Malo a ku Dziko Lolonjezedwa
Genesarete—‘Wodabwitsa ndi Wokongola’
“Kumbali kwa nyanja ya Genesarete kuli dziko lotambalala lokhala ndi dzina limodzimodzilo, lodabwitsa ndi lokongola m’kawonekedwe. Pokhala ndi nthaka yachonde palibe chomera chomwe sichimagudira kumeneko, ndipo nzika zake zimabzala chirichonse: mphepo njabwino kwakuti imayenerera mitundu yambirimbiri ya zomera. . . . Sikuti kumabala zipatso zosiyanasiyana zokha; kumakhala ndi zipatso mosalekeza. . . . Kumathiriridwa ndi kasupe wokhala ndi mphamvu zazikulu zobalitsa zipatso.”
Analemba motero wolemba mbiri Josephus, pofotokoza chigwa chambali zitatu m’mphepete kumpoto koma chakumadzulo kwa yomwe imadziŵika mofala monga Nyanja ya Galileya. Zithunzithunzi zapamwambazi zingakupatseni lingaliro la mmene chigwa chimenechi chinaliri chobala, chimodzi cha malo achonde kwambiri m’Galileya.a Dera limeneli linali lotchuka m’nthaŵi zakale kwakuti wolemba Uthenga Wabwino Luka anatcha nyanja yapafupi yamadzi opanda mchere kukhala “nyanja ya Genesarete.”—Luka 5:1.
Iye anagwiritsira ntchito mawu amenewo pamene anali kusimba kuti Yesu anadza kuderali napeza amuna anayi omwe anakhala atumwi ake. Kodi anali alimi omwe anali kudalira pa nthaka yachondeyo, akumalima mpesa, walnuts, azitona, kapena nkhuyu? Ayi. Mbewu zoterozo zinali zambiri m’Chigwa cha Genesarete, koma amuna ameneŵa anali asodzi, ndipo kuli kokhweka kumvetsetsa chifukwa chake.
Mwachidziŵikire mifuleni yodutsa m’chigwachi inakokololera kunyanjako zomera zomwe zinakhala chakudya cha nsomba. Chotero madziwo anadzaza ndi nsomba zamitundu yosiyanasiyana, kupangitsa indasitale yaikulu ndithu yansomba. Petro ndi Andreya anali asodzi amalonda kumeneko, monga momwenso analiri Yakobo ndi Yohane, ana a msodzi Zebedayo.—Mateyu 4:18-22; Luka 5:2-11.
Kaŵirikaŵiri kusodzako kunachitidwa mwakuponya makoka kuchokera m’ngalaŵa. Zimenezo nzimene Petro ndi Andreya anali kuchita pamene Yesu anawafikira. Ukonde wautali, kapena khoka, unaponyedwa mumpangidwe wozungulira pang’ono. Akafumphe amitengo ndiwo anauyandamitsa, pamene zinthu zolemera zomangiriridwa pansi zinapangitsa ukondewo kufutukukira pansi pa nyanja. Nsomba zambiri zinakhoza kugwidwa m’ukonde woterowo. Ndiyeno unakokedwera m’ngalaŵa kapena pamadzi osaya, kuti zikakhuthulidwire kumtunda. Nsomba zoyenera kudya zinasankhulidwa mwa zosadyedwa. Onani tsatanetsatane wolongosoka pa Luka 5:4-7 ndi Yohane 21:6-11. Kodi mukukumbukira kuti Yesu anatchula njira imeneyi yosodzera m’fanizo lake la khoka? (Mateyu 13:47, 48) Ndiponso, Mateyu 4:21 amagogomezera kuti kaŵirikaŵiri asodzi anayenera kuthera nthaŵi akusoka maukonde ong’ambika ndi matanthwe kapena nsomba.
Mukanati muyende m’mphepete mwa gombe la Genesarete, mwinamwake mukanawona malo angapo onenedwa kuti nkumene uminisitala wa Yesu unachitikira. Malo amodzi ali chitunda chobiriŵira pomwe, malinga ndi mwambo, Yesu anaperekerapo Ulaliki wa pa Phiri. Malo ameneŵa samasemphana ndi mbiri ya Uthenga Wabwino, popeza kuti Yesu anali pafupi ndi Chigwa cha Genesarete pamene anapereka ulalikiwo.—Mateyu 5:1–7:29; Luka 6:17–7:1.
Malo ena onenedwa kukhala owona samalingana ndi zenizeni za Baibulo. Mudzapeza tchalitchi chomwe chikulingaliridwa kuti chinamangidwa pamalo pamene Yesu anadyetsa anthu 4,000 ndi mikate isanu ndi iŵiri ndi tinsomba tochepa. (Mateyu 15:32-38; Marko 8:1-9) M’malo moika chochitikachi pa Chigwa cha Genesarete, cholembedwa cha Marko chikutchula “maiko a ku Dekapoli,” yomwe inali kutsidya lina la nyanjayo pamtunda wamakilomita khumi ndi limodzi.—Marko 7:31.
Mateyu ndi Marko amanena kuti pambuyo pochita chozizwitsachi, Yesu anayenda ndi ngalaŵa kunka ku Magadani, kapena Dalmanuta. (Mateyu 15:39; Marko 8:10) Akatswiri amagwirizanitsa chigawochi ndi Magdala (Migdal), chakum’mwera kwa Chigwa cha Genesarete, kulinga ku Tiberias. Malinga ndi kunena kwa The Macmillan Bible Atlas, Magdala anali “wotchuka chifukwa cha indasitale yake youmika nsomba.” Motsimikizirikadi usodzi wochuluka kumbali imeneyi ya nyanja ukapanga indasitale yoteroyo kukhala yothandiza ndiponso yaphindu.
Mosangalatsa, chilala cha mu 1985/86 chinachepetsa kuchuluka kwa madzi a Nyanja ya Galileya, kuwonetsera poyera gombe lotambalala. Pafupi ndi Chigwa cha Genesarete, amuna aŵiri anapeza zotsalira za ngalaŵa yamakedzana. Akatswiri a za m’mabwinja anakhoza kutenga ngalaŵa yamtengo yosodzera imeneyi yolingaliridwa kukhala ya pafupifupi ndi nthaŵi imene Yesu anayendera Nyanja ndi Chigwa cha Genesarete.
[Mawu a M’munsi]
a Onani chithunzi chachikulu mu Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1992.
[Mawu a Chithunzi patsamba 24]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Mawu a Chithunzi patsamba 24]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Mawu a Chithunzi patsamba 25]
Garo Nalbandian
[Mawu a Chithunzi patsamba 25]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.