Yendani Monga Ogwira Nawo Ntchito M’chowonadi
Mfundo Zazikulu Zochokera m’Yohane Wachiŵiri ndi Wachitatu
CHIDZIŴITSO cha chowonadi ndicho chizindikiro cha alambiri a Yehova. (Yohane 8:31, 32; 17:17) Kuyenda m’chowonadi chaumulungu nkofunika kaamba ka chipulumutso. Ndipo atumiki a Mulungu ayenera kukhala ogwira nawo ntchito m’chowonadi.
Kalata youziridwa yachiŵiri ndi yachitatu ya mtumwi Yohane imanena za ‘kuyenda m’chowonadi.’ (2 Yohane 4; 3 Yohane 3, 4) Yohane Wachitatu amalimbikitsanso kugwirizana monga “ogwira nawo ntchito m’chowonadi.” (3 Yohane 5-8, NW) Mwachiwonekere, makalata onse aŵiri analembedwa mu 98 C.E. ku Efeso kapena chapafupi. Koma zimene amanena zingapindulitse anthu a Yehova lerolino.
Yohane Wachiŵiri Amagogomezera Chowonadi
Choyamba Yohane Wachiŵiri anagogomezera chowonadi ndi chikondi nachenjeza motsutsana ndi “wokana Kristu.” (Mavesi 1-7) Kalatayi inalunjikitsidwa kwa “mkazi . . . wosankhika,” mwinamwake munthu payekha. Koma ngati inatumizidwa ku mpingo, “ana” ake anali Akristu odzozedwa ndi mzimu ‘osankhidwa’ ndi Mulungu kaamba ka moyo wakumwamba. (Aroma 8:16, 17; Afilipi 3:12-14) Yohane anakondwera kuti ena anali ‘kuyenda m’chowonadi’ ndipo mwakutero kukaniza mpatuko. Komabe, iwo anafunikira kukhala atcheru ndi “wokana Kristu,” amene amakana kuti Yesu anadza m’thupi. Mboni za Yehova lerolino zimalabadira machenjezo otero otsutsana ndi mpatuko.
Chotsatira Yohane anapereka uphungu wochita ndi ampatuko ndiyeno adamaliza ndi mafuno aumwini ndi moni. (Mavesi 8-13) Mwantchito zotero zonga kulalikira, iye ndi ena adabala zipatso zotulukapo kusintha kwa awo omwe anawatumizira kalata yake. Kokha mwa ‘kudzipenyerera’ okha mwauzimu mpamene ‘akalandira mphotho,’ mwachiwonekere kuphatikizapo “korona” wakumwamba wosungidwira odzozedwa okhulupirika. (2 Timoteo 4:7, 8) Ngati aliyense ‘wosakhala m’chiphunzitso cha Kristu’ anadza kwa iwo, iwo sanayenera ‘kumlandira iye kunyumba zawo kapena kumpatsa moni’ kuwopera kuti angayanjane nazo ‘ntchito zake zoipa.’ Pambuyo posonyeza chiyembekezo chakuti iye akabwera ndi kulankhula ndi akhulupiriri anzake maso ndi maso, Yohane anatseka kalatayo ndi moni.
Yohane Wachitatu Amagogomezera Chigwirizano
Yohane Wachitatu analunjikitsidwa kwa Gayo ndipo choyamba anadziŵikitsa chimene iye anali kuchita kwa akhulupiriri anzake. (Mavesi 1-8) Gayo anali ‘kuyenda m’chowonadi’ mwakumamatira ku ziphunzitso zonse za Chikristu. Iye analinso ‘kuchita ntchito yokhulupirika’ (NW) mwakuthandiza abale oyendayenda. Yohane analemba kuti: “Ife, tiri ndi thayo la kulandira anthu otere mochereza, kuti tikhale ogwira nawo ntchito m’chowonadi.” (NW) Mboni za Yehova zimasonyeza kuchereza alendo kofananako kwa oyang’anira oyendayenda lerolino.
Pambuyo posiyanitsa mkhalidwe woipa wa Diotrefe ndi uja wa Demetriyo, Yohane adamaliza kalata yake. (Mavesi 9-14) Diotrefe wofuna ulemerero sanasonyeze ulemu kwa Yohane ndipo anayesa ngakhale kuchotsa mumpingo awo olandira abale mochereza. Komabe, Demetriyo anafotokozedwa kukhala chitsanzo chabwino. Yohane anayembekezera kuwona Gayo posachedwa ndipo adamaliza ndi moni ndi mafuno akuti Gayo asangalale ndi mtendere.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 30]
Ndi Kalata, Peni, ndi Kapezi: Yohane anafunitsitsa kukachezera “mkazi . . . wosankhika” ndi “ana” ake mmalo molemba zinthu zambiri kwa iwo “ndi kalata ndi kapezi.” Mmalo mopitiriza kulembera Gayo “ndi kapezi ndi peni,” mtumwiyo anayembekezeranso kumuwona iye posachedwa. (2 Yohane 1, 12; 3 Yohane 1, 13, 14) Liwu Lachigiriki lotembenuzidwa “peni” (kaʹla·mos) limaloza ku psipe kapena bango ndipo lingamasuliridwe kukhala “bango lolembera.” Pakati pa Agiriki ndi Aroma, peni labango linali losongoka ndi lojembeka mofanana ndi mapeni ankaliriro a pambuyo pake. Liwu Lachigiriki lakuti meʹlan, lomasuliridwa “kapezi,” liri mumpangidwe wa chinthu wamba cha mfotokozi wa chinthu champhongo meʹlas, kutanthauza “chakuda.” Mu akapezi akale, mtundu wake unali wakuda ngati makala—mpangidwe wa mwaye wotengedwa kumafuta otenthedwa kapena nkhuni, kapena makala owundana kuchokera ku zomera kapena manyowa a nyama. Kaŵirikaŵiri, kapezi ankasungidwa monga timitengo touma kapena zipondipondi, zimene zinasungunulidwa ndi mlembi nazigwiritsira ntchito ndi bulasho yake kapena bango. Pepala la masikuwo linali nsalu yopyapyala yopangidwa m’zidutswa kuchokera ku nsambo zotengedwa ku gumbwa. Akristu oyambirira anagwiritsira ntchito pepala lotero kaamba ka makalata, mipukutu, ndi mabuku amakedzana.