Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 7/15 tsamba 23-26
  • Achichepere Achikristu Khalani Olimba M’chikhulupiriro

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Achichepere Achikristu Khalani Olimba M’chikhulupiriro
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chake Chikhulupiriro Cholimba Nchofunika
  • ‘Khalani Wokonzeka Kuchita Chodzikanira’
  • ‘Chitani Chodzikanira Kwa Aliyense’
  • Chithandizo Chiripo
  • Kukhulupirika Kumadzetsa Madalitso
  • Kodi Ndingatani Akamanditonza?
    Galamukani!—1999
  • Achinyamatanu—Yehova Sadzaiŵala Ntchto Yanu!
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kodi Ndingalalikire Bwanji Anzanga a Kusukulu?
    Galamukani!—2002
  • Achinyamata, Khalani ndi Mtima Wokonda Kwambiri Kutumikira Yehova
    Nsanja ya Olonda—2010
Nsanja ya Olonda—1991
w91 7/15 tsamba 23-26

Achichepere Achikristu Khalani Olimba M’chikhulupiriro

“ALIYENSE ayenera kupezekako.” Chimenechi ndicho chinali chilengezo. Ophunzira onse pasukulu inayake ku Japan anafunikira kupezeka kumsonkhano waukulu m’holo. Wophunzira Wachikristu wachichepere sanavomereze malingaliro ena olongosoledwa m’nyimbo ya sukuluyo. “Chabwino,” iye analingalira motero, “ndidziŵa kuti nyimbo ya sukulu idzaimbidwa. Koma sindidzakhala ndi vuto lirilonse. Ndidzangokhala kumbuyo mwanthaŵi zonse.”

Komabe, pamene Mboni ya Yehova yachichepereyo inaloŵa m’holomo, inapeza kuti aphunzitsi onse anakhala kale pa mipando yakumbuyo. Chotero, iye anayenera kukhala patsogolo pawo. Pamene ophunzira ena anaimirira kuti ayimbe nyimboyo, iye mwaulemu anali chikhalirebe. Koma aphunzitsiwo anakwiya nazo zimenezi. Anayesa kumkakamiza mwamphamvu kuti aimirire. Kodi mungadziyerekezere mumkhalidwe woterowo? Kodi inuyo mukanachitanji?

Chifukwa Chake Chikhulupiriro Cholimba Nchofunika

Kukanakhala bwino ngati anthu awaleka Akristu ndikuwalola kukhala ndi moyo mogwirizana ndi chikumbumtima chawo chophunzitsidwa ndi Baibulo. Komabe, kaŵirikaŵiri, Akristu amayang’anizana ndi mikhalidwe yopsinja. Izi siziyenera kutidabwitsa, popeza kuti Mwana weniweniyo wa Mulungu, Yesu Kristu, anati: “Ngati iwo andizunza, iwo adzakuzunzaninso.” (Yohane 15:20, NW) Kuwonjezera pa chizunzo chachindunji, atumiki a Yehova amayang’anizana ndi ziyeso zina zosiyanasiyana za chikhulupiriro.

Kaŵirikaŵiri achichepere Achikristu amafunikira chikhulupiriro cholimba kuti ayang’anizane ndi mayesero omwe amakumana nawo kusukulu. Iwo angakakamizidwe kumayanjana ndi anzawo am’kalasi amene amalankhula chinenero choipa kapena okhala ndi maganizo otonza Mulungu. Akristu achichepere angayang’anizane ndi chisonkhezero chachikulu cha kusankhana mtundu ndi kukakamizidwa kuloŵa m’makalabu, m’ndale zadziko zapasukulu, kapena machitachita ena amene angakhale onyonyotsola mwauzimu. Aphunzitsi kapena ophunzira anzawo angayese kuika chitsenderezo pa Akristu achichepere kuti alolere molakwa. Chifukwa chake, achichepere opembedza ayenera kudalira pa mzimu wa Yehova kaamba ka chikhulupiriro chofunikira kuti achite chodzikanira chowonekera bwino cha chiyembekezo chawo.​—Mateyu 10:19, 20; Agalatiya 5:22, 23.

‘Khalani Wokonzeka Kuchita Chodzikanira’

Uphungu wa mtumwi Petro ngwoyenerera ponse paŵiri kwa Akristu achichepere ndi achikulire omwe. Iye anati: ‘[Khalani] okonzeka nthaŵi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chiri mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha.’ (1 Petro 3:15) Kodi pamafunikira chiyani kuti mukonzeke kuchita chodzikanira choterocho? Choyamba, muyenera kumvetsetsa zimene Malemba amaphunzitsa. Kuti muchirimike kusukulu pa nkhani zonga kusankhana mtundu, ndale zadziko, kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala oledzeretsa, kapena makhalidwe, choyamba muyenera kumvetsetsa kaimidwe Kachikristu ndipo muyenera kukakhulupirira mowona mtima.

Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anauza Akristu anzake kuti: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Kodi mumakhulupirira zimenezo? Monga momwe Paulo anasonyezera, nkosavuta kunyengedwa m’nkhani za mayanjano. Munthu angawoneke kukhala waubwenzi ndi wovomerezeka. Koma ngati iye sagwirizana nanu m’nkhaŵa yanu ya utumiki wa Yehova kapena sakhulupirira m’malonjezo a Baibulo, ali woyanjana naye woipa. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti moyo wake ngwozikidwa pa malamulo amakhalidwe osiyana, ndipo zinthu zofunika kwambiri kwa Mkristu zingakhale za mtengo wotsika kwa iye.

Izi sizodabwitsa, popeza kuti Yesu anati ponena za otsatira ake: ‘Siali a dziko lapansi monga ine sindiri wa dziko lapansi.’ (Yohane 17:16) Nkosatheka kuti munthu akhale Mkristu ndipo panthaŵi imodzimodzi nkukhala mbali ya dziko lino, limene Satana ndiye mulungu wake. (2 Akorinto 4:4) Kodi mwawona mmene kupatuka ku dzikoli kumatetezerera Mkristu ku chinyengo ndi ndewu zimene zimavutitsa anthu ambiri lerolino? Ngati ndi choncho, pamenepo mukhoza kumvetsetsa chifukwa chake muyenera kusunga kudzipatula kwanu, ngakhale ngati kutero kungakuletseni kuloŵa m’machitachita ena apasukulu.a

Kufunika kwa kukhala wolimba m’chikhulupiriro ndi kuika zabwino za Ufumu patsogolo m’moyo kunasonyezedwa m’chochitika cha msungwana wina wachichepere Wachikristu. (Mateyu 6:33) Pamene tsiku la kuyeseza chikondwerero cha kumaliza maphunziro ake linalengezedwa, anapeza kuti linaikidwa pa tsiku limodzimodzi la msonkhano wadera wa Mboni za Yehova umene anakonzekera kukapezekako. Iye analemba kalata yaulemu akulongosola chifukwa chake sadzakhalapo pa kuyesezako naipereka kwa mphunzitsi wake kalasi isanayambe. Pambuyo pa kalasi, mphunzitsiyo anamuitanira pambali ndipo anampempha kufotokozanso chifukwa chake sakapezeka pakuyesezako. Msungwanayo akuti: “Iwo anafuna kuwona ngati mawu anga anali amodzimodzi. Kodi anali malingaliro anga, kapena kodi mawu am’kalatayo anali chabe a amayi anga? Atawona kutsimikiza maganizo kwanga m’nkhaniyo, iwo sananditsutse.”

‘Chitani Chodzikanira Kwa Aliyense’

Kaŵirikaŵiri achichepere Achikristu amapeza kuti ngati adziŵitsa kaimidwe kawo poyera kwa aphunzitsi ndi ophunzira pasanabuke mlandu, chitsenderezo sichimakhala chachikulu pamene iwo ayang’anizana ndi mavuto. Mkristu wachichepere wa ku Japan akusimba kuti pamene anali wazaka 11 zakubadwa, sukulu yake inafuna kuti ophunzira onse apezeke ku phwando la Krisimasi. Ophunzira a magiledi apamwamba anamkakamiza kukhalamo ndi phande, koma iye sanakhaleko, ndipo mphunzitsi wake anamvetsera kaimidwe kake. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti pamene kunatsala pang’ono kuti chaka chasukulu chiyambe, Mboniyo ndi makolo ake anakawonana ndi mphunzitsiyo ndi kumlongosolera mbali zosiyanasiyana za kaimidwe kawo Kachikristu.

Pogwira ntchito muuminisitala wakumunda, Akristu achichepere ena amawopa kukumana ndi anzawo a m’kalasi kapena aphunzitsi. Kodi mumadzimva mofananamo? Ngati ndichoncho, bwanji osayamba ndinu kuwadziŵitsa anzanu a m’kalasi kuti mumalalikira kunyumba ndi nyumba ndi chifukwa chimene mumachitira chimenecho. Mboni ya Yehova ina yazaka 14 zakubadwa inasimba kuti: “Aliyense pasukulu amadziŵa kaimidwe kanga monga Mkristu. Ndithudi, iwo amadziŵa bwino kwambiri kwakuti ngati ndikumana ndi mnzanga wa m’kalasi pamene ndiri muuminisitala, sindimachita manyazi. Kaŵirikaŵiri ophunzira anzanga amamvetsera, ndipo nthaŵi zambiri amalandira mabuku ofotokoza Baibulo.” Wazaka 12 zakubadwa akusimba kuti iye amayembekezera kukumana ndi anzake am’kalasi pamene akugwira ntchito muuminisitala. Mmalo modetsedwa nkhaŵa ndi lingaliroli, iye nthaŵi zonse amayeseza chimene adzanena zimenezo zitachitika. Chotero, iye amakhala wokonzeka kupereka zifukwa zabwino za chikhulupiriro chake.

M’sukulu zambiri, machitachita apambuyo pa makalasi amanenedwa kukhala nkhani yodzisankhira. Koma m’chenicheni, aphunzitsi ndi ophunzira amakakamiza ena kuti aloŵe m’machitachita oterowo. Mkristu wa zaka 20 zakubadwa anapeza njira yabwino yolakira chitsenderezo chimenechi. Iye akuti: “Ndinatumikira monga mpainiya wothandiza m’zaka zonse za sukulu yasekondale. Aliyense anadziŵa kuti ndinali wotanganitsidwa ndi machitachita anga achipembedzo kwakuti sindikatha kuloŵa m’zinthu zina.” Mchemwali wochepera wa Mboni imeneyi anatsatira njira yofananayo. Achichepere Achikristu ena amangopitirira kuchokera ku utumiki waupainiya wothandiza m’zaka za sukulu kuloŵa ntchito ya upainiya wokhazikika monga olengeza Ufumu anthaŵi zonse pamene amaliza maphunziro awo.

Musanyalanyaze konse ziyambukiro zabwino za mayendedwe anu abwino ndi umboni wolimba mtima. Mmalo mokhala chete, bwanji osasonyeza kuti ndinu wolimba m’chikhulupiriro mwakulankhula mwaulemu koma molimba mtima? Ichi nchimene buthu la Chiisrayeli linachita limene linatengedwa kuukapolo ndikukakhala m’banja la Namani, kazembe wa ku Suriya. (2 Mafumu 5:2-4) Dzina la Yehova linatamandidwa chifukwa cha zimene buthulo linachita. Ngati mukhala ndi chikhulupiriro chofananacho chikhozanso kudzetsa ulemu kwa Mulungu ndipo chingathandize ena kuchirimika monga olemekeza dzina lake.

Chenicheni nchakuti sitingalolere molakwa chikhulupiriro chathu ndikukhalabe Akristu. Yesu anati: ‘Yense amene adzavomereza ine pamaso pa anthu, inenso ndidzamvomereza pamaso pa Atate wanga wakumwamba. Koma yense amene adzandikana ine pamaso pa anthu, inenso ndidzamkana iye pamaso pa Atate wanga wakumwamba.’ (Mateyu 10:32, 33) Kukhala wolimba m’chikhulupiriro monga wotsatira wa Yesu ndinthayo lowopsa, sichoncho kodi?

Chithandizo Chiripo

Kuti mukhale ndi kaimidwe kolimba monga mmodzi wa Mboni za Yehova, mufunikira chikhulupiriro cholimba. Kuti mukhale nacho, muyenera kuliphunzira mwakhama Baibulo, kufika pamisonkhano Yachikristu, ndi kukhala ndi phande muuminisitala wakumunda. Ngati mulingalirabe kuti mukusoŵeka chinachake, kodi mungachitenji? Wophunzira Yakobo anati: ‘Wina wa inu ikamsoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, ndi wosatonza; ndipo adzampatsa iye.’ (Yakobo 1:5) Lankhulani kwa Yehova m’pemphero ponena za vuto lanu; iye angakulimbitseni kuyang’anizana ndi mayesero kapena ziyeso za chikhulupiriro chanu.

Kodi nchiyaninso chimene Mkristu wachichepere angachite? Bukhu la Miyambo limatiuza kuti: “Tamvera atate wako anakubala, usapeputse amako atakalamba.” (Miyambo 23:22) Mtumwi Paulo anachirikiza uphungu umenewu, popeza kuti iye anati: ‘Ana inu, mverani akubala inu m’zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho.’ (Akolose 3:20) Makolo Achikristu angakuthandizeni kukhala wolimba m’chikhulupiriro. Mvetserani malingaliro awo. Ndi chithandizo chawo, fufuzani Malemba ndi mabuku ozikidwa pa Baibulo, mukumafunafuna malingaliro, uphungu, ndi zokumana nazo. Ponse paŵiri inuyo ndi makolo anu mudzasangalala ndi chimenechi, ndipo chidzakuthandizani kulaka manyazi kapena mantha.​—2 Timoteo 1:7.

Utengeni mwaŵi wokwanira wa makonzedwe amene Yehova Mulungu wapereka kupyolera mwa mpingo Wachikristu. Konzekerani misonkhano bwino lomwe. Lankhulani kwa akulu oikidwa ndi ena omwe anakhala ndi zokumana nazo zimene inuyo mukuyang’anizana nazo tsopano. Solomo anati: “Munthu wanzeru adzamvetsera ndi kuphunzira zowonjezereka, ndipo munthu womvetsetsa ndiamene apeza chilangizo chaluntha.” (Miyambo 1:5, NW) Chotero phunzirani kwa achikulire ameneŵa. Mukhoza kuphunziranso kwa achichepere Achikristu amene mwachipambano akulaka mavuto ofanana ndi anu.

Kukhulupirika Kumadzetsa Madalitso

Mwakuchirimika zolimba m’chikhulupiriro, mudzakhala mukugwiritsira ntchito uphungu wa Paulo wakukhala ‘okhazikika, osasunthika, akuchuluka m’ntchito ya Ambuye.’ (1 Akorinto 15:58) Yehova amadziŵa ndi kuwamvetsetsa mavuto amene mukuyang’anizana nawo. Iye walimbikitsa ambiri omwe ayang’anizana ndi mavuto ofananawo, ndipo adzakulimbitsani. Ngati mudalira pa Mulungu, adzakuchirikizani, popeza kuti wamasalmo anati: ‘Umsenze Yehova nkhaŵa zako, ndipo iye adzakugwiriziza. Nthaŵi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.’​—Salmo 55:22.

Petro analemba kuti: ‘Khalani nacho chikumbumtima chabwino, kuti umo akunenerani, iwo akunenera konama mayendedwe anu abwino m’Kristu akachitidwe manyazi.’ (1 Petro 3:16) Ngati mukana kulolera molakwa malamulo olungama a Mulungu ndi malamulo amakhalidwe abwino, mudzakhala ndi chikumbumtima chabwino, chimene chiri dalitso lenileni lochokera kwa Yehova. Ndiponso, mudzakhazikitsa chitsanzo chabwino kwa achichepere Achikristu amene chikhulupiriro chawo chingakhale chofooka. (1 Timoteo 4:15, 16) Mayendedwe anu akhoza kuwalimbikitsa kukalamira kukhala olimba m’chikhulupiriro ndipo motero kukhala okhoza kupirira mayesero.

Mukhoza kuthandiza ngakhale amene poyamba amatsutsa kaimidwe Kachikristu. Kumbukirani mawu aŵa opatsa chiyembekezo: ‘Mamawa fesa mbewu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziŵa ziti zidzalola bwino ngakhale izizi, ngakhale izozo, kaya zonse ziŵiri zidzakhala bwino.’ (Mlaliki 11:6) Kodi ndani amene amadziŵa zotulukapo zabwino zimene zidzachokera m’kufesa kwanu mbewu zabwino mwanjira ya machitidwe anu okhulupirika?

Limodzi la madalitso aakulu koposa amene mudzatuta ndilo kaimidwe kovomerezeka pamaso pa Yehova. Pomalizira pake, kukhala wokhulupirika kudzatulukira m’moyo wamuyaya. (Yohane 17:3; yerekezerani ndi Yakobo 1:12.) Palibe mpumulo wakanthaŵi ku mayesero wopezedwa mwakulolera molakwa umene uli woyenerera kutairapo mphatsoyo.

Bwanji ponena za wachichepere wotchulidwa pachiyambi pa nkhani ino? Eya, iye anapirira tsoka lake. Msonkhano wasukuluwo utatha, anayesa kulongosolera aphunzitsiwo kaimidwe kake mwamachenjera. Ngakhale kuti mawu ake anagwera pa makutu ogontha, iye anali ndi chikhutiro chakudziŵa kuti anakondweretsa mtima wa Yehova. (Miyambo 27:11) Iye anapitirizabe kuchinjiriza chikhulupiriro chake mpaka anamaliza sukulu yake. Ndiyeno anakhala mpainiya. Lolani kuti chipiriro chanu chokhulupirika chikhale ndi chotulukapo chosangalatsa chofananacho. Chidzaterodi ngati mutsimikizira kukhala wolimba m’chikhulupiriro.

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mupeze kufotokozedwa kwa zimenezi ndi malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo ena, onani bukhu la Questions Young People Ask​—Answers That Work, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Bokosi patsamba 25]

CHITHANDIZO CHIRIPO

◻ Mvetserani nzeru ya makolo anu owopa Mulungu.

◻ Tengani mwaŵi wa makonzedwe auzimu mumpingo Wachikristu.

◻ Lankhulani ndi akulu oikidwa ndiponso ena amene angakhale anayang’anizana ndi mavuto onga anu.

◻ Lankhulani kwa Akristu achichepere amene akulaka mwachipambano zopinga zofananazo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena