Kodi “Dongosolo Latsopano la Dziko” la Anthu Layandikira?
1. Kodi chikhumbo chofuna ufulu wa ndale zadziko wowonjezereka chasonyezedwa motani m’zaka zaposachedwapa?
LEROLINO, mamiliyoni a anthu ali muukapolo ku chipembedzo chonyenga, ndipo ambiri amasankha kungokhala choncho basi. Panthaŵi imodzimodziyo, anthu ochulukirachulukira akufuna ufulu wandale zadziko. Zochitika zapadera m’zaka zingapo zapitazo Kum’maŵa kwa Yuropu ndi kwina kulikonse zinasonyeza kuti anthu amafuna maboma opereka ufulu wochulukirapo. Monga chotulukapo, ambiri akunena kuti nyengo yatsopano ya ufulu yayandikira. Prezidenti wa United States anaitcha “dongosolo latsopano la dziko.” Ndithudi, olamulira adziko kulikonse anali kunena kuti Nkhondo Yoputana ndi Mawu ndi mpikisano wazida zinatha ndi kuti nyengo yatsopano ya mtendere inayandikira kwa mtundu wa anthu.—Yerekezerani ndi 1 Atesalonika 5:3.
2, 3. Kodi ndimikhalidwe yotani imene imatsutsana ndi ufulu wowona?
2 Komabe, ngakhale ngati zoyesayesa za anthu zinakhoza kuchepetsa zida ndi kukhala ndi maulamuliro opereka ufulu wokulirapo, kodi ufulu wowona ukadakhalapo? Ayi, chifukwa cha mavuto owopsa omwe alipo m’maboma onse, kuphatikizapo ademokrase, kumene chiŵerengero cha osauka chikuwonjezereka ndipo mamiliyoni akuvutika kuti apeze ndalama zokhalira moyo. Lipoti la Mitundu Yogwirizana linanena kuti mosasamala kanthu ndi kupita patsogolo kwa sayansi ndi mankhwala, tsiku ndi tsiku padziko lonse, avareji ya ana 40,000 amamwalira ndi manyutirishoni kapena matenda ena okhoza kuchinjirizidwa. Katswiri m’zimenezi anati: “Umphaŵi ukukula kotero kuti ukuwopseza mibadwo yamtsogolo.”
3 Kuwonjezerapo, anthu owonjezereka kuposa ndi kale lonse akukanthidwa ndi upandu womakulakulabe. Nkhalwe za utundu, za ndale, ndi zachipembedzo zikuchititsa magawano m’maiko ambiri. M’malo ena mikhalidwe simasiyana kwenikweni ndi nthaŵi yamtsogolo yofotokozedwa pa Zekariya 14:13, pamene anthu adzakhala “osokonezeka maganizo ndi kuchita mantha kotero kuti aliyense a[dza]ukira munthu woyandikana naye.” (Today’s English Version) Kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala oledzeretsa ndi nthenda zopatsirana mwakugonana zafalikira konsekonse. Mamiliyoni a anthu akutenga AIDS; mu United States mokha, nthendayi yapha kale anthu oposa 120,000.
Ukapolo ku Uchimo ndi Imfa
4, 5. Mosasamala kanthu ndi maufulu amene alipo lerolino, kodi ndiukapolo wotani umene aliyense ali m’nsinga zake?
4 Komabe, ngakhale ngati panalibe iriyonse ya mikhalidwe yoipa imeneyo, anthu sakadakhalabe ndi ufulu wowona. Onse akadakhalabe muukapolo. Nchifukwa ninji ziri choncho? Tichitire fanizo: Bwanji ngati wolamulira wotsendereza anaika muukapolo munthu aliyense padziko lapansi ndiyeno nkuwapha onse? Inde, ichi nchimene chinachitikira mtundu wa anthu pamene makolo athu oyambirira anapandukira Mulungu ndikukhala akapolo ku ulamuliro wotsendereza wa Mdyerekezi.—2 Akorinto 4:4.
5 Pamene Mulungu analenga anthu, chifuno chake chinali chakuti akhale padziko lapansi kosatha muungwiro, m’paradaiso, monga momwe Genesis mutu 1 ndi 2 amasonyezera. Koma chifukwa cha kupandukira Mulungu kwa kholo lathu Adamu, tonsefe tiri pansi pa chiweruzo cha imfa kuchokera pamene amayi athu anangotenga pathupi pathu: ‘Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi [Adamu, mutu wa banja la mtundu wa anthu], ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse.’ Monga momwe Baibulo limanenera, ‘imfa inachita ufumu.’ (Aroma 5:12, 14) Chotero mosasamala kanthu ndi mlingo wa ufulu umene tingakhale nawo paumwini, tonsefe ndife akapolo a uchimo ndi imfa.
6. Kodi nchifukwa ninji pakhala kuwongokera kochepa kokha m’kutalika kwa moyo wa munthu chiyambire kulembedwa kwa Salmo 90:10?
6 Ndiponso, moyo umene tiri nawowu ngwaufupi kwambiri. Ngakhale kwa amene ali ndi mwaŵi, umangokhala wa zaka makumi angapo. Kwa opanda mwaŵi, umangokhala wa zaka zochepa, ngakhale kusafikapo. Ndipo kupenda kwatsopano kunasonyeza kuti: “Sayansi ndi mankhwala zabwezeretsa pang’ono pokha moyo wa munthu pautali wake wachibadwa.” Ziri choncho chifukwa chakuti dongosolo lathu lamajini nlopanda ungwiro ndipo likhoza kuchititsa imfa chifukwa cha uchimo wa Adamu. Nzachisoni chotani nanga kuti pamene tikhala ndi moyo kwa zaka 70 kapena 80, pamene tiyenera kupeza nzeru zowonjezereka ndi kusangalala bwinopo ndi moyo, mpamene matupi athu amanyonyotsoka ndipo tithera m’fumbi!—Salmo 90:10.
7. Kodi nchifukwa ninji anthu sangathe konse kukhala magwero a maufulu owona amene timawafuna ndi kuwasoŵa?
7 Kodi ndiulamuliro wa anthu wotani umene ungachinjirize ukapolo umenewu wa uchimo ndi imfa? Palibe ndiumodzi womwe. Palibe nduna za boma, asayansi, kapena adokotala kulikonse amene angatimasule ku masoka a matenda, ukalamba, ndi imfa, ndiponso palibe amene angachotsepo kupanda chisungiko, chisalungamo, upandu, njala, ndi umphaŵi. (Salmo 89:48) Mosasamala kanthu ndi zolinga zabwino za anthu, nkosatheka kwa iwo kukhala magwero a maufulu owona amene timawafuna ndi kuwasoŵa.—Salmo 146:3.
Kugwiritsira Ntchito Molakwa Ufulu wa Kusankha
8, 9. Kodi nchiyani chimene chinagwetsera mtundu wa anthu mumkhalidwe wake wochititsa chisoni ulipowu?
8 Banja la anthu liri mumkhalidwe wochititsa chisoni umenewu chifukwa chakuti Adamu ndi Hava anagwiritsira ntchito molakwa ufulu wawo wa kusankha. Petro Woyamba 2:16 amati, malinga nkunena kwa The Jerusalem Bible: “Khalani ngati mfulu, ndipo musagwiritsire ntchito ufulu wanu monga chodzikhululukira chochitira zoipa.” Motero, nzomveka kuti Mulungu sanafune kuti ufulu wa munthu ukhale wopanda malire. Unayenera kuchitidwa mkati mwa malire a malamulo a Mulungu, omwe anali olungama ndipo opindulitsa aliyense. Ndipo malire amenewo anali otakata mokwanira kulola ufulu wa kusankha waukulu kwa munthu aliyense, kotero kuti ulamuliro wa Mulungu usakhale wotsendereza.—Deuteronomo 32:4.
9 Komabe, makolo athu oyambirira anafuna kudzisankhira okha chabwino ndi choipa. Popeza kuti iwo anatulukamo dala muulamuliro wa Mulungu, iye anawachotsera chichirikizo chake. (Genesis 3:17-19) Chotero iwo anakhala opanda ungwiro, ndi kuyamba kumadwala ndi kufa. Mmalo mwa ufulu, anthu analoŵa muukapolo ku uchimo ndi imfa. Anakhalanso mikole ya zikhoterero za olamulira aumunthu opanda ungwiro, omwe kaŵirikaŵiri, amakhala ankhalwe.—Deuteronomo 32:5.
10. Kodi ndimotani mmene Yehova wasamalira nkhani mwachikondi?
10 Mulungu walola anthu kwanyengo yokhala ndi polekezera kuti ayese ufulu umene iwo akuulingalira kukhala wotheratu. Iye anadziŵa kuti zotulukapo zake zikasonyeza popanda chikaikiro chirichonse kuti ulamuliro wa anthu wosadalira pa Mulungu sungapambane. Popeza kuti ufulu wa kusankha, ndiwo chuma chamtengo wapatali utagwiritsiridwa bwino ntchito, Mulungu mwachikondi chake analola zimene zikuchitika kupitiriza kwakanthaŵi kuposa kuti alande mphatso ya ufulu wa kusankha imeneyo.
‘Munthu Sangalongosole Mapazi Ake’
11. Kodi ndimotani mmene mbiri yachirikizira kulongosoka kwa Baibulo?
11 Zochitika za m’mbiri zasonyeza kulondola kwa Yeremiya mutu 10, 23 ndi 24, pamene pamati: ‘Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake. Yehova, mundilangize.’ Mbiri yasonyezanso kulongosoka kwa Mlaliki 8:9, amene amalengeza kuti: ‘Wina apweteka mnzake pomlamulira.’ Nzowona chotani nanga! Banja la anthu lachoka m’tsoka limodzi kuloŵa m’lina, chimaliziro cha onsewo kukhala manda. Mtumwi Paulo anafotokoza mkhalidwewo molondola kwambiri pa Aroma 8:22 kuti: ‘Pakuti tidziŵa kuti cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zoŵaŵa pamodzi kufikira tsopano.’ Inde, kudziimira kunja kwa malamulo a Mulungu kwakhala kochititsa tsoka.
12. Kodi magwero ena akudziko amanenanji ponena za ufulu wotheratu?
12 Ponena za ufulu, bukhu lakuti Inquisition and Liberty linati: “Kudziimira pawekha mwa iko kokha, sikuli kwenikweni chinthu chofunika: sikuli chinthu chochinyadira kukapanda mbali zina zokuyeneretsa. Kwenikweni, ukhoza kukhala mtundu wa dyera loipitsitsa . . . Munthu sayenera kukalimira kukhala cholengedwa chodziimira pachokha kotheratu, ndipo sangatero popanda kudzivulaza.” Ndipo Kalonga Philip wa ku Mangalande nthaŵi ina ananena kuti: “Ufulu wakutsatira chikhoterero chirichonse ndi chibadwa ungakhale wosangalatsa, koma zokumana nazo zasonyeza mobwerezabwereza, kuti ufulu wopanda kudziletsa . . . ndipo kudzisungira kopanda kulingalira ena ndiko njira yotsimikizirika yoluluzira moyo wa chitaganya cha anthu, mosasamala kanthu ndi kulemera kwake.”
Kodi Ndani Amene Amadziŵa Bwino Koposa?
13, 14. Kodi ndani yekha amene angapatse banja la anthu ufulu wowona?
13 Kodi ndani amene amadziŵa bwino koposa zakulinganiza nyumba—makolo okhala ndi chidziŵitso chabwino ndi okhoza, kapena ana achichepere? Yankho nlodziŵikiratu. Mofananamo, Mlengi wa anthu, Atate wathu wakumwamba, amadziŵa zotiyenera bwino koposa. Iye amadziŵa bwino lomwe mmene chitaganya chiyenera kulinganizidwira ndi kulamuliridwa. Iye amadziŵa mmene ufulu wa kusankha uyenera kulamuliridwira kuti udzetsere aliyense mapindu a ufulu wowona. Yehova Mulungu wamphamvuyonse, ndiye yekhayo amadziŵa mmene angatulutsire banja la anthu muukapolo ndi kupereka ufulu wowona kwa onse.—Yesaya 48:17-19.
14 M’Mawu ake, pa Aroma 8:21, Yehova akupereka lonjezo losonkhezera maganizo ili: ‘Cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.’ Inde, Mulungu akulonjeza kumasula kotheratu banja la anthu ku mikhalidwe yoipa imene lirimo. Nkhani yotsatira idzafotokoza mmene zimenezo zidzachitikira.
Kodi Mungayankhe Motani?
(Kupenda masamba 3 mpaka 8)
◻ Kodi nchifukwa ninji anthu ali ndi malingaliro amphamvu ponena za ufulu?
◻ Kodi anthu akhala akapolo mwanjira zotani m’mbiri yonse?
◻ Kodi nchifukwa ninji Yehova walola kugwiritsira ntchito molakwa ufulu wa kusankha kwa nthaŵi yaitali motero?
◻ Kodi ndani yekha angabweretse ufulu wowona pa mtundu wonse wa anthu, ndipo chifukwa ninji?
[Chithunzi patsamba 7]
Utali wa moyo wa munthu uli kwenikweni monga zimene zinalembedwa zaka 3,500 zapitazo pa Salmo 90:10
[Mawu a Chithunzi]
Mwachilolezo cha The British Museum