Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 5/15 tsamba 8-9
  • Kudzanja Lamanja la Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kudzanja Lamanja la Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Kudzanja Lamanja la Mulungu
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Khristu Anakhala Kudzanja Lamanja la Mulungu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Pa Njira ya ku Damasiko
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Kodi Amene Amachita Zinthu Zoipa Angasinthe?
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 5/15 tsamba 8-9

Moyo ndi Uminisitala za Yesu

Kudzanja Lamanja la Mulungu

KUTSANULIDWA kwa mzimu woyera pa Pentekoste kuli umboni wakufika kwa Yesu kumwamba. Masomphenya opatsidwa mwamsanga pambuyo pake kwa wophunzira Stefano akutsimikiziranso kuti Iye wafika kumeneko. Asanaponyedwe miyala kaamba ka kuchitira umboni kokhulupirika, Stefano akufuula kuti: “Taonani, ndipenya m’Mwamba motseguka, ndi Mwana wa munthu alikuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu.”

Pamene ali ku dzanja lamanja la Mulungu, Yesu akudikira lamulo lochokera kwa Atate wake lakuti: ‘Chitani ufumu pakati pa adani anu.’ Koma pakali pano, kufikira pamene adzachitapo kanthu motsutsana ndi adani ake, kodi Yesu akuchitanji? Iye akulamulira, kapena kuchita ufumu, pa ophunzira ake odzozedwa, kuwatsogolera m’ntchito yawo yolalikira ndi kuwakonzekeretsa, mwachiukiriro, kukhala mafumu anzake mu Ufumu wa Atate wake.

Mwachitsanzo, Yesu akusankha Saulo (wodziŵika bwino pambuyo pake ndi dzina lake Lachiroma, Paulo) kupititsa patsogolo ntchito yopanga ophunzira m’maiko ena. Saulo ngwachangu m’kuchita Chilamulo cha Mulungu, komabe, iye ngosokeretsedwa ndi atsogoleri achipembedzo Achiyuda. Monga chotulukapo, Saulo sakungovomereza kuphedwa kwa Stefano komanso amkanso ku Damasiko mwachilolezo chochokera kwa mkulu wansembe Kayafa kuti akatenge omangidwa amuna ndi akazi onse omwe iye apeza kumeneko okhala atsatiri a Yesu ndi kuwabweretsa ku Yerusalemu. Komabe, pamene Saulo ali paulendowo, mwadzidzidzi pachezima kuunika komzinga ndipo agwera pansi.

“Saulo, Saulo, Undilondalonderanji?” likufunsa motero liwu lochokera kumagwero asawoneka. “Ndinu yani Ambuye?” Saulo afunsa motero.

Pamveka yankho lakuti: “Ndine Yesu amene umlondalonda.”

Saulo, yemwe wachititsidwa khungu ndi kuunika kozizwitsako, akuuzidwa ndi Yesu kuloŵa m’Damasiko ndikuyembezera malangizo. Kenaka Yesu awonekera m’masomphenya kwa Hananiya, mmodzi wa ophunzira ake. Ponena za Saulo, Yesu akuuza Hananiya kuti: ‘Iye ndiye chotengera changa chosankhika, chakunyamula dzina langa pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israyeli.’

Ndithudi, ndi chichirikizo cha Yesu, Saulo (tsopano wodziŵika monga Paulo) ndi olengeza ena akhala ndi chipambano chachikulu m’ntchito yawo yolalikira ndi kuphunzitsa. Kwenikweni, pafupifupi zaka 25 pambuyo pa kuwonekera kwa Yesu kwa iye pamsewu wopita ku Damasiko, Paulo akulemba kuti “uthenga wabwino” wakhala ‘ukulalikidwa m’chilengedwe chonse pansi pa thambo.’

Patapita zaka zambiri, Yesu apereka mpambo wa masomphenya kwa mtumwi wake wokondedwa, Yohane. Mwamasomphenya ameneŵa omwe Yohane akuwalongosola m’bukhu la Baibulo la Chibvumbulutso, iye, kwenikweni, akukhalabe ndimoyo ndikuwona Yesu akubweranso muulamuliro wa Ufumu. Yohane akunena kuti ‘mwakugwidwa ndi mzimu’ anaperekedwa kutsogolo m’nthaŵi ya “tsiku la Ambuye.” Kodi limeneli ndi “tsiku” lotani?

Kuphunzira kosamalitsa kwa maulosi a Baibulo, kuphatikizapo ulosi wa Yesu iyemwini wonena za masiku otsiriza, kumavumbula kuti “tsiku la Ambuye” linayamba m’chaka chopanga mbiri cha 1914, inde, mkati mwa mbadwo unowu! Chotero munali mu 1914 pamene Yesu anabweranso mosawoneka ndi maso, popanda dzoma lachisangalalo la anthu ndipo atumiki ake okhulupirika okha ndiwo anadziŵa za kubweranso kwake. M’chaka chimenecho Yehova anapatsa Yesu lamulo lakukachita ufumu pakati pa adani ake!

Pomvera lamulo la Atate wake, Yesu anayeretsa kumwamba mwakupitikitsa Satana ndi ziŵanda zake, akuwaponyera kudziko lapansi. Powona zimenezi zitachitika m’masomphenya, Yohane akumva liwu lakumwamba likulengeza kuti: ‘Tsopano zafika chipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Kristu wake.’ Inde, Kristu anayamba kulamulira monga Mfumu mu 1914!

Ha, imeneyi ndi mbiri yabwino chotani nanga kwa alambiri a Yehova akumwamba! Iwo asonkhezeredwa kuti: “Kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo.” Koma kodi mkhalidwe kwa awo okhala padziko lapansi ngwotani? Liwu lochokera kumwambalo likupitiriza kuti, ‘Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.’

Tikukhala m’kanthaŵi kameneko patsopanoli. Anthu tsopano lino akulekanitsidwa kaya kudzaloŵa m’dziko latsopano la Mulungu kapena kudzawonongedwa. Chowonadi nchakuti, mtsogolo mwanu tsopano mukusankhidwa ndi mmene mukuchitira ku mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu imene ikulalikidwa padziko lonse lapansi pansi pa chitsogozo cha Kristu.

Pamene kulekanitsidwa kwa anthu kwatha, Yesu Kristu adzatumikira monga Nthumwi ya Mulungu kuchotsa padziko lapansi dongosolo la zinthu lonse la Satana ndi onse olichirikiza. Yesu adzachotsa kuipa konseku pa nkhondo yotchedwa Harmagedo, kapena Armagedo m’Baibulo. Pambuyo pake, Yesu, Munthu wamkulu koposa m’chilengedwe chonse wachiŵiri kwa Yehova Mulungu mwiniyo, adzagwira Satana ndi ziŵanda zake ndi kuŵamanga kwa zaka chikwi ku “phompho,” ndiko kuti, kukhala mumkhalidwe wosakhoza kuchita kanthu monga wakufa. Machitidwe 7:55-60; 8:1-3; 9:1-19; 16:6-10; Salmo 110:1, 2; Ahebri 10:12, 13; 1 Petro 3:22; Luka 22:28-30; Akolose 1:13, 23; Chibvumbulutso 1:1, 10; 12:7-12; 16:14-16; 20:1-3; Mateyu 24:14; 25:31-33.

◆ Yesu atakwera kumwamba, kodi akuikidwa kuti, ndipo kodi akudikira chiyani?

◆ Kodi Yesu akulamulira pa yani pambuyo pokwera kumwamba, ndipo kodi ndimotani mmene ulamuliro wake ukuwonekera?

◆ Kodi “tsiku la Ambuye” linayamba liti, ndipo chinachitika nchiyani pakuyamba kwake?

◆ Kodi ndintchito yakulekanitsa yotani imene ikuchitika lerolino imene ikuyambukira aliyense wa ife, ndipo kodi kulekanitsako kukuchitidwa pamaziko otani?

◆ Pamene ntchito yolekanitsa itha, kodi padzatsatira zochitika zotani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena