Chenjerani ndi Ampatuko!
Mfundo Zazikulu Zochokera m’Kalata ya Yuda
ATUMIKI a Yehova ayenera ‘kudana nacho choipa’ ndi ‘kugwirizana nacho chabwino.’ (Aroma 12:9) Wolemba Baibulo Yuda anathandiza ena kuchita motero m’kalata yake yotumizidwa kuchokera ku Palestina mwinamwake pafupifupi 65 C.E.
Yuda anadzitcha iyemwini “kapolo wa Yesu Kristu, ndi mbale wa Yakobo.” Mwachiwonekere Yakobo ameneyu anali mbale wopeza wotchuka wa Yesu Kristu. (Marko 6:3; Machitidwe 15:13-21; Agalatiya 1:19) Chotero Yuda iyemwini anali mbale wopeza wa Yesu. Komabe, iye angakhale anakulingalira kukhala kosayenera kutchula ubale wakuthupiwu, popeza kuti panthaŵiyo Kristu anali munthu wauzimu wolemekezeka kumwamba. Kalata ya Yuda inali yolunjika kwambiri popereka uphungu umene ungatithandize ‘kugwirizana nacho chabwino’ ndikuchenjera ndi ampatuko.
“Mulimbanetu”
Chinkana kuti Yuda anafuna kulemba ponena za chipulumutso chimodzi chomwe Akristu anali nacho, iye anakuwona kukhala koyenera kulimbikitsa aŵerengi ake ‘kulimbikatu chifukwa cha chikhulupiriro.’ (Mavesi 1-4) Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti anthu osapembedza anakwaŵira mumpingo mwamseri ndipo anali ‘kusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa.’ Iwo analingalira molakwa kuti akakhoza kuswa malamulo a Mulungu ndiyeno nkukhalabe pakati pa anthu ake. Tisagonjere konse kukulingalira koipa koteroko koma nthaŵi zonse tilondole chilungamo, kuyamikira kuti kupyolera mwa mwazi wa Yesu, Mulungu anatiyeretsa machimo athu mwachifundo.—1 Akorinto 6:9-11; 1 Yohane 1:7.
Machenjezo Operekedwa Kwa Ife
Nkofunika kuchenjera ndi malingaliro ena, mikhalidwe, ndi anthu. (Mavesi 5-16) Chifukwa chakuti Aisrayeli ena opulumutsidwa ku Igupto anasoŵeka chikhulupiriro, iwo anawonongedwa. Angelo amene sanasunga chikhalidwe chawo choyamba ‘adawasunga m’ndende zosatha pansi pa mdima [wauzimu], kufikira chiweruziro cha tsiku lalikulu.’ Chisembwere chonyansa chinadzetsa ‘chilango cha moto wosatha’ pa Sodomu and Gomora. Chotero, tiyenitu nthaŵi zonse tikondweretse Mulungu ndikusasiya “njira ya moyo.”—Salmo 16:11.
Mosiyana ndi Mikayeli mngelo wamkuluyo, yemwe sakaweruzadi Mdyerekezi ndi mawu amwano, anthu osapembedza analankhula mwamwano za “maulemero,” mwachiwonekere awo okhala ndi ulemerero wina woikidwa pa iwo ndi Mulungu ndi Kristu monga akulu odzozedwa. Tisasonyezetu kupanda ulemu ku ulamuliro woikidwa ndi Mulungu!
Zitsanzo zoipa za Kaini, Balamu, ndi Kora zinatsatiridwa ndi anthu osapembedzawo. Iwo anapereka chiwopsezo chauzimu chofanana ndi matanthwe obisika pansi pamadzi ndipo anali ofanana ndi mitambo yopanda madzi ndiponso akufa, mitengo yozulidwa yosabala kanthu kalikonse kopindulitsa. Ampatukowo anali odandaula, oderera, ndi ‘otama anthu chifukwa cha kupindula nako.’
Pitirizanibe Kukana
Chotsatirapo Yuda anapereka malingaliro pa kukaniza zisonkhezero zoipa. (Mavesi 17-25) Kukakhala otonza ‘pa nthaŵi yotsiriza,’ ndipo Akristu owona ayenera kuwapirira iwo ndi mawu awo otonza lerolino. Kuti tikanize zisonkhezero zoipa zoterozo, tiyenera kuzamitsa ‘chikhulupiriro . . . choyeretsetsa,’ kupemphera ndi mzimu woyera, ndikukhalabe m’chikondi cha Mulungu, pamene tikuyembekezera kuti chifundo cha Yesu chisonyezedwe.
Mwachiwonekere monga aphunzitsi onyenga, anthu osapembedzawo anachititsa ena kukaikira. (Yerekezerani ndi 2 Petro 2:1-3.) Ndipo kodi nchiyani chimene okaikirawo anafunikira? Eya, thandizo lauzimu kuti akwatulidwe “kumoto,” chiwonongeko chosatha! (Mateyu 18:8, 9) Koma opembedza safunikira kuwopa chiyembekezocho, pakuti Yehova adzaŵachinjiriza ku ‘kukhumudwa’ kuloŵa muuchimo ndi chiwonongeko choyembekezera ampatuko.
[Bokosi patsamba 31]
Matanthwe Obisika: Yuda anachenjeza Akristu anzake za ‘matanthwe obisika pansi pamadzi m’mapwando awo achikondi.’ (Yuda 12, NW) Onyengezera kukhala ndi chikondi kaamba ka akhulupiriri, ampatuko oterowo anali ngati matanthwe ojenya apansi pamadzi omwe akakhoza kuwononga zombo kapena kusakaza ndi kupha osambira. Mapwando achikondi angakhale anali mapwando kumene Akristu okhupuka mwakuthupi anaitanira akhulupiriri anzawo osauka. Bambo Watchalitchi Chrysostom (347?–407 C.E.) anati: “Onse anakumana pa phwando la onse: olemera anabweretsa zofunikira, ndipo osauka ndi awo omwe analibe kanthu kalikonse anaitanidwa, iwo anadyera pamodzi mwachisawawa.” Mulimonse mmene unaliri mpangidwe wa mapwando achikondi oyambirirawo, chenjezo la Yuda linawathandiza okhulupirika kuchenjera ndi ampatuko onga ‘matanthwe obisika’ omwe akakhoza kudzetsa imfa yauzimu. Chinkana kuti Akristu sanalamulidwe kuchita mapwando achikondi, ndipo samachitidwa lerolino, anthu a Yehova amathandizana mwakuthupi m’nthaŵi zakusoŵa ndipo amakhala ndi kuyanjana kosangulutsa.