Dzazidwani ndi Chimwemwe
‘Ndipo akuphunzira anadzazidwa ndi chimwemwe ndi mzimu woyera.’—Machitidwe 13:52.
1. (a) Kodi chimwemwe n’chipatso cha mtundu wanji? (b) Kodi Mulungu ayenera kulemekezedwa kaamba ka makonzedwe achimwemwe otani?
CHIMWEMWE! Mkhalidwe Wachikristu umenewu wandandalitsidwa mmalo achiŵiri ku chikondi chokha m’kulongosola kwa Paulo kwa zipatso za mzimu. (Agalatiya 5:22-25) Ndipo kodi nchiyani chimene chimapangitsa chimwemwe chimenecho? Ndi mbiri yabwino iyi imene mngelo wa Mulungu anailengeza kwa abusa odzichepetsa zaka zoposa 1,900 zapitazo: ‘Onani, ndikuuzani inu uthenga wabwino wa chikondwero chachikulu, chimene chidzakhala kwa anthu onse; pakuti wakubadwirani inu lero m’mudzi wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Kristu Ambuye.’ Kenaka khamu la angelo linawonekera niligwirizana ndi mngeloyo m’kutamanda Mulungu mwachimwemwe nati: “Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba. Ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao.”—Luka 2:10-14.
2, 3. (a) Kodi nchifukwa ninji kudali koyenerera kwa Mulungu kutumiza Mwana wake wachisamba kudzakhala Moomboli wa anthu? (b) Kodi Yesu anatumikira m’njira zina zotani zifuno za Mulungu pamene anali padziko lapansi?
2 Kukondwera kwa Yehova ndi anthu kwasonyezedwa m’kupereka chipulumutso kupyolera mwa Kristu Ambuye. Mwana wachisamba wa Mulungu ameneyu ndiye chisonyezero cha nzeru yeniyeni ndipo akulongosoledwa kukhala akunena za Atate wake pamene ankalenga zinthu kuti: “Pamenepo ndinali pambali pake monga wantchito wolimba ndi wotsimikiza, kenaka ndinadzazidwa ndi chisangalalo tsiku ndi tsiku, ndinasangalala pamaso pake nthaŵi iriyonse; ndinakondwera ndi zipatso za dziko lake lapansi, inde kuchuluka kwa chisangalalo changa kunali mwa ana a anthu.”—Miyambo 8:30, 31, Rotherham.
3 Chotero, chidali choyenerera kuti Yehova atumize Mwana ameneyu, yemwe adapeza chisangalalo chotero mwa ana a anthu, kuti akhale Moomboli wa anthu. Ndipo kodi ichi chikambweretsera Mulungu ulemerero motani? Chikamtsegulira njira ya kukwaniritsa chifuno chake chachikulu chakudzaza dziko lapansi ndi anthu olungama ndi okonda mtendere. (Genesis 1:28) Kuwonjezerapo, pamene anali padziko lapansi, Mwana ameneyu, Yesu, akasonyeza pansi pa chiyeso choipitsitsa kuti munthu wangwiro angamvere Yehova mokhulupirika monga Mfumu Ambuye, mwakutero kuyeretsa kotheratu kuyenera kwa kulamulira kwa Atate wake pa zolengedwa Zake. (Ahebri 4:15; 5:8, 9) Njira yosunga umphumphu ya Yesu inasiiranso Akristu onse owona chitsanzo chakutsatira mapazi ake mosamalitsa.—1 Petro 2:21.
4. Kodi kupirira kwa Yesu kunatulukapo chimwemwe chachikulu chotani, ndipo kodi chimenechi chiyenera kutilimbikitsa motani?
4 Chotero Yesu anapeza chimwemwe chopambana m’kuchita chifuniro cha Atate wake, ndikuti m’chiyembekezo cha chimwemwe chachikulu koposa, monga momwe mtumwi Paulo akusonyezera pa Ahebri 12:1, 2: ‘Tithamange mwachipiriro makaniwo anatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtengo wozunzirapo nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.’ Kodi chimwemwe chimenechi nchiyani? Ndichimwemwe chimene Yesu ali nacho, osati kokha kuyeretsa dzina la Atate wake ndikupereka dipo lowonjola anthu ku imfa komanso kulamulira monga Mfumu ndi Mkulu wa Ansembe pamene akubwezeretsa anthu omvera ku moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi.—Mateyu 6:9; 20:28; Ahebri 7:23-26.
5. Kodi ndani omwe ali “abale” a Yesu, ndipo kodi amakhalamo ndi phande m’chimwemwe chapadera chotani?
5 Inde, Mwana wa Mulungu nthaŵi zonse wakhala akupeza chimwemwe m’kutumikira anthu. Ndipo chakhala chimwemwe chake kutumikira Atate wake m’kusankha kagulu ka anthu osunga umphumphu amene iye akuŵatcha “abale” ake amene amaukitsidwira kumwamba pamene amwalira. Awa amaloŵa m’chimwemwe chapadera ndi Yesu. Iwo amanenedwa kukhala ‘odala ndi oyera mtima,’ ndipo iwo ‘adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi iye zaka chikwizo.’—Ahebri 2:11; Chibvumbulutso 14:1, 4; 20:6.
6. (a) Kodi ndi chiitano chokondweretsa chotani chimene Mfumuyo ikupereka kwa “nkhosa [zake] zina”? (b) Kodi ndimwaŵi wotani umene ambiri a nkhosa zimenezi akusangalala nawo lerolino?
6 Kuwonjezerapo, khamu lalikulu la “nkhosa zina,” amene Mfumu yolamulirayo ikuwalekanitsira kudzanja lamanja lake lachivomerezo, akuvomereza chiitano chake ichi: ‘Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi.’ (Yohane 10:16; Mateyu 25:34) Ndimwaŵi wosangalatsa chotani nanga! Pakati pa awa amene adzaloŵa mbali ya dziko lapansi ya Ufumuwo, ambiri tsopano akulandira maudindo athayo limodzi ndi odzozedwa, monga momwe Yehova ananeneratu kuti: ‘Ndipo alendo adzaimirira ndi kudyetsa magulu ako, ndi anthu akunja adzakhala olima ako, ndi kukukonzera minda yampesa. Koma inu mudzatchedwa ansembe a Yehova; anthu adzakuyesani inu atumiki a Mulungu wathu.’ Onseŵa amagwirizana ndi mneneri wa Mulungu m’kunena kuti: ‘Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwera mwa Mulungu wanga; pakuti iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso.’—Yesaya 61:5, 6, 10.
7. Kodi nchifukwa ninji “tsiku” lino chiyambire 1914 liri lapadera kwambiri?
7 Tsopano tikukhala m’tsiku lapadera kwenikweni. Chiyambire 1914 ilo lakhala tsiku la kulamulira kwa Kristu monga Mfumu yakumwamba, yolongosoledwa pa Salmo 118:24, 25 motere: “Tsiku ili ndilo adaliika Yehova; tidzasekera ndi kukondwera m’mwemo. Tikupemphani, Yehova, tipulumutseni tsopano; tikupemphani, Yehova, tipindulitseni tsopano.” Nditsiku limene lidzafikira pachimake pamene Yehova adzawononga chipembedzo Chachibabulo ndikugwirizanitsa mkwatibwi wa Kristu wa abale 144,000 ndi Mfumu yawo yakumwamba. Anthu onse a Mulungu ‘adzakondwera ndi kusekera’ ndi zimenezi. Iwo adzakondweranso pamene Mfumu yawo Yaumesiya idzamenya nkhondo pa Armagedo kupulumutsa mtundu wake wokhulupirika kuloŵa m’dziko lake latsopano lolungama. (Chibvumbulutso 19:1-7, 11-16) Kodi Yehova amapereka chipambano pamene anthu ake akulengeza chiyembekezo chokondweretsachi? Lipoti lotsatirali lidzalongosola.
Kufutukuka Kwapadziko Lonse
8. (a) Kodi chimwemwe ndi mzimu woyera zimasonyezedwa motani m’lipoti lopezeka pa masamba 18 mpaka 21 a magazini ano? (b) Kodi nziti zimene ziri zina za mfundo zazikulu za lipotilo?
8 Mboni za Yehova zamakono ‘nzochuluka m’chiyembekezo.’ (Aroma 15:13) Izi zasonyezedwa m’tchati chomwe chiri pamasamba 18 mpaka 21 a magazini ano, kumene lipoti la dziko lonse la utumiki Waufumu la 1990 lasonyezedwa mwatsatanetsatane. Ndife osangalala chotani nanga kuwona chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha aminisitala 4,017,213 okangalika m’munda! Ichi chikuzindikiritsa chiwonjezeko cha 77 peresenti m’zaka khumi zapitazo, pamene ntchito yosonkhanitsa nkhosa ikunka patsogolo m’maiko 212 padziko lonse. Pambuyo pa zaka 15, maubatizo anafikiranso chiŵerengero chapamwamba cha nthaŵi zonse—301,518! Padali maubatizo ena omwe anali ndi ziŵerengero zapamwamba kwenikweni pamisonkhano yambiri, makamaka yosonkhanidwa ndi Mboni zochokera Kummawa kwa Yuropu. Pakati pawo padali achichepere ambiri, kutsimikizira bodza la kunena kwa sosholizimu kuti chipembedzo chidzafera pamodzi ndi nkhalamba.
9. (a) Kodi kuphunzitsa koyambirira kwa makolo kukubweretsa zotulukapo zosangalatsa zotani? (b) Kodi n’zokumana nazo zakumakolo kapena zinazake zotani zimene zikusonyeza zimenezi?
9 Makamu a achichepere akuvomereza chiitano cha pa Salmo 32:11 ichi: ‘Sekerani mwa Yehova, ndipo kondwerani inu olungama mtima.’ Zikuwoneka kuti makolo ambiri akugwiritsira ntchito uphungu wa kuphunzitsa ana awo aang’ono “kuyambira ukhanda.” (2 Timoteo 3:15) Akugwiritsira ntchito bwino mabuku ndi makaseti tepi opangidwira achichepere. Pamene achichepere ameneŵa apita kusukulu, mwamsanga amayamba kupereka umboni wabwino, monga chitsanzo, msungwana wazaka zakubadwa zisanu ndi zitatu wa ku Japan anasimba kuti: “Pamapeto pa tchuthi cha m’chilimwe, ndinafikira mphunzitsi wanga ndikumfunsa kuti: ‘Kodi mudapita kukawona manda a bambo anu patchuthi chino?’ Iwo anayankha kuti: ‘Inde, bambo anga adali achifundo, ndipo ndimapita pamanda pawo chaka ndi chaka.’ Ndinati: ‘Mutaphunzira Baibulo ndikutsatira ziphunzitso za Mulungu, mudzakhala wokhoza kudzawonanso atate anu achikondi m’dziko lapansi laparadaiso.’ Kenaka ndinawapatsa Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Tsopano mphunzitsi wathu amaŵerenga mutu umodzi wa bukhuli ku kalasi yonse nthaŵi ya chakudya chamasana mlungu uliwonse.”
10. Kodi bukhu la Young People Ask latumikira chifuno chabwino chotani, ndipo nziti zomwe ziri zitsanzo zina?
10 Achichepere amene ali m’zaka zawo zauchichepere agwiritsira bwino ntchito bukhu la Questions Young People Ask—Answers That Work, ponse paŵiri paphunziro laumwini ndi pochitira umboni kwa achichepere anzawo. Makolo nawonso aliyamikira bukhuli. Mlongo wina wa ku Switzerland, analembetsa monga mpainiya wothandiza, anasankha kuchezera makolo a anzake akusukulu a mwana wake. Ichi chinapereka mpata wa kukambitsirana ndi makolo ambiri, ndipo mabuku 20 (ambiri anali a Young People Ask) ndi magazini 27 anasiidwa kwa iwo. Pamene msungwana wapasukulu m’Trinidad anagaŵira bukhu limeneli kwa mphunzitsi wake pasukulu, amake anatsatira chikondwererocho, nagaŵira makope 25 pakati pa ogwira ntchito okwanira 36. Iye anapitiriza mwezi wotsatira nasumika chisamaliro chapadera kwa makolo omwe ankawadziŵa, nagaŵira mabuku ena 92 ndikuyambitsa maphunziro Abaibulo apanyumba atsopano. Ku Korea mphunzitsi wa pasukulu ya pulaimale anagwiritsira ntchito bukhu la Young People Ask popereka maulaliki ake achidule pankhani zonga ngati “Kodi Ndingawongolere Motani Magiredi Anga?” ndi “Kodi Ndingagwirizane Motani ndi Mphunzitsi Wanga?” kenaka nagaŵira bukhulo. Ophunzirawo atalandira mabuku 39, makolo ena anayamba kudandaula. Koma mphunzitsi wamkulu pasukulupo anasanthula kopelo, nalitcha kukhala “labwino,” naoda limodzi la mwana wake.
Maphunziro Abwino Koposa
11, 12. Kodi ndimaumboni ena ati osonyeza kuti mabuku a Watch Tower Society amapereka maphunziro abwino koposa?
11 Phindu lamaphunziro a magazini athu limayamikiridwanso ndi ambiri, monga chitsanzo pali sukulu ya ku U.S. imene idaoda makope 1,200 a Galamukani! ya July 22, 1990, (August 8, 1990 m’Chicheŵa yovumbula kumwerekera ndi crack) yogwiritsira ntchito m’makalasi ake. Kuwonjezerapo, mkhalidwe wosonyeza chitsanzo chabwino wa ana a Mboni za Yehova kusukulu ukupitirizabe kupereka umboni wabwino. M’kalasi yaphokoso mu Thailand, mphunzitsi anaitanira kutsogolo Racha wa zaka zakubadwa 11 nayamikira khalidwe lake, nati: “Kodi nchifukwa ninji nonsenu simutsatira chitsanzo chake? Iye ngwakhama m’maphunziro ake ndiponso wakhalidwe labwino.” Kenaka anawonjezera nati: “Eya, ndikhulupirira kuti nonsenu mufunikira kukhala Mboni za Yehova monga Racha kuti muwongolere khalidwe lanu.”—Yerekezerani ndi Miyambo 1:8; 23:22, 23.
12 Mlongo wachichepere wa ku Dominican Republic akulemba motere: “Pamene ndidali ndi zaka zinayi zokha, ndinali pafupi kumaliza maphunziro pa sukulu yanasale yachipembedzo, kumene ndinaphunzira kuŵerenga ndi kulemba. Monga mphatso, ndinapatsa m’virigo yemwe adali mphunzitsi wanga bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi ndi uthenga uwu: ‘Ndiri woyamikira kwambiri kuti munandiphunzitsa kuŵerenga ndi kulemba. Ndikukhumba kuti nanunso mumvetsetse chikhulupiriro changa ndikufikira kukhala ndi chiyembekezo changa chakukhala ndi moyo kosatha padziko lapansili pamene lidzapangidwa kukhala paradaiso.’ Ndinathamangitsidwa pasukulupo chifukwa cha chimenechi. Zaka zisanu ndi zitatu pambuyo pake ndinakumananso ndi mphunzitsiyu. Iye anasimba mmene anakhozera kuŵerenga bukhulo mosasamala kanthu za chitsutso chachikulu kuchokera kwa wansembe. Iye anasamukira ku likulu, kumene anali wokhoza kuphunzira Baibulo ndi Mboni. Iye ankabatizidwa pa Msonkhano Wachigawo wa ‘Chinenero Choyera’ limodzi nane.” Monga kunaloseredwa, nzeru zingachokere ngakhale “m’kamwa mwa makanda”!—Mateyu 21:16; Salmo 8:1, 2.
13. Kodi achichepere ambiri akuvomereza motani ku uphungu wa Solomo, ndipo kodi chimenechi chikusonyezedwa motani m’lipoti lapadziko lonse?
13 Solomo anapereka uphungu wolimbikitsa uwu: “Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako, nuyende m’njira za mtima wako.” (Mlaliki 11:9) Nzosangalatsa lerolino kuwona ana ambiri a Mboni za Yehova akugwiritsira ntchito mawu ameneŵa, kugwiritsira unyamata wawo kukonzekera kaamba ka moyo wa utumiki wa nthaŵi zonse kwa Yehova ndikuloŵa ntchito yopambanayi pambuyo pomaliza sukulu. Mathayo aupainiya akupitirizabe kuwonjezereka mofulumira, ndi anthu okwanira 821,108 akumachitira lipoti m’chakacho. Limodzi ndi abale ndi alongo okwanira 11,092 amene anatumikira pa Beteli, chimenecho chikuimira 21 peresenti ya chiwonkhetso chonse cha ofalitsa!
14. Kodi alongo athu akuthandizira motani, ndipo akufunikira chiyamikiro chotani?
14 Nzokondweretsa kuti m’maiko ambiri, monga ngati United States, pafupifupi 75 peresenti ya ofalitsa achipainiya onse ndi alongo, akumapereka mphamvu ku mawu a Salmo 68:11 limene limati: ‘Yehova anapatsa mawu: Akazi akulalikira uthengawo ndiwo khamu lalikulu.’ Alongo athu ayenera kuyamikiridwa chifukwa chakuti akuchita mbali yaikulu ya ntchito yakumunda. Kuphunzitsa kwawo kwaluso pamaphunziro Abaibulo apanyumba kukutsogolera ambiri ku chowonadi, ndipo alongo okwatiwa amene amachilikiza mokhulupirika amuna awo okhala ndi mathayo ambiri ampingo ayeneranso kutamandidwa kwambiri.—Miyambo 31:10-12; Aefeso 5:21-25, 33.
Maphunziro Abaibulo Akunka Patsogolo
15. (a) Kodi maiko ena ondandalitsidwa pa lipoti lapadziko lonse apambana motani m’ntchito ya maphunziro Abaibulo? (b) Kodi mungasimbe zokumana nazo zotani, zosonyeza mmene maphunziro Abaibulo obala zipatso angakhalire?
15 Ntchito yophunzitsa Baibulo ikunka patsogolo, maphunziro akuchititsidwa padziko lonse pa avareji ya malo 3,624,091 mwezi uliwonse. Chowonadi cha Baibulo chingasinthe maumunthu, monga mmene lipoti lochokera kutali likusonyezera. Kuchiyambiyambi kwa January 1987, munthu wina anathamangitsidwira ku New Zealand kuchokera ku Australia pambuyo potumikira ukaidi wa miyezi 25 chifukwa cha umbava ndi chinyengo. Iye adali womwerekera ndi mankhwala ogodomalitsanso ndipo anawagulitsa kwa zaka zoposa 17. Chaka chotsatira mkazi wake anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndipo pamene chidziŵitso chake chinakula, mwamunayo anawona kusintha kodabwitsa m’khalidwe la mkaziyo. Iye anakhala mkazi ndi mayi wabwino. Ndichikakamizo cha mkazi wake, iye anapezeka pa msonkhano wadera mu June 1989. Iye tsopano anavomera phunziro Labaibulo lapanyumba, ndipo masinthidwe aakulu anayamba kuwoneka m’kawonekedwe ndi njira yake yamoyo. Ziŵalo zisanu ndi ziŵiri zonse zabanja lake zinayamba kupezeka pamisonkhano. Iye anabatizidwa mu January 1990 monga yemwe anatsatira uphungu wabwino koposa wa Paulo wa pa Aefeso 4:17-24.
16. (a) Kodi ndimotani mmene malipoti a Chikumbutso cha 1990 aliri magwero a chimwemwe? (b) Kodi ndikufulumira kotani kumene kuyenera kuwonedwa, ndipo ndikuyesayesa kotani kumene tiyenera kukupanga kuti tithandize?
16 Mbali yapadera kwambiri ya lipoti la chaka chino nchiŵerengero chozizwitsa cha opezeka pa Chikumbutso 9,950,058, chomwe chidachitidwa Lachiŵiri, April 10, 1990. Maiko oposa 70 pa maiko 212 anachitira lipoti ziŵerengero za opezekapo zomwe zinali zoposa nthaŵi zitatu chiŵerengero chawo chapamwamba cha ofalitsa! Mwachitsanzo, mosasamala kanthu za ziletso, maiko asanu ndi aŵiri aku Afirika okhala ndi chiŵerengero chapamwamba chophatikizidwa cha ofalitsa 62,712 anasimba chiŵerengero cha opezekapo pa Chikumbutso cha 204,356. Ofalitsa 1,914 a mu Liberia yokanthidwa ndi nkhondo anasangalala kukhala ndi anthu okwanira 7,811 pa Chikumbutso. Haiti, yokhala ndi chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa 6,427, inasimba 36,551. Ofalitsa 886 a m’zisumbu zomwazikana za Micronesia anali ndi 3,958. Ofalitsa 1,298 aku Sri Lanka anasimba 4,521, ndipo Zambia, yokhala ndi ofalitsa 73,729, inali ndi anthu opezeka pa Chikumbutso okwanira 326,991, chiŵerengero cha munthu mmodzi mwa anthu 25 a m’Zambia monse. Lipoti ladziko lonse likuvumbulanso kuti padakali anthu owona mtima mamiliyoni ambiri amene akudikirira kuti asonkhanitsidwire m’khola lankhosa. Komatu kuwona mtima kokha nkosakwanira. Kodi tingawonjezere ndi kuwongolera mtundu wa ntchito yathu ya maphunziro Abaibulo apanyumba, kuthandiza opezeka pa Chikumbutso ambiri kumangirira chikhulupiriro champhamvu? Tikuŵafuna iwo kukhala mabwenzi athu okangalika, omatamanda Yehova. Ichi chimatanthauza miyoyo yawo yeniyeniyo!—Salmo 148:12, 13; Yohane 17:3; 1 Yohane 2:15-17.
Kuchuluka kwa Chimwemwe
17. Kodi ndizitsanzo za m’zaka za zana loyamba ziti zimene ziyenera kuthandiza kulimbikitsa kutsimikiza mtima kwathu kumamatira ku chimwemwe chathu?
17 Mosasamala kanthu za ziyeso zimene timakumana nazo, tiyeni titsimikize mtima kusungirirabe chimwemwe chathu. Mwinamwake sitidzafunikira kupyola chokumana nacho chovuta kwambiri chonga cha Stefano, komabe chitsanzo chake chingatilimbikitse. Akunenezedwa mlandu, iye anali wokhoza kusungabe kawonekedwe kake kachimwemwe. Adani ake ‘anawona nkhope yake ngati nkhope ya mngelo.’ Mulungu anali pambali pake m’nsautsoyi. Iye anachitira umboni molimba mtima, pokhala ‘wodzala ndi mzimu woyera’ kufikira imfa yake yofera chikhulupiriro. Pamene Paulo ndi Barnaba anatembenukira kwa amitundu m’kulalikira kwawo, awanso ‘anakondwera nalemekeza Yehova.’ Chizunzo chinabukanso. Koma sichinafooketse akhulupiriri ameneŵa. ‘Akuphunzira anadzazidwa ndi chimwemwe ndi mzimu woyera.’ (Machitidwe 6:15; 7:55; 13:48-52) Mosasamala kanthu za zimene adani athu angatichitire, mosasamala kanthu za ziyeso zathu zatsiku ndi tsiku m’moyo, sitiyenera konse kulola chimwemwe chathu cha mzimu woyera kuzilalitsidwa. Paulo akupereka uphungu uwu: ‘Kondwerani m’chiyembekezo, pirirani m’masautso; limbikani chilimbikire m’kupemphera.’—Aroma 12:12.
18. (a) Kodi Yerusalemu Watsopano nchiyani, ndipo nchifukwa ninji anthu a Mulungu ayenera kukondwera naye? (b) Kodi “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano” zidzawadalitsa motani anthu?
18 Ha, chiyembekezo chimenecho nchodabwitsa chotani nanga! Kwa anthu ake onse, Yehova akulengeza kuti: ‘Pakuti taonani, ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kuloŵa mumtima. Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthaŵi zonse ndi ichi ndichilenga.’ Kristu Ambuye limodzi ndi “Yerusalemu Watsopano” (yemwe tsopano ndi likulu la gulu lakumwamba la Mulungu, “Yerusalemu wa kumwamba”) ndi chitanganya cha dziko latsopano padziko lapansi adzabweretsa chimwemwe chachikulu kwa anthu. (Agalatiya 4:26) Kuukitsidwa kwa anthu akufa, kubwezeretsedwa kwa anthu onse omvera ku moyo wosatha wangwiro, moyo wosatha wothandiza, wosangalatsa padziko lapansi la paradaiso—ha, ndichiyembekezo chozizwitsa ndi chochititsa kukondwerera chotani nanga! Monga mmene Yehova iyemwini akupezera ‘chisangalalo mwa Yerusalemu ndi kukondwera mwa anthu ake,’ motero mneneri wake akupereka chiitano chowonjezereka ichi kwa anthu a Mulungu: ‘Sangalalani inu pamodzi ndi Yerusalemu, ndipo kondwani chifukwa cha iye, inu nonse amene mumkonda; sangalalani kokondwa pamodzi ndi iye.’ (Yesaya 65:17-19; 66:10; Chibvumbulutso 14:1; 20:12, 13; 21:2-4) Lolani kuti nthaŵi zonse tikhale odzazidwa ndi chimwemwe ndi mzimu woyera pamene tikulabadira chenjezo la mtumwi Paulo ili: ‘Kondwerani mwa Ambuye nthaŵi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.’—Afilipi 4:4.
Kufotokoza Mwachidule Chimwemwe Chathu:
◻ Kodi Yesu anatisiyira chitsanzo cha kupirira kwachimwemwe kotani?
◻ Kodi magulu aŵiri odzipereka ali ndi zifukwa zotani zokhalira achimwemwe?
◻ Kodi ndimotani mmene achichepere ndi achikulire akukondwerera m’chowonadi lerolino?
◻ Pobwereramo m’lipoti la 1990, kodi ndiyankho lotani lomwe likuperekedwa tsopano ku pemphero lakuti, “Yehova, tipindulitseni tsopano”?
◻ Kodi ndiliti ndipo ndimotani mmene chimwemwe chokwanira chidzafikiridwira?
[Tchati pamasamba 18-21]
LIPOTI LAUTUMIKI LA CHAKA CHA 1990 LA MBONI ZA YEHOVA DZIKO LONSE
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
[Chithunzi patsamba 16]
Mngelo wa Yehova analengeza kubadwa kwa Kristu, Ambuye kukhala ‘uthenga wabwino wa chikondwerero chachikulu’