Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 4/15 tsamba 30
  • Kodi Mumakumbukira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumakumbukira?
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Nkhani Yofanana
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Anali Kuikiradi Chikhristu Kumbuyo Kapena Ankaphunzitsa Nzeru za Anthu?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Yenderani Dzikolo, Yenderaninso Nkhosa!
    Nsanja ya Olonda—1992
  • “Kondani Choonadi ndi Mtendere”!
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 4/15 tsamba 30

Kodi Mumakumbukira?

Kodi mwapeza makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda kukhala othandiza kwa inu? Pamenepo bwanji osayesa chikumbukiro chanu ndi zotsatirazi:

▫ Kodi nchiyani chomwe chinali chifuno chachikulu cha kuchiritsa kwa Yesu?

Kunasonyeza, kaamba ka chilimbikitso cha khamu lalikulu la anthu onga nkhosa lerolino, kuti opulumuka Armagedo adzachiritsidwa mwamsanga pambuyo pa Armagedo. (Yesaya 33:24; 35:5, 6)​—12/15, tsamba 12.

▫ Kodi nchifukwa ninji timafunikira kukumbutsidwa nthaŵi zonse kuti: ‘Limbikani chilimbikire m’kupemphera’? (Aroma 12:12)

Zitsenderezo za moyo ndi mathayo zikhoza kutididikiza ndi kutiiŵalitsa kupemphera. Kapena mavuto akhoza kutikulira ndi kutipangitsa kuleka kukondwera m’chiyembekezo cha Ufumu ndi kulekanso kupemphera. Chifukwa cha zimenezi, tifunikira zokumbutsa zotilimbikitsa kupemphera ndipo motero kuyandikira kwenikweni kwa Yehova.​—12/15, tsamba 14.

▫ Kodi nchiyani chimene chimatsimikizira kuti Chigumula cha m’nthaŵi ya Nowa chinasiya umboni wosafafanizika pa fuko la anthu?

Kwayerekezeredwa kuti nthano za Chigumula zoposa 500 zimasimbidwa ndi mafuko ndi anthu oposa 250. Kufanana kwina kwakukulu kumapezeka m’nthano zonsezi.​—1/15, tsamba 5.

▫ Kodi ndimotani mmene aneneri onyenga alerolino aliri ofanana ndi a m’nthaŵi ya Yeremiya?

Aneneri onyenga alerolino amadzitcha kuti amaimira Mulungu, koma akuba mawu a Mulungu mwakulalikira zinthu zimene zikucheutsa anthu ku zimene Baibulo likunenadi. Izi nzowona makamaka pa chiphunzitso cha Ufumu. (Yeremiya 23:30)​—2/1, tsamba 4.

▫ Kodi pamene munthu abatizidwa m’dzina la mzimu woyera zimatanthauzanji?

Zimatanthauza kuti munthu amene akubatizidwayo watsimikiza mtima kugwirizana ndi mzimu, kusachita kalikonse kotsekereza kugwira ntchito kwake pa anthu a Yehova. Motero, munthuyo ayenera kugwirizana ndi kagulu ka kapolo wokhulupirika ndi wanzeru ndi kakonzedwe kakukhala ndi akulu mumpingo. (Ahebri 13:7, 17; 1 Petro 5:1-4)​—2/1, tsamba 18.

▫ Kodi nchifukwa ninji kulambira mafano kuli kosakaza kwa wolambirayo?

Baibulo limasonyeza kuti mafano amamnyansa Yehova Mulungu ndipo samathandiza owapembedzawo kuyandikira kwa Mulungu. (Deuteronomo 7:25; Salmo 115:4-8) Satana Mdyerekezi ‘wachititsa khungu maganizo’ a anthu kotero kuti chowonadi ‘chisawaŵalire.’ (2 Akorinto 4:4) Choncho polemekeza fano, munthuyo amatumikiradi zofuna za ziŵanda. (1 Akorinto 10:19, 20)​—2/15, masamba 6-7.

▫ Kodi nchifukwa ninji nkhosa zinalingaliridwa kukhala chuma chaphindu m’nthaŵi za Baibulo?

Ubweya unali chuma chomabwererapo ndipo unagwiritsiridwa ntchito kupangira zovala zabanja kapena kugulitsidwa. Nyanga za nkhosa zamphongo zinagwiritsiridwa ntchito kulengezera Chaka Choliza Lipenga kapena kuchenjezera tsoka kapena kutsogoza pomenya nkhondo. Popeza kuti nkhosa zinali zina za nyama zosadetsedwa zomwe Aisrayeli anakhoza kudya, gulu lankhosa linapereka chakudya, ndipo zinapereka mkaka wambiri wakumwa kapena kupangira tchizi.​—3/1, masamba 24-5.

▫ Kodi okonda Mulungu amapemphanji pamene apempherera kuti Ufumu wa Mulungu udze? (Mateyu 6:10)

Amapempha kuti Ufumu wa kumwamba wa Mulungu uchitepo kanthu mwakuwononga madongosolo aboma opangidwa ndi anthu, amene alephera kukwaniritsa lonjezo lawo lakubweretsa mtendere ndi chisungiko. (Danieli 2:44)​—3/15, tsamba 6.

▫ Kodi ndani omwe anali Ochilikiza, ndipo kodi anaphunzitsa Utatu?

Ochilikiza anali amuna a tchalitchi amene anakhalapo ku mbali yomalizira ya zaka za zana lachiŵiri. Iwo analemba kuchinjiriza Chikristu chomwe anadziŵa motsutsana ndi nthanthi za adani zomwe zinali zofala m’Roma. Palibe aliyense wa iwo amene anaphunzitsa Utatu.​—4/1, masamba 24-9.

▫ Kodi Zakariya, atate wa Yohane Mbatizi, anagonthetsedwa ndi kulepheretsedwa kulankhula, monga momwe Luka 1:62 akuwonekera kusonyeza?

Gabrieli anati kulankhula kwa Zakariya kukayambukiridwa, koma osati kumva kwake. (Luka 1:18-20) Luka 1:64 amati: ‘Pomwepo panatseguka pakamwa pake [pa Zakariya], ndi lilime lake linamasuka, ndipo iye analankhula.’ Onani kuti panopo sipakutchulidwa zakuti kumva kwake kunayambukiridwa mwanjira iliyonse. Kutchulidwa kwa “kukodola” pa Luka 1:62 kungatanthauze kuti jesichala linalake linagwiritsiridwa ntchito kufunsira chosankha cha Zakariya.​—4/1, tsamba 31.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena