Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 7/1 tsamba 3-4
  • Kodi Nchifukwa Ninji Pali Kutaya Mtima Konseko?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nchifukwa Ninji Pali Kutaya Mtima Konseko?
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Njira Yonkitsa Yotulukira m’Vutolo
  • Chiyembekezo Chimagonjetsa Kutaya Mtima!
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Njira Yogonjetsera Kutaya Mtima
    Galamukani!—2000
  • Posachedwapa—Dziko Lopanda Nkhaŵa
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Kodi ndingodzipha?
    Galamukani!—2008
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 7/1 tsamba 3-4

Kodi Nchifukwa Ninji Pali Kutaya Mtima Konseko?

CHIYEMBEKEZO cha moyo wabwinopo​—potsirizira pake chakwaniritsidwa! Anthu ambiri okhala m’dziko limene panthaŵiyo linatchedwa Jeremani Wakum’maŵa anakhulupirira zimenezo pamene Khoma la Berlin linagwetsedwa mu November 1989. Komabe, pambuyo pake patangopitirira pang’ono chaka chimodzi, anadandaula za “kupeza moyo wa demokrase yachikapitolizimu kukhala wovutirapo poyerekezera ndi moyo wotetezeredwa ndi Khoma la Berlin.” Kodi chotulukapo nchotani? Kukhwethemulidwa ndi kutaya mtima komakulakula.

Chiwawa pabanja ndi m’chitaganya chingakakamize anthu kusiya nyumba zawo kukafunafuna chisungiko, koma oŵerengeka okha ndiwo amachipeza. Ena amafikiradi kukhala pakati pa opanda malo okhala omwe amamanga timisasa pamakwalala a m’mizinda. M’maiko ena ambiri oterowo amavutika chifukwa cha kucholoŵana kwa malamulo. Amalephera kupeza malo okhala chifukwa cha ulova, sangathe kupezanso ntchito chifukwa chakuti alibe keyala ya kumalo kumene amakhala. Magulu aboma othandiza osoŵa amayesayesa kuthandiza, koma kumatenga nthaŵi kuti athetse mavutowo. Motero pamakhala kugwiritsidwa mwala ndi kutaya mtima.

Kutaya mtima kumapangitsa akazi ambiri kuchita zinthu zochititsadi kakasi. M’lipoti lakuti Women and Crime in the 1990s, mphunzitsi wa malamulo Dr. Susan Edwards anafotokoza kuti: “Kuphatikizidwa kwa asungwana [mu uhule] kuli chotulukapo chachindunji cha kusoŵa m’zachuma, osati kulephera kudzisungira kapena chiyambi cha m’banja.” Mofananamo, anyamata amene amachoka panyumba kukafuna ntchito kaŵirikaŵiri samaipeza. Ena, mwakutaya mtima, amakhala ‘anyamata a selo’ kwa amuna amathanyula kuti apeze chakudya ndi malo okhala, ndipo ena amakhala ogwiritsiridwa ntchito ndi magulu a apandu.

Mikhalidwe yovuta yochititsidwa ndi ndale zadziko, chiwawa, mavuto achuma, zonsezo zingachititse kutaya mtima. Ngakhale anthu antchito zapamwamba amaphatikizidwa m’vutoli, pamene akuyesayesa kusunga moyo wawo wokhupuka kwinaku akulimbana ndi mavuto achuma omakulakulabe. Nchotulukapo chotani? ‘Chitsenderezo chiyalutsa wanzeru,’ malinga nkunena kwa Mfumu yakale Solomo!a (Mlaliki 7:7) Ndithudi, kutaya mtima kumapangitsa ochuluka kutenga njira yonkitsa kuti atuluke m’vutolo​—kudzipha.

Njira Yonkitsa Yotulukira m’Vutolo

Zochitika zambiri zakudzipha pakati pa achichepere zimasonyeza kuti ngakhale iwo amayambukiridwa ndi mliri wa kutaya mtima. Mkonzi wa nyuzi ya ku Briteni anafunsa kuti: “Kodi nchiyani m’nthaŵi yathu chimene chikuchititsa kutaya mtima kwakukulu pakati pa achichepere?” M’kupenda ana amisinkhu yapakati pa 8 ndi 16 omwe anagonekedwa m’zipatala pambuyo pakuyesa kudzipha mwakumwa paizoni, Dr. Eric Taylor wa London’s Institute of Psychiatry anapereka lipoti lakuti: “Chinthu chodabwitsa kwambiri chinali kuchuluka mwa ana amene anali kutaya mtima ndi opanda chiyembekezo m’zinthu.” Briteni inali ndi chiŵerengero cha pafupifupi anthu 100,000 chaka chirichonse omwera dala paizoni koma amene sanafe, ndi cholinga chakudziŵitsa anthu kufunikira kwawo chithandizo chamwamsanga.

Gulu lina lothandiza osoŵa ku Briteni linachita mkupiti wakupempha anthu kutchera khutu ndi kuchitira chifundo otaya mtimawo. Mwakutero, aphungu ake ananena kuti analikupereka “njira zina mmalo mwakudzipha.” Chikhalirechobe, iwo amavomereza kuti sangathe kuthetsa mavuto amene amachititsa anthu kutaya mtima.

Mlingo wa kuwonjezereka kwakudzipha umasonyeza “ukulu wa kusagwirizana ndi kusoŵeka kwa umodzi mwa anthu m’chitaganya,” inatero nyuzipepala ya The Sunday Correspondent. Kodi nchifukwa ninji kudzipha kwachuluka kwambiri lerolino? Nyuzipepalayo inatchula “kusoŵa malo okhala, uchidakwa womakulakula, chiwopsezo cha Aids ndi kutsekedwa kwa zipatala za amisala” kukhala zochititsa anthu kutaya mtima kwambiri kotero kuti amawona kudzipha kukhala njira yokha yotulukira m’mavuto awo.

Kodi pali chiyembekezo chirichonse chakulaka kutaya mtima? Inde! Yesu akupereka chilimbikitso chakuti: “Ŵeramukani, tukulani mitu yanu”! (Luka 21:28) Kodi anatanthauzanji? Kodi pali chiyembekezo chotani?

[Mawu a M’munsi]

a Malinga nkunena kwa Theological Wordbook of the Old Testament, lokonzedwa ndi Harris, Archer, ndi Waltke, liwu la chinenero choyambirira lotembenuzidwa “kutsendereza” limapereka lingaliro la “kuthodwetsa, kupondereza, ndi kukanikiza okhala ndi malo otsika.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena