Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 8/15 tsamba 13-18
  • Ubwino Waukulu wa Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ubwino Waukulu wa Yehova
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ubwino wa Mulungu
  • Ubwino Wosonyezedwa m’Chilengedwe
  • Kuchimwa kwa Anthu ndi Kuomboledwa
  • Ubwino wa Mulungu Lerolino
  • Mbali Yodabwitsa ya Ubwino wa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Yehova Ndiye Chitsanzo Chachikulu Pankhani Yosonyeza Ubwino
    Nsanja ya Olonda—2002
  • “Ubwino Wake Ndi Waukulu Kwambiri!”
    Yandikirani Yehova
  • Ubwino​—Kodi Tingatani Kuti Tikhale ndi Khalidweli?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 8/15 tsamba 13-18

Ubwino Waukulu wa Yehova

“Ubwino wanu uli waukulu chotani nanga, umene munasungira iwo akuwopa inu!”​—SALMO 31:19, NW.

1, 2. (a) Kodi ndintchito yaikulu yotani imene Yehova anaichita panthaŵi ina kalelo? (b) Kodi Yehova anafotokoza motani chotulukapo cha ntchito zake zakulenga?

PANALI nthaŵi imene Mulungu anayamba kulenga ‘kumwamba monga mpando wake wachifumu ndi dziko lapansi monga choikapo mapazi ake.’ (Yesaya 66:1) Cholembedwa chaumulungucho sichimavumbula pamene izi zinachitika. Chimangonena kuti: ‘Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.’ (Genesis 1:1) Mkati mwa nyengo yakulenga, mamiliyoni osaŵerengeka a milalang’amba anapangidwa, ambiri okhala ndi zikwi mamiliyoni ambirimbiri a nyenyezi. Chakunja kwa umodzi wa milalang’amba yoteroyo kunali nyenyezi yowala yomwe inazunguliridwa ndi unyinji wa mapulaneti aang’onoko, amdima. Imodzi ya mapulanetiwo inatchedwa dziko lapansi. Poyerekezeredwa ndi nyenyezi zazikulu zowala, dziko lapansi silinali kanthu. Komabe, ilo ndilimene Yehova anafuna kuti likhale choikapo mapazi ake.

2 Choncho Yehova anapereka maluso ake akulenga ku pulaneti Dziko Lapansi. ‘Woyamba wa chilengedwe chonse’ anali pambali pake monga Mmisiri Wamkulu pamene mulu wamdima, waung’ono umenewu unasinthidwa m’nyengo yaitali ya “masiku” asanu ndi limodzi akulenga. Mophiphiritsira, unakhala malo oyenerera a mapazi a Mulungu. (Akolose 1:15; Eksodo 20:11; Miyambo 8:30) Pano ndipo pamene Mulungu analinganiza kukhazikapo mtundu watsopano wa moyo waluntha: anthu. Anthu aŵiri oyambirira, olengedwa ndi zinthu zopezeka m’nthaka, anaikidwa m’malo abwino aparadaiso. (Genesis 1:26, 27; 2:7, 8) Chotulukapo chomalizira cha kachitidwe kapadera kakulenga kameneka, chinali changwiro ndiponso chokongola koposa, kotero kuti Baibulo limavumbula malingaliro a Mulungu ponena za chilengedwe chake m’mawa​—mbali yomalizira​—ya tsiku lakulenga lachisanu ndi chimodzi motere: “Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu.”​—Genesis 1:31.

Ubwino wa Mulungu

3. Kodi ndimkhalidwe wapadera wa Mulungu uti umene chilengedwe chimavumbula?

3 Zaka zikwi zambiri pambuyo pake, mbadwa ya anthu aŵiri oyambirira amenewo inayang’ana m’mbuyo ku nthaŵi yachilengedwe ndikulemba kuti: ‘Pakuti chilengedwere dziko lapansi zawoneka bwino zosawoneka za [Mulungu] ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa.’ (Aroma 1:20) Inde, kukongola kopambana kwa dziko lapansi ndi zolengedwa zake kunalidi chisonyezero chabwino koposa cha mikhalidwe yosawoneka ya Mulungu​—wosachepera pa yonseyo ndiwo ubwino waukulu wa Mulungu. Pamenepo, kuli koyenerera chotani nanga kuti Mulungu analengeza kuti zonse zimene anazilenga zinali zabwino!​—Salmo 31:19.

4, 5. Kodi ubwino nchiyani?

4 Ubwino ndiwo mbali yachisanu ndi chimodzi ya zipatso za mzimu wa Mulungu zofotokozedwa ndi mtumwi Paulo pa Agalatiya 5:22. (NW) Maphunziro apapitapo m’magazini a Nsanja ya Olonda anafotokoza zipatso zisanu zoyambirira za mzimu, kusonyeza kufunika kwake pokulitsa umunthu wabwino Wachikristu.a Komabe, kuli kofunika chotani nanga kuti tisaiwale ubwino! Moyenerera, tsopano tikusumika chidwi chathu pa mkhalidwe umenewu.

5 Kodi ubwino nchiyani? Ndi khalidwe kapena mkhalidwe wakukhala wabwino. Ndi khalidwe labwino, ukoma. Choncho, ndimkhalidwe wabwino umene umadzisonyeza wokha m’kuchitira ena ntchito zabwino ndi zopindulitsa. Kodi tingausonyeze motani mkhalidwe wabwino umenewu? Kwakukulukulu, mwakutsanzira Yehova. Chifukwa chake, tisanafotokoze mowonjezereka mmene ifeyo monga Akristu aliyense payekha tingasonyezere ubwino, tiyeni tisanthule ubwino umene Mulungu wathu wachikondi, Yehova, wasonyeza posamalira ndi kuchita ndi banja la anthu.

Ubwino Wosonyezedwa m’Chilengedwe

6. Kodi nchiyani chimene chinasonkhezera Yehova kulenga mitundu ina yaluntha ya moyo?

6 Kodi nchiyani chimene poyambapo chinapangitsa Atate wathu wakumwamba kugaŵana chisangalalo cha moyo ndi zolengedwa zamoyo zaluntha? Mtumwi Yohane akuyankha funso limenelo pamene akunena kuti: ‘Mulungu ndiye chikondi.’ (1 Yohane 4:8) Inde, chikondi chopanda dyera chinasonkhezera Magwero amoyo aakuluwo kulenga mitundu ina yamoyo, kuipatsa ina mudzi wakumwamba ndi ina mudzi wapadziko lapansi. Ndithudi, timadziŵa zochepa ponena za mmene kumwamba kumawonekera kapena mmene zolengedwa zakumwamba zimawonekera. Izo ndimizimu​—zosawoneka ndi maso a anthu​—ndipo mudzi wawo uli kumalo okhala mizimu. Koma tayang’anani mudzi wapadziko lapansi wokuzingani umene Yehova anapereka kwa ana ake aumunthu. Ndipo talingalirani anthu enieniwo. Ndiyeno mudzayamba kuwona ndi maso anu enieniwo umboni wamphamvu wa ubwino wa Mulungu.

7-9. Kodi ubwino wa Mulungu umawonekera motani m’njira imene analengera dziko lapansi ndi munthu amene amakhalapo?

7 Yehova anapatsa makolo athu oyamba moyo. Kuwonjezera pa zimenezo, anakupangitsa kukhala kotheka kuti moyowo ukhale wosangalatsa kwambiri, wokondweretsa. Choyamba, iye analenga mudzi wawo, dziko lapansi, kuzungulira kwake, kusinthasintha kwa kutentha ndi kuzizira, ndi thambo zomwe zinali zoyenerera. Iye anayambitsa zungulirezungulire wa madzi, nitrogen, ndi oxygen zomwe zimagwira ntchito mwangwiro kaamba ka phindu ndi chisangalalo cha anthu. Iye anakuta nkhope ya dziko lapansi ndi mitundu zikwizikwi za zomera, zina zoti munthu adzidya ndipo zina zongosangalatsa maso. Iye anadzaza thambo ndi mbalame zomwe zimasangalatsa kwambiri ndi kukongola kwawo ndi nyimbo zawo. Iye anadzaza nyanja ndi unyinji wa nsomba ndipo mtunda anaudzaza ndi mitundu yambiri ya zinyama, zina zakuthengo ndipo zina zoŵeta. Ha, ndikuoloŵa manja kodabwitsa kotani nanga! Ndipo ndiumboni wotani nanga wa ubwino wa mtima wa Mulungu!​—Salmo 104:24.

8 Tsopano, tayang’anani njira imene Mulungu anapangira munthu. Mikono yake, miyendo, ndi manja ndizo zimene zimafunikira kuti akhoze kukhala wolinganizika ndi kuyenda mosavuta. Chotero, kuchokera ku zinthu zochuluka zomwe zimapezeka padziko lapansi, akhoza kudzipezera chakudya ndi zofunikira zina. Yehova anampatsa zolaŵira kotero kuti kudya ndi kumwa siziri kokha ntchito zochitidwa zopezera nyonga​—monga ngati kusomeka chiwiya chamagetsi ku malo otulukira magetsi lerolino. Ayi, kudya ndi kumwa zinalinganizidwa kuti zitipatse chisangalalo, popeza kuti sizimangokhutitsa mimba komanso zimasangalatsa mphamvu za kulaŵa. Yehova anapatsa munthu makutu limodzinso ndi kumzinga ndi mawu oti adzisangalatsa makutuwo. Kumakhala kosangalatsa chotani nanga kumvetsera ku kuthithima kotonthoza kwa mtsinje, kuitana kwa nkhunda, kapena kuseka kwa khanda! Inde, tiyamika ubwino wa Mulungu kuti mosasamala kanthu za zinthu zonse zoipa zimene zakhala zikuchitika chiyambire chilengedwe, kukhala ndimoyo kudakali kosangalatsa.

9 Tayang’ananinso pa mphamvu zathu zina. Pali mitundu yambiri yosiyanasiyana, yosangalatsa yotani nanga imene imasangalatsa maso athu! Ndipo kuli kokhutiritsa chotani nanga kununkhiza fungo lokoma la maluŵa! Nkosadabwitsa kuti wamasalmo anafuula kwa Yehova kuti: ‘Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchowopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa’!​—Salmo 139:14.

Kuchimwa kwa Anthu ndi Kuomboledwa

10. Kodi anthu ambiri achitapo motani pa ubwino wa Mulungu, komabe kodi ndimotani mmene amapitirizira kupindula nawo?

10 Momvetsa chisoni, m’kupita kwa nthaŵi makolo athu oyambirira anasonyeza kusoŵa chiyamikiro kaamba ka ubwino wonse wa Mulungu kwa iwo. Iwo anasonyeza zimenezi pamene sanamvere malamulo a Yehova ndipo analakwira chiletso chachikulu chomwe anawaikira. Monga chotulukapo, iwo ndi ana awo anadziŵa chisoni, kuvutika, ndi imfa. (Genesis 2:16, 17; 3:16-19; Aroma 5:12) M’zaka zikwi zambiri zomwe zapitapo kuyambira pa kusamvera kumeneko, anthu ambiri asonyeza mphwayi kapena kusoŵa chiyamikiro kaamba ka ubwino wa Mulungu. Komabe, mosasamala kanthu za zimenezi, anthu osathokoza ndi osayamika amapindulabe ndi ubwino wa Mulungu. Mwanjira yotani? Mtumwi Paulo anafotokozera nzika za Lustra ku Middle East motere: ‘[Mulungu] sanadzisiyira iyemwini wopanda umboni, popeza anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero.’​—Machitidwe 14:17.

11. Kodi ndimwanjira yotani mmene ubwino wa Mulungu umaposera pa kungopatsa anthu mudzi wosangalatsa?

11 Koma ubwino wa Mulungu sunalekezere pa kupitiriza kupereka zakudya zosangalatsa, zochilikiza moyo zomwe ziri zochuluka padziko lapansi. Ayi, iye anapyola pamenepo. Yehova anadzisonyeza kukhala wokonzekera kukhululukira machimo a ana a Adamu ndikupitiriza kukhala ndi unansi ndi anthu okhulupirika. Mbali imeneyi ya ubwino wa Mulungu inadziŵikitsidwa kwa Mose pamene Yehova analonjeza kuti ‘adzapititsa [ubwino, NW] wake wonse pamaso pa [Mose].’ Ndiyeno Mose anamva chilengezo chakuti: ‘Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachowonadi; wakusungira anthu osaŵerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa.’​—Eksodo 33:19; 34:6, 7.

12. Kodi ndimakonzedwe otani a Chilamulo cha Mose amene anasonyeza ubwino wa Yehova?

12 M’nthaŵi ya Mose, Yehova anakhazikitsa dongosolo lalamulo kaamba ka mtundu watsopano wa Israyeli mwa limene ochimwa mwangozi akanapeza kukhululukidwa kwa tchimo kophiphiritsira. Kupyolera m’pangano la Chilamulo chimene Mose anali nkhoswe yake, Aisrayeli anakhala mtundu wapadera wa Mulungu ndipo anaphunzitsidwa kupereka kwa Yehova nsembe zanyama zosiyanasiyana zomwe zikatetezera machimo ndi machitidwe awo olakwa. Chotero, mosasamala kanthu za mkhalidwe wawo wopanda ungwiro, Aisrayeli olapa anapitiriza kufikira Yehova molandirika ndikudziŵa kuti kulambira kwawo kunali kosangalatsa kwa iye. Mfumu Davide, chiŵalo cha mtundu umenewo wokhala pansi pa Chilamulo, anafotokoza kuzindikira kwake ubwino wa Mulungu motere: ‘Musakumbukire zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu; mundikumbukire monga mwa chifundo chanu, chifukwa cha ubwino wanu, Yehova.’​—Salmo 25:7.

13. Kodi ndimotani mmene Yehova anaperekera njira yogwira mtima koposa yokhululukira machimo kuposa nsembe zanyama?

13 M’kupita kwanthaŵi ubwino wa Yehova unamsonkhezera kupereka njira yogwira mtima ndi yokhalitsa yokhululukira machimo. Izi zinachitidwa kupyolera m’nsembe ya Yesu, yemwe anali mbadwa ya Mfumu Davide. (Mateyu 1:6-16; Luka 3:23-31) Yesu sanachimwe. Chifukwa chake, pamene anafa, moyo wake woperekedwa nsembe unali ndi mtengo waukulu, ndipo Mulungu anailandira nsembeyo monga dipo lomwe likagwira ntchito kwa ana onse ochimwa a Adamu. Mtumwi Paulo analemba kuti: ‘Onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu; ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi chisomo chake, mwa [dipo la, NW] mwa Kristu Yesu; amene Mulungu anamuika poyera akhale chotetezera mwa chikhulupiriro cha m’mwazi wake.’​—Aroma 3:23-26.

14. Kodi ndiziyembekezo zabwino koposa zotani zimene zinatheketsedwa kwa anthu kupyolera m’nsembe yadipo?

14 Chikhulupiriro m’nsembe yadipo ya Yesu chimakwaniritsa zochuluka kwa Akristu, zochuluka kuposa zimene zinakwaniritsidwa ndi nsembe zanyama pansi pa pangano la Chilamulo kwa Aisrayeli. Chinapangitsa chiŵerengero chochepa cha Akristu kulengezedwa kukhala olungama ndikutengedwa kukhala ana auzimu a Mulungu. Chotero iwo anakhala abale a Yesu ndipo anakhala ndi chiyembekezo chakuukitsidwa monga zolengedwa zauzimu kukakhala ndi phande limodzi naye mu Ufumu wake wakumwamba. (Luka 22:29, 30; Aroma 8:14-17) Tangolingalirani kuti Mulungu akapereka ziyembekezo zakumwamba zoterozo kwa zolengedwa zokhala ndimoyo papulaneti laling’onoli, dziko lapansi! Kagulu kakang’ono kokhala ndi chiyembekezo chimenechi kadakalipo. Koma kwa mamiliyoni ena a Akristu, kusonyeza chikhulupiriro m’dipo kumatsegula njira yakusangalala ndi zimene Adamu ndi Hava anataya​—moyo wamuyaya padziko lapansi laparadaiso, longa munda. Pangano la Chilamulo lokha silinali lokhoza kupereka ziyembekezo zakumwamba kapena zapadziko lapansi kwa achirikizi ake.

15. Kodi nchiyani chimene chikuphatikizidwa mu mbiri yabwino?

15 Kuli koyenerera chotani nanga kuti makonzedwe atsopano amene Mulungu anawakhazikitsa kupyolera mwa Yesu Kristu akutchedwa “mbiri yabwino,” popeza kuti amasonyeza ubwino wa Mulungu. (2 Timoteo 1:9, 10, NW) M’Baibulo, nthaŵi zina mbiri yabwino imatchedwa “mbiri yabwino ya ufumu.” Lerolino yazikidwa pa chowonadi chakuti Ufumuwo unakhazikitsidwa pansi pa ulamuliro wa Yesu woukitsidwayo. (Mateyu 24:14, NW; Chibvumbulutso 11:15; 14:6, 7) Komabe, mbiri yabwinoyo imaphatikizapo zochuluka. Monga momwe kwasonyezedwera ndi mawu a Paulo kwa Timoteo omwe angogwidwa kumenewo, imaphatikizapo chidziŵitso chakuti Yesu anapereka nsembe yadipo m’malo mwathu. Popanda nsembe imeneyo, unansi wathu ndi Mulungu, chipulumutso chathu chenichenicho​—kuwonjezapo Ufumu wa Yesu ndi ansembe ndi mafumu 144,000 otengedwa padziko lapansi​—zikanakhala zosatheka. Dipo liri chisonyezero chabwino koposa chotani nanga cha ubwino wa Mulungu!

Ubwino wa Mulungu Lerolino

16, 17. Kodi ndimotani mmene Hoseya 3:5 anakwaniritsidwira (a) mu 537 B.C.E.? (b) mu 1919 C.E.?

16 Akumayang’ana kutsogolo ku “masiku otsiriza,” mtumwi Paulo anachenjeza kuti: “Anthu adzakhala . . . osakonda abwino.” (2 Timoteo 3:1-3) Ngakhale kusonyezedwa kwachibadwa kwa ubwino, monga ngati kuoloŵa manja ndi unansi, sizikayamikiridwa. Pamenepo, uli wolimbikitsa chotani nanga ulosi uwu wa pa Hoseya 3:5: ‘Ana a Israyeli adzabwera, nadzafuna Yehova Mulungu wawo, ndi Davide mfumu yawo, nadzafika ndi mantha kwa Yehova, ndi ku [ubwino wake, NW] masiku otsiriza.’

17 Ulosiwu unakwaniritsidwa choyamba mu 537 B.C.E. pamene Ayuda anabwerera ku Dziko Lolonjezedwa kuchokera ku ukapolo mu Babulo. M’nthaŵi zamakono, unayamba kukwaniritsidwa m’chaka cha 1919 pamene otsalira a Israyeli wauzimu anatuluka m’gulu la Satana ndikuyamba kufunafuna Yehova ndi ubwino wake mwakhama. Iwo anapeza kuti munthuyo Yesu Kristu anakhala akulamulira muulamuliro wakumwamba monga “Davide mfumu yawo” chiyambire 1914. Pansi pa chiyang’aniro chake chakumwamba, iwo anavomereza motenthedwa maganizo thayo lakulengeza mbiri yabwino imeneyi kwa amitundu. Chotero iwo anayamba kukwaniritsa ntchito yolembedwa pa Mateyu 24:14 (NW) iyi: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu [wokhazikitsidwa] idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.”

18. Kodi ndani omwe agwirizana ndi otsalira a Israyeli wauzimu m’kulengeza mbiri yabwino?

18 Lerolino, otsalira odzozedwa agwirizana ndi ‘khamu lalikulu,’ lomwe nalonso limatamanda ubwino wa Yehova. (Chibvumbulutso 7:9) Tsopano, oposa mamiliyoni anayi akubwereza mawu a mngelo wowonedwa ndi mtumwi Yohane m’masomphenya pamene akulengeza kwa mitundu yonse kuti: ‘Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthaŵi ya chiweruziro chake; ndipo mlambireni iye amene analenga m’mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe amadzi.’​—Chibvumbulutso 14:7.

19. Tchulani umodzi wa maumboni aakulu koposa a ubwino wa Mulungu.

19 Umodzi wa maumboni aakulu koposa a ubwino wa Mulungu uli wakuti amatilola kukhala antchito anzake m’ntchito yomwe yafika pachimake imeneyi. Ndimwaŵi wapadera wotani nanga kuikiziridwa “mbiri yawino ya ulemerero ya Mulungu wachimwemwe”! (1 Timoteo 1:11, NW) Mwakulalikira kwathu ndi kuphunzitsa ena zimenezi, timasonyeza kumlingo waukulu chipatso chofunika chimenecho cha mzimu wa Mulungu, ubwino. Chotero, tiri ndi mkhalidwe wa Davide, mtumiki wakale wa Mulungu amene ananena kuti: ‘Adzabukitsa chikumbukiro cha ubwino wanu waukulu, nadzaimbira chilungamo chanu.’​—Salmo 145:7.

20. Kodi ndichidziŵitso chowonjezereka chotani chonena za ubwino chimene chidzafotokozedwa m’nkhani yotsatira?

20 Komabe, kodi kukhala ndi phande m’kulalikira mbiri yabwino ndiko njira yokha yosonyezera ubwino m’miyoyo yathu? Kutalitali! Timalimbikitsidwa kukhala “akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa.” (Aefeso 5:1) Ubwino wa Mulungu umasonyezedwa m’njira zosiyanasiyana. Chifukwa chake, ubwino wathu nawonso uyenera kuyambukira mbali zambiri za miyoyo yathu. Zina za zimenezi zidzalingaliridwa m’nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

a Zipatso za mzimuzo ndizo chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, ubwino, chikhulupiriro, chifatso, ndi chiletso.

Kodi Mungayankhe?

◻ Kodi ndimwanjira yotani mmene chilengedwe chimasonyezera ubwino wa Mulungu?

◻ Kodi ndimakonzedwe otani amene Yehova anapanga a kukhululukira machimo a anthu olapa?

◻ Pokwaniritsa Hoseya 3:5, kodi ndiliti pamene otsalira odzozedwa anafika kwa Yehova ndi ku ubwino wake, ndipo kodi ichi chinatsogolera ku chiyani?

◻ Kodi ndi uti umene uli umodzi wa maumboni aakulu koposa a ubwino wa Mulungu lerolino?

[Chithunzi patsamba 15]

Chilengedwe chimapereka umboni wa kuchuluka kwa ubwino wa Mulungu

[Chithunzi patsamba 16]

Kuloledwa kwathu kukhala ndi phande m’ntchito yolalikira kuli umboni wapadera wa ubwino wa Mulungu

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena