Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 1/15 tsamba 5-6
  • Mmene Mzimu wa Mulungu Ungakuyambukirireni

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Mzimu wa Mulungu Ungakuyambukirireni
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mzimu Woyera ndi Ntchito Yolalikira
  • Ubatizo ndi Mzimu Woyera
  • Mzimu Woyera m’Moyo Wanu
  • Mzimu wa Mulungu ndi Inu
  • ‘M’Dzina la Mzimu Woyera’
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Muziyenda mwa Mzimu Kuti Mukwaniritse Kudzipereka Kwanu
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kuuzindikira Mzimu Woyera
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Mzimu wa Mulungu Unkatsogolera Akhristu Oyambirira Ndipo Ukutsogoleranso Akhristu Masiku Ano
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 1/15 tsamba 5-6

Mmene Mzimu wa Mulungu Ungakuyambukirireni

“PACHIYAMBI Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Dziko lapansi linali losaumbidwa ndi lopanda kanthu, ndipo mdima unali pamwamba pa madzi akuya; ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madzi.” (Genesis 1:1, 2, Revised Standard Version) Ndemanga Yamalemba imeneyi ikugogomezera njira yapadera imene aliyense amene ali ndi moyo wapindulira ndi mzimu woyera. Mzimu umenewo udali wokangalika ndi ntchito pachilengedwe, ndipo tikuthokoza ntchito yake, popeza kuti dziko lapansi linakhala mudzi wosangalatsa wa anthu.

Koma anthu angapindule zinthu zambiri kuchokera ku mzimu woyera. Mwambi wouziridwa umati: ‘Tembenukani pamene ndikudzudzulani; tawonani, nditsanulira pa inu mzimu wanga, ndikudziŵitsani mawu anga.’ (Miyambo 1:23) M’tsiku lathu ‘mawu’ osonkhanitsidwa a Mulungu akupezeka m’Baibulo Lopatulika, lolembedwa ndi anthu amene ‘anagwidwa ndi mzimu woyera.’ (2 Petro 1:21; Marko 12:36; 2 Timoteo 3:16) Pamene munthu wofatsa aŵerenga Baibulo, iye amapindula ndi mzimu woyera.

Mzimu Woyera ndi Ntchito Yolalikira

Pamene mmodzi wa Mboni za Yehova afika panyumba panu kudzalankhula nanu ponena za mbiri yabwino ya Ufumu, mzimu woyera ungayambukire moyo wanu m’njira ina. Kodi tikudziŵa bwanji? Eya, pamene Yesu Kristu anayamba kulalikira mbiri yabwino, iye anagwiritsira mawu a mneneri Yesaya kwa iye mwini, nati: ‘Mzimu wa Yehova uli pa ine, chifukwa chake Yehova anandidzoza ine ndiuze anthu osauka uthenga wabwino; . . . kulalikira chaka chosankhika cha Yehova.’ (Luka 4:18, 19; Yesaya 61:1, 2) Inde, Yesu anadzozedwa ndi mzimu woyera kuti alalikire mbiri yabwino.

Kuwonjezerapo, Yesu ananeneratu kuti kulalikidwa kwa mbiri yabwino kukapitiriza pambuyo pa imfa yake. Iye analosera kuti: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14, NW) Nthaŵi yochepa Yesu asanakwere kumwamba, iye anapatsa atsatiri ake ntchito iyi: ‘Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.’ (Mateyu 28:19, 20) Chotero, pambuyo pa kukwera kumwamba kwa Kristu, ophunzira ake anapitirizabe ntchito yovomerezedwa ndi mzimu yolalikira ndi kuphunzitsa. Mboni za Yehova lerolino zimatsanzira ophunzira oyambirira amenewo m’kulalikira mbiri yabwino padziko lonse.

Ubatizo ndi Mzimu Woyera

Yesu ananena kuti pamene munthu avomereza mwachiyanjo mbiri yabwino, ayenera kubatizidwa ‘m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera.’ Chotero ophunzira atsopano amayambukiridwa mowonjezereka ndi mzimu woyera. Mawu akuti “m’dzina la” kwenikweni amatanthauza “ndi ulamuliro wa” kapena “kuzindikira malo a.”a Chotero, kubatizidwa m’dzina la Atate kumatanthauza kuvomereza mosakaikira uchifumu wa Mulungu m’miyoyo yathu. Ubatizo wochitidwa m’dzina la Mwana umatanthauza kuvomereza Yesu monga Moomboli, Wopereka Chitsanzo, ndi Mfumu. Ndipo ubatizo wochitidwa m’dzina la mzimu woyera umaloŵetsamo kudalira pa mzimu ndi kugonjera ku mphamvu yake.b

Mzimu Woyera m’Moyo Wanu

Momvetsa chisoni, kusawona mtima, chisembwere, chiwawa, ndi kusayeruzika kofala kumene timakuwona m’maiko “Achikristu” kumasonyeza mfundo yakuti anthu ambiri odzinenera kukhala Akristu kwenikweni amaukana mzimu woyera. Koma awo amene amaugonjera amadalitsidwa kwakukulu. Choyamba, amatenga mosamalitsa zimene amaŵerenga m’Baibulo louziridwa ndi mzimu ndikuzigwiritsira ntchito m’miyoyo yawo. Motero, iwo ali ndi nzeru, chidziŵitso, chiweruzo, kuchenjera, kudziŵa, ndi kulingalira. (Miyambo 1:1-4) Imeneyi ndi mikhalidwe yabwino koposa m’nthaŵi zathu zovutazi.

Mzimu woyera umathandizanso anthu oterowo kulaka mavuto aakulu. M’nthaŵi zakale, Mulungu anasonyeza anthu ake mmene akakhozera kukwaniritsa ntchito yovuta kwambiri. Yehova anati ikachitidwa ‘ndi khamu la nkhondo ayi, ndi mphamvu ayi, koma ndi mzimu [wake].’ (Zekariya 4:6) Ngati tigonjera kwa Mulungu ndi mzimu wake, tidzathandizidwanso kukwaniritsa ntchito ndi kulaka zopinga zimene zingawoneke kukhala zazikulu kwa ife.​—Mateyu 6:33; Afilipi 4:13.

Kuwonjezerapo, mzimu wa Mulungu umatithandiza kusangalala ndi ufulu wosadziŵika ku dziko lonse. Mtumwi Paulo analemba kuti: ‘Pamene pali mzimu wa Yehova pali ufulu.’ (2 Akorinto 3:17) Anthu amene amagonjera ku mzimu wa Mulungu amasangalala ndi ufulu ku chipembedzo chonyenga, malaulo, kuwopa za mtsogolo, ndi zinthu zina zambiri zoika muukapolo. Mzimu wa Mulungu ulidi mphamvu yopangitsa zabwino! Iwo ungakhoze kusintha anthu. Baibulo limakhudza pa chimenechi pamene limati: ‘Chipatso cha mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.’ (Agalatiya 5:22, 23) Ha, dzikoli likadakhala losiyana chotani nanga ngati anthu onse akadagonjera ku chisonkhezero cha mzimu wa Mulungu!

Monga gulu, Akristu owona amasangalalanso ndi ‘umodzi wa mzimu mwa chimangiriro cha mtendere.’ (Aefeso 4:3) Umodzi ndi mtendere ndi zinthu zosawonekawoneka masiku ano. Koma izo zimakhalapo pamene mzimu wa Mulungu uli wokangalika. Ndithudi, pakati pa Mboni za Yehova umodzi wachimangiriro cha mzimu woyera wabweretsa anthu a mafuko onse, zinenero, ndi mitundu mu ‘ubale’ weniweni.​—1 Petro 2:17.

Mzimu wa Mulungu ndi Inu

Kodi mukuliwona phindu lokhala ndi nzeru yopatsidwa ndi Mulungu ndi kusangalala ndi ufulu weniweni? Kodi sizingakhale zosangalatsa kukhala ndi thandizo laumulungu m’kuthetsa mavuto ndi kukulitsa chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, ndi chiletso? Pamenepo gonjerani ku mphamvu ya mzimu woyera wa Mulungu. Koma kodi ndimotani mmene munthu angachitire chimenechi?

Lolani Mawu a Mulungu, Baibulo, asonkhezere maganizo ndi mtima wanu. Yanjanani ndi anthu amene amalola mzimu woyera kusonkhezera miyoyo yawo. Tengani masitepe tsopano akuphunzira ndi kuchita chifuniro chaumulungu. Kenaka, ‘Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m’kukhulupira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya mzimu woyera.’​—Aroma 15:13.

[Mawu a M’munsi]

a Yerekezerani ndi mawu Achingelezi akuti “m’dzina la lamulo.” Onaninso Mateyu 10:41 mu King James Version, kumene Yesu anagwiritsira ntchito mawu akuti “m’dzina la mneneri” ndi “m’dzina la munthu wolungama.”

b Onani nkhani imene Petro anaipereka kwa Ayuda pa Pentekoste wa 33 C.E., pamene analongosola mbali zambiri za ntchito ya Yesu ndi mzimu woyera m’miyoyo ya akhulupiriri obatizidwa. Pambuyo pa nkhani yake, anthu 3,000 anabatizidwa m’dzina la Atate, la Mwana, ndi la mzimu woyera.​—Machitidwe 2:14-42.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena