Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Kodi nchifukwa ninji Yesu anakhazikitsa Chikumbutso ndi atumwi okha ndipo osati ndi ophunzira ena amene akaloŵetsedwa m’pangano latsopano?
Funso limeneli likuwonekera kukhala lozikidwa pa lingaliro lolakwika lakuti Yesu anasonkhana ndi atumwi madzulowo kukhazikitsa Mgonero wa Ambuye mpingo Wachikristu wa odzozedwa uli kale m’pangano latsopnano. Mmalomwake, pa Nisani 14, 33 C.E., mpingo Wachikristu unali usanapangidwebe, ndipo Yesu anasonkhana ndi atumwi ake kaamba ka chakudya chapachaka cha Paskha Wachiyuda.
Ndithudi, Yesu anali ndi ophunzira ena kuwonjezera pa atumwi odziŵika 12 amenewo. Chaka chimodzi imfa yake isanachitike, iye anatumiza ophunzira 70 paulendo wolalikira. Pambuyo pa kuuka kwake, ‘anawoneka pa nthaŵi imodzi kwa abale oposa mazana asanu.’ Ndipo panali atumwi ‘ngati zana limodzi ndi makumi aŵiri’ osonkhana patsiku la Pentekoste. (1 Akorinto 15:6; Machitidwe 1:15, 16, 23; Luka 10:1-24) Koma tiyeni tilingalire gulu lokhala ndi Yesu pamene iye anakhazikitsa phwando lapachaka lodziŵika kukhala Mgonero wa Ambuye.
Luka 22:7, 8 amatipatsa ndandanda ya nthaŵi, akumati: ‘Ndipo tsiku la mikate yopanda chotupitsa linafika, limene inayenera kuphedwa nsembe ya paskha. Ndipo iye anatumiza Petro ndi Yohane, nati, Pitani mutikonzere ife paskha, kuti tidye.’ Cholembedwacho chimapitiriza kuti: ‘Ndipo mukanene kwa mwininyumbayo, Mphunzitsi anena nawe, Chipinda cha alendo chiri kuti, mmene ndikadye paskha pamodzi ndi ophunzira anga?’ Chotero madzulowo Yesu anali ndi atumwi 12 pa phwando Lachiyudalo. Iye anaŵauza kuti: “Ndinalakalaka ndithu kudya Paskha uwu pamodzi ndinu, ndisanayambe kusautsidwa.”—Luka 22:11, 15.
Kuchokera pamene anayamba ku Igupto, Paskha anali phwando labanja. Pokhazikitsa Paskha, Mulungu anauza Mose kuti nkhosa inayenera kuphedwera banja lirilonse. Ngati banjalo linali laling’ono kwambiri losakhoza kudya nkhosa yonseyo, banja lapafupi likaitanidwa ndi kudya nawo chakudyacho. Chotero, kuli koyenera kuti pa Paskha wa 33 C.E., ambiri a ophunzira a Yesu anasonkhana mwanthaŵi zonse ndi mabanja awo kaamba ka chakudya chimenechi.
Koma Yesu ‘analakalaka ndithu’ kudya chimene chikakhala Paskha walamulo womalizira, ndi usiku womalizira imfa yake isanachitike, ndi otsatira ake apamtima, amene anali atayenda naye mkati mwa utumiki wake waukulu. Pamapeto a chakudya cha Paskha chimenecho, Yesu anaŵauza za phwando latsopano limene likachitidwa ndi otsatira ake mtsogolo. Vinyo wa phwando Lachikristu lamtsogololo akaimira mwazi wa “pangano latsopano” lomwe likaloŵa mmalo pangano Lachilamulo.—Luka 22:20.
Komabe, madzulo a Nisani 14, 33 C.E., pangano latsopano linali lisanayambe kugwira ntchito, popeza kuti nsembe yolipangitsa kukhala lalamulo—Yesu—inali isanaperekedwe. Pangano Lachilamulo linali kugwirabe ntchito. Linali lisanakhomeredwe pamtengo. Ndiponso, sikukawoneka kuti pangano lakale ndi Israyeli wakuthupi linaloŵedwa mmalo ndi pangano latsopano ndi Israyeli wauzimu kufikira tsiku la Pentekoste.—Agalatiya 6:16; Akolose 2:14.
Chotero, kaya atumwi okhulupirika 11 kapena ophunzira enawo sanali m’pangano latsopano madzulowo. Ndipo Yesu sanasonyeze kuŵakana ophunzira ena Achiyudawo mwakuŵalola kusonkhana ndi mabanja awo kuchita phwando la Paskha.