Kodi Kuleza Mtima kwa Mulungu Kudzapitirizabe Kwautali Wotani?
PAFUPIFUPI zaka 3,000 zapitazo, mwamuna wanzeru analemba kuti: ‘Wina apweteka mnzake pomlamulira.’ (Mlaliki 8:9) Chiyambire pamene ananena mawu amenewo, mikhalidwe siinawongokere. M’mbiri yonse, anthu kapena magulu akhala akulandana ulamuliro, kulamulira ndi kupondereza anthu ena. Yehova Mulungu wapirira zonsezi moleza mtima.
Yehova waleza mtima pamene maboma akhala akuphetsa mamiliyoni a anthu m’nkhondo ndi kulola chisalungamo chochuluka m’zachuma. Lerolino, iye akusonyezabe kuleza mtima pamene anthu akuwononga chiphimba thambo ndi kuipitsa thambo ndi nyanja. Ha, ziyenera kukhala zikumpweteka chotani nanga kuwona kuwonongedwa kwa nthaka yobala ndi kwa nkhalango ndi nyama zakutchire!
Kodi Nchifukwa Ninji Mulungu Ali Woleza Mtima Motero?
Fanizo lokhweka lingatithandize kuyankha funsoli. Talingalirani chimene chikachitikira malonda pamene wantchito afika mochedwa nthaŵi zonse. Kodi mwinintchito ayenera kuchitanji? Chilungamo chosavuta chingafune kuti wantchitoyo achotsedwe mwamsanga. Koma iye angakumbukire mwambi wa Baibulo wakuti: “Wosakwiya msanga apambana kumvetsa; Koma wansontho akuza utsiru.” (Miyambo 14:29) Kumvetsa kungampangitse kuyembekeza asanachitepo kanthu. Iye angasankhe kulola nthaŵi yakuti woikidwa pamalopo aphunzitsidwe kotero kuti malondawo asadodometsedwe moposerapo.
Chifundo chingampangitsenso kuyembekeza. Bwanji ngati amchenjeza wantchito wosasamalayo kuwona ngati adzasintha mkhalidwe wake? Bwanji osalankhula naye ndi kuwona ngati chizoloŵezi chake chakuchedwa chimachititsidwa ndi vuto limene likhoza kuthetsedwa kapena ndi mkhalidwe woipa wosachiritsika? Komabe, ngakhale kuti mwinimalondayo angafune kukhala woleza mtima, kuleza mtima kwakeko sikudzakhala kopanda malire. Wantchitoyo adzangofunikira kaya kusintha kapena kuchotsedwa ntchito potsirizira pake. Zimenezo zikakhala chilungamo ku malonda enieniwo ndi kwa antchito amene amatsatira malamulo.
Mwa njira yofananayo, Yehova Mulungu amasonyeza kuleza mtima pamene alakwiridwa kotero kuti alole nthaŵi kaamba ka njira yolungama yothetsera mavuto ena. Ndiponso, kuleza mtima kwake kumapatsa ochimwawo mwaŵi wakusintha njira zawo ndi kupeza mapindu amuyaya. Chifukwa chake, Baibulo limatilimbikitsa kusakhumudwa ndi kuleza mtima kwa Mulungu. Mmalo mwake, limati: ‘Yesani kulekerera kwa Ambuye wathu chipulumutso.’—2 Petro 3:15.
Chitsanzo cha Kuleza Mtima kwa Mulungu
Yehova Mulungu anali woleza mtima pamene Chigumula chachikulu cha m’tsiku la Nowa chinali chisanadze. Dziko lapanthaŵiyo linadzala ndi chiwawa ndipo linali loipa kwenikweni. Timaŵerenga kuti: ‘Anawona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu pa dziko lapansi, . . . Ndipo anati Yehova, Ndidzafafaniza anthu amene ndawalenga pa dziko lapansi.’ (Genesis 6:5, 7) Inde, Yehova anali ndi yankho lotheratu ku vuto la kuipa kokhalako panthaŵiyo: kuchotsedwapo kwa anthu oipa. Koma iye sanachitepo kanthu mwamsanga. Chifukwa ninji sanatero?
Chifukwa chakuti sialiyense anali woipa. Nowa ndi banja lake anali olungama pamaso pa Mulungu. Motero chifukwa cha iwo, Yehova anayembekezera moleza mtima kuti alole anthu olungama oŵerengekawo kukonzekera kaamba ka chipulumutso. Ndiponso, kuyembekezera kwakutali kumeneko kunapatsa Nowa mwaŵi wakukhala ‘mlaliki wa chilungamo,’ akupereka mwaŵi kwa anthu oipawo wakusintha njira zawo. Baibulo limati: ‘Kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira, m’masiku a Nowa, pokhala m’kukonzeka chingalaŵa, m’menemo oŵerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi.’—2 Petro 2:5; 1 Petro 3:20.
Chifukwa Chake Mulungu Ali Woleza Mtima Tsopano
Lerolino, mkhalidwe uli wofanana. Dziko lirinso lodzaza ndi chiwawa. Monga m’tsiku la Nowa, Mulungu waliweruza kale dziko lino, limene, malinga ndi kunena kwa Baibulo, ‘lasungika kufikira tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osapembedza.’ (2 Petro 3:7) Chimenecho chitachitika, sipadzakhalanso kuwononga malo okhala, kudidikiza ofooka, kapena kugwiritsira ntchito ulamuliro mwaumbombo.
Pamenepa, kodi nchifukwa ninji Mulungu sanawawononge kalekale anthu osapembedza? Chifukwa chakuti panabuka nkhani zofunikira kuthetsedwa ndipo pali zinthu zazikulu zoti zikonzedwe. Ndithudi, Yehova akukonza yankho lokhalitsa lothetsera vuto la kuipa loloŵetsamo zambiri, kuphatikizapo kumasulidwa kwa anthu owongoka mtima ku matenda ndi imfa.
Pokhala ndi cholinga chomalizira chimenechi, Yehova anafuna kupereka Mpulumutsi yemwe akapereka dipo kaamba ka machimo athu. Ponena za iye, Baibulo limati: ‘Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asataike, koma akhale nawo moyo wosatha.’ (Yohane 3:16) Kunatenga zaka zikwizikwi kukonzekera njira yakuti Yesu abwere ndi kupereka moyo wake nsembe kaamba ka anthu. Mkati mwa zaka zonsezo, Mulungu anali woleza mtima mwachikondi. Koma kodi makonzedwe oterowo sanali oyenerera kuyembekezera?
Yesu anapereka dipo kaamba ka anthu pafupifupi zaka zikwi ziŵiri zapitazo. Nangano, nchifukwa ninji Mulungu akusonyezabe kuleza mtima? Chimodzi cha zifukwa nchakuti, imfa ya Yesu inazindikiritsa kuyambika kwa ndawala ya kuphunzitsa. Anthu anafunikira kuphunzira ponena za makonzedwe achikondi ameneŵa ndi kupatsidwa mwaŵi wakuwalandira kapena kuwakana. Zimenezo zikatenga nthaŵi, koma ikakhala nthaŵi yowonongedwa bwino. Baibulo limati: ‘[Yehova, NW] sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.’—2 Petro 3:9.
Nkhani ya Boma
Chinthu china chofunika chikatenganso nthaŵi. Panali kufunika kwakuthetsa vuto la boma la anthu. Poyamba, munthu anali pansi pa boma laumulungu. Koma m’munda wa Edene, makolo anthu oyambirira anafulatira chimenecho. Iwo anasankha kusadalira Mulungu, nafuna kudzilamulira okha. (Genesis 3:1-5) Komatu, munthu sanalengedwe kuti adzilamulire yekha. Mneneri Yeremiya analemba kuti: ‘Inu Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu siiri mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.’—Yeremiya 10:23; Miyambo 20:24.
Komabe, chiyambire pamene nkhani ya boma inabuka, Yehova walola nthaŵi yoithetsera moleza mtima. Ndithudi, iye mooloŵa manja walola zaka zikwizikwi kuti munthu ayese mtundu uliwonse wa boma. Ndi chotulukapo chotani? Kwakhala kowonekera kuti palibe boma laumunthu limene lingachotsepo kutsendereza, tsankho, kapena zifukwa zina zosoŵetsa chimwemwe.
Ndithudi, polingalira mbiri ya anthu, kodi wina anganene kuti Mulungu ali wosalungama pamene akulengeza chifuno chake chakuchotsapo maboma onse aumunthu ndi kuwaloŵa m’malo ndi limodzi la iye mwini? Ndithudi ayi! Timakulandira ndi manja aŵiri kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo uwu: ‘Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.’—Danieli 2:44.
Mfumu yakumwamba ya Ufumu umenewo ali Yesu woukitsidwayo. Kumkonzekeretsa kaamba ka malo amenewo—limodzinso ndi kusankha anthu omwe adzakhala olamulira anzake—kwatenga nthaŵi. Mkati mwa nthaŵi yonseyo, Mulungu wasonyeza kuleza mtima.
Pindulani Tsopano ndi Kuleza Mtima kwa Mulungu
Lerolino, mamiliyoni a anthu m’maiko osachepera pa 212 akupindula ndi kuleza mtima kwa Mulungu. Iwo agwirizana m’chikhumbo chawo chakumvera Mulungu ndi kutumikira boma lake lakumwamba. Pamene asonkhana pamodzi m’Nyumba zawo Zaufumu, amaphunzira mmene kuliri kwabwinopo kugwiritsira ntchito miyezo yamakhalidwe abwino ya Baibulo m’miyoyo yawo. Iwo samakhala ndi phande m’ndale zogaŵanitsa za dziko lino, ngakhale kuti amagonjera ku maboma aumunthu malinga ngati Mulungu moleza mtima akuwalolabe kulamulira.—Mateyu 22:21; Aroma 13:1-5.
Kugwirizana kotero kwa anthu ambiri kumalemekeza Yehova monga Uyo amene akhoza kubweretsa chigwirizano pakati pa anthu okhala ndi ufulu wodzisankhira omwe amaphunzira kumkonda ndi ofuna kumtumikira. Mosakaikira inu mwakumana nawo ameneŵa pamene akupitiriza ndi ntchito imodzimodzi imene Yesu iyemwini anaiyamba, yakufalitsa mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. Yesu ananeneratu za chimake cha ntchito imeneyi pamene anati: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.”—Mateyu 24:14, NW.
Sikunatsale Nthaŵi Yaitali!
Maumboni owoneka amatsimikizira kuti makonzedwe akuti boma lolungama la Mulungu lilande kulamulira kwa tsiku ndi tsiku kwa dziko lapansi atsala pang’ono kumalizidwa. Pambuyo pofotokoza zotulukapo zoipitsitsa za kulephera kwa boma laumunthu zimene taziwona m’zaka za zana lino, Yesu anati: ‘Pakuwona zinthu izi zirikuchitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi.’—Luka 21:10, 11, 31.
Posachedwapa, Mulungu adzachotsapo oipa pa nkhope ya dziko lapansi. Mawu a wamasalmo aŵa adzakhala ndi tanthauzo m’lingaliro lenileni: ‘Ochita zoipa adzadulidwa . . . Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti: Inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe.’ (Salmo 37:9, 10) Kodi mutha kuyerekezera dziko lopanda kuipa? Kodi ndani amene adzayendetsa zinthu panthaŵiyo? Baibulo limati: ‘Mfumu [Kristu Yesu wovekedwa ufumu kumwamba] idzalamulira m’chilungamo, ndi akalonga [oikidwa ake okhulupirika padziko lapansi] adzalamulira m’chiweruzo. Ndi ntchito ya chilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata chilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika ku nthaŵi zonse. Ndipo anthu anga adzakhala m’malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phe.’—Yesaya 32:1, 17, 18.
Chotero, boma lakumwamba la Mulungu lidzachotsapo ziyambukiro zoipa za zolakwa zochitidwa ndi anthu ndi kulinganiza awo oyembekezera Iye kukhala chitaganya cha anthu ogwirizana. Polongosola kugwirizana kumeneku, Baibulo limati: ‘Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango ndi choweta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera. . . . Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.’—Yesaya 11:6-9.
Ha, nchotulukapo cholemekezeka chotani nanga cha kusonyeza kuleza mtima kwa Mulungu! Chifukwa chake, mmalo moŵiringula kuti Mulungu wayembekeza mopambanitsa, bwanji osautenga mwaŵi wa kuleza mtima kwake kudzigonjeretsa ku Ufumu wake? Phunzirani miyezo yake m’Baibulo ndipo mamatirani ku iyo. Yanjanani ndi ena omwe amadzigonjetsera kwa iye mogwirizana. Pamenepo, kuleza mtima kwa Mulungu kudzatulukapo madalitso osatha kwa inuyo.