Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 5/15 tsamba 3-4
  • Kodi Nchiyani Chimachititsa Chipsinjo M’banja?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nchiyani Chimachititsa Chipsinjo M’banja?
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zifukwa Zina Zochititsa Chipsinjo m’Banja
  • Mavuto A Banja—Chizindikiro cha Nthaŵi
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Pali Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja?
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Ikani Mulungu Patsogolo m’Moyo Wanu Wabanja!
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Yehova Ndiye ‘Linga Lathu M’nyengo ya Nsautso’
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 5/15 tsamba 3-4

Kodi Nchiyani Chimachititsa Chipsinjo M’banja?

‘NGWAULESI uyu!’ Anazaza motero Bob. ‘Iye sadziŵa konse kusamala nyumba!’

‘Sizowona zimenezo!’ anayankha mwaukali Jean. ‘Iye samayamikira chirichonse chimene ndimachita. Sindinawonepo mwamuna wosuliza wotere.’

Kodi chinalakwika nchiyani m’moyo wa Bob ndi Jean?a Ukwati wawo watsopanowo unali wa miyezi inayi yokha, koma udayandikira kale tsoka. Komabe, nkhani yawo siyapadera, popeza kuti kupenda koŵerangera kumasonyeza kuti kusamvana kwa muukwati nkofala. Akatswiri tsopano akunena kuti theka la maukwati onse mu United States adzathera m’chisudzulo. Mofananamo kupenda koŵerengera kochititsa chisoni kumachokera ku maiko ena ambiri. Chikhalirechobe, chisudzulo changokhala mbali ya chithunzicho. Mabanja ali m’kupsinjika, m’ziŵerengero zopambana koposa ndi zifukwa zosiyanasiyana.

Zifukwa Zina Zochititsa Chipsinjo m’Banja

Ana amayambukiridwa kwakukulu patakhala mikhalidwe yopsinja m’banja. Magazini a Newsweek akusimba kuti: “Chigawo chimodzi mwa zitatu cha ana onse obadwa m’zaka khumi zapitazo [mu United States] mwinamwake adzakhala m’banja la kholo lopeza asanafike msinkhu wa zaka 18. Mmodzi mwa ana anayi alionse lerolino amaleredwa ndi kholo limodzi. Pafupifupi 22 peresenti ya ana lerolino anabadwira kunja kwaukwati; mwa amenewo, pafupifupi chigawo chimodzi mwa zitatu anabadwa kwa mayi wa zaka zapakati pa 13 ndi 19.”

Posonyeza chochititsa kupsinjika m’banja china, katswiri wopenda nkhanza pa ana J. Patrick Gannon akuti: “Kupenda kwaposachedwapa kukusonyeza kuti anthu mamiliyoni makumi ambiri anakulira m’mabanja a moyo woipa mmene chiwawa, kugonana kwapachibale, kapena nkhanza ya malingaliro zochititsidwa ndi uchidakwa zinali chochitika cha tsiku ndi tsiku.” Nzosadabwitsa kuti ana ambiri okhala m’zinthu zoterozo sangadziŵe kupeŵa chipsinjo cha m’banja atakula.

Openyerera ena angaike mlandu wa kupsinjika kwa m’banja pa masinthidwe a zachuma, mayanjano, ndi makhalidwe omwe afalikira m’maiko otsungula. Mwachitsanzo, kuloŵa ntchito kwa akazi ochuluka kwadzetsa kulinganizanso kovutitsa kwa ntchito ndi mathayo apanyumba. Anakubala amasusukira maluso a ntchito zovuta, atate amalimbana ndi ntchito zapanyumba monyumwa, ndipo ana amakakamizika mwamisozi kuzoloŵera moyo wa ku malo olererako ana masana.

Mabanja ambiri ali pansi pachipsinjo chachikulu m’maiko onse padziko lapansi. Kholo lina logwira ntchito linayerekezera chimenechi ndi “kukhala m’dziko lokhala pachiletso chosatha.” Nzosadabwitsa kuti pafupifupi theka la ofunsidwa mkati mwa kufufuza kwa Gallup kwaposachedwapa ananena kuti ‘banja la Chimereka lerolino laipa kuposa mmene linaliri zaka 10 zapitazo,’ ndipo ochepa okha ndiwo anakhulupirira kuti mkhalidwewo udzawongokera.

Chotero chipsinjo cha m’banja chiri mutu wa nkhani yokambirana yosatha pa wailesi yakanema ndi pa wailesi wamba. Anthu amasanthula m’mabuku opereka uphungu wodzithandiza pawekha m’zabanja, ena akumapereka uphungu wina wabwino ndi wogwira ntchito. Ngakhale kuti chilangizo cha ‘kulankhulana momasuka kwambiri’ kapena ‘kukambitsirana zakukhosi’ chingakhale chothandiza, icho chimalephera kuthetsa chochititsa chenicheni cha mavuto a m’banja. Nkhani yotsatira idzatero ndipo idzasonyeza mmene tingalakire chipsinjo m’banja.

[Mawu a M’munsi]

a Maina opeka agwiritsiridwa ntchito kusunga chinsinsi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena