Ntchito ya Mwamuna
“¡Ropa, zapato, casa, y comida!” Mawuŵa akuchokera ku nyimbo yakale Yachisipanya imene imandandalika zinthu zazikulu zinayi zimene mwamuna ayenera kupezera banja lake: zovala, nsapato, nyumba, ndi chakudya. Ndipo amuna athayo koposa amayesayesa monyadira kuusenza mtolo umenewo.
Komabe, ngati ndinu mwamuna wabanja, kodi mumasamalira zosoŵa zauzimu zofunika koposa za banja lanu? Kapena kodi, mofanana ndi amuna ambiri, mumaganiza kuti kusamalira nkhani zachipembedzo panyumba sikuli kwenikweni ntchito ya mwamuna? M’miyambo ina sizimayembekezeredwa konse kuti mwamuna angakhale ndi nthaŵi yakuphunzitsa ana ake ponena za Mulungu ndi Baibulo.
Mawu a Mulungu amaika makamaka pa mwamuna wa m’nyumba thayo lakuphunzitsa banja lake chikondi kwa Mulungu ndi chiyamikiro chozama cha miyezo yaumulungu. Mwachitsanzo, pa Aefeso 6:4, Malemba amafulumiza amuna Achikristu motere: ‘Atate inu, musakwiitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova, NW].’
Komabe, ena ngakhale kuti amawadziŵa mawuŵa, sangamvetsetse mofikapo kuti lembalo limasonya mwachindunji kwa tate, mwamuna wa m’nyumba. Mwachitsanzo, anthu olankhula Chisipanya ndi Chipwitikizi angamve mawu a Aefeso 6:4 kukhala akusonya kwa onse aŵiri tate ndi mayi. M’zinenero zimenezi liwu limodzimodzi lotanthauza “atate [ambiri]” limatanthauzanso “makolo.” Komabe, m’vesi 1 la Aefeso mutu 6, mtumwi Paulo analozera kwa onse aŵiri tate ndi mayi mwakugwiritsira ntchito liwu Lachigiriki lakuti go·neuʹsin, lochokera ku liwu lakuti go·neusʹ, lotanthauza “kholo.” Koma m’vesi 4, liwu Lachigiriki logwiritsiridwa ntchito linali pa·teʹres, lotanthauza “atate [ambiri].” Inde, pa Aefeso 6:4, Paulo analozeretsa mawu ake mwachindunji kwa mwamuna m’banja.
Ndithudi, ngati m’banja mulibe mwamuna wotsogoza, pamenepo mkazi ayenera kulitenga thayo limeneli. Ndi thandizo la Yehova amayi ambiri atha kulera ana awo mwachipambano m’maleredwe ndi chilangizo cha Yehova. Komabe, pamene mwamuna Wachikristu alipo, iye ayenera kutsogolera. Ngati anyalanyaza thayo limeneli, kumakhala kovuta kwambiri kwa enawo m’banja kusunga programu yabwino ya chakudya chauzimu. Ndipo mwamuna woteroyo amakhala ndi mlandu kwa Yehova wa kunyalanyaza kwakeko.
Malingaliro a Mulungu pankhaniyi ngowonekeratu m’ziyeneretso za m’Malemba zoikidwira oyang’anira ndi atumiki otumikira m’mpingo Wachikristu. Baibulo limatchula mwachindunji kuti amene amasankhidwa kaamba ka malo oterowo ndi “mwamuna wotsogoza banja lake la iye yekha m’mkhalidwe wabwino kwambiri, wokhala ndi ana ogonjera limodzi ndi kulingalira konse; (ngati ndithudi mwamuna aliyense sadziŵa kutsogoza banja lake la iye yekha, kodi iye adzasamalira bwanji mpingo wa Mulungu?).”—1 Timoteo 3:4, 5, 12, NW; Tito 1:6.
Mwamuna wabanja ayenera kukhala wofunitsitsa kudzimana zosangulutsa ndi ubwino waumwini chifukwa cha mkhalidwe wabwino wauzimu wa ana ake. Panthaŵi zina angafunikire kuchepetsako nthaŵi yochita zinthu kotero kuti apeze nthaŵi yokulirapo yoithera ndi ana ake mokhazikika. (Deuteronomo 6:6, 7) Ndiponso, iye sayenera kutulira ena thayo limeneli lopatsidwa ndi Mulungu. Chikondi chake ndi chikondwerero chake mwa ana ake chidzapitirira pakugaŵira zovala, nsapato, nyumba, ndi chakudya.
Kulera ana ‘m’maleredwe ndi chilangizo cha Yehova’ kulidi chitokoso. Ndicho chifukwa chake thayo lalikulu ndilo la mwamuna. Pamene tate Wachikristu achita mbali yake bwino lomwe, pamenepo akhoza kuyang’ana pa ana ake opatsidwa ndi Mulungu monga dalitso lochokera kwa Yehova. Iye akhoza kunena mawu a wamasalmo akuti: ‘Ana a ubwana wake wa munthu akunga mivi m’dzanja lake la chiphona. Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lake: Sadzachita manyazi iwo, pakulankhula nawo adani kuchipata.’—Salmo 127:4, 5.