Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Kodi ndi mlembi wa Baibulo uti amene anali “kazembe,” monga zatchulidwira m’bukhu la The Bible—God’s Word or Man’s?a
Bukhu lothandiza limenelo lonena za Mawu a Mulungu limafotokoza motere patsamba 10: “Baibulo nlapadera chifukwa cha kunena kopangidwa ndi alembi ake ambiri. Anthu okwanira 40, kuphatikizapo mafumu, abusa, asodzi, ogwira ntchito zaboma, ansembe, pafupifupi kazembe mmodzi, ndi sing’anga, anakhala ndi phande m’kulemba mbali zosiyanasiyana za Baibulo. Koma mobwerezabwereza, olembawo amanena zofanana: kuti iwo ankalemba osati malingaliro awo koma a Mulungu.”
Anthu ena afunsa kuti kodi ndi olemba Baibulo ati amene anali ndi ntchito zosiyanasiyana zimenezo kapena zochita. Mogwirizana ndi zimenezi, chonde lingalirani zotsatirazi:
Mafumu: Anthu angapo amene analemba Baibulo anali mafumu. Davide ndi Solomo angakumbukirike mwamsanga. (Salmo 3, mawu apamwamba; Miyambo 1:1; Mlaliki 1:1) Komabe, nyimbo yopezeka mu Yesaya 38:10-20 inalembedwa ndi Hezekiya. (Vesi 9) Akatswiri ambiri amakhulupirira kuti ndiye analembanso Salmo 119, mwinamwake asanakhale mfumu. Ndipo Hezekiya anali ndi mbali m’kulemba Miyambo mitu 25–29. (Miyambo 25:1) Mutu womalizira wa Miyambo unakonzedwa ndi ‘mfumu Lemueli.’ Ena amamuzindikiritsa ndi Mfumu Hezekiya, ngakhale kuti ena amaganiza kuti Lemueli anali Mfumu Solomo.—Miyambo 31:1.
Abusa: Davide ndi mneneri Amosi ankagwira ntchito yaubusa. (1 Samueli 16:11-13; 17:15, 28, 34; Amosi 1:1) Amosi analemba bukhu la Baibulo lokhala ndi dzina lake, ndipo Davide analemba masalmo ambiri. Salmo 23 lotchuka motsimikizikadi limasonyeza kuzoloŵerana kwa Davide ndi ubusa.
Asodzi: Pa atumwi a Yesu omwe anali asodzi, Yohane ndi Petro pambuyo pake anauziridwa kulemba mabuku a Baibulo. (Mateyu 4:18-22) Mwakuuziridwa kwaumulungu, Yohane analemba mbiri ya Uthenga Wabwino limodzinso ndi makalata atatu ndi bukhu la Chibvumbulutso. Petro analemba makalata ouziridwa aŵiri.
Ogwira ntchito zaboma: Onse aŵiri Danieli ndi Nehemiya anali ogwira ntchito zaboma m’maboma achilendo amene anali ndi ulamuliro pa anthu a Mulungu. (Nehemiya 1:1, 11; 2:1, 2; Danieli 1:19; 2:49; 6:1-3) Mabuku aŵiri a Baibulo ali ndi maina a amuna ameneŵa.
Ansembe: Aneneri aŵiri a Mulungu amene anagwiritsiridwa ntchito kulemba mabuku a Baibulo anali ansembe. Iwo anali Yeremiya ndi Ezekieli. (Yeremiya 1:1; Ezekieli 1:1-3) Kuwonjezerapo, Ezara anali wansembe wa Chiaroni yemwe anali ‘mlembi waluntha m’chilamulo cha Mose.’ Iye ‘adaikiratu mtima wake kuchifuna chilamulo cha Yehova, ndi kuchichita, ndi kuphunzitsa m’Israyeli malemba ndi maweruzo.’—Ezara 7:1-6, 10, 11.
Kazembe: Mbali imene Yoswa anaichita potsogolera gulu lankhondo pamene Aisrayeli ankapita ku Dziko Lolonjezedwa ndi kumenyana ndi adani ambiri imamuyeneretsa kukhala kazembe. (Yoswa 1:1-3; 11:5, 6) Iye anapatsidwa mwaŵi wakulemba bukhu la Yoswa. Kenakanso, oŵerenga Baibulo ena angalingalire kuti Davide adali munthu yemwe anachita ntchito ya ukazembe asanakhale mfumu.—1 Samueli 19:8; 23:1-5.
Sing’anga: Pomalizira pake, Akolose 4:14 amatcha “Luka sing’anga wokondedwa.” Luka analemba Uthenga Wabwino wokhala ndi dzina lake, ndiponso mwachiwonekere Machitidwe a Atumwi.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa mu 1989 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.