Mmene Chikhulupiriro Chingathandizire Odwala
ZOLEMBEDWA za machiritso ozizwitsa za Baibulo zimatitsimikizira kuti Mulungu amadera nkhaŵa za umoyo wathu, ndipo zimasonyeza mphamvu yake yakuchiritsa. Popeza kuti machiritso ozizwitsa analemekeza Mulungu ndipo anadzetsa chimwemwe chachikulu, nkwanzeru kufunsa kuti, Kodi mphatso ya kuchiritsa mwa mzimu woyera ikugwirabe ntchito?
Yankho la funsolo nlakuti ayi—ndipo chifukwa chake chingadabwitse ena. Machiritso ozizwitsa amenewo a m’zaka za zana loyamba anakwaniritsa chifuno chawo. The Illustrated Bible Dictionary imafotokoza molondola kuti: “Chifuno cha zozizwitsa zakuchiritsa chinali chachipembedzo, osati mankhwala.” Kodi nzifukwa zina zachipembedzo zotani zomwe zozizwitsa zimenezo zinatumikira?
Choyamba, zozizwitsa zochiritsa za Yesu zinatumikira chifuno cha kumzindikiritsa monga Mesiya. Ndipo pambuyo pa imfa yake, zinathandiza kutsimikizira kuti dalitso la Mulungu linali pampingo Wachikristu watsopano. (Mateyu 11:2-6; Ahebri 2:3, 4) Ndiponso, zinasonyeza kuti lonjezo la Mulungu lakuchiritsa mtundu wa anthu m’dziko latsopano lidzakwaniritsidwa. Zimachilikiza chikhulupiriro chathu chakuti idzabweradi nthaŵi imene ‘wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala; anthu okhala m’menemo, adzakhululukidwa mphulupulu zawo.’ (Yesaya 33:24) Pamene zifuno za m’zaka za zana loyamba zimenezi zinakwaniritsidwa, zozizwitsa sizinafunikirenso.
Nkwachidziŵikire kuti ophunzira a Yesu a m’zaka za zana loyamba anadwala matenda omwe sanachiritsidwe mozizwitsa. Umenewu uli umboni wowonjezereka wakuti kuchiritsa kozizwitsa kwa Yesu ndi atumwi kunalinganizidwira kuphunzitsa chowonadi chofunika, osati kuchiritsa basi. Povomereza mankhwala a matenda osalekeza a Timoteo, Paulo anachilikiza kugwiritsira ntchito vinyo monga mankhwala, osati kuchiritsa kwa chikhulupiriro. Paulo, yemwe anachita zozizwitsa zakuchiritsa, sanapeze mpumulo ku “munga m’thupi” womwe unapitiriza ‘kumtundudza.’—2 Akorinto 12:7; 1 Timoteo 5:23.
Pamene atumwi onse anatha kumwalira, mphatso yakuchiritsa inatha. Paulo mwiniyo anasonyeza kuti zimenezo zikachitika. Akumayerekezera mpingo Wachikristu ndi khanda, Paulo anati: ‘Pamene ndinali mwana, ndinalankhula ngati mwana, ndinalingirira ngati mwana, ndinaŵerenga ngati mwana; tsopano ndakhala munthu, ndayesa chabe zachibwana.’ Mfundo ya fanizo lake inali yakuti mphatso zozizwitsa za mzimu zinali mbali ya ubwana wa mpingo Wachikristu. Izo zinali ‘zachibwana.’ Chifukwa chake, iye anati: ‘[Mphatso zozizwitsazo] zidzaleka.’—1 Akorinto 13:8-11.
Kodi Chikhulupiriro Chingatithandize Titadwala?
Komabe, ngakhale ngati sitidalira pa kuchiritsa kwa chikhulupiriro, nkoyeneradi kupemphera kwa Mulungu kaamba ka chithandizo titadwala. Ndipo ndithudi palibe cholakwika ngati ena atipempherera. Koma mapemphero ayenera kukhala atanthauzo ndipo ogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. (1 Yohane 5:14, 15) Palibe paliponse pamene Baibulo limatilamula kupempherera kuchiritsa kwa chikhulupiriro.a Mmalomwake, timapempherera chichilikizo chachikondi cha Yehova mkati mwa ziyeso zochititsidwa ndi matenda.
Baibulo limasonyeza zimene okhulupirika angapempherere podwala pamene likunena kuti: ‘Yehova adzamgwiriziza pa kama wodwalira; podwala iye mukonza pogona pake.’ (Salmo 41:3) Kusinkhasinkha pa Mawu a Mulungu kudzathandiza odwala maganizo. Wamasalmo analemba kuti: ‘Chifundo chanu [Yehova, NW] chinandichirikiza. Pondichulukira zolingalira zanga mkati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.’—Salmo 94:18, 19; onaninso 63:6-8.
Kuwonjezerapo, tifunikira kusonyeza nzeru pankhani ya thanzi, ndipo Baibulo limapereka uphungu pankhaniyi. Nkwabwino koposa kukhala mogwirizana ndi malamulo abwino a Baibulo koposa kumwerekera ndi mankhwala oledzeretsa, kusuta, kuledzera, kapena kudya mopambanitsa ndiyeno, titadwala, nkutembenukira mothedwa nzeru ku kuchiritsa kwa chikhulupiriro. Kupempherera chozizwitsa pamene wina agwidwa ndi matenda sindiko njira ina yanzeru yopeŵera matenda okhoza kupeŵeka, monga ngati kudya chakudya chopatsa thanzi ngati chiripo kapena kufuna thandizo lamankhwala ngati kuli kotheka.
Mawu a Mulungu amatilimbikitsanso kukulitsa mikhalidwe yamaganizo yabwino imene ingathandize thanzi lathu lakuthupi. Bukhu la Miyambo limapereka uphungu uwu: ‘Mtima wabwino ndi moyo wa thupi; koma nsanje ivunditsa mafupa.’ ‘Mtima wosekerera uchiritsa bwino; koma mzimu wosweka uphwetsa mafupa.’ (Miyambo 14:30; 17:22) Kupempherera mzimu woyera kuti utichititse bata ndi chimwemwe kungakhale ndi zotulukapo zopindulitsa pa thanzi lathu lakuthupi.—Afilipi 4:6, 7.
Bwanji Nanga za Kuchiritsa kwa Chikhulupiriro?
Ndithudi, ngakhale ngati munthu akhala ndi thanzi labwino monga momwe mkhalidwe ungalolere, matenda amakhalapobe. Kodi tingachitenji? Kodi pali chivulazo chirichonse ngati tipita kwa wochiritsa mwa chikhulupiriro kuti tikachiritsidwe? Inde, pali chivulazo. Ochiritsa mwa chikhulupiriro amakono samachiritsa popanda malipiro. Ndipo kulipira wochiritsa mwa chikhulupiriro kungatitaitse ndalama zambiri zimene tingagwiritsire ntchito kupeza chithandizo cha mankhwala. Ndiponso, kodi nkupatsiranji ndalama munthu amene amadyerera chikhulupiriro cha anthu?
Ena angatsutse kuti: ‘Ndithudi, kuchiritsa kwa chikhulupiriro kuyenera kukhala kwaphindu ngati ena amene amapita kwa “ochiritsa” amachiritsidwa.’ Koma nkokaikiritsa ngati ochiritsa mwa chikhulupiriro amachiritsadi munthu m’njira yokhalitsa. Encyclopædia Britannica ikuvomereza kuti: “Kupenda kochepa kochitidwa mogwirizana ndi njira zokhazikika zofufuzira kwafikiridwa pa mfundo zambiri zosadziŵika za kuchiritsa kwa chikhulupiriro.”
Ngakhale ngati chiŵerengero chaching’ono chimawoneka kuchiritsidwa, umenewu sindiwo umboni wa kugwira ntchito kwa mzimu woyera. Mu Ulaliki wa pa Phiri, Yesu anati: ‘Ambiri adzati kwa ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mawu m’dzina lanu, ndi m’dzina lanunso kutulutsa mizimu yoipa, ndi kuchita m’dzina lanunso zamphamvu zambiri? Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziŵani inu nthaŵi zonse; chokani kwa ine, inu akuchita kusayeruzika.’ (Mateyu 7:22, 23) Yesu ananenanso kuti anthu ena, ngakhale kuti sakavomerezedwa ndi Mulungu, akakopa ambiri ndi zizindikiro: ‘Chifukwa Akristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe.’ (Mateyu 24:24) Ndithudi, ochiritsa mwa chikhulupiriro amakono angaphatikizidwe m’mawu amenewo, pokhala ndi maulaliki awo ochititsa chidwi, kupempha ndalama kosalekeza, ndi kudzinenera kuti amachititsa machiritso ozizwitsa.
Oterowo sakutsatira mapazi a Yesu. Pamenepo, kodi akutsatira yani? Mtumwi Paulo anatipatsa chizindikiro pamene ananena kuti: ‘Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika. Chifukwa chake sikuli kanthu kwakukulu ngatinso atumiki ake adzionetsa monga atumiki a chilungamo; amene chimaliziro chawo chidzakhala monga ntchito zawo.’ (2 Akorinto 11:14, 15) Ngati ochiritsa mwachikhulupiriro samachita machiritso amene amanena, ndiye kuti ali onyenga, otsatira mayendedwe a Satana “wonyenga wa dziko lonse.” (Chivumbulutso 12:9) Koma bwanji ngati m’zochitika zochepa, iwo amachiritsadi? Kodi sitinganene kuti “zamphamvu” zawo zimachititsidwa mwa mphamvu ya Satana ndi ziŵanda zake? Inde, ndimo mmene ziyenera kukhalira!
Nthaŵi ya Kuchiritsa Kwenikweni
Machiritso ozizwitsa a Yesu anachitidwa mwachithandizo cha mzimu woyera wa Mulungu. Iwo anasonyeza chifuniro chake chakuthetsa mavuto aumoyo a anthu panthaŵi yake yoyenera. Yehova akulonjeza ‘kuchiritsa . . . amitundu.’ (Chivumbulutso 22:2) Ndipo sadzangochiritsa matenda okha komanso adzachotsa imfa. Yohane anafotokoza kuti Yesu anadza “kuti yense wakukhulupirira iye asataike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Ha, kumeneko kudzakhala kuchiritsa kwabwino chotani nanga! Yesu adzachitanso machiritso ofanana ndi amene analembedwa m’Baibulo koma adzawachita pamlingo waukulu. Iye adzaukitsa ngakhale akufa! (Yohane 5:28, 29) Kodi zimenezi zidzachitika liti?
M’dziko latsopano la Mulungu, limene, malinga ndi umboni wonse, liri pafupi kwenikweni. Dziko latsopano limenelo, lomwe lidzabweretsedwa pambuyo pa kuchotsedwa kotheratu kwa dongosolo lonse loipa, lidzakhaladi dalitso kwa anthu owongoka mtima. Lidzakhala dziko lopanda mavuto. ‘[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.’ (Chivumbulutso 21:4) Ha, zidzakhala zosiyana chotani nanga ndi zimene tikuwona tsopano!
Chifukwa chake, pakakhala matenda, pempherani kwa Mulungu kaamba ka chichirikizo. Ndipo kaya mukudwala kapena muli ndi thanzi labwino, phunzirani mmene moyo wamuyaya wopanda matenda udzakhalira wothekadi. Mangirirani chikhulupiriro chanu pa lonjezo lodalirika limeneli la Mulungu mwakuphunzira zilozero zambiri za Baibulo. Phunzirani mmene chifuno cha Mulungu pankhaniyi chayandikirira kukwaniritsidwa molingana ndi ndandanda yake ya nthaŵi. Musakaikire, Mawu a Mulungu akutitsimikizira kuti: ‘Iye wameza imfa ku nthaŵi yonse; ndipo [Mfumu Ambuye Yehova, NW] adzapukuta misozi pa nkhope zonse.’—Yesaya 25:8.
[Mawu a M’munsi]
a Ena amaganiza kuti mawu a pa Yakobo 5:14, 15 amalankhula za kuchiritsa kwa chikhulupiriro. Koma mawu ozungulira lembalo amasonyeza kuti panopa Yakobo akulankhula za kudwala kwauzimu. (Yakobo 5:15b, 16, 19, 20) Iye akupereka uphungu kwa anthu amene afooka m’chikhulupiriro kuti afikire akulu kaamba ka chithandizo.
[Chithunzi patsamba 7]
Machiritso ozizwitsa a Yesu anakwaniritsa chifuno chawo
[Chithunzi patsamba 8]
Yesu adzabwereza ndi kuchulukitsa zozizwitsa zochiritsa