeka, Yesu adzasonyeza chikondi choposachi mwakupereka moyo wake chifukwa cha atumwi ake, limodzinso ndi ena omwe adzakhala ndi chikhulupiriro mwa iye. Chitsanzo chake chiyenera kufulumiza otsatira ake kukhala ndi chikondi chodzimana chofananacho kwa wina ndi mnzake. Chikondi chimenechi chikawazindikiritsa iwo, monga momwe Yesu ananenera poyambirira kuti: ‘Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.’
Pozindikiritsa mabwenzi ake, Yesu akuti: ‘Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulirani inu. Sinditchanso inu akapolo; chifukwa kapolo sadziwa chimene mbuye wake achita; koma ndatcha inu abwenzi; chifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.’
Ndi unansi wamtengo wake wotani nanga wokhala nawo—kukhala mabwenzi athithithi a Yesu! Koma kuti apitirize kusangalala ndi unansi umenewu, atsatiri ake ayenera ‘kubala chipatso.’ Ngati iwo atero, Yesu akuti, ‘chimene chirichonse mukapempha Atate m’dzina langa a[dza]kupatsani inu.’ Ndithudi, iyi ndi mphotho yaikulu ya kubala chipatso cha Ufumu!
Pambuyo powasonkhezeranso atumwiwo ‘kukondana wina ndi mnzake,’ Yesu akulongosola kuti dziko lidzawada iwo. Komabe, iye akuwatonthoza motere: “Ngati dziko lapansi lida inu, mudziwa kuti lidada ine lisanayambe kuda inu.” Kenaka Yesu akuvumbula chifukwa chimene dziko lapansi lidera atsatiri ake, akumati: ‘Simuli a dziko lapansi, koma ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu.’
Polongosola mowonjezera chifukwa cha chidani cha dziko lapansi, Yesu akupitiriza motere: ‘Izi zonse adzakuchitirani chifukwa cha dzina langa, chifukwa sadziwa wondituma [Yehova Mulungu] ine.’ Ntchito zozizwitsa za Yesu, kwenikweni, zikuweruza anthu amene amamuda iye, monga momwe akudziŵitsira kuti: ‘Sindikadachita mwa iwo ntchito zosachita wina, sakadakhala nalo chimo; koma tsopano anaona, nada ine ndi Atate wanganso.’ Motero, monga momwe Yesu akunenera, lembo lakwaniritsidwa: ‘Anandida ine kopanda chifukwa.’
Monga momwe anachitira koyambirirako, Yesu akuwatonthozanso mwakuwalonjeza kutumiza mthandizi, mzimu woyera, umene uli mphamvu yogwira ntchito ya nyonga ya Mulungu. ‘Iyeyu adzandichitira ine umboni. Ndipo inunso muchita umboni.’ Yohane 14:31–15:27; 13:3, 35; Agalatiya 6:16; Salmo 35:19; 69:4.
▪ Kodi ndiliti ndiponso mmotani mmene Yehova anadzala mpesa wophiphiritsira, ndipo ndiliti pamene ena anakhala mbali ya mpesawo?
▪ Pomalizira pake, kodi ndi nthambi zingati zimene mpesa wophiphiritsirawo ukukhala nazo?
▪ Kodi n’chipatso chotani chimene Mulungu amafuna ku nthambizo?
▪ Kodi tingakhale motani abwenzi a Yesu?
▪ Kodi dziko lapansi limaderanji atsatiri a Yesu?