Kodi kugonjera mu Ukwati Kumatanthauzanji?
PAMENE mkazi Wachikristu akwatiwa, afunikira kupanga masinthidwe ambiri. Mwinamwake masinthidwe aakulu koposa amayambukira ufulu wake. Monga mbeta yachikulire, iye angakhale anali ndi ufulu wakupanga zosankha zake zambiri popanda kufunsa aliyense. Koma popeza tsopano ali ndi mwamuna, ali ndi thayo la kumfunsa ndi kupempha chilolezo chake kuchita zinthu zambiri zimene ankadzichitira yekha. Kodi nchifukwa ninji ziri choncho?
Chifukwa chakuti pamene Mlengi wa munthu anapereka mkazi woyamba muukwati kwa mwamuna woyamba, Iye anaika mwamunayo kukhala mutu wa mkazi wake ndi ana awo a mtsogolo. Ichi chinali chanzeru. M’gulu lirilonse lolinganizika la anthu, munthu wina amafunikira kutsogolera ndi kupanga zosankha zomalizira. Muukwati, Mlengi analamula kuti “mwamuna ndiye mutu wa mkazi.”—Aefeso 5:23.
Pochilikiza chimenechi, lamulo la Mulungu limati: “Akazi inu, mverani amuna anu a inu eni.” (Aefeso 5:22) Kuyambukiridwa kwa mkazi ndi kakonzedwe kameneka kumadalira pa zinthu ziŵiri: Choyamba, kodi ali wofunitsitsa motani kugonjera ku kakonzedweka? ndipo chachiŵiri, kodi mwamuna wake adzasonyeza motani ulamuliro wake? Kunena zowona, pamene okwatirana onse aŵiri awona kakonzedweka moyenerera, iwo amapeza kuti kali dalitso kwa mkazi, mwamuna, ndi ana awo.
Osati Wankhalwe
Kodi mwamuna ayenera kusonyeza motani ulamuliro wake? Mwakutsatira chitsanzo chabwino cha Mwana wa Mulungu. Baibulo limati: ‘Mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Kristu ndiye mutu wa [mpingo, NW] ali yekha Mpulumutsi wa thupilo. Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Kristu anakonda [mpingo, NW] nadzipereka yekha m’malo mwake.’ (Aefeso 5:23, 25) Kusonyeza umutu kwa Yesu Kristu kunali dalitso ku mpingo. Iye sanali wankhalwe. Sanapangitse ophunzira ake kumva kukhala otchingiridwa kapena oponderezedwa. M’malomwake, analandira ulemu wa onse chifukwa cha kachitidwe kake kachikondi ndi kachifundo kwa iwo. Ha, chiri chitsanzo chabwino chotani nanga kwa amuna kuchitsatira m’kuchita kwawo ndi akazi awo!
Komabe, pali amuna amene samatsatira chitsanzo chabwino chimenechi. Iwo amagwiritsira ntchito umutu wawo wopatsidwa ndi Mulungu mwadyera, m’malo mwa ubwino wa akazi awo. Amalamulira akazi awo m’njira yankhalwe, akumalamula kuti awagonjere kotheratu ndipo kaŵirikaŵiri samawalola kupanga zosankha zawo zirizonse. Momvekera bwino, akazi a amuna oterowo kaŵirikaŵiri amakhala osasangalala. Ndipo mwamuna woteroyo amavutikanso chifukwa chakuti amalephera kulandira ulemu wachikondi wa mkazi wake.
Zowonadi, Mulungu amafuna kuti mkazi alemekeze udindo umene mwamuna wake ali nawo monga mutu wa banja. Koma ngati mwamunayo akufuna kusangalala ndi ulemu wochokera mumtima wa mkaziyo kwa iye monga munthu, ayenera kuuyenerera, ndipo njira yabwino koposa yochitira zimenezo ndiyo kuchita mwathayo ndi kukulitsa mikhalidwe yabwino, yaumulungu monga mutu wa banja.
Kugonjera Kuli ndi Malire
Ulamuliro wa mwamuna pa mkazi wake suli wotheratu. M’njira zina kugonjera kwa mkazi kungayerekezeredwe ndi kugonjera kwa Mkristu kwa wolamulira wakudziko. Mulungu analamula kuti Mkristu ayenera “kugonjera maulamuliro aakulu.” (Aroma 13:1, NW) Komabe nthaŵi zonse kugonjera kumeneku kumalinganizidwa ndi mangawa athu kwa Mulungu. Yesu anati: ‘Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu.’ (Marko 12:17) Ngati Kaisara (boma ladziko) afuna kuti timpatse zimene ziri za Mulungu, timakumbukira zimene mtumwi Petro ananena: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”—Machitidwe 5:29.
Mwanjira yofananayo, ngati mkazi Wachikristu wakwatiwa ndi mwamuna amene samamvetsetsa kapena amalephera kulemekeza malamulo amakhalidwe abwino Achikristu, mkaziyo akali ndi thayo lakugonjera kwa mwamunayo. M’malo mopandukira kakonzedwe koikidwa ndi Mulungu kameneka, mkaziyo akachita bwino kumsonyeza mwamunayo chikondi ndi kulingalira ndipo motero kuyesa kupeza chidaliro cha mwamunayo. Mwinamwake khalidwe labwino loterolo lidzampangitsa mwamuna wake kusintha; mwinamwake lingampindule kukhala m’chowonadi. (1 Petro 3:1, 2) Ngati mwamuna wake alamula kuti achite chinthu choletsedwa ndi Mulungu, mkaziyo ayenera kukumbukira kuti Mulungu ndiye Wolamulira wake wamkulu. Mwachitsanzo, ngati mwamunayo afuna kuti mkaziyo achite machitachita ena oluluzika akugonana, monga ngati kusinthana akazi, mkaziyo ali ndi thayo la kusagonjera. (1 Akorinto 6:9, 10) Kugonjera mwamuna wake kuli kolamuliridwa ndi chikumbumtima chake ndi kugonjera kwake koyambirira kwa Mulungu.
M’nthaŵi ya Mfumu Davide, Abigayeli anakwatiwa ndi Nabala, mwamuna amene sanalemekeze malamulo amakhalidwe abwino aumulungu ndipo anachita mwankhanza ndi mopanda chikondi kwa Davide ndi anyamata a Davide. Anthuwa anachinjiriza zikwi za nkhosa ndi mbuzi za Nabala, koma pamene Davide anapempha chakudya, Nabala anakana kupereka kalikonse.
Pamene anamva kuti mkhalidwe waumbombo wa mwamuna wake ukabweretsa tsoka pabanjapo, Abigayeli anasankha yekha kukapereka chakudya kwa Davide. ‘Abigayeli anafulumira, natenga mikate mazana aŵiri, ndi zikopa ziŵiri za vinyo, ndi nkhosa zisanu zootchaotcha, ndi miyeso isanu ya tirigu wokazinga, ndi ntchintchi za mpesa zouma zana limodzi, ndi ntchintchi za nkhuyu mazana aŵiri, naziika pa aburu. Nati kwa anyamata ake, Nditsogolereni; onani ndidza m’mbuyo mwanu. Koma sanauza mwamuna wake Nabala.’—1 Samueli 25:18, 19.
Kodi Abigayeli analakwa mwakuchita mosemphana ndi chifuniro cha mwamuna wake? Osati pankhaniyi. Kugonjera kwa Abigayeli sikunafunikire kuti akhale wopanda chikondi mofanana ndi mwamuna wake, makamaka popeza kuti kachitidwe kopanda nzeru ka Nabala kanaika paupandu banja lake lonse. Chifukwa chake, Davide anati kwa mkaziyo: ‘Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israyeli, amene anakutumiza lero kudzandichingamira ine; ndipo, kudalitsike kuchenjera kwako.’ (1 Samueli 25:32, 33) Mofananamo, akazi Achikristu lerolino sayenera kudodometsa ndi kupandukira umutu wa amuna awo, koma ngati amunawa achita kachitidwe kosakhala Kachikristu, akaziwo sayenera kuwatsatira pachimenechi.
Zowonadi, m’kalata yake yopita kwa Aefeso Paulo anati: ‘Komatu monga [mpingo, NW] umvera Kristu, koteronso akazi amvere amuna awo m’zinthu zonse.’ (Aefeso 5:24) Kugwiritsira ntchito kwa mtumwiyo mawu akuti “zinthu zonse” panopa sikumatanthauza kuti kugonjera kwa mkazi kulibe malire. Mawu a Paulo akuti, ‘monga mpingo umvera Kristu,’ amasonyeza zimene anali kulingalira. Zinthu zonse zimene Kristu amafuna kuchita ku mpingo wake ziri zolungama, zogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Chotero, mpingo ukhoza kugonjera iye mosavuta ndiponso mwachimwemwe m’zinthu zonse. Mofananamo, mkazi wa mwamuna Wachikristu amene amayesayesa mwamphamphu kutsatira chitsanzo cha Yesu adzakhala wachimwemwe kukhala wogonjera kwa iye m’zinthu zonse. Mkaziyo amadziŵa kuti mwamunayo ali wodera nkhaŵa kwambiri ndi zabwino za mkaziyo, ndipo mwamunayo sadzampempha dala kuchita chinachake chosemphana ndi chifuniro cha Mulungu.
Mwamuna adzasunga chikondi ndi ulemu wa mkazi wake pamene asonyeza mikhalidwe yaumulungu ya mutu wake, Yesu Kristu, amene analamula otsatira ake kukondana wina ndi mnzake. (Yohane 13:34) Ngakhale kuti mwamunayo ali wokhoza kulakwa ndi wopanda ungwiro, ngati asamalira ulamuliro wake mogwirizana ndi umutu wapamwamba wa Kristu, amakupanga kukhala kosavuta kwa mkazi wake kukhala wachimwemwe kukhala naye monga mutu wake. (1 Akorinto 11:3) Ngati mkazi akulitsa mikhalidwe Yachikristu ya kudzichepetsa ndi chikondi chokoma mtima, sikumakhala kovuta kwa iye kugonjera kwa mwamuna wake.
Wodzichepetsa ndi Wolingalira
Amuna okwatira ndi akazi okwatiwa mumpingo ali abale ndi alongo auzimu okhala ndi kaimidwe kolingana pamaso pa Yehova. (Yerekezerani ndi Agalatiya 3:28.) Komabe, amuna anagaŵiridwa ndi Mulungu kukhala oyang’anira mpingo. Ichi chimalandiridwa mwachimwemwe ndi akazi owongoka mtima mogonjera kotheratu. Ndipo thayo lolemera limene limaikidwa pa amuna la kusaŵeta nkhosa mokangamiza limalandiridwa modzichepetsa ndi amuna achikulire mumpingo.—1 Petro 5:2, 3.
Ngati pali unansi woterowo pakati pa amuna ndi akazi mumpingo, kodi ndimotani mmene mwamuna Wachikristu angalungamitsire kuchitira kwake mkazi wake, mlongo wake wauzimu, mwankhalwe? Ndipo kodi mkaziyo angalungamitse motani kupikisana kwake ndi mwamuna wake kaamba ka umutu? M’malomwake, iwo ayenera kuchitirana monga momwe Petro akuchenjezera ziŵalo zonse za mpingo kuti: ‘Khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa.’ (1 Petro 3:8) Paulo nayenso anapereka uphungu wakuti: ‘Valani, . . . mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso [Yehova, NW] anakhululukira inu, teroni inunso.’—Akolose 3:12, 13.
Mikhalidwe yoteroyo iyenera kukulitsidwa mumpingo. Ndipo iyenera kukulitsidwa makamaka pakati pa mwamuna ndi mkazi m’nyumba Yachikristu. Mwamuna angasonyeze chikondi chake ndi chifatso mwakumvetsera ku malingaliro a mkazi wake. Ayenera kulingalira mfundo ya mkazi wake asanapange chosankha chokhudza banja. Akazi Achikrsitu sali opanda nzeru. Kaŵirikaŵiri akhoza kupatsa amuna awo malingaliro opindulitsa, monga momwe Sara anaperekera kwa mwamuna wake, Abrahamu. (Genesis 21:12) Kumbali ina, mkazi Wachikristu sadzapempha mosayenerera kwa mwamuna wake. Iye adzasonyeza kukoma mtima kwake ndi kudzichepetsa maganizo mwakutsatira chitsogozo chake ndi kuchilikiza zosankha zake, ngakhale kuti nthaŵi zina zingasiyane ndi zofuna zake.
Mwamuna wolingalira, mofanana ndi mkulu wolingalira, ali wofikirika ndi wokoma mtima. Mkazi wachikondi amavomereza mwakukhala wokoma mtima ndi woleza mtima, kuzindikira zoyesayesa zimene mwamunayo amapanga kukwaniritsa mathayo ake mosasamala kanthu za kupanda ungwiro ndi zitsenderezo za moyo. Pamene mikhalidwe yoteroyo ikulitsidwa ndi onse aŵiri mwamuna ndi mkazi, kugonjera mu ukwati sikudzakhala vuto. M’malomwake, kumakhala magwero a chimwemwe, chisungiko, ndi chikhutiro chosatha.