Kodi Pali Uminisitala Umene Mungachite?
YEHOVA wasonyeza kuoloŵa manja kwake mwakugaŵira zochuluka padziko lapansi kuti tisangalale ndi moyo. Mwakuoloŵa manja kwake analola zogaŵira zimenezi kukhalapobe ngakhale pambuyo pa kupanduka kwa Adamu ndi Hava. Kuwonjezerapo, iye anasonyeza chikondi chake chopambana mwakutumiza Mwana wake kudzapulumutsa anthu okhulupirira ku tsoka la tchimo.—Mateyu 5:45; Yohane 3:16.
Kodi tingalabadire motani ku chikondi choterocho? Yesu anati tiyenera kukonda Yehova Mulungu wathu ndi mtima wathu wonse, moyo, nzeru ndi mphamvu. Ichi chimasonyeza kuti tiri ndi thayo lakupereka kulambira kwathu ndi kukhulupirika kwa iye ndikuti tiyenera kukhala ndi moyo mogwirizana ndi chifuniro chake.—Marko 12:30; 1 Petro 4:2.
Koma kodi kuchita chifuniro cha Mulungu kumaphatikizapo chiyani? Kodi pali utumiki umene tingamchitire—uminisitala umene tiyenera kukhalamo ndi phande?
Kufunika kwa Aminisitala
Matchalitchi asocheretsa anthu m’kulambira ndi kutumikira Mulungu. Komabe, Baibulo limasonyeza kuti pali chipembedzo chowona chimodzi chokha, ‘Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi; Mulungu mmodzi ndi Atate wa anthu onse.’ Yesu anati: ‘Olambira owona adzalambira Atate mumzimu ndi m’chowonadi.’ Chotero akupatsidwa uphungu wakuti: “Muyenera nonse kulankhula mogwirizana, ndikuti . . . pasakhale magaŵano pakati panu.”—Aefeso 4:3-6; Yohane 4:23; 1 Akorinto 1:10, NW.
Chisokonezo chakusadziŵa chipembedzo chowona chinayambira m’Edene pamene Satana anatokosa kuyenerera kwa ulamuliro wa Yehova mwakukaikiritsa njira ya kulamulira ya Mulungu. (Genesis 3:1-6, 13) Satana tsopano akuchirikiza kutsutsa Mulungu kumeneku mwaziphunzitso zonyenga zofalitsidwa ndi aminisitala achipembedzo onyenga amene ‘adziwonetsa monga atumiki achilungamo.’ Chotero Baibulo limati: ‘Okondedwa, musamakhulupirira [mawu owuziridwa aliwonse, NW] . . . popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kuloŵa m’dziko lapansi.’—2 Akorinto 11:14, 15; 1 Yohane 4:1.
Ubwino wake ngwakuti, Mulungu akuchitapo kanthu kuthetsa nkhani imeneyi ya ulamuliro. Popeza kuti anatumiza Mwana wake kudzawombola anthu, iye tsopano waika Yesu kukhala Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu, ndi kumpatsa ulamuliro wakuwononga Satana ndi aneneri ake, kapena aminisitala. Ichi chidzatsimikiziritsa kuchitidwa kwa chifuniro cha Mulungu padziko lapansi, kaamba ka madalitso osatha kwa anthu omvera.—Danieli 7:13, 14; Ahebri 2:9.
Satana waphimba zowona zimenezi. (2 Akorinto 4:4) Chotero, pali chifuno chakuti titumikire monga aminisitala a Mulungu, tikumavumbula zinyengo za Satana ndi kuchitira umboni chowonadi. Yehova samatikakamiziramo muutumiki umenewu. Iye amafuna kuti ife, mofanana ndi Yesu, tidzipereke mofunitsitsa kaamba ka chiyamikiro chathu kwa iye ndi zimene watichitira.—Salmo 110:3; Ahebri 12:1-3.
Uminisitala Wachikristu
Yesu ‘anayendayenda kumizinda ndi kumidzi, kulalikira ndi kuwauza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.’ (Luka 8:1) Iye anaphunzitsanso ophunzira ake kukhala aminisitala monga iye ndi kuwatumiza kukalalikira. (Mateyu 10:1-14, 27) Pambuyo pake, iye anawatuma kupitiriza uminisitala kumbali zakutali za dziko lapansi.—Mateyu 28:19, 20; Machitidwe 1:8.
Ntchito imeneyi iri pa Akristu owona, ndipo mzimu wa Mulungu umawasonkhezera kulalikira. Monga momwe zinachitikira pa Pentekoste wa 33 C.E., onse amene amalandira mbiri yabwino amatenga thayo lakupanga chilengezo chapoyera cha chikhulupiriro chawo.—Machitidwe 2:1-4, 16-21; Aroma 10:9, 13-15.
Komabe, anthu ambiri samafuna kukhala aminisitala. Peter, mmodzi wa Mboni za Yehova, akunena kuti: “Anthu ambiri ku Jeremani kaŵirikaŵiri amawona kulankhula ponena za chipembedzo kukhala chinthu chowachotsera ulemu wawo. ‘Atsogoleri achipembedzo ndiwo ayenera kuchita zimenezo,’ iwo amatero.” Tony, yemwe wakhala mishonale kwa zaka makumi ambiri, anati anthu m’Mangalande amanena kuti: “Zimene mumanena nzabwino, ndipo ndiganiza kuti Mboni za Yehova ndianthu abwino. Koma kumalalikira kunyumba ndi nyumba—sindingachite zimenezo.” Ben anaphunzira Baibulo kwa nyengo yakutiyakuti ndi mwamuna wa ku Nigeria amene anamuuza kuti: “Sindingapite kukawonekera poyera ndikulalikira kunyumba ndi nyumba; koma ndikhoza kupereka ndalama kumpingo wanu kuthandiza aja ofunitsitsa kuchita zimenezo.” Inde, anthu ochuluka amasoŵa chikhulupiriro ndi chikhutiritso zofunikira kaamba ka uminisitala Wachikristu.
Komabe, kulalikira poyera kuli thayo la onse mumpingo Wachikristu, mosasamala kanthu za msinkhu kapena kuti ndimwamuna kapena mkazi. Suli wa akulu okha ndi atumiki otumikira, amene ‘amatsogolera,’ komanso wa Akristu onse. Onse akufulumizidwa kuti: ‘Perekani chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake. . . . Mverani atsogoleri anu.’—Ahebri 13:15, 17.
Polankhula kwa khamu la anthu osiyanasiyana mu Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu anati: ‘Si yense wakunena kwa ine, Ambuye, Ambuye, adzaloŵa mu ufumu wakumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wakumwamba.’ Pachochitika china iye anasonyeza kuti kuchita chifuniro cha Mulungu kumaphatikizapo kulalikira kwa osakhulupirira. Ophunzira ake anamkokosa kuleka kulalikira kwa Asamariya kuti adye, koma iye anati: ‘Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha iye amene anandituma ine, ndi kutsiriza ntchito yake.’—Mateyu 7:21; Yohane 4:27-38.
Kodi Uyenera Kukhala Ntchito Yanu?
Kaŵirikaŵiri anthu amakonda kulondola zakudya zakuthupi ndi chuma. Koma kuchiyambi kwa Ulaliki wa pa Phiri, Yesu anawachenjeza omvetsera ake ponena za kulondola zinthu zoterezo mofunitsitsa. ‘Koma,’ iye anatero, ‘mudzikundikire nokha chuma m’mwamba . . . Muthange mwafuna ufumu wake ndi chilungamo [cha Mulungu].’—Mateyu 6:20, 33.
Kufuna choyamba Ufumu kumatanthauza kusalola zikondwerero zina kuphimba uminisitala wathu. Komabe, kuchita chimenechi sikumatanthauza kuleka zina zonse. Mwachitsanzo, Baibulo limatilimbikitsa kusanyalanyaza mathayo abanja oyenerera. Anthu tonsefe tiri nawo mathayo ameneŵa. Kuwanyalanyaza ndikuchita mwanjira yosemphana ndi chikhulupiriro Chachikristu. (1 Timoteo 5:8) Komabe, tiyenera kuchita zonse zimene tingathe moyenera muuminisitala pamene tikusamalira mathayo ena mwanjira yolinganizika.
Yesu anati: “Mbiri yabwino imeneyi ya Ufumu idzalalikidwa . . . kaamba ka umboni ku mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14, NW) Mawu apatsogolo ndi apambuyo a ulosiwo amaika kukwaniritsidwa kwake m’tsiku lathu. Chiyambire mu 1914 mbiri yabwino njakuti Ufumuwo wapatsidwa mphamvu yakuchitapo kanthu mochirikiza ufumu wa Yehova ndi kutsutsa Satana ndi dziko lake. (Chibvumbulutso 11:15-18) Tiyenera kuganiza mwamphamvu pa zimene izi zikutanthauza. Mapeto adzafika, ndipo tiyenera kumaliza ntchito yolalikira nthaŵiyo isanafike. Miyoyo iri pachiswe; tikhoza kuthandiza ambiri kupulumuka.
Kalimirani Uminisitala Wowonjezereka
Mboni za Yehova zambiri zimapereka maola khumi kapena kuposapo mwezi uliwonse kugaŵana mbiri yabwino ndi ena. Zikwizikwi amathera maola aŵiri kapena kuposapo patsiku akulalikira monga apainiya othandiza, ndipo ena amatumikira mopitiriza monga apainiya okhazikika ndi apadera. Iwo amazindikira kufulumira kwa ntchitoyi ndipo amafuna kukhala ndi phande lokwanira koposa kuti imalizidwe mapeto a dziko lino lopanda chimwemwe asanafike.
Kodi ndinu kale Mboni yokangalika ya Yehova? Pamenepo kalimirani kukhala ndi phande lowonjezereka muutumikiwo. Wongolerani luso lanu m’kulalikira ndi kuphunzitsa, mukuyesa kukwaniritsa zowonjezereka muuminisitala. Ngati muli mumkhalidwe wokhoza kukhala mpainiya, chitani tero. Ngati mikhalidwe yanu sikulolani kwenikweni, pamenepo limbikitsani awo amene angathe kukalimirira utumiki umenewu.
Ngati sindinu Mboni yodzipereka ya Yehova, musanene kuti uminisitalawo suli wanu. Mwamuna wina wotchedwa Peter, injiniya waumakanika, anatsutsa mwamphamvu kuti mkazi wake adzikhala ndi phande m’kugawana mbiri yabwino ndi ena. “Mkazi wanga angamalalikire bwanji kunyumba ndi nyumba?” iye ankafunsa tero. Pambuyo pa zaka zakuwona kutsimikiza mtima kwa mkaziyo m’chowonadi cha Mawu a Mulungu, iye anasankha kuyamba kuphunzira Baibulo nayenso. Tsopano, mofanana ndi mkazi wake, ali minisitala wodzipereka, wobatizidwa wa mbiri yabwino.
Chotero musadzimane mwaŵi wakutumikira Yehova. Tikukulimbikitsani kuphunzira Baibulo ndi kuyanjana ndi Akristu owona pamisonkhano yawo. Izi zidzakuthandizani kuwumba moyo wanu mogwirizana ndi chilungamo cha Mulungu ndi kumanga chikhulupiriro cholimba m’zifuniro zake. Ngati mupanga kupita patsogolo m’zimenezi, nanunso mudzayeneretsedwa kukhala minisitala wa Mulungu. Pamenepo mudzakhala ndi mwaŵi wakukhala ndi phande m’kukwaniritsa lamulo la Yesu ili: “Chifukwa chake mukani ndi kupanga ophunzira . . . mukumawaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndakulamulirani.”—Mateyu 28:19, 20, NW.
Inde, pali uminisitala umene mungakhalemo ndi phande, ndipo muyenera kutero mofulumira kuposa ndi kale lonse.
[Bokosi patsamba 25]
Nesi wokhala ndi banja lolisamalira akunena kuti: “Ndimayenda koposa ola limodzi tsiku lirilonse kupita ku chipatala kumene ndimagwira ntchito, choncho ndinaganiza kuti sindingathe kuchita upainiya wothandiza. Koma ndinalinganiza zochita zanga mosamalitsa kuti ndikhale ndi phande muutumiki wakumunda m’maŵa uliwonse ndisanapite kuntchito, panthaŵi yakupuma kuntchito, ndi pamasiku atchuthi. Tangolingalirani chisangalalo changa pamene, pakutha mwezi umodzi, ndinathera maola 117 muulaliki! Ndinagaŵira magazini 263, masabusikripishoni amagazini 22 ndipo ndinayambitsa maphunziro Abaibulo 3.”
[Bokosi patsamba 27]
Michael ali ndi ana aang’ono asanu ndi aŵiri, ndipo ali ndi malo aakulu pantchito pa koleji ya ku Nigeria. Iye alinso mkulu mumpingo Wachikristu. Alinso ndi malingaliro ofanana ndi a zikwi zambiri za Mboni akuti:
“Ndimawona uminisitala monga ntchito yanga ndipo nthaŵi zonse ndimakumbukira kuti Paulo anati: ‘Ndinaoka, Apolo anathirira, koma Mulungu anapitizira kuzikulitsa.’ Mkazi wanga ndi ine ‘timaoka’ mwakukambitsirana mwachidule mbiri yabwino kunyumba ndi nyumba. ‘Timathirira’ mwakubwererako kwa amene anasonyeza chikondwerero kuwaphunzitsa kuchokera m’Baibulo, monga momwe Yesu anatiuzira kutero. Maphunziro Abaibulo apanyumba a mlungu ndi mlungu athandiza ambiri—m’zochitika zina mabanja athunthu—kupeza chidziŵitso cha chowonadi.”