Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 9/15 tsamba 3
  • Kodi Mulungu Amayankha Mapemphero Anu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mulungu Amayankha Mapemphero Anu?
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nchiyani Chimene Ena Amapempherera?
  • Mawu Oyamba
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2021
  • Kodi Ndimapemphero Ayani Omwe Amayankhidwa?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Mapemphero Amene Amayankhidwa
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 9/15 tsamba 3

Kodi Mulungu Amayankha Mapemphero Anu?

“SINDINADZIMVEPO kuti mapemphero anga ayankhidwa,” anatero mkazi wina yemwe amakhala ku Hokkaido, m’Japani. Iye sali yekha m’nkhaniyi. Anthu ambiri amalingalira kuti mapemphero awo sayankhidwa konse. Kwenikwenidi, mungakhale mukukaikira kuti kaya Mulungu amayankha mapemphero anu.

Mamiliyoni ambiri amapereka mapemphero ambirimbiri kwa milungu yosaŵerengeka. Kodi nchifukwa ninji zimawoneka kuti mapemphero ambiri samayankhidwa? Kuti tipeze yankho, tiyeni choyamba tisanthule mitundu ya mapemphero omwe amaperekedwa.

Kodi Nchiyani Chimene Ena Amapempherera?

Mkati mwa nyengo ya Chaka Chatsopano, zigawo ziŵiri mwa zitatu za anthu a ku Japani, kapena pafupifupi anthu 80 miliyoni, amapemphera mu akachisi Achishinto kapena Achibuda. Iwo amapereka makobiri monga nsembe ndi kupempherera mwaŵi ndi chisungiko cha banja.

Mu January ndi February​—mayeso odetsa nkhaŵa oloŵera makoleji otchuka asanayambe​—ophunzira amapita ku akachisi monga wa ku Tokyo wodziŵika chifukwa cha mulungu wake wamaphunziro. Iwo amalemba zokhumba zawo pa masileti amatabwa a mapemphero ndi kuwakoloweka pa mipikizo yamatabwa pa bwalo la akachisiwo. Masileti osachepera pa 100,000 ameneŵa anakometsera malo ozungulira kachisi wotchuka ku Tokyo mkati mwa nyengo yamayeso ya 1990.

Mapemphero ambiri amaloŵetsamo thanzi. Pakachisi wina ku Kawasaki, m’Japani, anthu amapempherera kutetezeredwa ku matenda a AIDS. “Cholinga chopempherera kutetezeredwa ku AIDS nchakupangitsa anthu kukhala ochenjera m’khalidwe lawo,” anafotokoza motero wansembe wakachisiyo. Koma kodi pemphero limangophatikizapo zimenezi?

Pa kachisi wina, mkazi wokalamba anapempherera “imfa yamwadzidzidzi.” Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti anafuna kupeŵa kuvutika ndi matenda kwanthaŵi yaitali ndipo sanafune kukhala chothodwetsa ku banja lake.

M’dziko lina lotchedwa Lachikristu, kaputeni wa timu ya mpira anapempherera chipambano cha timu yake ndi kutetezeredwa ku kuvulala. Akatolika ku Poland amapempherera ubwino waumwini ndipo amakometsera Namwali Mariya wawo ndi zokometsera pamene akhulupirira kuti mapemphero awo amvedwa. Anthu ambiri amapita ku matchalitchi onga ngati Guadalupe yotchuka mu Mexico City, ndi Lourdes, ku Falansa, kupempha kuchiritsa kozizwitsa.

Kukhale Kum’maŵa kapena Kumadzulo, anthu amapereka mapemphero kaamba ka zifukwa zaumwini zambiri zosiyanasiyana. Mwachiwonekere, iwo amafuna kuti mapemphero awo amvedwe ndi kuyankhidwa. Komabe, kodi kuli koyenera kuyembekezera kuti mapemphero onse adzamvedwa mwachiyanjo? Bwanji ponena za mapemphero anu? Kodi amayankhidwa? Kwenikwenidi, kodi Mulungu amayankha konse mapemphero?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena