Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 2/1 tsamba 29-30
  • “Kukoma Mtima Kwake Kwachikondi Kwakhala Kochuluka”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kukoma Mtima Kwake Kwachikondi Kwakhala Kochuluka”
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mu Gulu Lankhondolo ndi Pambuyo Pake
  • Moyo Wanga Usintha
  • Uminisitala Wanthaŵi Zonse
  • Kutumikira ndi Moyo Wonse Mosasamala Kanthu za Mayesero
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kodi Mungakatumikire Kumene Kukufunika Ofalitsa Ufumu Ambiri?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Ndinasankha Ntchito Yabwino Kwambiri
    Galamukani!—2007
  • Kusumika Maso ndi Mtima Pamphoto
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 2/1 tsamba 29-30

“Kukoma Mtima Kwake Kwachikondi Kwakhala Kochuluka”

MONGA MOMWE YASIMBIDWIRA NDI JOSÉ VERGARA OROZCO

Kodi muganiza kuti moyo wanu ungadzazidwe ndi nyonga yatsopano pausinkhu wa zaka 70? Wanga unatero. Ndipo zimenezo zinachitika zaka 35 zapitazo.

Chiyambire 1962, ndakhala ndikutumikira monga mpainiya wokhazikika, ndipo chiyambire 1972, ndakhala woyang’anira mochirikizidwa ndi kukoma mtima kwa Yehova m’Mpingo wa Mboni za Yehova wa El Carrizal m’boma la Jalisco, Mexico. Lekani ndikusimbireni pang’ono mbiri yanga.

NDINABADWIRA m’boma la Michoacán, ku Mexico, pa August 18, 1886. Atate ŵanga anali a Mason (chipembedzo cha madzoma achinsinsi), chotero banja lathu silinapitepo ku Tchalitchi cha Katolika, ndipo sitinakhale ndi phande m’mapwando alionse achipembedzo Achikatolika kapena kukhala ndi mafano alionse achipembedzo m’nyumba mwathu.

Pamene ndinali wazaka 16, atate anapita kukagwira ntchito ku United States, koma analinganiza kuti mwamuna wina andiphunzitse ntchito. Komabe, zaka ziŵiri pambuyo pake, mwamunayo ananditengera ku Mexico City kukaphunzira pasukulu ya zankhondo. Pambuyo pake ndinayamba ntchito m’gulu lankhondo la Mexico.

Mu Gulu Lankhondolo ndi Pambuyo Pake

Ndinamenya nkhondo m’Chipanduko cha Mexico chimene chinayamba mu 1910. Tonsefe achichepere pasukulupo tinachirikiza Francisco I. Madero, amene anali wopandukira ulamuliro wotsendereza wa Porfirio Díaz. Tinamchirikiza Madero mpaka imfa yake mu 1913, ndipo pambuyo pa zimenezo, tinachirikiza Venustiano Carranza, yemwe anatumikira monga presidenti wa Dzikolo kuyambira 1915 mpaka 1920. Tinkatchedwa a Carranzistas.

Pazochitika zinayi zosiyana, ndinayesa, mosaphula kanthu, kupempha kumasulidwa ku gulu lankhondolo. Pomalizira pake ndinathaŵa nkukhala wothaŵathaŵa. Monga chotulukapo, atate ŵanga, amene anali atabwerera ku Mexico, anaponyedwa m’ndende. Tsiku lina, ndikunamizira kukhala mphwawo, ndinawachezera m’ndendemo. Tinalankhulana mwakulemba patidutswa tamapepala kotero kuti alonda asakhoze kutimva. Ndinadya timapepalato kuti aliyense asadziŵe amene ndinali.

Atate atachoka m’ndende, anandichezera nandipempha kuti ndidzipereke kwa akulu a boma. Ndinatero, ndipo ndinadabwa kuti kazembe wamkulu sanandigwire. Mmalomwake, anapereka lingaliro lakuti ndisamukire ku United States. Ndinatsatira lingaliro lake ndipo ndinakhala kumeneko kuyambira 1916 mpaka 1926.

Mu 1923, ndinakwatira mkazi yemwe ndinzika ya Mexico amene anali kukhala mu United States. Ndinaphunzira ntchito yomanga, ndipo tinalera mwana wamkazi. Pamene anafika miyezi 17, tinabwerera ku Mexico ndi kukhala ku Jalpa, Tabasco. Kenako ‘chipanduko cha Cristero’ chinayamba, ndipo chinatenga nthaŵi kuyambira 1926 mpaka 1929.

Ochirikiza Cristero anafuna kuti ndigwirizane nawo. Komabe, ineyo ndi banja langa tinasankha kuthaŵira ku Dera la Aguascalientes. Pambuyo pokhala m’malo osiyanasiyana m’dziko la Mexico, tinadzakhala ku Matamoros, Tamaulipas mu 1956, kumene ndinayamba kuyang’anira ntchito zomanga.

Moyo Wanga Usintha

Apapa mpamene moyo wanga unayambira kusintha. Mwana wanga wamkazi, amene tsopano anali wokwatiwa ndipo anali kukhala kutsidya la malire a dzikoli ku Brownsville, Texas, U.S.A., akatichezera kaŵirikaŵiri. Tsiku lina iye anati: “Atate, mabanja ambiri akusonkhana m’holo yosonkhanira tsopanoli. Tiyeni tikawone zimene zikuchitika.” Unali msonkhano wa Mboni za Yehova. Mwana wanga wamkazi, mkamwini, mdzukulu, mkazi wanga, ndi ineyo tinapezekapo pamsonkhanowo masiku onse anayi.

Kuyambira chaka chimenecho, tinapezeka pamisonkhano Yachikristu ya Mboni za Yehova. Ndinapita patsogolo mwauzimu mu Mexico, pamene mwana wanga wamkazi anateronso ku United States. Mwamsanga ndinali kuuza anzanga a kuntchito zowona Zabaibulo zimene ndinali kuziphunzira. Ndinalandira magazini khumi a khope lirilonse la Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, amene ndinagaŵira kwa anzanga a kuntchitowo. Asanu ogwira ntchito m’ofesi ndi ainjiniya atatu pamodzi ndi antchito ena anakhala Mboni.

Ha, tsikulo December 19, 1959, linali lozizira chotani nanga, pamene ndinabatizidwa m’mtsinje! Aliyense amene anabatizidwa patsikulo anadwala chifukwa cha madzi ozizira kwambiri. Mwana wangayo wamkazi anayamba kubatizidwa ine ndisanatero, ndipo ngakhale kuti mkazi wanga sanabatizidwe, anafikira pakudziŵa chowonadi cha Babiulo, ndipo anali wogwirizanika kwambiri.

Uminisitala Wanthaŵi Zonse

Ndinadzimva wamangaŵa kwa Mulungu chifukwa cha kukoma mtima kwake konse, chotero mu February 1962, pamene ndinali ndi zaka 75, ndinayamba uminisitala wanthaŵi zonse monga mpainiya. Zaka zingapo pambuyo pake, mu 1968, mkazi wanga anamwalira. Panthaŵiyo ndinafuna kukatumikira m’dziko lina, koma chifukwa cha msinkhu wanga, abale anaganizira kuti zimenezo sizinali zoyenera. Komabe, mu 1970, ndinagaŵiridwa kukachita upainiya ku Colotlán m’boma la Jalisco, kumene kunali mpingo waung’ono.

Mu September 1972, woyang’anira dera anandipempha kusamukira kumzinda waung’ono wa El Carrizal, pafupi ndi Colotlán. Mu November chakacho, mpingo unakhazikitsidwa kumeneko, ndipo ndinaikidwa kukhala mkulu. Ngakhale kuti ndimzinda wakutali kwambiri, okwanira 31 amapezeka pamisonkhano yampingo.

Mosasamala kanthu za msinkhu wanga, ndikali wokangalika muuminisitala, kuyesa zolimba kuthandiza anthu kupenda zikhulupiriro zawo. Mwachitsanzo, popereka Mapemphero, Akatolika odzipereka amabwereza mawu akuti Tikuwoneni Mariya kumati: ‘Tikuwoneni, Mariya, wodzala chisomo; Ambuye ali ndi inu.’ Pempherolo limapitiriza kuti: ‘Mariya Woyera, Amayi ŵa Mulungu.’ Ineyo ndimawafunsa kuti: ‘Kodi zimenezo zingakhale bwanji tero? Ngati Mulungu ndiye amene amapulumutsa Mariya, ndimotani mmene Iye panthaŵi imodzimodziyo angakhalire mwana wake?’

Ndiri ndi zaka zakubadwa 105 tsopano ndipo ndakhala ndikutumikira monga mkulu ndi mpainiya wokhazikika mu El Carrizal, Jalisco, kwa pafupifupi zaka 20. Ndiganiza kuti chiri chifuniro cha Yehova kuti ndikhale ndi moyo kwa zaka zambiri motero, popeza kuti mwanjirayi ndikhoza kulipirira nthaŵi imene ndinataya pamene sindinali kumtumikira Iye.

Chinthu chimodzi chimene ndaphunzira nchakuti tiyenera nthaŵi zonse kukhala ndi chidaliro chakuti Woweruza wathu Wamkulu akutiyang’ana ali pampando wake wachifumu wolungama ndi kutipatsa zosoŵa zathu. Monga momwe Salmo 117:2, (NW) limanenera: “Kukoma mtima kwake kwachikondi kwakhala kochuluka kwa ife.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena