Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 8/15 tsamba 3-4
  • Kulankhula m’Malilime—Chochitika Chozizwitsa Chomakulakula

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulankhula m’Malilime—Chochitika Chozizwitsa Chomakulakula
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nkukhumbiranji Mphatso ya Malilime Lerolino?
  • Kodi Munthuyo Amachitanji?
  • M’Malirime, Kulankhula
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Kodi Baibulo Limaphunzitsa Zotani pa Nkhani ya Malilime?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Mphatso ya Malilime Ndimbali ya Chikristu Chowona?
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Masiku Ano Mulungu Ndi Amene Amachititsa Anthu Kulankhula Malilime?
    Nsanja ya Olonda—2010
Nsanja ya Olonda—1992
w92 8/15 tsamba 3-4

Kulankhula m’Malilime​—Chochitika Chozizwitsa Chomakulakula

“MPHAMVU inalamulira lilime langa ndipo mawu anangosefukira ngati madzi. Chinali chisangalalo chotani nanga! Panali lingaliro la chiyero chachikulu koposa. Sindinakhale wofanana chiyambire panthaŵiyo,” anadzuma motero munthu wina amene anali ndi chochitika chachilendo cha kulankhula mu ‘chinenero chosadziwika.’

Panopa munthu akukufotokozerani chokumana nacho chake choyamba cha kulankhula mu ‘chinenero chosadziwika.’ ‘Koma kodi chimenecho nchiyani?’ moyenerera ena angafunse motero. Zimasonya kumchitidwe kapena chikhulupiriro m’matchalitchi ena mmene amuna ndi akazi amanena kukhala osonkhezeredwa ndi mzimu wa Mulungu kulankhula m’zinenero zakwina kapena zachilendo zimene iwo samadziwa.

Nchochitika chozizwitsa chachipembedzo chomakulakula. Kalelo kunali kulingaliridwa kukhala chochitika cha achipembedzo cha Apentekostala okha, kulankhula m’malilime tsopano kukuphatikizapo zipembedzo zakalekale ndi kuphatikizapo Abaptisti, Aepiskopal, Alutheran, Amethodist, Apresbyterian, ndi Aroma Katolika. Mkhalidwe wa munthu pamene ali mumkhalidwewu wafotokozedwa kukhala kukwatulidwa m’maganizo, kunyanyuka, kulota, ndi kubwebweta. Ena amakutchadi kukhala chochitika cha kuchita misala. Pali mkhalidwe wachinsinsi ndi wachilendo wogwirizanitsidwa ndi kulankhula m’malilime, kapena m’chinenero china.

Kodi Nkukhumbiranji Mphatso ya Malilime Lerolino?

M’bukhu lake lakuti Tongues of the Spirit, Cyril G. Williams akupereka lingaliro lakuti pangakhale “mgwirizano pakati pa lingaliro la kulephera, ndi kukhumba kulankhula mu ‘malilime.’” Iye akukufotokoza kukhala mchitidwe wa kumasuka umene uli ndi “phindu la kuchiritsa monga lochepetsa chipsinjo” ndi “lothetsa kuwombana kwamkati.” Kugwiritsidwa mwala m’ntchito yatchalitchi, kupsinjika maganizo, kulephera ntchito yodzisankhira, kuferedwa, mavuto apanyumba, kapena kudwala m’banja ziri zochititsa zotchulidwa zimene zimawonjezera kulankhula kotengeka maganizo koteroko.

Mofananamo, mu The Psychology of Speaking in Tongues, John P. Kildahl akunena kuti “nkhawa ndizo chofunika choyamba kuti mukhale ndi luso la kulankhula m’malilime.” Kupyolera mwa kufufuza kwaumwini ndi kufunsa kosamalitsa, kunapezeka kuti “oposa 85% mwa olankhula m’malilimewo anali ndi vuto la kuda nkhawa kotsimikizirika asanayambe kulankhula m’malilime.” Mwachitsanzo, nakubala wina anafuna kulankhula m’malilime kotero kuti apempherere mwana wake wamwamuna amene anali kudwala kensa. Mwamuna wina anayamba kulankhula m’malilime panthaŵi ya kukhala kwake wokaikakaika ponena za kukwezedwa pantchito kolonjezedwa. Mkazi wina anayamba kulankhula m’malilime mkati mwa mlungu umodzi mwamuna wake atagwirizana ndi Gulu Lothandiza Kulaka Uchidakwa.

Kodi Munthuyo Amachitanji?

Munthu wina amene analankhula m’malilime kwanthaŵi yoyamba anasimba kuti: “Ndinamva kutentha mkati mwanga, ndi kuzizira ndi kutuluka thukuta, kunjenjemera ndi kufoka kwakutikwakuti m’ziwalo zanga.” Kogwirizanitsidwa ndi chokumana nacho cha kulankhula m’malilime, ndiko kudzisungira kumene kawirikawiri kuli kwachilendo kumene ena apeza kukhala kododometsa. Mwachitsanzo, “msungwana wina anatsala nenene kutsamwitsidwa ndi malovu a iyemwini pamene anatambalala pampando, khosi lake linali litatsamira mpandowo, zitende zake zinali pansi, miyendo yake inangoti kangalala.” Mkati mwa kusonkhana kwampingo kwina “mwamuna wina anali kungochita kapidigoli kuchokera kumapeto ena a tchalitchi kumka ku ena.”

“Kwa anthu ena,” akulemba motero Profesala William J. Samarin, “kulankhula m’malilime nkofunika kuti ubatizidwe Mumzimu Woyera.” Popanda uwo, iwo “amachititsidwa kulingalira kukhala operewera pang’ono.” Kukuwonedwanso kukhala “yankho la pemphero, chitsimikiziro cha chikondi chaumulungu ndi kuvomerezedwa.” Ena anena kuti kumawasiya ali ndi lingaliro la kugwirizana kwamkati, chisangalalo, ndi mtendere, limodzi ndi “lingaliro lokulirapo la mphamvu” ndi “lingaliro lamphamvupo la kudziwika.”

Kodi kulankhula mawu konyanyukako kulidi umboni wa kugwira ntchito kwa mzimu woyera? Kodi chochitikacho chimadziwikitsa munthuyo kukhala Mkristu wowona? Kodi kulankhula m’malilime ndiko mbali ya kulambira kovomerezedwa lerolino? Mafunso amenewa afunikira yankho loposa kuti inde kapena ayi. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti tikufuna kuti kulambira kwathu kukhale ndi chivomerezo ndi dalitso za Mulungu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena