Chirimikani mu Ufulu Wachikristu!
Mfundo Zazikulu Kuchokera mu Agalatiya
YEHOVA ndi Mulungu waufulu. (2 Akorinto 3:17) Mwana wake, Yesu Kristu, anati: ‘Mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.’ (Yohane 8:32) Ndipo potsanzira Kristu, mtumwi Paulo analalikira mbiri yabwino ya ufulu.—Aroma 6:18; 8:21.
Polalikira uthenga womasula umenewo, Paulo anakhazikitsa mipingo ya ku Galatiya (chigawo cha Roma mu Asia Minor) mu ulendo wake woyamba waumishonale (47-48 C.E.). Agalatiya anadziŵa za chosankha cha bungwe lolamulira chakuti mdulidwe sufunikira kwa Akristu. (Machitidwe 15:22-29) Koma ochilikiza Chiyuda ankafunafuna kuwaloŵetsa m’nsinga mwakuumirira kuti iwo adulidwe. Chotero Paulo anagogomezera ufulu Wachikristu m’kalata imene analembera Agalatiya ali ku Korinto kapena Antiokeya wa ku Syria pafupifupi 50-52 C.E. Mwachitsanzo, iye anati: ‘Kristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; chifukwa chake chirimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo.’—Agalatiya 5:1.
Paulo Achinjiriza Utumwi Wake
Poyamba Paulo anasonyeza kuti utumwi wake unali “mwa Yesu Kristu, ndi Mulungu.” (1:1–2:14) Chifukwa cha vumbulutso, Paulo (limodzi ndi Barnaba ndi Tito) ananka ku Yerusalemu ponena za funso la mdulidwe. Kumeneko, Yakobo, Kefa (Petro), ndi Yohane anazindikira kuti iye anapatsidwa mphamvu ya kukhala mtumwi kwa amitundu. Ndipo pamene Petro pambuyo pake anapatukana ndi okhulupirira Achikunja ku Antiokeya chifukwa choopa Akristu Achiyuda ochokera ku Yerusalemu, Paulo anamdzudzula.
Kodi Amayesedwa Bwanji Wolungama?
Mtumwiyo anapanganso mfundo yamphamvu kuti ndikokha mwa chikhulupiriro mwa Yesu Kristu pamene munthu angayesedwe wolungama. (2:15–3:29) Agalatiya analandira mzimu wa Mulungu, osati chifukwa cha ntchito za lamulo, koma chifukwa chovomereza mbiri yabwino m’chikhulupiriro. Ana enieni a Abrahamu ali ndi chikhulupiriro, koma anthu oyesayesa kukhala olungama mwa ‘ntchito za lamulo akhala otembereredwa.’ Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti sangathe kusunga Lamulo mwangwiro. Kwenikweni, Lamulo linawonetsera zolakwa ndipo linali ‘namkungwi wakufikitsa kwa Kristu.’
Chirimikani!
Mwa imfa yake, Kristu ‘anaombola omvera lamulo.’ Koma atsatiri ake ayenera kuchilimika m’ufulu Wachikristu. (4:1–6:18) Chotero Agalatiya anafunikira kutsutsa aliyense woyesayesa kuwasonkhezera kulandira goli la ukapolo. Kuwonjezerapo, iwo sadayenera kulakwira ufulu wawo koma kukana ‘ntchito za thupi’ ndikusonyeza zipatso za mzimu wa Mulungu. Awo ofuna kuŵaloŵetsa m’nsinga ku Lamulo anafuna “kuonekera okoma m’thupi,” kupeŵa chizunzo, ndikukhala ndi chifukwa chodzitukumulira. Komabe, Paulo anasonyeza kuti kaya kudulidwa kapena kusadulidwa sizinali kanthu. Mmalomwake, “komatu wolengedwa watsopano.” Iye anapempherera mtendere ndi chifundo kuti zikhale pa Israyeli wauzimu, aja a chilengedwe chatsopanocho.
Kalata ya Paulo kwa Agalatiya inaŵathandiza kutsutsa awo ofuna kuwaika muukapolo wauzimu. Lolani kuti itithandizenso kusonyeza zipatso za mzimu ndikuchirimika mu ufulu Wachikristu.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 23]
Mikwingwirima: ‘Palibe munthu andivute,’ analemba motero Paulo, “pakuti ndiri nayo ine m’thupi mwanga mikwingwirima ya [kapolo wa, NW] Yesu.” (Agalatayi 6:17) Pakati pa akunja akale ena, akapolo ankaikidwa mikwingwirima kuzindikiritsa eni ake. Zisonyezero zosiyanasiyana zinkatenthedwa kapena kulembedwa pathupi pawo. Mosakaikira, kuchitiridwa moipa kwakuthupi kochuluka kumene kunachitidwa pathupi la Paulo chifukwa cha utumiki Wachikristu kunasiya zipsera zina, kutsimikizira kunena kwake kwakuti anali kapolo wokhulupirika wa Kristu, wozunzidwa chifukwa cha Iye. (2 Akorinto 11:23-27) Imeneyi ingakhale “mikwingwirima” imene Paulo anasonyako, kapena angakhale ankaganiza za moyo womwe anakhala nawo monga Mkristu, kusonyeza zipatso za mzimu wa Mulungu ndikuchita uminisitala wake.
[Chithunzi]
Akapolo Achiroma anakakamizidwa kutumikira ambuye awo, koma Paulo adali kapolo wofuna yekha ndiwosangalala wa Yesu Kristu