‘Kubzala ndi Misozi ndi Kututa ndi Mfuu Yachikondwerero’
Monga momwe yasimbidwira ndi Miyo Idei
“Ndikufa ine! Ndikufa ine! Thandizeni!” Abambo ŵanga ankayesayesa zolimba kufuula. Liwu lawo linamveka mofuula pamene ndinathamanga kutuluka m’nyumba. Panali pakati pausiku, ndipo bambo anadwala mtima. Ndinathamangira kwa amalume, omwe ankakhala chapafupi, koma pamene tinabwerera, mtima wa Bambo unaleka kumveka kugunda.
ZIMENEZO zinachitika pa December 14, 1918. Pamsinkhu wa zaka 13 zakubadwa, ndinasiidwa wopanda makolo. Amayi adamwalira pamene ndidaali wazaka zisanu ndi ziŵiri. Potaikiridwa makolo onse aŵiri ndiri wochepa choncho, ndinayamba kuzizwa, ‘Kodi nchifukwa ninji anthu amafa? Kodi nchiyani chimene chimachitika pambuyo pa imfa?’
Pamene ndinamaliza maphunziro pasukulu ya aphunzitsi, ndinakhala mphunzitsi m’Tokyo ndi kuyamba kuphunzitsa pa Sukulu Yapulaimale ya Shinagawa. Pambuyo pake, bwenzi langa linandisonyeza kwa mwamuna wachichepere, Motohiro, amene ndinakwatirana naye pamsinkhu wa zaka 22 zakubadwa. Kwazaka 64 zapitazo, tagaŵana zokumana nazo ponse paŵiri zokoma ndi zoŵaŵa m’moyo. Posapita nthaŵi tinasamukira ku Taiwan, imene panthaŵiyo inali pansi paulamuliro wa Japani. Panthaŵiyo sindinaganize konse kuti ndikapeza chifukwa cha mfuu yachikondwerero m’dziko limenelo.
Kuphunzira Chowonadi
M’ngululu ya 1932, pamene tinali kukhala kumalo akumidzi a Chiai chapakati pa Taiwan, mwamuna wotchedwa Saburo Ochiai anatichezera. Iye anatisonyeza kuti maulosi a Baibulo amaphatikizapo lonjezo la kuuka kwa akufa. (Yohane 5:28, 29) Ha, nchiyembekezo chabwino chotani nanga! Ndinafuna kwambiri kukawaonanso amayi ndi abambo ŵanga. Ndi zigomeko zake zanzeru, malongosoledwe omveka, ndi maumboni amphamvu Abaibulo, mawu ake anawonekera kukhala ndi chowonadi. Nthaŵi inathamanga pamene tinatha tsiku lathunthu tikukambitsirana Baibulo. Mwadzidzidzi linakhala bukhu lokongola kwa ine.
Mwamsanga Bambo Ochiai anasamukira kumalo ena, natisiira mabuku monga Creation, Zeze wa Mulungu, Boma, Ulosi, Light, ndi Reconciliation, onsewo ofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society. Ndinatengeka maganizo ndi kuwaŵerenga, ndipo pamene ndinkatero, ndinachimva chisonkhezero chakufuna kuuza ena zimene ndinali kuŵerenga. Ngati Yesu anayambira uminisitala wake m’mudzi wakwawo wa Nazarete, bwanji osayambira kumene ndinkakhala? Ndinafikira mnansi wanga wa pakhomo lotsatira. Palibe amene anandiphunzitsa kulalikira, chotero ndinapita kunyumba ndi nyumba ndi Baibulo langa ndi mabuku amene ndinaŵerenga, ndikulalikira monga momwe ndikanathera. Anthu anavomereza ndi kulandira magazini. Ndinapempha Todaisha, monga momwe Watch Tower Society inatchedwera panthaŵiyo m’Japani, kunditumizira makope 150 a kabukhu kamutu wakuti The Kingdom, the Hope of the World, ndipo ndinawagaŵira.
Tsiku lina munthu wina yemwe adalandira mabuku anandiuza kuti apolisi adabwera pamene ndinachoka ndi kulanda mabukuwo. Mwamsanga pambuyo pake, atifitifi anayi anabwera kunyumba kwanga ndi kulanda mabuku anga onse ndi magazini. Anangosiya Baibulo lokha. Kwazaka zisanu, sindinakumane ndi aliyense wa anthu a Yehova, koma changu cha chowonadi chinkatukusirabe mumtima mwanga.
Ndiyeno inafika December 1937! Akoputala aŵiri ochokera ku Japani anatichezera. Modabwa, ndinafunsa kuti: “Kodi munadziŵa bwanji za ife?” Iwo anati: “Tiri nalo dzina lanu pano tiri.” Yehova anatikumbukira! Mboni ziŵirizo, Yoriichi Oe ndi Yoshiuchi Kosaka, adatchova njinga zawo zakale kwa makilomita 240 kuchokera ku Taipei kumka ku Chiai, atanyamula mitolo yaikulu ya katundu wawo kumbuyo. Pamene anali kulankhula nafe, ndinadzimva ngati munthu wa ku Aitiopiya uja amene anati: ‘Chindiletsa ine nchiyani ndisabatizidwe?’ (Machitidwe 8:36) Usiku umene anafika, tonse aŵirife mwamuna wanga ndi ine tinabatizidwa.
Kusamalira Abale Omangidwa
Mu 1939 kumanga Mboni za Yehova kunabuka kuzungulira Japani yonse. Funde la chizunzocho mwamsanga linafika ku Taiwan. Mu April Abale aŵiriwo Oe ndi Kosaka anamangidwa. Miyezi iŵiri pambuyo pake nafenso tinamangidwa. Chifukwa chakuti ndinali mphunzitsi, ndinamasulidwa tsiku lotsatira, koma mwamuna wanga anasungidwa m’lumande kwa miyezi inayi. Pamene mwamuna wanga anamasulidwa, tinasamukira ku Taipei. Popeza kuti tsopano tinali pafupi ndi ndende kumene abale aŵiriwo anasungidwako, ameneŵa anatsimikizira kukhala makonzedwe abwino kwabasi.
Ndende ya ku Taipei inali ndende yolondedwa zolimba. Nditatenga zovala ndi chakudya, ndinakawona abalewo. Choyamba, Mbale Kosaka anabwera ndi mlonda ndi tifitifi kumbuyo kwa zenera lotsekedwa ndi waya wopiringizapiringiza wa masentimita 30. Iye anali wotumbuluka ndipo milomo yake inali psu kufiira. Anadwala chifuwa chachikulu.
Ndiyeno Mbale Oe anatuluka akumwetulira, mwachimwemwe akubwerezabwereza kuti: “Chakhala bwino zedi kuti mwabwera.” Popeza kuti nkhope yake inawoneka yachikasu ndi yotupa, ndinamfunsa ponena za thanzi lake. “Ndiribwino kwabasi!” anayankha tero. “Ano ndimalo abwino zedi. Alibe nsikidzi kapena nsabwe. Ndikhoza kudyeramo zotsekemera munomu. Maloŵa ali ngati nyumba yaikulu yokhala m’paki yokongola,” iye anatero. Wapolisi ndi mlonda analephera kugwira kuseka naati: “He! sitingamuthe Oe uyu.”
Kumangidwanso
Chapakati pausiku pa November 30, 1941, masiku ochepa pamene ndinabwerera kunyumba kuchokera kumene ndidakaona abalewo, ndinamva kugunda kuchitseko. Ndinawona zithunzi za zipewa zowoneka ngati mapiri kupyolera m’galasi la pachitseko. Ndinaŵerenga zokwanira zisanu ndi zitatu. Anali apolisi. Iwo analoŵa m’nyumba mwamphamvu nagubuduza chinthu chirichonse m’nyumbamo—koma osanunkha kanthu. Pambuyo pakufufuza malowo kwa ola limodzi, analanda mabuku azithunzithunzi zojambulidwa angapo natiuza kupita nawo. Ndinakumbukira kuti Yesu anamangidwa pakati pausiku. (Mateyu 26:31, 55-57; Yohane 18:3-12) Lingaliro lakuti amuna asanu ndi atatu akutakasatakasa modzivutitsa pa aŵirife linandisangalatsa.
Tinapititsidwa kuchinyumba chosadziŵika chachikulu ndi chamdima. Pambuyo pake tinadziŵa kuti inali Ndende ya Taipei Hichisei. Tinakhazikidwa patsogolo pa chidesiki chachikulu, ndipo kufunsidwa kunayamba. Anafunsa mobwerezabwereza kuti: “Kodi udziŵa ndani kuno?” ndipo aliyense wa ife anayankha kuti: “Sindidziŵa aliyense.” Kodi tikanawadziŵa bwanji abale okhala kumtunda m’Japani? Tinangodziŵa Mbale Oe ndi Kosaka, ndipo tinasunga pakamwa pathu osatchula maina ena alionse amene tinamvapo.
Posapita nthaŵi inali 5 koloko m’mawa, ndipo atifitifi aŵiri anandipereka ku lumande langa. Kunanditengera nthaŵi kuti ndizoloŵere mkhalidwe watsopanowo. Kwanthaŵi yoyamba m’moyo wanga, ndinakumana ndi nsikidzi. Tizirombo tating’ono timeneti, tokondetsa kupeza chakudya pa atsopano, tinandivutisa mosalekeza, tikusiya akazi ena aŵiri m’lumandemo osawakhudza—mosasamala kanthu zakuti ndinaphwanya timene tinanditsata. Pomalizira pake ndinatopa ndi kutisiya kuti tipange phwando pa ine.
Chakudya chathu chinali phala lampunga losapsa, koma mkamwa mwanga linamveka ngati mpunga wosaphika. Chodyera pamodzi ndi phalalo anali masamba a daikon (radish ya ku Japani) oikidwa mchere komanso okhalabe ndi mchenga. Poyamba, chifukwa chakuti chakudyacho chinandinunkhira moipa ndipo chinali chauve, sindinathe kuchidya, ndipo akaidi enawo anadzachidya. Ndithudi, pang’onopang’ono ndinasintha kotero kuti ndikhalebe ndi moyo.
Moyo m’ndende unali woopsa. Panthaŵi ina, ndinamva mwamuna, wolingaliridwa kukhala mzondi, akukuŵa tsiku ndi tsiku kaamba kozunzidwa mwankhalwe. Ndinawonanso munthu wina m’lumande lotsatira akufa ndi kupweteka. Ndi zonsezi zikuchitika pamaso panga, ndinalingaliradi kuti dongosolo lakaleli liyenera kutha, ndipo chiyembekezo changa m’malonjezo a Mulungu chinakhala champhamvu kuposa ndi kalelonse.
Kufunsidwa
Ndinabindikiritsidwa m’ndende kwa pafupifupi chaka chimodzi ndipo ndinafunsidwa kasanu. Tsiku lina wondiimba mlandu anabwera kwa nthaŵi yoyamba, ndipo ndinapititsidwa ku kachipinda kakang’ono kofunsiramo. Chinthu choyamba chimene ananena chinali chakuti: “Kodi wamkulu ndani, Amaterasu Omikami [mulungu dzuŵa wamkazi] kapena Yehova? Tandiuza!” Ndinalingalira kwakamphindi mmene ndikayankhira.
“Tandiuza wamkulu ndani, ngati sutero ndidzakupanda!” Iye anandituzulira maso.
Ndinayankha mokhazika mtima kuti: “Kuchiyambi kwenikweni kwa Baibulo, kunalembedwa kuti, ‘Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.’” Sindinafune kuwonjezerapo zina. Anangondiyang’anitsitsa kumaso osanena chirichonse ndiyeno nkusintha nkhani.
Ndiiko komwe, kodi nchifukwa chotani chimene anandisungira m’lumande? Cholembedwa chakufufuza chinanena kuti: “Tikuopa kuti iye angasokeretse anthu ndi zolankhula zake ndi machitidwe.” Icho ndicho chifukwa chake ndinabindikiritsidwa popanda kuzengedwa mlandu.
Yehova anali pafupi ndi ine nthaŵi zonse pamene ndinkapirira zonsezi. Mwa kukoma mtima kwa Yehova, ndinapatsidwa Kabaibulo kokwana m’thumba ka Malemba Achikristu Achigiriki. Tifitifi anakaponyera m’lumande langa tsiku lina, ndikunena kuti: “Ndidzakulola ukhale nako.” Ndinakaŵerenga masiku onse moti ndinatha kuloŵeza zimene ndinkaŵerenga. Zitsanzo za kulimba mtima kwa Akristu a m’zaka za zana loyamba m’bukhu la Machitidwe zinakhala magwero amphamvu a chilimbikitso. Makalata 14 a Paulo nawonso anandilimbitsa. Paulo anakumana ndi chizunzo chachikulu, koma mzimu woyera nthaŵi zonse unamchirikiza. Zolembedwa zoterozo zinandilimbitsa.
Ndinaonda kwambiri ndi kufooka, koma Yehova anandichirikiza, kaŵirikaŵiri mwanjira zosayembekezera. Pasande ina tifitifi amene sindinakumanepo naye anabwera ndi phukusi lokulungidwa m’handikachifi. Anatsegula chitseko cha lumandelo nanditulutsira pabwalo. Pamene tinabwera pamtengo waukulu, anatsegula phukusilo. Hi, mwaona nanga! Nthochi ndi masikono zinali m’katimo. Anandiuza kudyera pompo. Tifitifiyo ananena kuti: “Nonsenu ndinu anthu abwino kwambiri. Komabe tingoyenera kukuchitirani motere. Ndifuna kusiya ntchitoyi posachedwapa.” Chotero alonda ndi atifitifi anayamba kundichitira mokoma mtima. Anandidalira ndi kundilola kuyeretsa zipinda zawo ndi kundipatsa ntchito zina zabwino.
Chakumapeto kwa 1942, ndinaitanidwa ndi mmodzi wa atifitifi amene anandimanga. “Chinkana kuti iweyo uyenera chilango cha imfa, udzamasulidwa lero,” iye analengeza tero. Mwamuna wanga anabwerera kunyumba pafupifupi mwezi umodzi ndisanamasulidwe.
Kuyambiranso Kuyanjana Ndi Mboni
Pamene tidali m’ndende, Japani inaloŵa m’Nkhondo Yadziko ya II. Ndiyeno, mu 1945, tinamva kuti Japani inagonjetsedwa m’nkhondoyo, ndipo tinaŵerenga m’nyuzipepala kuti akaidi andale zadziko akamasulidwa. Tinadziŵa kuti Mbale Kosaka adamwalira m’ndende chifukwa cha kudwala, koma ndinatumiza makalata mwamsanga ku ndende za ku Taipei, Hsinchu, ndi mizinda ina ndikufunsa kumene kunali Mbale Oe. Komabe, sindinalandire yankho lirilonse. Pambuyo pake ndinadziŵa kuti Mbale Oe adanyongedwa ndi gulu lowombera mfuti.
Mu 1948 tinalandira kalata yamwadzidzidzi kuchokera ku Shanghai. Inachokera kwa Mbale Stanley Jones, yemwe adatumizidwa ku Chaina kuchokera ku Gileadi, sukulu ya amishonale yokhazikitsidwa chatsopano ya Mboni za Yehova. Yehova adatikumbukiranso! Ndinasangalala zedi pogwirizana ndi gulu la Yehova. Panapita zaka zisanu ndi ziŵiri kuchokera pamene tinawona Mbale Oe. Ngakhale kuti ndinali wolekanitsidwa kotheratu kwa Mboni zina nthaŵi yonseyo, ndinali kuuza ena ponena za mbiri yabwino.
Pamene Mbale Jones anatichezera kwa nthaŵi yoyamba, inali nthaŵi yachisangalalo. Iye anali waubwenzi kwambiri. Ngakhale kuti sitidakumanepo naye chikhalire, zinali ngati kuti tinali kulandira wachibale wapafupi kwambiri m’nyumba mwathu. Mwamsanga pambuyo pake, Mbale Jones anapita ku T’ai-tung, kutsidya kwa mapiri, ndi mwamuna wanga monga womasulira wake. Iwo anabwerako pafupifupi mlungu umodzi pambuyo pake, m’nthaŵi imene anachititsa msonkhano wa tsiku limodzi ndi kubatiza anthu 300 a fuko la Amis a ku gombe lakum’maŵa.
Ulendo wa Mbale Jones unali wothandiza mwanjira yapadera kwa ine. Ndinali kulalikira ndekha kufikira panthaŵiyo. Ndipo tsopano aŵiri okwatirana, amene mwamuna anali mwini malo omwe tinkakhalapo, anabatizidwa mkati mwa ulendo wa Mbale Jones. Chiyambire pamenepo, ndakhala ndi chisangalalo chakupanga ophunzira kwa nthaŵi zambiri kuwonjezera pa chisangalalo cha kulengeza Ufumuwo. Pambuyo pake tinasamukira ku Hsinchu, kumene Mbale Jones anatichezera katatu, paulendo uliwonse kwa milungu iŵiri. Ndinasangalala kwambiri ndi mayanjano opindulitsawo. Panthaŵi yomalizira, iye anati: “Nthaŵi yotsatira, ndidzabwera ndi mnzanga, Harold King.” Koma “nthaŵi yotsatira” imeneyo sinabwere konse, pakuti mwamsanga pambuyo pake onse aŵiri anamangidwa m’Chaina.
Mu 1949, Joseph McGrath ndi Cyril Charles, amishonale a kalasi ya Gileadi ya 11, anafika m’Taiwan. Iwo anafutukula ntchito m’Taiwan, akugwiritsira ntchito nyumba yathu monga malo apakati ogwirirapo ntchito. Zitsanzo zawo zinandilimbikitsadi. Komabe, mkhalidwe wa ndale zadziko unawakakamiza kuchoka ndi kupita ku Hong Kong. Ndinalephera kugwira misozi pamene iwo ankapita ndi wapolisi. “Usalire, Miyo,” anatero Joe. Natinso: “Zikomo,” ndi kundipatsa peni yolemba bwino kwambiri monga chikumbukiro.
Kuphunzitsa Mwana
Mwamuna wanga ndi ine sitinakhale ndi mwana aliyense, chotero tinayamba kulera mwana wamkazi wa mbale wa mwamuna wanga pamene anali ndi miyezi inayi yakubadwa. Amayi ake anali ndi moyo wakayakaya chifukwa cha chifuŵa cha mphumo.
Mu 1952, Mbale Lloyd Barry, yemwe anali kutumikira monga mishonale m’Japani, anachezera Taiwan kuti apeze chivomerezo chalamulo cha ntchito ya Mboni za Yehova. Iye anakhala nafe ndipo anatilimbikitsa kwambiri. Panthaŵiyo mwana wathu wamkaziyo anali ndi miyezi 18 yakubadwa. Iye anamnyamula ndi kumfunsa kuti: “Kodi dzina la Mulungu ndani?” Modabwa, ndinafunsa kuti: “Kodi mutanthauza kuti tiyenera kumphunzitsa pamene ali wamng’ono motere?” “Inde,” iye anayankha mwamphamvu. Ndiyeno anandipatsa uphungu pakufunika kwakuphunzitsa mwana kuchokera pa zaka zaubwana weniweni. Mawu ake akuti: “Iye ndimphatso yochokera kwa Yehova yokupatsani chitonthozo,” anandikhala m’maganizo.
Mwamsanga, ndinayamba kuphunzitsa mwana wanga wamkaziyo, Akemi, kuti adziŵe Yehova ndi kumkonda ndi kukhala mtumiki wake. Ndinamphunzitsa zizindikiro zotchulira mawu, kuyambira ndi zilembo zitatu za e, ho, ndi ba, zimene zimapanga liwu lakuti “Ehoba,” kapena Yehova, m’Chijapanizi. Pofika zaka ziŵiri, anali wokhoza kumvetsetsa zimene ndinali kumuuza. Choncho usiku uliwonse asanagone, ndinamuuza nkhani za m’Baibulo. Iye anamvetsera ndi chikondwerero ndi kuzikumbukira.
Pamene anali wazaka zitatu ndi theka, Mbale Barry anatichezeranso ndi kupatsa Akemi Baibulo lolembedwa m’mawu Achijapanizi chozoloŵereka. Iye anayendayenda m’chipinda ndi Baibulolo, akumati: “Baibulo la Akemi! Baibulo la Akemi!” Ndiyeno pambuyo pa mphindi zochepa, iye anazaza nati: “Baibulo la Akemi liribe Yehova! Sindilifuna!” Analiponya pansi. Ndinadabwa, ndipo ndinayang’ana zamkati mwake. Choyamba ndinatsegula Yesaya mutu 42, vesi 8. Dzina la Yehova apa linaloŵetsedwa m’malo ndi “Ambuye.” Ndinayang’ananso malemba ena, koma sindinalipeze dzina laumulungu, Yehova. Akemi anatonthozedwa pamene ndinamsonyezanso dzina la Yehova m’Baibulo langa lakale, limene linali m’Chijapanizi chakale.
Kubwerera ku Japani
Tinabwerera ku Japani mu 1958 ndipo tinakagwirizana ndi Mpingo wa Sannomiya ku Kobe. Pokhala ndi zifukwa zambiri zoyamikirira Yehova, ndinafuna kusonyeza chiyamikirocho mwakukhala mpainiya—minisitala wa nthaŵi zonse wa Mboni za Yehova. Ndinadzipereka ku utumiki waupainiya. Monga chotulukapo, ndinakhoza kuchititsa maphunziro Abaibulo ambiri ndi kuchilaŵa chisangalalo chakuthandiza anthu okwanira 70 mpaka 80 kubwera m’chowonadi. Kwa nthaŵi inayake ndinakhala ndi mwaŵi wakutumikira monga mpainiya wapadera, ndikumagwira ntchito m’munda kwa maola oposa pa 150 mwezi uliwonse, pamenenso ndinasamalira mwamuna wanga ndi mwana wanga wamkazi.
Popeza kuti tinakhala m’Taiwan kwa zaka zoposa 30, moyo m’Japani unali wa miyambo yodabwitsa, ndipo ndinapyola m’zokumana nazo zovuta zambiri. Panthaŵi zoterozo Akemi anakhala chitonthozo ndi chichirikizo changa, monga momwedi Mbale Barry anandiuzira zaka zambiri kalelo. Pamene ndinachita tondovi, iye ankandiuza kuti: “Mama, limbikirani. Yehova adzakuthandizani.” “Inde, iye adzatero, sichoncho kodi?” ndinkayankha motero ndi kumkupatira mwamphamvu. Ha, iye anali chilimbikitso chotani nanga! Sindikanachitira mwina koma kumyamikiradi Yehova!
Kupereka Mwana Wanga Wamkazi kwa Yehova
Akemi anakhala wofalitsa pamene anali wazaka 7 ndipo anabatizidwa pamene anali wazaka 12, m’chilimwe cha 1963. Ndinayesa kuthera naye nthaŵi yochuluka monga momwe kunathekera. (Deuteronomo 6:6, 7) Panali nthaŵi zovuta m’nthaŵi yaunamwali wake, koma ndi zitsanzo zabwino ndi chilimbikitso kuchokera kwa apainiya apadera omwe anatumizidwa kumpingo wathu, Akemi m’kupita kwanthaŵi anachipanga kukhala chonulirapo chake kukatumikira m’magawo atsopano.
Pamsonkhano wachigawo mu 1968, iye anaseŵera mbali ya mwana wamkazi wa Yefita m’drama ya Baibulo. Pamene ndinkapenyerera dramayo, ndinapanga chosankha, monga momwe Yefita anachitira, kupereka mwana wanga wamkazi yekhayo, yemwe ndinamkonda kufikira panthaŵiyo, kwa Yehova kaamba ka uminisitala wanthaŵi zonse. Kodi moyo ukakhala wotani popanda mwana wangayo pafupi nane? Chinalidi chitokoso, popeza kuti ndinali kale woposa pazaka 60.
Mu 1970 nthaŵi inafika yakuti mwana wathu atisiye. Anapempha chilolezo kwa mwamuna wanga ndi kupita ku Kyoto kukatumikira monga mpainiya. Pokhala kuti anadziŵa mmene malingaliro athu anatikhudzira, anavutikadi mtima pamene ankatisiya. Ndinagwira mawu Salmo 126:5, 6 kumpatsa lemba lotsazikirana kuti: ‘Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera. Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbewu yakufesa; Adzabweranso ndithu ndi kufuula mokondwera, alikunyamula mitolo yake.’ Mawuŵa anakhala otonthozadi kwa inenso.
Pambuyo pake Akemi anakwatiwa ndi kupitiriza upainiya wapadera ndi mwamuna wake. Chiyambire mu 1977, pamene mwamuna wake anaikidwa kukhala woyang’anira dera, iwo akhala akutumikira m’ntchito yoyendayenda. Nthaŵi zonse ndinatambasula mapu ndi “kuyenda” pamapupo ndi mwana wanga wamkazi. Ndine wachisangalalo kumva zokumana nazo zawo ndi kudziŵana ndi alongo ambiri kupyolera mwa mwana wangayo.
Ndafikitsa kale zaka 86. Masiku omwe apitapo akuwonekera kokha ngati ulonda umodzi mkati mwa usiku. Sindithanso kugwira ntchito monga kale, koma utumiki wakumunda umandipatsabe chisangalalo. Pamene ndisinkhasinkha pa zaka 60 zimene zapitapo chiyambire pamene ndinaphunzira chowonadi, lonjezo lotsimikizirika la Mulungu limazamirako mumtima mwanga. Inde, Yehova amene adzachita mokhulupirika ndi okhulupirika akutilola kututa chisangalalo chochuluka.—Salmo 18:25.