Malo Kuchokera ku Dziko Lolonjezedwa
Kodi Mudzaphunzira Kuchokera Kunyengo?
YEHOVA anati: ‘Pakukhalabe masiku a dziko lapansi, nthaŵi yakudzala ndi yakukunkha, chirimwe ndi chisanu, sizidzalekai.’ (Genesis 8:22) Motero iye anagogomezera nyengo zaulimi.
Kodi mudziŵanji ponena za nyengo ndi kugwirizana kwake ndi ulimi? Ngakhale ngati mukukhala mum’zinda kapena simumalima, muyenera kuphunzira zanyengo za Israyeli ndi ntchito zaulimi. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti pamene mudziŵa zowonjezereka ponena za zimenezi, ndipamenenso mudzamvetsetsa bwinopo Mawu a Mulungu.
Alimi amalima nthaka, kudzala mbewu, ndiyeno kukolola ndi kupuntha dzinthu zawo. Koma kuti timvetsetse bwino lomwe zimene Baibulo limanena, tiyenera kudziŵa zowonjezereka, kuphatikizapo pamene ntchitozo zinachitidwa. Mwachitsanzo tiyeni titenge kulima, monga momwe tikuwonera pamwambapo panthaka yotsetsereka imene inali Yudeya wakale.a Kodi muganiza kuti ndimwezi uti umene chithunzithunzi chimenechi chinajambulidwa? Kudziŵa nthaŵi yolima m’dziko lanu kungakusokeretseni. Nthaŵi yolima njosiyana Kumpoto Kwadziko ndi Kummwera Kwadziko; imasiyananso malinga ndi utali kuchokera panyanja ndiponso malinga ndi nthaŵi ya nyengo yadzinja.
Izi zingayambukire lingaliro lanu la zochitika za m’Baibulo. Mungaŵerenge za kusankha kwa Eliya womloŵa m’malo wake: “Tsono . . . napeza Elisa mwana wa Safati alikukoketsa chikhasu ng’ombe ziŵiriziŵiri magoli khumi ndi aŵiri.” (1 Mafumu 19:19) Kodi muganiza kuti zimenezo zinachitika m’mwezi uti, ndipo kodi nthaka iyenera kukhala inawoneka motani? Ndipo pa Yohane 4:35 Yesu anati: “Kodi simunena inu, kuti, yatsala miyezi inayi, ndipo kudza kumweta? . . . Kwezani maso anu, nimuyang’ane m’minda, kuti mwayera kale kufikira kumweta.” Ngakhale kuti iye anailongosola nthaŵiyo, kodi mukumvetsetsa kuti nliti?
Tchaticho chimapereka malongosoledwe achidule abwino koposa anyengo ndi ntchito zaulimi m’Dziko Lolonjezedwa. Chigawo chozungulira kunja chimapereka miyezi ya kalenda yopatulika Yachiyuda.b Mutaiyerekezera ndi miyezi yathu, mudzawona kuti imaloŵana, monga Nisani (kapena, Abibu) umafola mapeto a Malichi ndi kuchiyambiyambi kwa Epulo. Chigawo chotsatira kumka chamkati chimasonyeza pamene dzinthu zinacha, chimene chikukuthandizani kudziŵa pamene ntchito zina zaulimi, zonga ngati kukolola ndi kupuntha, zinachitidwa. Chigawo chapakati cha tchaticho chimakulolani kuyerekezera kusintha kwa nyengo m’kati mwa chaka.
Gwiritsirani ntchito tchaticho kuzamitsa kumvetsetsa kwanu ndi chiyamikiro cha zolembedwa m’Baibulo, zonga ngati zitsanzo ziŵiri zotchulidwazo.
Elisa ankachita ntchito yaulumi pamene anaitanidwa kukhala mneneri. Mwachiwonekere zimenezi zimasonya nthaŵiyo kukhala Tishiri (Seputembala-Okutobala), pamene kutentha kwakukulu kwachirimwe kunali kupita. Mvula ya mnyundo inali itayamba kufeŵetsa nthaka, kutheketsa kulima, kotsatiridwa ndi kudzala.
Ndipo kodi nliti pamene Yesu analankhula mawu apa Yohane 4:35? Kukolola kunali miyezi inayi mtsogolo. Wonani kuti kukolola barele kunayamba mu Nisani (Malichi-Epulo), pafupifupi nthaŵi ya Paskha. Ŵerengani miyezi inayi chafutambuyo. Mufika ku Kisilevi (Novembala-Disembala). Mvula inkawonjezereka, ndi mvula yamvumbi ndi mphepo yachisanu mtsogolo. Chotero Yesu mwachiwonekere anatanthauza kukolola kophiphiritsira pamene anati: “Kwezani maso anu, nimuyang’ane m’minda, kuti mwayera kale kufikira kumweta.”
Mafunso otsatiraŵa ngaphunziro lanu laumwini kapena ogwiritsira ntchito panyengo yabwino ya kuphunzira ndi banja lanu:
▪ Kukolola thonje m’Yeriko kunali m’mwezi wa Adara; motero, kodi ndimotani mmene tsatanetsatane wapa Yoswa 2:6 ndi 3:15 amatsimikizirira kulondola kwa Baibulo?—Yoswa 4:19; 5:11.
▪ Kupuntha kunatsatira kukololedwa kwa dzinthu, chotero kodi ndimotani mmene lonjezo la pa Levitiko 26:5 limasonyezera kukhala ndi zakudya zamwana alilenji?
▪ Kodi ndimotani mmene 2 Samueli 21:10 amaperekera lingaliro lakuti Rizipa anachita mlindiro wautali pa ana ake aamuna aŵiri, amene analoledwa kuphedwa kuti achotse liwongo lamwazi pa anthu a Mulungu?
▪ Kodi nchifukwa ninji mabingu ndi mvula zotchulidwa pa 1 Samueli 12:17 zinawonedwa kukhala kulabadira kwa Mulungu?—Miyambo 26:1.
▪ Kodi Rute anali ndi chifukwa chotani cholingalirira kuti kachitidwe ka Boazi kulinga kwa iye sikanali kakamphindi chabe?—Rute 1:22; 2:23.
Bwanji osakhala ndi tchati chimenechi pamene muŵerenga Baibulo?
KISILEVI NISANI
25 Phwando la Kukonzetsanso 14 Paskha
15-21 Mkate Wopanda Chotupitsa
16 Chopereka cha zipatso zoyamba
IYARA ADARA
14 Paskha Wamadzulo 14, 15 Purimu
SIVANI TISHIRI
6 Madyerero a Masabata 1 Kuliza Malipenga
(Pentekoste) 10 Tsiku Lachitetezero
15-21 Madyerero a Misas
22 Msonkhano Wopatulika
[Mawu a M’munsi]
a Wonaninso 1990 Kalendala ya Mboni za Yehova.
b Mwezi wowonjezereka, kapena wophatikizidwa, (Vedara) unawonjezeredwa nthaŵi zisanu ndi ziŵiri m’kati mwa kuzungulira kwa zaka 19 zirizonse.
[Chithunzi patsamba 17]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
NISANI (ABIBU)
Malichi-Epulo
Barele
IYARA (ZIVI)
Epulo-Meyi
Tirigu
SIVANI
Meyi-Juni
Nkhuyu Zosapsa
TAMUZI
Juni-Julayi
Mpesa Woyamba
ABU
Julayi-Ogasiti
Zipatso za Chirimwe
ELULI
Ogasiti-Seputembala
Kanjedza Mpesa Nkhuyu
TISHIRI (ETANIMU)
Seputembala-Okutobala
Kulima
HESHIVANI (BULI)
Okutobala-Novembala
Azitona
KISILEVI
Novembala-Disembala
Nkhosa m’Chisanu
TEBETE
Disembala-Januwale
Kukula kwa Zomera
SEGATI
Januwale-Febuluwale
Katungulume
ADARA
Febuluwale-Malichi
Malalanje
VEDARA
Malichi
[Mawu a Chithunzi patsamba 16]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Mawu a Chithunzi patsamba 17]
Garo Nalbandian
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.