Khalani Ogwirizana mwa Chinenero Choyera
“Pakuti pamenepo ndidzapereka kwa mitundu kusinthira ku chinenero choyera, kuti iwo onse aitanire pa dzina la Yehova, kuti amtumikire mogwirizana.”—ZEFANIYA 3:9, NW.
1. Kodi anthu anamumvapo Yehova Mulungu akulankhula?
CHINENERO cha Yehova Mulungu nchoyera. Koma kodi anthu anamumvapo akulankhula? Eya, indedi anatero! Chimenecho chinachitika pamene Mwana wake, Yesu Kristu, anali padziko lapansi zaka mazana 19 zapitazo. Mwachitsanzo, pamene Yesu anabatizidwa, Mulungu anamvedwa akunena kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.” (Mateyu 3:13-17) Imeneyo inali ndemanga ya chowonadi choyera, yomvedwa ndi Yesu ndi Yohane Mbatizi m’chinenero cha anthu.
2. Kodi nchiyani chikusonyezedwa pamene mtumwi Paulo akulozera ku “malilime a . . . angelo”?
2 Zaka zingapo pambuyo pake mtumwi Wachikristu Paulo analankhula za “malilime a anthu, ndi a angelo.” (1 Akorinto 13:1) Kodi ichi chikusonyezanji? Eya, chikusonyeza kuti sianthu athupi okha komanso anthu auzimu nawonso ali nacho chinenero ndi chilankhulo! Ndithudi, Mulungu ndi angelo samalankhulana mwakugwiritsira ntchito mawu ndi chinenero chomvekera ndi chomveka kwa ife. Kulekeranji? Chifukwa chakuti thambo lozinga dziko lapansi limafunikira kotero kuti lipereke mafunde a mawu amene anthu atha kuwamva ndi kuwazindikira.
3. Kodi chinenero cha anthu chinayamba motani?
3 Kodi chinenero cha anthu chinayamba motani? Ena amati makolo athu ankavutika polankhulana namangodzuma ndi kubuula. Bukhu lakuti Evolution (Life Nature Library) limati: “Munthu wonga nyani wa zaka pafupifupi miliyoni imodzi zapitazo . . . mothekera anaphunzira mawu oŵerengeka a kulankhula.” Koma Ludwig Koehler, wolemba madikishonale wotchuka anati: “Chilankhulo cha anthu nchinsinsi; ndi mphatso yaumulungu, chozizwitsa.” Inde, chilankhulo cha anthu ndi mphatso yaumulungu, popeza kuti Mulungu anapatsa munthu woyamba, Adamu, chinenero. Mwachiwonekere ndicho chomwe m’kupita kwa nthaŵi chinadzatchedwa Chihebri. Chinenero chimenecho chinalankhulidwa ndi mbadwa Zachiisrayeli za “Abramu Mhebri,” kholo lokhulupirika lomwe kholo lake Semu anali mwana wa Nowa yemwe anamanga chingalawa. (Genesis 11:10-26; 14:13; 17:3-6) Polingalira za dalitso laulosi la Mulungu pa Semu, nkwanzeru kugamula kuti chinenero chake sichinayambukiridwe ndi chozizwitsa chimene Yehova Mulungu anachita zaka mazana 43 zapitazo.—Genesis 9:26.
4. Kodi Nimrode anali yani, ndipo kodi anagwiritsiridwa ntchito motani ndi Satana Mdyerekezi?
4 Panthaŵiyo ‘dziko lapansi linali la chinenedwe chimodzi ndi chilankhulidwe chimodzi.’ (Genesis 11:1) Mwamuna wotchedwa Nimrode adaali wamoyo panthaŵi imeneyo, “mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova.” (Genesis 10:8, 9) Nimrode anagwiritsiridwa ntchito mwapadera ndi mdani wa anthu wamkulu wosawoneka, Satana, kukhazikitsa mbali yapadziko lapansi ya gulu la Mdyerekezi. Nimrode anafuna kudzipangira dzina, ndipo mkhalidwe wodzitukumula umenewo unafalikira kwa otsatira ake, omwe anayamba projekiti yapadera yakumanga m’dziko la Sinara. Mogwirizana ndi Genesis mutu 11, vesi 4, iwo anati: ‘Tiyeni, timange mudzi ndi nsanja, pamutu pake pafikire kumwamba; ndipo tidzipangire ife tokha dzina kuti tisabalalike pa dziko lonse lapansi.’ Projekiti imeneyo yotsutsana ndi lamulo la Mulungu lakuti “mudzaze dziko lapansi” inatha pamene Yehova anasokoneza chinenero cha opandukawo. “Ndipo,” limatero Baibulo, “Yehova anabalalitsa iwo pa dziko lonse lapansi, ndipo analeka kumanga mudzi.” (Genesis 9:1; 11:2-9) Mzindawo unatchedwa Babele, kapena Babulo (kutanthauza, “Chisokonezo”), “chifukwa chakuti kumeneko Yehova anasokoneza chilankhulo cha dziko lonse lapansi.”—Byington.
5. (a) Kodi nchiyani chimene chinaletsedwa pamene Mulungu anasokoneza chinenero cha anthu? (b) Kodi tingagamuleponji ponena za chinenero cha Nowa ndi Semu?
5 Chozizwitsa chimenecho—chisokonezo cha chinenero chimodzi cha anthu—chinatsogolera kukudzazidwa kwa dziko lapansi monga momwe Mulungu analamulira Nowa, ndipo chinalepheretsa makonzedwe alionse omwe Satana angakhale adali nawo okhazikitsa kulambira konyansa kogwirizana kwa iye mwini kochitidwa ndi anthu opandukira Ambuye Mfumu ya kumwamba ndi dziko lapansi. Zowona, mwakuchita chipembedzo chonyenga cha mtundu uliwonse, anthuwo anali minkhole ya Mdyerekezi, ndipo iwo ankatumikira ziŵanda pamene anapanga milungu ndi milungu yachikazi, ndikuitcha maina m’zinenero zawo zosiyanasiyana, ndi kuilambira. (1 Akorinto 10:20) Koma kachitidwe ka Mulungu yekha wowona pa Babele kanaletsa kupangidwa kwa chipembedzo chonyenga chimodzi chogwirizana chopereka kulambira kwa Mdyerekezi kumene mwachiwonekere iye anakulakalaka. Ndithudi, Nowa wolungama ndi mwana wake Semu sanasokonekere m’chisokonezeko cha m’dziko la Sinara chimenecho. Motero tingagamule mwanzeru kuti chinenero chawo chinakhalabe chomwe chinalankhulidwa ndi Abramu (kapena Abrahamu) wokhulupirikayo—lilime m’limene Mulungu analankhula kwa mwamuna Adamu m’munda wa Edene.
6. Pa tsiku la Pentekoste wa 33 C.E., kodi Yehova anasonyeza motani kuti ali wokhoza kupereka luso lakulankhula m’malilime?
6 Yehova, yemwe anasokoneza chinenero choyambirira cha anthu, akhozanso kupereka luso la kulankhula m’malilime. Eya, iye anachitadi chimenecho patsiku la Pentekoste m’chaka cha 33 C.E. m’Nyengo Yathu ino! Mogwirizana ndi Machitidwe 2:1-11, atsatiri a Yesu Kristu okwanira pafupifupi 120 panthaŵi imeneyo adasonkhana m’chipinda chapamwamba m’Yerusalemu. (Machitidwe 1:13, 15) Mwadzidzidzi, panabuka phokoso lochokera kumwamba “ngati mkokomo wa mphepo yolimba.” Panawoneka “malilime . . . onga amoto” ndipo anagawidwa kwa iwo. Pamenepo ophunzirawo ‘anadzazidwa onse ndi mzimu woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga mzimu unawalankhulitsa.’ M’zinenero zopatsidwa ndi Mulungu zimenezo, iwo analankhula ‘zazikulu za Mulungu.’ Ndipo chinali chozizwitsa chotani nanga chimenecho, pamene Ayuda ndi otembenuzidwira ku Chiyuda a malilime osiyanasiyana, ochokera ku malo akutali monga Mesopotamiya, Igupto, Libiya, ndi Roma, anatha kumvetsetsa uthenga wopatsa moyo!
Chinenero Chopatsidwa ndi Mulungu Lerolino!
7. Kodi pangakhale ziyembekezo zotani ngati chinenero chimodzi ndicho chinalankhulidwa ndi kumvedwa padziko lonse?
7 Popeza kuti Mulungu akhoza kupereka malilime osiyanasiyana mozizwitsa, kodi sikukakhala kwabwino koposa ngati akanatheketsa kuti pakhale chinenero chimodzi chokha cholankhulidwa ndi kumvedwa padziko lonse? Chimenecho chikapititsa patsogolo kumvana kwabwinopo m’banja la anthu. Monga momwe The World Book Encyclopedia imanenera kuti: “Ngati anthu onse akadalankhula lilime limodzi, kugwirizana kwa mwambo ndi zachuma kukadakhala kwathithithi, ndipo chimvano chikadakula pakati pa maiko.” Eya, zinenero zadziko lonse zosachepera pa 600 zapangidwa m’kati mwa zaka. Mwa zimenezi, chinenero cha Esperanto chakhala ndi chisonkhezero chachikulu koposa chifukwa chakuti pafupifupi anthu 10,000,000 achiphunzira kuchokera pamene chinayambidwa m’chaka cha 1887. Komabe, zoyesayesa za anthu zofuna kugwirizanitsa anthu mwa njira ya chinenero chimodzi cha padziko lonse sizinakhalepo ndi chipambano. Kwenikweni, mavuto owonjezerekawonjezereka akuchititsa magaŵano m’dziko lino pamene ‘anthu oipa aipa chiipire.’—2 Timoteo 3:13.
8. Ngakhale ngati chinenero chimodzi chinatengedwa kukhala cha dziko lonse m’dziko lamakono, kodi nchiyani chimene chikanakhalapobe, ndipo chifukwa ninji?
8 Kudza ku chipembedzo, pali chisokonezo chachikulu. Koma kodi sitiyenera kuziyembekezera zimenezi, popeza kuti bukhu la Baibulo la Chibvumbulutso limatcha ulamuliro wa dziko wa chipembedzo chonyenga kukhala ‘Babulo Wamkulu’? (Chibvumbulutso 18:2) Inde, popeza kuti “Babulo” amatanthauza “Chisokonezo.” Ngakhale ngati chinenero chopanga kapena chachibadwa monga Chingelezi, Chifalansa, Chijeremani, kapena Chirasha chinati chitengedwe kukhala chinenero cha dziko lonse m’dziko lamakono, kusagwirizana kukakhalapobe m’zipembedzo ndi mbali zina. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo,” Satana Mdyerekezi. (1 Yohane 5:19) Iye ndiye magwero enieni a dyera, ndipo mwaumbombo amalakalaka kulambiridwa ndi anthu onse, monga momwe anachitira m’masiku a Nimrode ndi Nsanja ya Babele. Eya, chinenero cha padziko lonse cholankhulidwa ndi anthu ochimwa chingapatsedi Satana mwaŵi wakukhazikitsa kulambira Kwauchiwanda kogwirizana! Koma Yehova sadzalola konse chimenecho; ndithudi, iye posachedwapa adzachotsapo chipembedzo chonse chonyenga, chouziridwa ndi Mdyerekezi.
9. Kodi ndimotani mmene anthu a mitundu yonse ndi mafuko akugwirizanitsidwira tsopanoli?
9 Komabe, chenicheni chozizwitsa nchakuti anthu abwino a mitundu yonse ndi mafuko akugwirizanitsidwa tsopano lino. Ichi chikuchitika pamaziko a Mulungu ndi kaamba ka kulambiridwa kwake. Lerolino, Mulungu akuwatheketsa anthu kuphunzira ndi kulankhula chinenero chokha choyera padziko lapansi. Ndipo icho chiridi chinenero cha padziko lonse. Ndithudi, Yehova Mulungu akuphunzitsa chinenero choyera chimenechi kwa anthu ambiri ochokera m’mitundu yonse ya dziko lapansi lerolino. Uku nkukwaniritsidwa kwa lonjezo laulosi la Mulungu loperekedwa kupyolera mwa mneneri wake ndi mboni Zefaniya lakuti: “Pakuti pamenepo ndidzapereka kwa amitundu kusinthira ku chinenero choyera [m’lingaliro lenileni, “mlomo waudongo”], kuti iwo onse aitanire padzina la Yehova, kuti amtumikire mogwirizana.” (Zefaniya 3:9, NW) Kodi chinenero choyera chimenechi nchiyani?
Chinenero Choyera Chilongosoledwa
10. Kodi chinenero choyera nchiyani?
10 Chinenero choyera ndicho chowonadi cha Mulungu chopezedwa m’Mawu ake, Malemba Opatulika. Icho makamaka ndicho chowonadi chonena za Ufumu wa Mulungu, umene udzabweretsa mtendere ndi madalitso ena kwa anthu. Chinenero choyera chimataya zolakwa zachipembedzo ndi kulambira konyenga. Chimagwirizanitsa onse ochilankhula m’kulambira koyera, kwaudongo, kwabwino kwa Mulungu wamoyo ndi wowona, Yehova. Lerolino, zinenero zokwanira 3,000 zimachita monga zopinga kumvetsetsa, ndipo mazana a zipembedzo zonyenga zimasokoneza anthu. Motero ndife okondwa chotani nanga kuti Mulungu akupatsa anthu kusinthira ku chinenero choyera ndi chabwino koposa chimenechi!
11. Kodi chinenero choyera chawachitiranji anthu a mitundu yonse ndi mafuko?
11 Inde, chinenero choyera chikuphunziridwa ndi anthu a mitundu yonse ndi mafuko. Monga lilime lauzimu loyera lokha padziko lapansi, chimatumikira monga mphamvu yaikulu yogwirizanitsa. Icho chimatheketsa onse ochilankhula “kuitanira padzina la Yehova, kuti amtumikire mogwirizana,” kapena m’lingaliro lenileni, “ndi phewa limodzi.” Motero iwo amatumikira Mulungu “ndi maganizo amodzi,” “ndi maganizo amodzi chapamodzi ndi phewa limodzi logwirizana.” (The New English Bible; The Amplified Bible) Matembenuzidwe a Steven T. Byington amati: “Pamenepo ine [Yehova Mulungu] ndidzasintha milomo ya anthu onse ikhale yaudongo, kuti onse aitanire pa dzina la Yehova ndi kugwirizana muutumiki wake.” Kugwirizana kwa zinenero zambiri kumeneko kwa dziko lonse muutumiki wa Mulungu kumapezeka kokha pakati pa Mboni za Yehova. M’maiko 212 lerolino, oposa mamiliyoni anayi a alengezi a Ufumu ameneŵa akulalikira mbiri yabwino m’zinenero zambiri za anthu. Komabe, Mbonizo ‘zimalankhula mogwirizana’ ndipo ali ‘ogwirizana bwino lomwe m’maganizo amodzimodzi ndi mu mzera umodzimodzi wa ganizo.’ (1 Akorinto 1:10, NW) Izi ziri choncho chifukwa chakuti, mosasamala kanthu ndikumene ziri padziko lapansi, Mboni za Yehova zonse zimalankhula chinenero choyera chimodzicho, ku chitamando ndi ulemerero wa Atate wawo wakumwamba.
Phunzirani Chinenero Choyera Tsopano!
12, 13. (a) Kodi nchifukwa ninji muyenera kudera nkhaŵa ponena za kulankhula chinenero choyera? (b) Kodi nchifukwa ninji mawu a pa Zefaniya 3:8, 9 ali ofunika kwambiri lerolino?
12 Kodi nchifukwa ninji inu muyenera kudera nkhaŵa ponena za kulankhula chinenero choyera? Chifukwa chimodzi ndi ichi, moyo wanu umadalira pakuchiphunzira ndi kuchilankhula. Nthaŵi pang’ono Mulungu asanalonjeze “kupereka kwa mitundu kusinthira ku chinenero choyera,” iye anachenjeza kuti: ‘Mundilindire, ati Yehova, kufikira tsiku loukira ine zofunkha; pakuti ndatsimikiza mtima ine kusonkhanitsa amitundu, kuti ndimemeze maufumu kuwatsanulira kulunda kwanga, ndilo mkwiyo wanga wonse waukali; pakuti dziko lonse lapansi lidzathedwa ndi moto wa nsanje yanga.’—Zefaniya 3:8.
13 Mawu amenewo a Ambuye Mfumu Yehova analankhulidwa choyamba zaka mazana 26 zapitazo mu Yuda, amene Yerusalemu adali likulu lake. Koma ndemanga imeneyo inalinganizidwiradi tsiku lathu chifukwa chakuti Yerusalemu anali wofanana ndi Chikristu Chadziko. Ndipo nthaŵi yathu, chiyambire kukhazikitsidwa kwa Ufumu wakumwamba wa Mulungu mu 1914, ndiyo tsiku la Yehova lakusonkhanitsa mitundu yonse ndi kumemeza maufumu. Iye wawabweretsa onse pamodzi pansi pa chisamaliro chake mwanjira ya ntchito yaikulu ya kuchitira umboni. Chimenechinso, chawaputa kutsutsana ndi chifuniro chake. Komabe, Yehova Mulungu mwachifundo akukhozetsa anthu ochokera m’mitundu yonseyi kugwirizana m’kulankhula chinenero choyera. Ndi chinenero chimenechi, onse ofunafuna moyo m’dziko lake latsopano lolonjezedwa angamtumikire mogwirizana pamene mitundu yonse isanamezedwe ndi ukali wa mkwiyo waumulungu pa ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse,’ mofala lotchedwa Armagedo. (Chibvumbulutso 16:14, 16; 2 Petro 3:13) Mokondweretsa, olankhula chinenero choyera ndikuitanira padzina la Yehova mwachikhulupiriro monga alambiri owona ogwirizana adzasangalala ndi chitetezo chaumulungu mkati mwa ukali wa ngozi ya dziko lonse imeneyo. Mulungu adzawaloŵetsa mwachisungiko m’dziko latsopano, kumene pomalizira pake chinenero choyera chokha ndicho chidzakhala pamilomo ya anthu onse.
14. Kupyolera mwa Zefaniya, kodi Mulungu anasonyeza motani kuti kupulumuka mapeto a dongosolo lazinthu liripoli kumafunikiritsa kuchitapo kanthu mwamsanga?
14 Kupyolera mwa mneneri wake Zefaniya, Yehova akuchimveketsa bwino kuti oyembekezera kupulumuka mapeto a dongosolo lazinthu loipa liripoli ayenera kuchitapo kanthu mwamsanga. Mogwirizana ndi Zefaniya 2:1-3, Mulungu akuti: ‘Dzisanthuleni, inde santhulani; inu mtundu wosakhumba kanthu; lamulo lisanabale, tsiku lisanapitirire ngati mungu, usanakugwereni mkwiyo waukali wa Yehova, lisanakugwereni tsiku la mkwiyo wa Yehova. Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.’
15. (a) Kodi kukwaniritsidwa koyambirira kwa Zefaniya 2:1-3 kunali kotani? (b) Kodi ndani anapulumuka chiweruzo cha Mulungu choperekedwa pa Yuda, ndipo kodi nchiyani chimene chidzafanana ndi chipulumutso chimenecho m’tsiku lathu?
15 Mawu amenewo anali ndi kukwaniritsidwa kwake koyamba pa Yuda wakale ndi Yerusalemu. Anthu ochimwa a Yuda sanavomereze kuchonderera kwa Mulungu, monga momwe zasonyezedwa ndi kuperekedwa kwa chiweruzo chake pa iwo pamanja a Ababulo m’chaka cha 607 B.C.E. Monga momwe Yuda analiri “mtundu wosakhumba kanthu” pamaso pa Mulungu, momwemonso Chikristu Chadziko chakhala “mtundu” wopanda manyazi pamaso pa Yehova. Komabe, chifukwa chakulabadira mawu a Mulungu, Ayuda ena ndi anthu ena anapulumuka, ndi mneneri wokhulupirika wa Yehova, Yeremiya anali pakati pawo. Opulumuka ena anali Ebedi-Meleki Mkusi ndi mbadwa za Yonadabu. (Yeremiya 35:18, 19; 39:11, 12, 16-18) Mofananamo lerolino, ‘khamu lalikulu’ la “nkhosa zina” za Yesu zosonkhanitsidwa kuchokera m’mitundu yonse zidzapulumuka Armagedo kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu. (Chibvumbulutso 7:9; Yohane 10:14-16) Kokha awo ophunzira ndi kulankhula chinenero choyera ndiwo adzakhala opulumuka okondwa.
16. Kodi munthu ayenera kuchitanji kuti akabisike pa “tsiku la mkwiyo wa Yehova”?
16 Monga momwe linaliri lamulo la Yehova kuti Yuda ndi Yerusalemu anayenera kupasulidwa, choteronso Chikristu Chadziko chiyenera kuwonongedwa. Ndithudi, chiwonongeko cha chipembedzo chonse chonyenga chiri pafupi, ndipo awo okhumba kupulumuka ayenera kuchitapo kanthu mwamsanga. Iwo ayenera kutero “tsiku lisanapitirire ngati mungu,” woulutsidwa mwamsanga ndi mphepo, monga pamene mapira amaulutsidwa popunthira. Kuti tipulumutsidwe ku mkwiyo wa Mulungu, tiyenera kulankhula chinenero choyera ndi kulabadira chenjezo la Mulungu pamene tsiku la mkwiyo waukali wa Yehova lisanafike pa ife. M’tsiku la Zefaniya ndi lerolino, ofatsa amafunafuna Yehova Mulungu, limodzi ndi chilungamo ndi chifatso. Kufunafuna kwathu Yehova kumatanthauza kumkonda ndi mtima wathu wonse, moyo, maganizo, ndi nyonga. (Marko 12:29, 30) ‘Kapena [awo ochita tero] angabisike pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.’ Koma kodi nchifukwa ninji ulosiwo umanena kuti “kapena”? Chifukwa chakuti chipulumutso chimadalira pa kukhulupirika ndi chipiriro. (Mateyu 24:13) Amene amamamatira ku miyezo yolungama ya Mulungu napitirizabe kulankhula chinenero choyera adzabisika pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.
17. Kodi ndimafunso ati omwe afunikira kuti tiwalingalire?
17 Popeza kuti tsiku la mkwiyo wa Yehova liri pafupi ndipo chipulumutso chimadalira pa kuphunzira ndikugwiritsira ntchito chinenero choyera, lerolino ndiyo nthaŵi yakudziloŵetsamo mozama m’kuchiphunzira ndi kuchilankhula. Koma kodi ndimotani mmene munthu angaphunzirire chinenero choyera? Ndipo kodi mungapindule motani?
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi chilankhulo cha anthu chinayamba motani?
◻ Kodi chinenero choyera nchiyani?
◻ Kodi nchifukwa ninji mawu a pa Zefaniya 3:8, 9 ngofunika kwambiri lerolino?
◻ Kodi tiyenera kuchitanji kuti tibisike pa “tsiku la mkwiyo wa Yehova”?
[Chithunzi patsamba 10]
Pa Babele, Mulungu anabalalitsa anthu mwakusokoneza chinenero chawo