Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 7/15 tsamba 8-13
  • Kristu Anada Kusayeruzika—Kodi Mumatero?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kristu Anada Kusayeruzika—Kodi Mumatero?
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mitundu Itatu ya Udani
  • Chifukwa Chake Tiyenera Kuda Kusayeruzika
  • Awo Amene Amada Kusayeruzika
  • Kusonyeza Udani wa Kusayeruzika
  • Kuda Chidetso cha Kugonana
  • Kuda Chipembedzo Chonyenga ndi Mpatuko
  • Kodi Mumadana Ndi Kusamvera Malamulo?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Anthu Sakumvera Malamulo Padziko Lonse—Kodi Baibulo Limanena Zotani?
    Nkhani Zina
  • Kuzindikira “Munthu Wosayeruzika”
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Njira Yokhayo Yothetsera Chidani
    Nsanja ya Olonda—2000
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 7/15 tsamba 8-13

Kristu Anada Kusayeruzika​—Kodi Mumatero?

“Inu munakonda chilungamo, ndipo munadana nako kusayeruzika. Ndicho chifukwa chake Mulungu, Mulungu wanu, anakudzozani inu ndi mafuta a chipambano kwambiri koposa anzanu.”​—AHEBRI 1:9, NW.

1. Kuwonjezera pakukonda chilungamo, kodi nchiyaninso chimene chimafunika kwa atumiki owona onse a Yehova Mulungu?

ATUMIKI owona a Yehova amamkonda ndi mtima wawo wonse, moyo, maganizo, ndi nyonga. (Marko 12:30) Amafuna kuchititsa mtima wa Yehova kukondwa mwa kusunga umphumphu. (Miyambo 27:11) Kuti achite zimenezo, sikokha kuti iwo ayenera kukonda chilungamo komanso ayenera kuda kusayeruzika. Chitsanzo chawo, Yesu Kristu, anaterodi. Kunanenedwa za iye kuti: “Inu munakonda chilungamo, ndipo munadana nako kusayeruzika.”​—Ahebri 1:9, NW.

2. Kodi nchiyani chimene chimaphatikizidwa ndi kusayeruzika?

2 Kodi kusayeruzika nchiyani? Ndiko tchimo, monga momwe mtumwi Yohane anasonyezera pamene analemba kuti: “Yense wakuchita tchimo achitanso kusayeruzika; ndipo tchimo ndilo kusayeruzika.” (1 Yohane 3:4) Munthu wosayeruzika “samamangika kapena kulamulidwa ndi lamulo.” (Webster’s Ninth New Collegiate Dictionary) Kusayeruzika kumaphatikizapo zonse zimene ziri zachabe, zoipa, zachisembwere, zoluluzika, ndi zosawona mtima. Kupenda dzikoli kumatisonyeza kuti kusayeruzika nkofala lerolino koposa ndi kale lonse. Palibe kukayikira kwakuti tikukhala mu “nthaŵi zoŵaŵitsa” zimene mtumwi Paulo ananeneratu pa 2 Timoteo 3:1-5. Polingalira kusayeruzika konseku, nkwabwino chotani nanga kuti tikulamulidwa kuda kuipa konse! Mwachitsanzo, timauzidwa kuti: “Inu okonda Yehova, danani nacho choipa.” (Salmo 97:10) Mofananamo, timaŵerenga kuti: “Danani nacho choipa, nimukonde chokoma.”​—Amosi 5:15.

Mitundu Itatu ya Udani

3-5. Kodi ndim’njira zitatu ziti m’zimene liwulo ‘kuda’ limagwiritsiridwa ntchito m’Mawu a Mulungu?

3 Kodi kuda kumatanthauzanji? M’Mawu a Mulungu, ‘kuda’ kukugwiritsiridwa ntchito m’njira zitatu zosiyana. Pali udani wosonkhezeredwa ndi chiwembu ndi umene umafunafuna kuvulaza mkhole wake. Akristu ayenera kupeŵa mtundu umenewu wa udani. Ndiwo udani umene unasonkhezera Kaini kupha mbale wake wolungamayo Abele. (1 Yohane 3:12) Ndiponso umenewu ndiwo udani umene atsogoleri achipembedzo anali nawo pa Yesu Kristu.​—Mateyu 26:3, 4.

4 Ndiponso, liwulo ‘kuda’ limagwiritsiridwa ntchito m’Malemba m’lingaliro la kukonda pang’ono. Mwachitsanzo, Yesu anati: “Munthu akadza kwa ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iye mwini, sakhoza kukhala wophunzira wanga.” (Luka 14:26) Mwachiwonekere, Yesu anatanthauza kokha kuti tikonde ameneŵa pang’ono koposa ndi mmene timamkondera. Yakobo ‘anada Leya,’ komatu iye kwenikweni anamkonda pang’ono koposa mmene anakondera Rakele.​—Genesis 29:30, 31.

5 Ndiyeno pali tanthauzo lina la liwulo ‘kuda’ limene makamaka tikulifuna pano. Liri ndi lingaliro la kukhala ndi lingaliro lamphamvu la kusakonda kapena kunyansidwa mwamphamvu ndi munthu wina kapena kanthu kena kotero kuti timapeŵa kukhala ndi chochita nako. Mu Salmo 139 kumeneku kukunenedwa monga “udani weniweni.” Mmenemo Davide anati: “Kodi sindidana nawo iwo akudana ndi inu, Yehova? Ndipo kodi sindimva nawo chisoni iwo akuukira inu? Ndidana nawo ndi udani weniweni: ndiwayesa adani.”​—Salmo 139:21, 22.

Chifukwa Chake Tiyenera Kuda Kusayeruzika

6, 7. (a) Kodi nchifukwa ninji, kwakukulukulu tiyenera kuda kusayeruzika? (b) Kodi nchiti chimene chiri chifukwa chachiŵiri champhamvu chodera kusayeruzika?

6 Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuda kusayeruzika? Chifukwa chimodzi nchakuti kuti tikhale ndi kudzilemekeza ndi chikumbumtima chabwino. Kuli kokha mwanjira imeneyi kuti tingakhale ndi unansi wabwino ndi Atate wathu, wachikondi ndi wolungamayo Yehova. Davide anapereka chitsanzo chabwino kwambiri ponena za zimenezi, monga momwe kungawonedwere mwa kuŵerenga Salmo 26. Mwachitsanzo, iye anati: “Ndidana nawo msonkhano wa ochimwa, ndipo sindidzakhala nawo pansi ochita zoipa.” (Salmo 26:5) Chikondi chathu pa Mulungu ndi chilungamo ziyenera kutisonkhezera kukhala ndi kunyansidwa kolungama​—inde, udani​—kaamba ka zonse zimene ziri kusayeruzika m’lingaliro lake, kuphatikizapo machitachita a kusayeruzika a awo amene samvera ndi kuda Yehova. Ndiponso, tiyenera kuda kusayeruzika chifukwa cha chitonzo chimene kumabweretsa padzina la Mulungu.

7 Chifukwa china chimene anthu a Yehova ayenera kudera kusayeruzika ndicho chakuti iko nkwaupandu ndi kovulaza. Kodi kufesa m’thupi, kumene kumatanthauza kufesa kusayeruzika, kudzatulutsanji? Paulo anachenjeza kuti: “Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta. Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m’thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa mzimu, chochokera mumzimu adzatuta moyo wosatha.” (Agalatiya 6:7, 8) Chotero tiyenera kufuna kukhala osagwirizana kotheratu ndi kusayeruzika. Ndithudi, tifunikira kuda kusayeruzika konse kaamba ka ubwino wathu ndi mtendere wa maganizo.

Awo Amene Amada Kusayeruzika

8. Kodi ndani amene wapereka chitsanzo chachikulu m’kuda kusayeruzika, monga momwe kwasonyezedwera ndi malemba ati?

8 M’kuda kusayeruzika, Mulungu amapereka chitsanzo chachikulu kwa zolengedwa zonse zanzeru. Iye amakwiya molungama ndi kusayeruzika, ndipo Mawu ake amati: “Ziripo zinthu zisanu ndi chimodzi Mulungu azida; ngakhale zisanu ndi ziŵiri zimnyansa: maso akunyada, lilime lonama, ndi manja akupha anthu osachimwa; mtima woganizira ziwembu zoipa, mapazi akuthamangira mphulupulu mmangummangu; mboni yonama yonong’ona mabodza, ndi wopikisanitsa abale.” Timaŵerenganso kuti: “Kuwopa Yehova ndiko kuda zoipa; kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m’kamwa mokhota, ndizida.” (Miyambo 6:16-19; 8:13) Ndiponso, timauzidwa kuti: “Pakuti ine Yehova ndikonda chiweruziro, ndida chifwamba ndi choipa.”​—Yesaya 61:8.

9, 10. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti anada kusayeruzika?

9 Yesu Kristu anatsanzira Atate wake m’kuda kusayeruzika. Motero, timaŵerenga kuti: “Inu munakonda chilungamo, ndipo munadana nako kusayeruzika. Ndicho chifukwa chake Mulungu, Mulungu wanu, anakudzozani inu ndi mafuta a chipambano kwambiri koposa anzanu.” (Ahebri 1:9, NW) Yesu anatipatsa chitsanzo cha udani wa mtundu umenewu. Iye anasonyeza kuda kwake kusayeruzika mwa kuvumbula anthu okuchita modzifunira​—atsogoleri achipembedzo chonyenga. Mobwerezabwereza, anawatsutsa kukhala onyenga. (Mateyu, chaputala 23) Panthaŵi ina Yesu anawauza kuti: “Inu muli ochokera kwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita.” (Yohane 8:44) Yesu anasonyeza chidani chake pakusayeruzika ngakhale kufikira kumlingo wa kugwiritsira ntchito nyonga yakuthupi, pazochitika ziŵiri akumathamangitsa onyenga achipembedzo adyerawo m’kachisi.​—Mateyu 21:12, 13; Yohane 2:13-17.

10 Yesu anasonyezanso kuda kwake kusayeruzika ndi tchimo mwa kusaphatikizidwa nazo kotheratu. Chifukwa cha chimenecho, iye akanatha bwino lomwe kufunsa omtsutsawo kuti: “Ndani mwa inu anditsutsa ine za tchimo?” (Yohane 8:46) Yesu anali “wokhulupirika, wopanda chinyengo, wosadetsedwa, wopatulidwa kwa ochimwa.” (Ahebri 7:26, NW) Potsimikizira zimenezi, Petro analemba kuti Yesu “sanachita tchimo, ndipo mkamwa mwake sichinapezedwa chinyengo.”​—1 Petro 2:22.

11. Kodi ndizitsanzo Zamalemba zotani zimene tiri nazo za anthu opanda ungwiro amene anada kusayeruzika?

11 Komabe, Yesu, anali munthu wangwiro. Kodi ife tiri ndi zitsanzo Zamalemba za anthu opanda ungwiro amene anadadi kusayeruzika? Ndithudi tiri nazo! Mwachitsanzo, Mose ndi Alevi anzake anasonyeza udani waukulu pakulambiridwa kwa mafano mwa kupha pafupifupi olambira mafano 3,000 Yehova atalamula. (Eksodo 32:27, 28) Pinehasi anasonyeza udani waukulu pakusayeruzika pamene anapha anthu aŵiri adamawo ndi nthungo.​—Numeri 25:7, 8.

Kusonyeza Udani wa Kusayeruzika

12. (a) Kodi tingasonyeze motani udani wathu pakusayeruzika? (b) Kodi ndinjira zina zogwira ntchito ziti zopeŵera malingaliro a kusayeruzika?

12 Pofika kunthaŵi yathu ino, kodi tingasonyeze motani udani wathu pakusayeruzika? Mwakulamulira malingaliro athu, mawu, ndi machitidwe. Tifunikira kukulitsa chizoloŵezi cha kuganiza zinthu zomangirira pamene maganizo athu sali otanganitsidwa ndi ntchito imene tiri nayo. Ngati zichitika kuti tiri ogalamuka usiku, pangakhale chikhoterero cha kuganiza zinthu zosagwira ntchito, monga ngati kusumika maganizo mosalekeza pamadandaulo, kapena kudziphatikiza m’zoyerekezera zachisembwere. Musapereke konse malo kuzinthu zotero, koma khalani ndi chizoloŵezi cha kuganiza kopindulitsa. Mwachitsanzo, yesani kuloŵeza pamtima malemba, a ma odala asanu ndi anayi, ndi zipatso zisanu ndi zinayi za mzimu. (Mateyu 5:3-12; Agalatiya 5:22, 23) Kodi mungathe kutchula maina a atumwi 12? Kodi mumadziŵa Malamulo Khumi? Kodi nchiyani chimene chiri mipingo isanu ndi iŵiri yonenedwa m’Chivumbulutso? Kuloŵeza pamtima nyimbo Zaufumu kumathandizanso kuchititsa kuganizira zinthu zowona, zofunika kwambiri, zolungama, zoyera, zokondeka, za mbiri yabwino, zopatulika, ndi zotamandika.​—Afilipi 4:8.

13. Kodi kuda kusayeruzika kudzatichititsa kuda nkhani za mtundu wotani?

13 Ndiponso, timasonyeza kuti timada kusayeruzika mwa kupeŵa nkhani zonse zonyansa. Anthu ambiri adziko amasangalala kunena ndi kumvetsera njerengo zonyansa, koma Akristu sayenera ngakhale kukhoterera kukuzimvetsera. Mmalomwake, tiyenera kuchoka ndi kupeŵa kutenga nawo mbali m’makambitsirano ena alionse amene amaluluza kufikira kumlingo woterowo. Ngati tiri osakhoza kuchokapo, tingasonyeze zimenezi ngakhale ndi mawonekedwe a nkhope yathu kuti timada nkhani zotero. Tifunikira kulabadira uphungu wabwino kwambiri uwu: “Nkhani yonse yovunda isatuluke mkamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.” (Aefeso 4:29) Sitiyenera kudzidetsa mwa kulankhula zinthu zimene ziri zonyansa kapena mwa kuzimvetsera.

14. Kodi nditchinjirizo lotani limene kuda kusayeruzika kudzapereka ponena za zizoloŵezi za zamalonda ndi pantchito?

14 Kuda kwathu kusayeruzika kuyenera kulunjikitsidwanso pazizoloŵezi zonse zauchimo. Kuda kusayeruzika kudzatithandiza kupeŵa msampha wa kulolera molakwa ponena za nkhaniyi. Akristu enieni sali ndi chizoloŵezi cha kuchita tchimo. (Yerekezerani ndi 1 Yohane 5:18.) Mwachitsanzo, tiyenera kuda zizoloŵezi zonse zosawona mtima za zamalonda. Lerolino, Mboni za Yehova zambiri zapanikizidwa kuchitira zinthu zosawona mtima owalemba ntchito koma iwo akana kutero. Akristu akhaladi ofunitsitsa kutayikiridwa ndi ntchito zawo koposa kuchita kanthu kena kamene kamaswa chikumbumtima chawo chophunzitsidwa Baibulo. Ndiponso, timafunanso kusonyeza kuda kwathu kusayeruzika mwa kusaswa malamulo apamsewu ndi mwa kusachita chinyengo pamene tiyenera kulipira misonkho kapena misonkho ya akatundu ogulidwa kunja.​—Machitidwe 23:1; Ahebri 13:18.

Kuda Chidetso cha Kugonana

15. Kodi kulenga anthu ndi chibadwa champhamvu m’zakugonana kunatumikira zifuno zabwino ziti?

15 Monga Akristu, ife tiyenera makamaka kuda chidetso chonse chimene chimaphatikizapo nkhani za kugonana. Mwa kulenga anthu ndi chibadwa champhamvu cha kufuna kugonana, Mulungu anali ndi zifuno ziŵiri zabwino kwambiri. Iye anatsimikizira kuti mtundu wa anthu sukasoloka, ndiponso analinganiza makonzedwe achikondi abwino oposa opezera chimwemwe. Ngakhale anthu omwe ali osauka, osaphunzira, kapena osoŵa mwanjira ina angathe kupeza chimwemwe chachikulu m’maunansi aukwati. Komabe, Yehova waika malire mkati mwa unansi umenewu umene ungasangalalidwe. Malire onenedwa ndi Mulungu ameneŵa ayenera kulemekezedwa.​—Genesis 2:24; Ahebri 13:4.

16. Kodi kaimidwe kathu kamaganizo kayenera kukhala kotani kulinga ku zosangulutsa zodetsedwa m’zakugonana ndi zizoloŵezi zake?

16 Ngati tida kusayeruzika, tidzapeŵa mwamphamvu zizoloŵezi zodetsedwa zakugonana zonse ndi zosangulutsa zachisembwere. Chifukwa chake tidzapeŵa mabukhu onse akhalidwe lokayikitsa, magazini, ndi manyuzipepala. Mofananamo, ngati tida kusayeruzika, sitidzawonerera zithunzithunzi zirizonse zautchisi, kaya pawailesi yakanema, pazithunzithunzi zoyenda, kapena m’nyumba zamaseŵero. Ngati tiwona programu ina kukhala yachisembwere, tiyenera kusonkhezereka kuzimitsa wailesi yakanema nthaŵi yomweyo kapena kukhala ndi kulimba mtima kwakuchoka m’nyumba yamaseŵeroyo. Mofananamo, kuda kusayeruzika kudzatipangitsa kusamala nyimbo zonse zimene ziri zodzutsa chilakolako m’mawu ake kapena kamvekedwe kake. Sitidzafunafuna chidziŵitso cha nkhani zachisembwere koma tidzakhala ‘makanda ponena za choipa, komabe aakulu msinkhu m’mphamvu za kuzindikira.’​—1 Akorinto 14:20.

17. Kodi ndiuphungu wotani umene Akolose 3:5 amapereka umene ungatithandize kuti tikhale oyera mwamakhalidwe?

17 Moyenera kwambiri, timalangizidwa kuti: “Fetsani ziŵalozo ziri padziko; dama, chidetso, chifunitso cha manyazi, chilakolako choipa.” (Akolose 3:5) Palibe chikayikiro chakuti tifunikira kuchitapo kanthu mwamphamvu ngati titi tikhalebe oyera mwamakhalidwe. Ponena za mneni Wachigrikiyo wotembenuzidwa “fetsani” pa Akolose 3:5, The Expositor’s Bible Commentary imati: “Liwulo limapereka lingaliro lakuti sitingofunikira kokha kutsendereza kapena kulamulira machitidwe oipa ndi kaimidwe ka maganizo. Tiyenera kuwachotseratu, kudula kotheratu njira yakale ya moyo. ‘Kupheratu’ kungafotokoze mphamvu yake. . . . Ponse paŵiri tanthauzo la mneni ndi mphamvu ya mkhalidwe wa nthaŵi zimapereka lingaliro la mchitidwe wamphamvu waumwini, wopweteka wotsimikizirika.” Chifukwa chake tiyenera kupeŵa mabukhu owonetsa zonyansa monga ngati kuti anali nthenda yowopsa, yopatsirana, ndi yakupha, pakuti ndimo mmene ziriri m’makhalidwe abwino ndi auzimu. Kristu anasonyeza lingaliro lofananalo pamene ananena za kudula dzanja, phazi, kapena ngakhale diso ngati likutikhumudwitsa.​—Marko 9:43-48.

Kuda Chipembedzo Chonyenga ndi Mpatuko

18. Kodi tingasonyeze motani kuda kwathu kusayeruzika kwachipembedzo?

18 Ndiyenso, monga momwe Yesu anasonyezera udani wake pakusayeruzika mwa kuvumbula achipembedzo onyengawo, chotero lerolino Mboni za Yehova zikusonyeza kuda kwawo kusayeruzika konse konyenga kwachipembedzo. Motani? Mwakufalitsa mabukhu Abaibulo amene amavumbula Babulo Wamkulu ponena za zimene iye alidi, hule lachipembedzo. Ngati timadadi chinyengo cha kusayeruzika cha chipembedzo, tidzakhala olunjika m’kuvumbula Babulo Wamkulu, ulamuliro wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga. Tidzatero kaamba ka anthu owona mtima amene iye wachititsa khungu ndi kuwaika m’ndende yauzimu. Kumlingo umene timada nawo kusayeruzika kwa Babulo Wamkulu, ndiwo mlingo mwa umene tidzakhala achangu m’kukhala ndi phande m’mbali zonse za uminisitala Waufumu.​—Mateyu 15:1-3, 7-9; Tito 2:13, 14; Chivumbulutso 18:1-5.

19. Kodi ampatuko tiyenera kuwalingalira motani, ndipo chifukwa ninji?

19 Thayo la kuda kusayeruzika limagwiranso ntchito kumachitachita onse ochitidwa ndi ampatuko. Kaimidwe kathu ka maganizo kulinga kwa ampatuko kayenera kukhala kofanana ndi ka Davide, amene analengeza kuti: “Kodi sindidana nawo iwo akudana ndi inu, Yehova? Ndipo kodi sindimva nawo chisoni iwo akuukira inu? Ndidana nawo ndi udani weniweni: ndiwayesa adani.” (Salmo 139:21, 22) Ampatuko amakono agwirizana ndi “munthu wosayeruzika,” atsogoleri a Chikristu Chadziko. (2 Atesalonika 2:3) Chifukwa chake, ife monga Mboni zokhulupirika za Yehova, tiribiretu nawo chochita. Pokhala opanda ungwiro, mitima yathu ikatha mosavuta kukhala ndi chikhoterero cha kusuliza abale athu. Monga alionse paokha, awo a “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndianthu opanda ungwiro. (Mateyu 24:45-47) Komatu kagulu kameneka kali kokhulupirika ndi kanzeru. Ampatuko amagogomezera pazolakwa kapena zowonekera kukhala zophophonya zopangidwa ndi abale amene amatsogolera. Kutetezereka kwathu kuli m’kupeŵa manenanena okopa a ampatuko monga ngati kuti anali poizoni, amene iwo alidi.​—Aroma 16:17, 18.

20, 21. Kodi zifukwa za kudera kusayeruzika zingasimbidwe motani mwachidule?

20 Tawona kuti dziko nlodzazidwa ndi kusayeruzika, kumene kuli kogwirizana ndi tchimo. Sikuli kokwanira kwa ife kukonda chilungamo; tiyeneranso kuda kusayeruzika. Ena a awo amene achotsedwa mumpingo Wachikristu angakhale atalingalira kuti anakonda chilungamo, koma iwo sanade mokwanira kusayeruzika. Tawonanso chifukwa chake tiyenera kuda kusayeruzika. Sitingakhale ndi chikumbumtima chabwino ndi olemekezeka pokhapokhapo ngati titero. Ndiponso, kusayeruzika kumatanthauza kusakhulupirika kwa Yehova Mulungu. Ndipo kusayeruzika kumatichititsa kututa zipatso zoipa kwambiri​—chisoni, chivundi, ndi imfa.

21 Tawonanso mmene timasonyezera kuti timada kusayeruzika. Timatero mwakusakhala ndi chochita chirichonse ndi mtundu uliwonse wa kusawona mtima, chisembwere, kapena mpatuko. Popeza kuti tikufuna kukhala ndi phande m’kulemekezedwa kwa Yehova ndi chikhumbo cha kupangitsa mtima wake kukondwera, tiyenera kukonda osati kokha chilungamo ndi kukhala otanganitsidwa muutumiki wake komanso kuda kusayeruzika, monga momwe anachitira Mtsogoleri wathu ndi Kazembe Wankhondo, Yesu Kristu.

Kodi Mukayankha Motani?

◻ Kodi Malemba amagwiritsira ntchito motani liwulo ‘kuda’?

◻ Kodi nziti zimene ziri zifukwa zina zabwino za kudera kwathu kusayeruzika?

◻ Kodi ndizitsanzo zabwino kwambiri zotani zomwe tiri nazo za awo amene anada kusayeruzika?

◻ Kodi tingasonyeze motani udani wathu pakusayeruzika?

[Chithunzi patsamba 8]

Yesu anayeretsa kachisi chifukwa chakuti anada kusayeruzika

[Chithunzi patsamba 10]

Ngati tida kusayeruzika, tidzapeŵa zosangulutsa zachisembwere

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena