Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 7/1 tsamba 20-23
  • ‘Kukhala ndi Moyo Tikukumbukira Kuyandikira kwa Tsiku la Yehova’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Kukhala ndi Moyo Tikukumbukira Kuyandikira kwa Tsiku la Yehova’
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Utumiki wa pa Beteli
  • Sukulu Yautumiki Wateokratiki
  • Kuyendayenda
  • Ndipeza Mnzanga
  • Kuwona Dalitso la Yehova
  • Ndikuyembekezerabe Tsiku la Yehova
  • Madalitso Amene Ndapeza mu Utumiki wa Nthawi Zonse
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Moyo Waulemerero Potumikira Yehova
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Moyo Wanga m’Gulu Lotsogozedwa ndi Mzimu la Yehova
    Nsanja ya Olonda—1988
  • “Tangochita Zimene Tayenera Kuzichita”
    Nsanja ya Olonda—1998
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 7/1 tsamba 20-23

‘Kukhala ndi Moyo Tikukumbukira Kuyandikira kwa Tsiku la Yehova’

MONGA MOMWE YASIMBIDWIRA NDI LYLE REUSCH

KUCHOKERA pamene ndikuyambira kukumbukira, moyo wathu wabanja unazikidwa pa chikhulupiriro cholimba chakubwera kwa dziko latsopano lolungama. Amayi ndi abambo ankatiŵerengera Baibulo anafe ponena za ‘miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano’ ndi ponena za ‘ng’ombe yaikazi ndi chirombo zikudyera pamodzi, mkango ukudya udzu ngati ng’ombe, ndi mwana wam’ng’ono akuzitsogolera.’ Iwo anadzimvetsa kukhala zenizeni kwakuti, ndinadziyerekeza kukhala mwana wamng’ono ameneyo.​—2 Petro 3:11-13; Yesaya 11:6-9.

M’ma 1890 agogo anga aamuna, a August Reusch, adaphunzira zowonadi zoyambirira za Baibulo kupyolera mwa kulemberana makalata ndi Charles T. Russell. Iwo analalikira kwambiri mkati ndi kunja kwa mudzi wawo mu Chigawo cha Kumpoto koma Chakumadzulo kwa Canada, tsopano chotchedwa Yorkton, ku Saskatchewan. Iwo analangiza ana awo aamuna mobwerezabwereza kuti: “Anyamatanu, chenjeranitu ndi 1914!” Chitsimikizo chakuti tsiku la Yehova linayandikira chinawapatsa abambo ŵanga lingaliro la kufulumira limene linapitirizabe m’nthaŵi ya moyo wawo wonse ndipo imeneyo ndiyo yakhala njira ya moyo wanga.

Amayi ndi Atate adali ochereza kwabasi. Gulu lophunzira Baibulo la Saskatoon, Saskatchewan, Mpingo wa Ophunzira Baibulo linakumana mokhazikika m’nyumba mwathu. Aminisitala oyendayenda (otchedwa oyendayenda achipembedzo) kaŵirikaŵiri anakhala m’nyumba mwathu. Mchimwene wanga, Verne, ndi mchemwali wanga, Vera, ndi ine tinapindula mwauzimu. Nthaŵi zonse panali lingaliro la zinthu zenizeni za uthenga wa Ufumuwo ndi kufunika kofulumira kwa kuuza ena ponena za uwo. (Mateyu 24:14) Sindinalingalire kuti m’zaka zamtsogolo ndikathera mbali yaikulu ya moyo wanga ndikupitiriza ntchito ya oyendayenda achipembedzo ameneŵa mwakutumikira monga woyang’anira woyendayenda wa Mboni za Yehova.

Mu 1927, Atate anasamutsira banja ku Berkeley, California. Kenaka, mkati mwenimweni mwa chipsinjo chachuma mu 1933, ndinamaliza sukulu ya sekondale. Mchimwene wanga, Verne, ndi ine tinadziwona kukhala amwaŵi kuti tinapeza ntchito pa fakitale ya Ford Motor Company mu Richmond, California. Komabe, tsiku lina m’ngululu ya mu 1935, ndinalingalira kuti: ‘Ngati ndiyenera kugwira ntchito zolimba, ndingagwirire ntchito zolimba chimene chiri chaphindu.’ Tsiku limenelo ndinaleka ntchito, ndipo tsiku lotsatira ndinalemba kalata yopempha chofunsirapo utumiki wa pa Beteli, malikulu a padziko lonse a Mboni za Yehova, mu Brooklyn, New York. Pambuyo popezeka pamsonkhano wosangalatsa mu Washington, D.C., mu June 1935, ndinaitanidwa ku utumiki wa pa Beteli.

Utumiki wa pa Beteli

Nathan Knorr, manijala wa fakitale, anandiika pantchito yosamala zimango. Ndinalimo ndekha. Monga mnyamata wa zaka 20, ndinadzimva kukhala wofunika kwambiri. Ndinali ndi ufulu wakufika ku mbali zonse za fakitale, ndipo palibe amene anandifunsa chomwe ndinkachita. Mbale Knorr anayamikira mmene ndinagwirira ntchito yanga, koma anazindikira vuto la mkhalidwe. Anapitirizabe kumandisonkhezera kuti ndikulitse mkhalidwe wodzichepetsa.

Komabe, m’kupita kwanthaŵi, ndinazindikira kuti Mbale Knorr ankayesayesadi kundithandiza. Chotero ndinapepesa kaamba ka mkhalidwe wanga ndikusonyeza kutsimikiza mtima kwakuti ndikachita bwinopo. Ndiko kunali kuyambika kwa unansi wabwino, wautali ndi Mbale Knorr, yemwe mu January 1942 anakhala pulezidenti wachitatu wa Watch Tower Society.

Kuwonjezera pa kugwira ntchito yosamalira zimango, ndinaphunzira kugwiritsira ntchito makina ambiri m’dipatimenti yomanga mabuku kapena kuthandiza. M’kupita kwa nthaŵi ndinagwira ntchito ya muofesi, kulemba ndikutumiza maoda a ntchito m’fakitale. Nyengo za ngululu ndi chilimwe mu 1943 zinalidi zotanganitsa kwenikweni ndi zosangalatsa. Dziko lidali mkati mwa Nkhondo Yadziko ya II, ndipo Mboni za Yehova zinapirira kuvutidwa, kumangidwa, ndi zilango za m’ndende pa milandu yosalungama ya mtundu uliwonse. Mu 1940 Khoti Lalikulu la ku United States lidalamula kuti masukulu akafuna ophunzira kupereka sawatcha ku mbendera. Ichi chinabutsa funde la chiwawa m’madera 44 a madera 48 panthaŵiyo. Ana a Mboni anapitikitsidwa pasukulu, makolo anamangidwa, ndipo magulu achiwawa anapitikitsa Mboni kuchoka mumzinda. Ena anawomberedwa mfuti, enanso anapakidwa phula ndikusomekedwa nthenga.

Pamene Mboni za Yehova zinalimbana m’makhoti, mtokoma wa zikalata za khoti, za loya, ndi zolembedwa ndi bungwe lalamulo la Sosaite zinabwera pa desiki langa kuti zisindikizidwe. Tonsefe tinagwira ntchito kwa maola ambiri kuti timalize m’nthaŵi yake. Zigamulo zotulukapo za Khoti Lalikulu mu May ndi June mu 1943​—pamene milandu 12 mwa 13 inaweruzidwa moyanja Mboni za Yehova​—zakhala mbali ya zolembedwa zosungidwa za mbiri yakale yalamulo. Ndiri wachisangalalo kudziwonera ndekha mmene Yehova anatsegulira njira ya kutetezeredwa ndi kukhazikitsidwa mwalamulo kwa mbiri yabwino.​—Afilipi 1:7.

Sukulu Yautumiki Wateokratiki

M’njira zina sitinali okonzekeretsedwa mokwanira m’masikuwo kukwaniritsa ntchito yaikuluyo yonenedweratu pa Mateyu 24:14, ndiyo, ‘kulalikira [mbiri yabwino, NW] ya Ufumu m’dziko lonse lapansi mapeto asanafike.’ Mbale Knorr, monga pulezidenti wa Sosaite, anawona kufunika kwa programu yakuphunzitsa. Pamodzi ndi ziŵalo zina zazimuna za banja la Beteli, ndinalandira kalata yondipempha kulembetsa mu “Kosi Yopita Patsogolo mu Utumiki Wateokratiki.” M’kupita kwa nthaŵi inafikira kukhala Sukulu Yautumiki Wateokratiki, imene yakhala ikugwira ntchito m’mipingo ya Mboni za Yehova chiyambire mu 1943.

Tinasonkhana m’chipinda chokumanira cha banja la Beteli pa Lolemba madzulo, February 16, 1942, ndipo Mbale Knorr anapereka nkhani yachilangizo yoyamba. Mutu wa nkhani yake unali wakuti “Malembo Apamanja a Baibulo.” Mbale T. J. Sullivan anali woyang’anira sukulu ndipo anatipatsa uphungu kutithandiza kuwongokera. M’kupita kwa nthaŵi ndinapatsidwa gawo limeneli la woyang’anira sukulu ya Beteli, limene ndinaliwona kukhala mwaŵi waukulu kwabasi. Koma inalinso nthaŵi yakulangidwa.

Ndinali wosuliza mopambanitsa ndi wopanda ulemu woyenera popatsa uphungu mbale wokulirapo, chotero Mbale Knorr anandiuza mosabisa kuti: “Palibe amene amasangalatsidwa pamene umasonyeza ulamuliro modzikuza.” Pamene anafotokoza mfundo yake momvekera ndipo makutu anga anafiira chifukwa cha manyazi, maso aakulu a Mbale Knorr anafeŵa. Ndi liwu lachifundo, anaŵerenga Salmo 141:5 kuti: “Akandipanda munthu wolungama; chidzakhala chifundo: ndipo akandidzudzula; adzakhala mafuta abwino koposa, amene sadzaswa mutu wanga.” (King James Version) Ndagwiritsira ntchito lembali nthaŵi zambiri pamene lakhala thayo langa kupereka uphungu wowongolera kwa ena.

Sukulu Yautumiki Wateokratiki isanayambe, ochepa okha aife ndife tinali ndi mwaŵi wakulankhula poyera. Pamene Mbale Rutherford anamwalira, Mbale Knorr anagwira ntchito zolimba kukulitsa luso lake lakulankhula. Chipinda changa cha pa Beteli chinali mwachindunji pansi pa chipinda chake, ndipo ndinkamumva akuyeseza nkhani zake. Nthaŵi zambiri, anaŵerenga mofuula nkhani yapoyera yakuti “Mtendere​—Kodi Ungakhalitse?” asanaikambe pamsonkhano wa ku Cleveland mu 1942.

Kuyendayenda

Pambuyo pakutumikira pa Beteli kwa zaka 13, Mbale Knorr anandigaŵira kukatumikira m’munda monga woyang’anira chigawo. Pondilimbikitsa pa gawo langa latsopano, iye anati: “Lyle, tsopano uli ndi mwaŵi wakudziwonera wekha mmene Yehova amachitiradi ndi anthu ake.” Ndi mfundo imeneyi m’maganizo ndi masutikesi aŵiri kumanja, ndinayamba ntchito yanga monga woyang’anira woyendayenda pa May 15, 1948. Ndisanayambe ntchito yamgawo, ndinatumikira monga woyang’anira dera kwa miyezi yoŵerengeka.

Gulu loyamba, kapena mpingo, umene ndinatumikira unali waung’ono wakumudzi ku Waseca, Minnesota. Ndinalemba kalata pasadakhale kwa Dick Cain, mtumiki wa gululo (mmene anatchedwera woyang’anira wotsogoza panthaŵiyo) kuti akandichingamire ku sitima. Iye adali mpainiya wapadera, ndipo kuti achepetseko ndalama zowonongedwa, anali atangosamuka kumene kuchoka mu chipinda chake chomwe ankachita lendi m’nyengo yachisanu, kupita kunyumba yake ya m’nyengo yachilimwe, hema. Komabe, Minnesota siimatentha kwenikweni mu May! Usikuwo, ndikunthunthumira m’hemamo, ndinazizwa kaya ngati ndinali woyenera njira imeneyi ya moyo. Ndinadwala chimfine chimene chinatha milungu yambiri, koma ndinachira.

Mkati mwa zaka zoyambirira zimenezo pochezetsa mipingo yosiyanasiyana ndi madera, ndinakhala m’nyumba za abale, ndi katundu yongokwana m’sutikesi. Ndinagona m’nyumba za mitundu yonse, kuphatikizapo kugona pansi m’kitchini, pa makama a m’chipinda chochezeramo, m’tizipinda totentha topanda mazenera. Nthaŵi zina ndinakhala m’nyumba zimene chiŵalo cha banja chinali chotsutsa zikhulupiriro zathu. Mu Wisconsin mwamuna wosakhulupirira ankandiyang’ana ndi diso lankhalwe pamene ndinkabwera ndi kuchoka panyumba kwa mlungu wonse. Pamene anabwera kunyumba woledzera usiku wina, ndipo ndinamumva akuwopseza “kuwombera mfuti munthu wakutiwakuti,” ndinagamula kuti basi ndiyo nthaŵi yakuti ndichokepo. Koma zokumana nazo zodzitsutsa ndekha zinali zakamodzikamodzi ndipo zinangowonjezera ubwino wa gawo langa. Izo zinali chinthu chosangalala nacho pambuyo pake.

Ndipeza Mnzanga

Ndikukumbukira bwino lomwe. Pamsonkhano wadera mu Tiffin, Ohio, ndinakumana ndi dona wachichepere wokongola, wa maso obiriŵira, Leona Ehrman, wochokera ku Fort Wayne, Indiana. Iyenso analeredwa m’chikhulupiriro Chachikristu ndipo adali mpainiya wokhulupirika kwa zaka zingapo. Kuyendayenda kwa nthaŵi zonse sikunachipangitse kukakhala chotheka kumakumana monga opalana ubwenzi, koma tinalemberana makalata. Ndiyeno, mu 1952, ndinafunsa kuti, “Kodi udzatero?” ndipo anati, “Inde, ndidzatero!” choncho tinatero. Tinakwatirana. Kaŵirikaŵiri takhala tikufunsidwa chifukwa chake sitinakhazikike kuti tikhale ndi nyumba ndi banja, koma timati tiri nalo banja​—abale, alongo, atate, ndi amayi m’madera 44 kumene tatumikira.​—Marko 10:29, 30.

Ena afunsa kuti, ‘Kodi simunatopepo ndikufuna kuleka?’ Indedi, koposa kamodzi. Koma pakati pa aŵirife, pamene wina wafooka, wina amakhala wolimba. Panthaŵi inayake ndinalemberadi kalata mchimwene wanga, Verne, kumfunsa ngati kunali kotheka kugwira naye ntchito m’bizinesi yake yopaka utoto. Iye anandiyankha kuti kaŵirikaŵiri anayembekezera chimenecho chifukwa chakuti tinkamvana kwambiri pamene tinali kukula. Komabe, iye anandilangiza kuti ndiyenera kuchipenda mosamalitsa chosankha changa. Kenaka ndinakumbukira mawu obwerezedwabwerezedwa a Mbale Knorr kwa ziŵalo za banja la Beteli akuti: “Kuleka sikumalira kuyesayesa kwamphamvu; koma kukhalabe m’gawo lanu kumalira kulimbika mtima ndi umphumphu.” Umenewo udali uphungu wabwinobe.

Palibe woyang’anira woyendayenda wokwatira yemwe angakhale kwa nthaŵi yaitali m’gawo lake popanda mkazi wokhulupirika ndi wochirikiza, monga momwe Leona wakhaliradi kwa ine. Umunthu wake wachifundo, ndi wachikondi ndi mkhalidwe wansangala m’mipingo unampangitsa kukondedwa ndi anthu zikwizikwi. Sindimatopa konse kumuuza mmene ndimamkondera. Ndine wotsimikiza kuti, chimenecho chimamthandiza nayenso kumamatira ku ntchitoyo.

Kuwona Dalitso la Yehova

Ntchito yaikulu ya woyang’anira chigawo imakhala pa msonkhano wadera, kumene amatumikira mlungu uliwonse monga tcheyamani, wokamba nkhani poyera, ndi woyang’anira sukulu. Dalitso la Yehova pa kakonzedweka likuwoneka m’chenicheni chakuti mwa mazana a misonkhano yadera imene ndaiyang’anira, palibe ndi umodzi womwe umene unalephera kuchitidwa. Zowona, ina inadodometsedwa, koma palibe umene unachotsedwapo.

Mu Wooster, Ohio, m’ngululu ya 1950, pamene ndinaitanira nyimbo yotsekera gawo lausiku pa Loŵeruka, gulu lachiwawa la otsutsa oposa chikwi chimodzi anasonkhana panja pa holo imene msonkhanowo unkachitidwira. Gululo linabweretsa mabokosi a mazira owola oti atiponye nawo potuluka. Chotero tinapenda mkhalidwewo ndikupitirizabe programuyo ndi nyimbo, zokumana nazo, ndi nkhani Zabaibulo zamwadzidzidzi. Mbonizo zokwanira 800 zinakhala bata ndi kukhazika mtima.

Pa 2:00 a.m., mphepo inazizira kwenikweni. Monga ngati kuti tikukonzekera kutuluka, akalinde anatulutsa mapaipi ozimira moto ndikuyamba kutsuka mazira omwe anagwera pa kanjira ka kutsogolo. Gululo linasonkhananso, likuchoka pa depo ya mabasi pofunda. Koma mchitidwe wa akalindewo unali machenjera, ndipo tinauza omvetserawo kutulukira khomo lakumbuyo mwakachetechete. Onse anafika ku magalimoto awo mwachisungiko. Kudodometsedwa ndi gulu lachiwawa kunachitikanso pa misonkhano ina ya ku Ohio, mu Canton, Defiance, ndi Chillicothe. Koma chiwawa cha gulu chinali kucheperachepera, pamene zigamulo za Khoti Lalikulu la ku United States zotiyanja zinayamba kukhala ndi chiyambukiro pa osayeruzika.

M’kupita kwa nthaŵi mavuto a thanzi anapangitsa kusintha kukhala kofunika. Chotero m’kati mwa ma 1970, Sosaite mwachifundo inandigaŵira kukatumikira monga woyang’anira dera kum’mwera kwa California kumene mipingo iri pafupipafupi ndipo zipatala ziriko. Pamene kuli kwakuti ntchito za woyang’anira chigawo zimaloŵetsamo kuyenda maulendo aatali ndi kusamalira ndi kuyang’anira madera ambiri, ntchito za woyang’anira dera zimaloŵetsamo kukonza misonkhano yadera ndi kugaŵira ndi kuyeseza mbali za programu. Kuwonjezerapo, Sukulu Zautumiki Waupainiya zimafunika kukonzedwa ndi kutumikiridwa. Chotero ntchito ya oyang’anira oyendayenda, kaya achigawo kapena adera, ndinjira ya moyo yanthaŵi yonse, ndi yofupa.

Ndikuyembekezerabe Tsiku la Yehova

Kuchokera pa zikumbukiro zanga zoyambirira zaka zoposa 70 zapitazo, nthaŵi zonse ndakhala ndi lingaliro lakufulumira. Nthaŵi zonse Armagedo, m’kuganiza kwanga, yakhala mkucha. (Chibvumbulutso 16:14, 16) Mofanana ndi abambo ŵanga, ndi abambo awo iwo asanakhale, ndakhala ndi moyo monga momwe mtumwi anafulumizira kuti, ‘khalani akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu.’ Nthaŵi zonse ndakhala ndikulingalira dziko latsopano lolonjezedwalo kukhala ‘chenicheni chosapenyeka.’​—2 Petro 3:11, 12; Ahebri 11:1, NW.

Chiyembekezo chimenechi chokhomerezedwa mwa ine kuchokera kuubwana chidzakwaniritsidwa posachedwapa. ‘Ngo’mbe yaikazi ndi chirombo zidzadya pamodzi,’ “mkango udzadya udzu ngati ng’ombe,” ndipo “mwana wamng’ono adzazitsogolera.” (Yesaya 11:6-9) Malonjezo osangalatsa mtima oterowo akutsimikiziridwa ndi mawu a Yesu kwa Yohane pa Chibvumbulutso 21:5: ‘Iye wakukhala pa mpando wachifumu anati, Tawonani, ndichita zonse zikhale zatsopano.’ Ndiponso, iye anati: ‘Talemba; pakuti mawu aŵa ndi okhulupirika ndi owona.’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena