Kodi Iripo Njira Imene Anthu Angatulukire Mumkhalidwe Wawo Wauchimo?
NDI ana ake anayi, mkazi wina wotchedwa Chisako ankagwira ntchito yoyeretsa zimbudzi mumzinda wokhala pamtuda wa makilomita 600 kuchokera kumene ankakhala. Pogwira ntchito yake, anali kumaimba nyimbo yachipembedzo imene sanadziŵe tanthauzo lake. Ndimmene ankachitira anthu opembedza pofuna kudziŵa chifuno chenicheni cha zipembedzo zonse.
“Mosasamala kanthu za machitidwe anga akudziphumphuntha mtima,” Chisako akukumbukira kuti, “sindinathe kusintha umunthu wanga. Pansi pamtima wanga, sindinakhululukire ena ndipo sindinasonyeze chikondi chopanda mpeni kuphasa.”
Ngakhale m’maiko a Kum’maŵa, kumene anthu ambiri samalidziŵa tchimo monga momwe Baibulo limaphunzitsira, ambiri amavutikabe ndi chikumbumtima chifukwa cha zikhoterero zawo zauchimo, monga momwe anachitira Chisako. (Aroma 2:14, 15) Kodi ndani amene sanakhalepo ndi malingaliro opsinjika chifukwa chosakomera mtima munthu wina wokhala mumkhalidwe womvetsa chisoni, kapena amene sanavutikepo maganizo kwambiri chifukwa chokamba mawu osayenera? (Yakobo 4:17) Ndipo kodi mkhalidwe woipa wa kusirira sumakhala mwa ana ndi akulu omwe?
Kodi nchifukwa ninji anthu amakhala ndi malingaliro ovutitsa oterowo? Chifukwa chakuti, kaya akhale akudziŵa kapena ayi, ali ndi lingaliro lachibadwa lakuzindikira choipa, lakuzindikira uchimo. Ndithudi, mosasamala kanthu kuti anthu akudziŵa zimene Baibulo limaphunzitsa ponena za uchimo kapena ayi, onse amayambukiridwa ndi zikhoterero zauchimo. Katswiri pankhani imeneyi ananena kuti: “Onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu.”—Aroma 3:23.
Kodi Uchimo Ungafafanizidwe?
Anthu ambiri lerolino, kwenikweni m’Chikristu Chadziko, amayesayesa kufafaniza malingaliro a uchimo ndi liŵongo m’chikumbumtima chawo. “Liwu lenilenilo lakuti ‘uchimo’ . . . silimatchulidwanso kwenikweni,” anatero Dr. Karl Menninger m’bukhu lake la Whatever Became of Sin? Komabe, kupeŵa liwu lakuti “uchimo” sikumathandiza kanthu monga momwe kusafuna kwa nkhalamba kutchula liwu lakuti “kukalamba” sikumasinthira kukalamba kwake. Tiyenera kuvomereza chenicheni chakuti tiri ndi zikhoterero zauchimo ndipo tifunikira kumasulidwa ku mkhalidwe wovutitsa umenewo. Koma kumasulidwa ndi yani?
Mtumwi Wachikristu Paulo anafunsa funso limenelo atavomereza zikhoterero zake zakuchita uchimo ngakhale kuti sanafune kutero: “Munthu wosauka ine; adzandilanditsa ndani m’thupi la imfa iyi?” Kenako Paulo mwiniyo anayakha kuti: “Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Kristu Ambuye wathu.” Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti Mulungu anapanga makonzedwe akukhululukira machimo kupyolera mwa nsembe ya Yesu yadipo.—Aroma 7:14-25.
Komabe, ambiri mwa 3,500,000,000 osakhala Akristu a dziko (kuŵirikiza kaŵiri chiŵerengero cha otchedwa Akristu) amapeza lingaliro la dipo kukhala lovuta kwambiri kumva. Mwachitsanzo, chiphunzitso cha dipo chinakhala chopinga chachikulu kwa Msilamu wokhala m’Japani yemwe anaphunzira Baibulo kwakanthaŵi. Kwa anthu a Kum’maŵa ambiri, lingaliro lakuti munthu mmodzi akhoza kufera anthu onse nlachilendo kwambiri.
Zimenezi sizodabwitsa kwenikweni, popeza kuti ngakhale ena mu Chikristu Chadziko kumawakhalira kovuta kukhulupirira chiphunzitso chachikulu chimenechi. “Chiphunzitso cha Kuwomboledwa,” inavomereza tero New Catholic Encyclopedia, “sichimakhulupiririka m’mbali zina ndipo chikupitirizabe kukhala vuto m’maphunziro azaumulungu.”
Ukulu wa chisokonezo pachiphunzitso chimenechi umasonyezedwa bwino lomwe m’mawu a wolemba nkhani zachipembedzo N. H. Barbour akuti: “Kuwona imfa ya Kristu kukhala yofafaniza chilango cha machimo a anthu kumafanana ndi kholo la padziko lapansi limene lingawone imfa yoŵaŵa ya ntchentche, yochititsidwa ndi kubaidwa ndi singano, kukhala njira yolungama yofafanizira chilango cha kulakwa kwa mwana wake.” Panthaŵi imeneyo, Charles T. Russell anali wogwirizana naye wa Barbour, ndipo iye anawona kufunika kwamwamsanga kwa kutchinjiriza chiphunzitso cha dipo. Chotero analekana ndi Barbour ndipo mu 1879 anayamba kufalitsa magazini atsopano, omwe anafikira kukhala magazini amene mukuŵerengaŵa. Kuyambira pachiyambi pake, Nsanja ya Olonda yachirikiza chiphunzitso cha nsembe ya Kristu yadipo.
Koma kodi chiphunzitso chimenechi chingalandirike kwa anthu osakhala ndi chiyambi cha “Chikristu”? Kuti tidziŵe, tiyeni tichipende mosamalitsa chiphunzitsochi cha munthu mmodzi kufera anthu onse.