Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 5/1 tsamba 21-23
  • Masomphenya Osangalatsa Omwe Amalimbitsa Chikhulupiriro

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Masomphenya Osangalatsa Omwe Amalimbitsa Chikhulupiriro
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kristu Apereka Uphungu Wachikondi
  • Mwanawankhosa Atsegula Bukhu
  • Ufumu Wabadwa!
  • Atumiki a Yehova Achitapo Kanthu
  • Akazi Aŵiri Ophiphiritsira
  • Kristu Alakika ndi Kulamulira
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Chivumbulutso—Gawo 2
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Zimene Zili Mʼbuku la Chivumbulutso
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Chivumbulutso—Gawo 1
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kumalizitsa Mkwiyo wa Mulungu
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 5/1 tsamba 21-23

Masomphenya Osangalatsa Omwe Amalimbitsa Chikhulupiriro

Mfundo Zazikulu Zochokera m’Chibvumbulutso

YOHANE, mtumiki wa Yehova ali pa kachisumbu kakang’ono kotchedwa Patmo, kusiya gombe lakumadzulo kwa Asia Minor. Kumeneko mtumwi wokalambayu awona zinthu zodabwitsa​—zophiphiritsira, kaŵirikaŵiri zochititsa mantha, ndipo zofunika kwenikweni! Iye afikira kukhala m’tsiku la Ambuye, loyambira pa kukhazikitsidwa pampando wachifumu kwa Yesu mu 1914 mpaka mapeto a Ulamuliro Wake Wazaka Chikwi. Chinkana kuti Yohane awona zinthu zimene zidzachitika mkati mwa nyengo yamdima wandiweyani ya anthu, nkosangalatsa chotani nanga kuwoneratu kwake Kulamulira kwa Kristu Kwazaka Chikwi! Ha, ndimadalitso otani nanga amene anthu omvera adzasangalala nawo panthaŵiyo!

Yohane analemba masomphenya ameneŵa m’bukhu Labaibulo la Chibvumbulutso. Lolembedwa pafupifupi 96 C.E., ilo lingalimbitse chikhulupiriro chathu mwa Mulungu wa ulosi, Yehova, ndi mwa Mwana wake, Yesu Kristu.​—Kaamba ka tsatanetsatane, onani bukhu la Revelation​—Its Grand Climax At Hand!, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

Kristu Apereka Uphungu Wachikondi

M’kuvumbulutsa koyambirira kochokera kwa Mulungu kupyolera mwa Kristu muli makalata ku mipingo isanu ndi iŵiri ya oloŵa Ufumu anzake a Yesu. (1:1–3:22) Onse pamodzi, makalatawo amapereka chiyamikiro, kuzindikiritsa mavuto, kupereka chiwongolero ndi/​kapena chilimbikitso, ndi kutchula madalitso otulukapo m’kumvera kokhulupirika. Chinkana kuti Aefeso anapirira, iwo adataya chikondi chomwe anali nacho poyamba. Mpingo wolemera mwauzimu wa ku Smurna ukulimbikitsidwa kukhalabe wokhulupirika mkati mwansautso. Chizunzo sichinagonjetse mpingo wa ku Pergamo, koma iwo walekerera magaŵano. Mosasamala kanthu za ntchito yowonjezereka yochitidwa ndi Akristu ku Tiyatira, chisonkhezero cha Yezebeli chikupezeka kumeneko. Mpingo wa ku Sarde ufunikira kugalamuka mwauzimu, wa ku Filadelfeya ukulimbikitsidwa kumamatira ku zomwe uli nazo, ndipo Alaodikaya ofunda afunikira kuchiritsa kwauzimu.

Ndimawu abwino chotani nanga ophunzitsira mafumu amtsogolo akumwamba​—kwenikweni, Akristu onse! Mwachitsanzo, kodi aliyense wa ife wakhala wofunda? Chotero chitanipo kanthu! Khalani otsitsimula monga chikho cha madzi ozizira pa tsiku lotentha koma yambaninso kusonyeza changu chotentha kaamba ka Yehova ndi utumiki wake.​—Yerekezerani ndi Mateyu 11:28, 29; Yohane 2:17.

Mwanawankhosa Atsegula Bukhu

Chotsatira Yehova awoneka atakhala pampando wake wachifumu muulemerero. (4:1–5:14) Iye wazingidwa ndi akulu 24 ndi zamoyo zinayi. Bukhu losindikizidwa ndi zizindikiro zisanu ndi ziŵiri liri m’dzanja lake. Kodi ndani angatsegule bukhulo? Eya, Mwanawankhosa, Yesu Krsitu, ali woyenerera kutero!

Zochitika zochititsa chidwi zivumbuluka pamene Mwanawankhosayo atsegula zizindikiro zisanu ndi chimodzi. (6:1–7:17) Pamene chizindikiro choyamba chitsegulidwa, Kristu awonekera atakwera pa kavalo woyera, alandira korona (mu 1914), natuluka kukalakika. Pamene zizindikiro zotsatira zitatu zitsegulidwa, apakavalo ena adzetsa nkhondo, njala, ndi imfa kwa anthu. Pamene chizindikiro chachisanu chitsegulidwa, awo ophedwa chifukwa cha Kristu afuula kaamba ka kubwezera chilango mwazi wawo, ndipo aliyense apatsidwa “mwinjiro woyera,” kutanthauza kaimidwe kolungama kogwirizana ndi kuuka kwawo ku moyo wosakhoza kufa monga zolengedwa zauzimu limodzi ndi mathayo achifumu. (Yerekezerani ndi Chibvumbulutso 3:5; 4:4.) Pamene chizindikiro chachisanu ndi chimodzi chitsegulidwa, tsiku la mkwiyo wa Mulungu ndi la Mwanawankhosa likulengezedwa ndi chivomezi. Koma ‘mphepo zinayi za dziko,’ zophiphiritsira chiweruzo chowononga, zagwidwa kufikira akapolo a Mulungu a 144,000 atasindikizidwa chizindikiro. Pamene iwo adzozedwa ndi mzimu wa Mulungu nalandiridwa kukhala ana ake auzimu, iwo alandira chizindikiro chapasadakhale​—chosindikiza, kapena chikole​—cha choloŵa chawo chakumwamba. Ndikokha pambuyo pakuyesedwa pamene kuikidwa chizindikiro kudzakhala kwa chikhalire. (Aroma 8:15-17; 2 Akorinto 1:21, 22) Ndipo Yohane ayenera kukhala wodabwa chotani nanga kuwona ‘khamu lalikulu’ lochokera m’mitundu yonse​—khamu lokhala ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya m’dziko lapansi laparadaiso! Iwo atuluka ‘m’chisautso chachikulu,’ nthaŵi ya tsoka la anthu lopanda lina lofanana nalo.

Nzochitika zochitsa mantha chotani nanga zimene zikuchitika pamene chizindikiro chachisanu ndi chiŵiri chitsegulidwa! (8:1–11:14) Kukhala chete kwa theka la ola, kulola mapemphero a oyera mtima kuti amvedwe, kutsatiridwa ndi kuponyedwa ku dziko lapansi kwa moto wotengedwa kuguwa lansembe. Kenaka angelo asanu ndi aŵiri akonzekera kuwomba malipenga kulengeza miliri ya Mulungu pa Chikristu Chadziko. Malipengawo alizidwa m’nthaŵi ya mapeto yonse kufikira chisautso chachikulu. Malipenga anayi alengeza miliri padziko lapansi, nyanja, akasupe amadzi, ndi padzuŵa, mwezi, ndi nyenyezi. Kuwombedwa kwa lachisanu kuitanira dzombe lomwe lichitira chithunzi Akristu odzozedwa akuguduka kukachita nkhondo kuyambira 1919 kunkabe mtsogolo. Pamene lipenga lachisanu ndi chimodzi liwombedwa, kuukira kwa ankhondo kuchitika. M’kukwaniritsidwa kwake, odzozedwa, ochirikizidwa ndi ‘khamu lalikulu’ chiyambire 1935, amalengeza uthenga wachiweruzo wozunza motsutsana ndi atsogoleri achipembezo a Chikristu Chadziko.

Kenaka Yohane akudya kabukhu, kutanthauza kuti odzozedwa alandira ntchito yawo ndipo iwo amapeza chichirikizo kuchokera m’chigawo cha Mawu a Mulungu okhala ndi mawu a ziweruzo zaumulungu zimene amalengeza motsutsana ndi Chikristu Chadziko. Mtumwiyo akulamulidwa kuyesa malo opatulika akachisi, kutanthauza kukwaniritsidwa kotsimikizirika kwa zifuno za Yehova kuloza ku makonzedwe akachisi ndikuti miyezo yaumulungu ifitsidwe ndi awo ogwirizana nayo. Ndiyeno ‘mboni ziŵiri’ zodzozedwa za Mulungu zikulosera zitavala chiguduli, ziphedwa, koma ziukitsidwa. Izi zikusonya ku nyengo ya 1918-19, pamene ntchito yawo yolalikira inatsala pang’ono kuphedweratu ndi adani, koma atumiki a Yehova anakhalitsidwanso amphamvu mozizwitsa kaamba ka uminisitala wawo.

Ufumu Wabadwa!

Kumveka kwa lipenga lachisanu ndi chiŵiri kulengeza kubadwa kwa Ufumu. (11:15–12:17) Kumwamba, mkazi wophiphiritsira (gulu lakumwamba la Yehova Mulungu) abala mwana wamwamuna (Ufumu wa Mulungu wokhala ndi Kristu monga Mfumu), koma chinjoka (Satana) chiyesa mosaphula kanthu kuulikwila. Mikayeli wolakika (Yesu Kristu) adzetsa nkhondo m’mwamba pachimake pambuyo pakubadwa kwa Ufumu mu 1914, kugwetsera ku dziko lapansi chinjokacho ndi angelo ake. Kumeneko chinjokacho chipitirizabe kuchita nkhondo ndi otsalira odzozedwa a mbewu ya mkazi wakumwamba.

Kenaka Yohane awona chilombo chimene chapangidwira fano lonyansa. (13:1-18) Chilombo chandale zadzikocho chimenechi chokhala ndi mitu isanu ndi iŵiri, ndi nyanga khumi chivuuka “m’nyanja,” magulu a anthu owinduka mwa amene maboma aumunthu achokera. (Yerekezerani ndi Danieli 7:2-8; 8:3-8, 20-25.) Kodi ndani yemwe ali magwero a ulamuliro wa cholengedwa chophiphiritsirachi? Eya, palibe wina kusiyapo kokha Satana, chinjokacho! Ndipo tangolingalirani! Ku chonyansa chandale zadzikocho, chilombo cha nyanga ziŵiri (Mphamvu Yadziko ya Anglo-Amereka) chiwoneka chikupanga “fano,” lodziŵika tsopano kukhala Mitundu Yogwirizana. Ambiri akakamizidwa kulambira chilombo ndi kulandira ‘chilembo’ chake mwakuchita zinthu m’njira yake ndi kumachilola kulamulira miyoyo yawo. Koma Mboni za Yehova zimakana kwamtu wagalu chilembo chauchiŵanda cha chilombocho!

Atumiki a Yehova Achitapo Kanthu

Atumiki a Mulungu osiyanasiyana awoneka akuchitapo kanthu pamene mbale zisanu ndi ziŵiri za mkwiyo wake zitsanulidwa. (14:1–16:21) Tamverani! Pa Phiri la Ziyoni lakumwamba, Yohane akhoza kumva a 144,000 akuimba ngati nyimbo yatsopano. Mngelo wouluka m’mlengalenga ali ndi uthenga wabwino wosatha woti aulalikire kwa okhala padziko lapansi. Kodi zimenezi zikusonyezanji? Kuti Mboni za Yehova ziri ndi chithandizo chaungelo m’kulengeza uthenga wa Ufumu.

Yohane ayenera kuzizwa powona mpesa wa dziko lapansi ukudulidwa ndi mitundu yonse ikuphwanyidwa pamene moponderamo mpesa mwa mkwiyo wa Mulungu mupondedwa. (Yerekezerani ndi Yesaya 63:3-6; Yoweli 3:12-14.) Polamulidwa ndi Yehova, angelo asanu ndi aŵiri atsanulira mbale zisanu ndi ziŵiri za mkwiyo waumulungu. Dziko lapansi, nyanja, ndi akasupe amadzi, limodzinso ndi dzuŵa, mpando wachifumu wa chilombo, ndi Mtsinje wa Firate, ziyambukiridwa ndi kutsanulidwa kwa mbale zisanu ndi imodzi zoyambirira. Talingalirani chisangalalo cha Yohane powona kuti manenanena auchiŵanda akusonkhanitsira mafumu aumunthu ku nkhondo ya Mulungu ya Harmagedo. Ndipo zotulukapo nzosakaza pamene mbale yachisanu ndi chiŵiri itsanulidwira pamphepo.

Akazi Aŵiri Ophiphiritsira

Ndithudi, Yohane asangalatsidwa ndi kuchitira umboni mapeto a Babulo Wamkulu, ulamuliro wadziko lonse wa chipembezo chonyenga, ndikuwona zochitika zokondweretsa zimene zitsatira chiwonongeko chake. (17:1–19:10) Woledzera ndi mwazi wa oyera mtima, iye awoneka atakwera pa chilombo chofiira chokhala ndi mitu isanu ndi iŵiri ndi nyanga khumi (Chigwirizano cha Mitundu ndi chochiloŵa m’malo, Mitundu Yogwirizana). Ha, nchiwonongeko chotani nanga chimene chikumgwera pamene nyangazo zitembenuka motsutsana naye!

Mawu ochokera kumwamba amveka kutamanda Ya chifukwa cha chiwonongeko cha Babulo Wamkulu. Ndipo nchitamando chomveka mwamphamvu chotani nanga chimene chilengeza ukwati wa Mwanawankhosa ndi mkwatibwi wake, odzozedwa oukitsidwawo!

Kristu Alakika ndi Kulamulira

Chotsatira Yohane awona Mfumu ya mafumu pamene iyo itsogolera magulu ankhondo akumwamba kuwononga dongosolo la zinthu la Satana. (19:11-21) Inde, Yesu, ‘Mawu a Mulungu,’ amenya nkhondo ndi amitundu. Mtumwiyo awona chilombo (gulu landale zadziko la Satana) ndi mneneri wonyenga (Mphamvu Yadziko ya Anglo-Amereka) zikuponyedwa “m’nyanja yamoto,” yophiphiritsira chiwonongeko chotheratu, chamuyaya.

Kodi nchiyani chikutsatira? Eya, Yohane awona kuponyedwa m’phompho kwa Satana. Pakutsatira chisonyezero chapasadakhale cha Kulamulira kwa Kristu Kwazaka Chikwi, pamene Yesu ndi olamulira anzake oukitsidwawo aweruza anthu, kufikitsa anthu omvera ku ungwiro! (20:1-10) Tsopano ndinthaŵi yachiyeso chomalizira. Atamasulidwa ku phompho, Satana adzanka kukasokeretsa anthu angwirowo, koma chiwonongeko chidzathetsa ntchito ya ziŵanda zonse ndi anthu opandukira Mulungu.

Kubwereranso kumbuyo m’nthaŵi, Yohane ayenera kukhala wotengeka maganizo chotani nanga kuwona onse akufa, ali m’Hade (manda wamba a anthu), ndi m’nyanja akuukitsidwa ndi kuweruzidwa pamaso pa Mulungu, amene wakhala pa mpando wachifumu waukulu woyera! (20:11-15) Ndipo ndimpumulo wotani nanga umene olungama adzasangalala nawo pamene imfa ndi Hade ziponyedwa m’nyanja yamoto, zosakhozanso kuwononga anthu!

Pamene masomphenya a Yohane afika kumapeto, iye awona Yerusalemu Watsopano. (21:1–22:21) Likulu laboma limenelo likutsika kuchokera kumwamba nilibweretsa kuwunika kwa mitundu. Woyenda kupyola m’Yerusalemu Watsopanoyo ndi “mtsinje wa madzi a moyo,” wochitira chithunzi chowonadi Chamalemba ndi makonzedwe ena onse operekedwa ndi Mulungu pamaziko a nsembe ya Yesu akuchiritsira anthu ku uchimo ndi imfa ndi kuŵapatsa moyo wosatha. (Yohane 1:29; 17:3; 1 Yohane 2:1, 2) Pamagombe onse aŵiri a mtsinjewu, Yohane awona mitengo yokhala ndi masamba ochiritsa, ochitira chithunzi mbali ya makonzedwe a Yehova yopereka moyo wamuyaya kwa anthu omvera. Mauthenga omalizira ochokera kwa Mulungu ndi Kristu atsatiridwa ndi chiitano. Ha, nkwabwino chotani nanga kumva mzimu ndi mkwatibwi akuitanira aliyense wakumva ludzu ‘kudzatenga madzi amoyo kwaulere’! Ndipo pamene tiŵerenga mawu otsekera a Chibvumbulutso, mosakaikira timagaŵanamo m’chilengezo chachangu cha Yohane chakuti: “Amen; idzani, Ambuye Yesu.”

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 21]

Khalani Ogalamuka: Mkati mwa mawu aulosi onena za nkhondo ya Mulungu ya Harmagedo (Armagedo), mukunenedwa kuti: ‘Tawonani, ndidza [Yesu Kristu] ngati mbala. Wodala iye amene adikira, nasunga zovala zake, kuti angayende wausiwa, nangapenye anthu usiwa wake.’ (Chibvumbulutso 16:15) Uku kungakhale kuloza ku maudindo a woyang’anira, kapena ofisala, wakachisi paphiri m’Yerusalemu. Mkati mwa ulonda, iye anayendayenda m’kachisi kuwona ngati alonda ake Achilevi anali ogalamuka kapena anali mtulo m’mbuto mwawo. Mlonda aliyense wopezedwa ali mtulo anakwapulidwa ndi mtengo, ndipo zovala zake zikatenthedwa monga chilango chonyazitsa. Popeza kuti Armagedo iri pafupi kwambiri tsopano, otsalira odzozedwa ‘ansembe achifumu’ kapena ‘nyumba yauzimu,’ ali otsimikiza mtima kukhala ogalamuka mwauzimu. Momwemonso ayenera kukhalira atsamwali awo, a ‘khamu lalikulu,’ okhala ndi chiyembekezo cha padziko lapansi, popeza kuti nawonso akutumikira Mulungu pa kachisi. (1 Petro 2:5, 9; Chibvumbulutso 7:9-17) Makamaka oyang’anira Achikristu ayenera kukhala atcheru kuyang’anira kuyambika kwa mikhalidwe yoipa mumpingo. Chifukwa chakuti iwo amakhala ogalamuka, alambiri okhulupirika onse pa kachisi wauzimu wa Mulungu amavalabe ‘zovala’ zawo, kutanthauza utumiki wawo wolemekezeka monga Mboni za Yehova.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena