Chikondi cha pa Abale Nchokangaza
Mfundo Zazikulu Zochokera m’Filemoni
YESU KRISTU anapatsa atsatiri ake “lamulo latsopano” kuti akondane wina ndi mnzake monga momwe anaŵakondera. (Yohane 13:34, 35) Chifukwa cha chikondicho, iwo akaferana wina ndi mnzake. Inde, chikondi cha paabale nchamphamvu kwambiri ndipo nchokangaza.
Mtumwi Paulo anali wotsimikiza kuti chikondi cha paabale chikasonkhezera Filemoni, Mkristu wogwirizana ndi mpingo wa ku Kolose, mzinda wa m’Asia Minor. Chikondi chidafulumiza kale Filemoni kutsegula nyumba yake kuti igwiritsiridwe ntchito monga malo osonkhanira Akristu. Kapolo wa Filemoni, Onesimo adathaŵa, mwachiwonekere ataba ndalama zoti alipirire ulendo wonka ku Roma, kumene pambuyo pake anakumana ndi Paulo ndi kuvomereza Chikristu.
Adakali m’ndende m’Roma pafupifupi 60-61 C.E., Paulo analemba kalata yonka kwa Filemoni. Iyo inachonderera Filemoni kulandira Onesimo wobwererayo ndi mzimu wa chikondi cha paabale. Taŵerengani kalatayi, ndipo mudzawona kuti njachitsanzo chabwino chosonyeza chikondi ndi luso—zimene anthu a Yehova angachite bwino kuzitsanzira.
Chiyamikiro Kaamba ka Chikondi ndi Chikhulupiriro
M’mawu olembedwera kwa Filemoni ndi ena, choyamba Paulo anapereka chiyamikiro. (Mavesi 1-7) Mtumwiyo adamva kusimbidwa kwa chikondi chomwe Filemoni anali nacho kwa Kristu ndi kwa oyera onse ndi za chikhulupiriro chake. Ichi chinasonkhezera Paulo kuyamika Yehova ndipo chinamsangalatsa ndi kumtonthoza kwambiri. Kodi ife mwaumwini timayamikira akhulupiriri anzathu omwe akhazikitsa chitsanzo chabwino chachikhulupiriro ndi chikondi? Tiyeneradi kutero.
Kuchenjeza kozikidwa pa chikondi nkofunikira nthaŵi zonse pochita ndi Akristu anzathu, monga momwe akusonyezera mawu a Paulo. (Mavesi 8-14) Pambuyo pakufikira kwake kwaluso, mtumwiyo adati chinkana kuti akadamulamulira Filemoni ‘kuchita chimene chiyenera,’ mmalomwake anasankhapo kumlangiza iye. Kuti achite chiyani? Eya, kuti alandirenso Onesimo kapoloyo mwachifundo! Paulo akadakonda kukhala nawobe mautumiki opindulitsa a Onesimo komano sakadatero popanda chivomerezo cha Filemoni.
Zochitika zowonekera kukhala zosakondweretsa kaŵirikaŵiri zimatsimikizira kukhala zopindulitsa, monga momwe Paulo akusonyezera chotsatirapo. (Mavesi 15-21) Kwenikweni, panatuluka zabwino pamene Onesimo adathaŵa. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti Filemoni tsopano akamlandiranso iye monga mbale wofunitsitsa, wowona mtima Wachikristu, osati monga kapolo wosafunitsitsa, mwinamwake wosawona mtima. Paulo anapempha Filemoni kuti amlandirenso Onesimo mongadi momwe Paulo ankalandiridwira. Ngati Onesimo adalakwira Filemoni m’njira iriyonse, mtumwiyo akamlipirira. Kuti achititse Filemoni kufika pa kufunitsitsa kugwirizana naye, Paulo anamkumbutsa kuti nayenso anali ndi mangaŵa kwa mtumwiyo kaamba ka kukhala Mkristu. Chotero, Paulo anali wotsimikizira kuti Filemoni akachita zambiri kuposadi zimene anampempha kuti achite. Ha, ndikuchonderera kwaluso, ndikwachikondi chotani nanga! Ndithudi, iyi ndiyo njira imene tiyenera kuchitira ndi Akristu anzathu.
Paulo anatsiriza kalata yake mwakupereka chiyembekezo, natumiza malonje ndi mafuno abwino. (Mavesi 22-25) Iye anayembekezera kuti kupyolera m’mapemphero omupempherera, akamasulidwa m’ndende mofulumira. (Monga momwe kalata yachiŵiri ya Paulo kwa Timoteo ikusonyezera, mapempherowo anayankhidwa.) Pomaliza kalata yake, Paulo anatumiza moni nafotokozamo mafuno akuti chisomo cha Yesu Kristu chingakhale ndi mzimu umene Filemoni ndi alambiri anzake a Yehova anausonyeza.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 23]
Woposa Kapolo: Ponena za kubwerera kwa Onesimo kapolo wothaŵa wa Filemoni, Paulo anati: ‘Kapena anasiyanitsidwa ndi iwe kanthaŵi . . . kuti udzakhala naye nthaŵi zonse; osatinso monga kapolo, koma woposa kapolo, mbale wokondedwa, makamaka ndi ine, koma koposa nanga ndi iwe, m’thupi, ndiponso mwa Ambuye.’ (Pilemoni 15, 16) Muufumu wa Roma, ukapolo unaikidwa ndi boma lolamulira, ndipo Paulo anazindikira ‘maulamuliro aakulu’ oterowo. (Aroma 13:1-7) Iye sanachirikize kugalukira kwa akapolo koma anaŵathandiza anthuwo kupeza ufulu wauzimu monga Akristu. Mogwirizana ndi uphungu wake wakuti akapolo akhale ogonjera kwa ambuye awo, Paulo anabwezanso Onesimo kwa Filemoni. (Akolose 3:22-24; Tito 2:9, 10) Onesimo tsopano anali woposa kapolo wakudziko. Iye adali wokhulupirira mnzake wokondedwa amene akakhala wogonjera pang’ono kwa Filemoni monga kapolo wabwino, wotsogozedwa ndi malamulo amakhalidwe abwino aumulungu ndi kusonyeza chikondi cha pa abale.