Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 8/15 tsamba 26-29
  • Kodi Mwaŵerengera Mtengo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mwaŵerengera Mtengo?
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoposa Kulingalira Kwachidziŵikire
  • Kulingalira Kwabwino
  • Nzeru Yeniyeni Ndiyo Chitetezo
  • Pindulani Polimbikira Kuchita Zinthu Zauzimu
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kodi Chikhulupiriro Chanu mwa Mulungu N’cholimba Motani?
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Muzisankha Zochita Mwanzeru
    Nsanja ya Olonda—2013
  • “Yehova Apatsa Nzeru”
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 8/15 tsamba 26-29

Kodi Mwaŵerengera Mtengo?

“CHIYANI! Kodi ukukana mwaŵi waukulu koposa umenewo?” Kapitawoyo sanakhulupirire zimene anali atangomva kumene. Wogwira ntchito pansi pake, mkazi wolemekezeka kaamba ka luso lake ndi makhalidwe abwino, anali atakana kumene mwaŵi wolipiriridwa ndi kampani wokaphunzira kudziko lakunja kwazaka ziŵiri. Kodi nchifukwa ninji anatero?

Kuvomera mwaŵiwo, anafotokoza motero mkaziyo, kukatanthauza kulekanitsidwa ndi mwamuna wake ndi ana ake aŵiri kwa zaka ziŵiri. Iye akawalakalaka kwambiri. Chachikulu koposa, iye akanyalanyaza mathayo ake opatsidwa ndi Mulungu monga mkazi ndi amayi. Mtengo umene akanaulipira wa mkhalidwe wamtima ndi wauzimu ukakhala waukulu koposa kuulipira. Chifukwa chake, ataŵerengera mtengo, anasankha kukana mwaŵiwo.

Kodi mukanatani mukadakhala kuti ndinu? Mwachiwonekere, sialiyense amene akavomereza chosankha chimene mkazi Wachikristu ameneyu anapanga. Ena, monga ngati antchito anzake, angalingalire kuti anaphonya mwaŵi waukulu wakupititsa patsogolo ntchito yake. Ena angamnenezedi kukhala wosalingalira mtsogolo mwa banja lake, popeza kuti, zaka ziŵiri zikhoza kutha mofulumira. Komabe, chosankha chake sichinali chopangidwa mwasontho kapena mwakungotengeka maganizo. Chinazikidwa pakulingalira kwabwino ndi pamalamulo amakhalidwe abwino owona patali. Kodi ameneŵa ngotani?

Zoposa Kulingalira Kwachidziŵikire

Mwamuna wanzeru koposa onse amene anakhalapo padziko lapansi, Yesu Kristu, anapereka chitsogozo mu limodzi la mafanizo ake. “Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, naŵerengera mtengo wake, awone ngati ali nazo zakuimaliza?” Yesu anafunsa motero. “Kuti kungachitike, pamene atakhazika pansi miyala ya kumaziko ake, osakhoza kuimaliza, anthu onse akuyang’ana adzayamba kumseka iye, ndi kunena kuti, Munthu uyu anayamba kumanga, koma sanathe kumaliza.”​—Luka 14:28-30.

Aliyense akhoza kuvomereza kuti limakhala lingaliro labwino kuŵerengera mtengo usanasankhe kuchita chinthu chirichonse chofunika. Mwachitsanzo, ngati munthu afuna kugula nyumba, kodi angafulumire kusaina chipangano asanadziŵe konse mtengo wake ndi kutsimikizira kuti ali nazo ndalama zokwanira zoigulira? Akalingaliridwa kukhala wopusa kwambiri ngati angachite chinthu choterocho. Inde, ndilingaliro lachidziŵikire kwa munthu kuŵerengera mtengo asanayambe kuchita chinthu.

Komabe, kodi kwenikweni ndimfundo iti imene Yesu anali kuyesa kuimveketsa m’fanizo limenelo? Asanafotokoze fanizolo, anati: “Amene aliyense sazenza [mtengo wozunzirapo, NW] wa mwini yekha, ndi kudza pambuyo panga, sakhoza kukhala wophunzira wanga.” (Luka 14:27) Motero, mawu apatsogolo ndi pambuyo amasonyeza kuti Yesu sanapereke chabe uphungu wachidziŵikire wokhudza zochita zathu zamasiku onse. Mmalomwake, anali kunena za kuŵerengera mtengo ponena za kukhala wophunzira wake.

Mwafanizo lake, Yesu anasonyeza kuti kukhala wophunzira wake kumaphatikizapo kusintha ndi kudzimana. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti dongosolo lazinthu liripoli nlokhoterera pakukondetsa zinthu zakuthupi ndi dyera. Anthu ochuluka ali otanganitsidwa ndi kukhutiritsa zikhumbo zawo zakuthupi, akumapereka chisamaliro chochepa kapena kusapereka chirichonse kuzosoŵa zawo zauzimu kapena unansi wawo ndi Mulungu. (2 Timoteo 3:1-4) Komabe, kaimidwe kamaganizo kapena mzimu umenewu, umasemphana kwambiri ndi umene unasonyezedwa ndi Yesu Kristu. “Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa,” iye anatero, “koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.” Iye anaika phindu lalikulu koposa pa zinthu zauzimu mmalo mwa zakuthupi pamene anati: “Wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse.”​—Mateyu 20:28; Yohane 6:63.

Chifukwa chake, pamene Yesu analangiza amene anafuna kukhala ophunzira ake kuŵerengera mtengo, kwakukulukulu sanali kunena za mapindu akuthupi, koma auzimu. Kodi chofunika kwambiri kwa iwo nchiyani, maubwino akuthupi amene dziko limapereka kapena mapindu amene kukhala wophunzira kumapereka? Ndicho chifukwa chake pamene anatha kufotokoza fanizolo ndi lina lofanana nalo, anamaliza ndi mawu akuti: “Chifukwa chake tsono, yense wa inu amene sakaniza zonse ali nazo, sakhoza kukhala wophunzira wanga.” (Luka 14:33) Kodi woyembekezera kukhala wotsatirayo ali wofunitsitsa ndi wokonzekera kudzimana koteroko, kapena kodi uli mtengo waukulu kwambiri umene sangafune kulipira?

Kulingalira Kwabwino

Ngakhale kuti zinthu zakuthupi zingabweretse mapindu amene amawonekera kwambiri ndi amwamsanga, mapindu a kulondola zinthu zauzimu ali okhalitsa ndi okhutiritsa kwambiri. Yesu analingalira motere: ‘Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziwononga; ndi pamene mbala zibowola ndi kuba: Koma mudzikundikire nokha chuma m’mwamba, m’mene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndipo mbala sizibowola ndi kuba.’ (Mateyu 6:19, 20) M’nthaŵi yathu, kukwera mitengo kwa zinthu, kutsika kwa malonda pamsika, kulephera kwa mabanki, ndi zina zotero, zawononga ambiri amene amaika chidaliro chawo chonse pachuma chakuthupi. Komabe mtumwi Paulo akutifulumiza ‘kusapenyerera zinthu zowoneka, koma zinthu zosawoneka. Pakuti zinthu zowoneka ziri zakanthaŵi, koma zinthu zosawoneka ziri zosatha.’ (2 Akorinto 4:18) Komabe, kodi ndimotani mmene tingakulitsire kulingalira kumeneku?

Tikhoza kutero mwakutsanzira Chitsanzo chathu, Yesu Kristu. Pamene anali padziko lapansi, sanali konse wodzimana mopambanitsa, malinga ndi umboni wakuti nthaŵi zina anakhala ndi phande m’mapwando aukwati ndi madyerero. Komabe, iye mwachiwonekere anaika patsogolo zinthu zauzimu. Kuti akwaniritse chifuniro cha Atate wake, iye anali wofunitsitsa kulepa ngakhale zinthu zolingaliridwa kukhala zofunikira. Panthaŵi ina analengeza kuti: “Nkhandwe ziri nazo nkhwimba, ndi mbalame zakumwamba zisa, koma Mwana wa munthu alibe potsamira mutu.” (Luka 9:58) Iye anawona kuchita chifuniro cha Atate wake kukhala kofunika kwambiri ndi kokondweretsa kotero kuti anati mowona mtima: “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha iye amene anandituma ine, ndi kutsiriza ntchito yake.”​—Yohane 4:34.

Yesu anasonyeza lingaliro lake lakuzindikira zinthu zopindulitsa mwa njira imene anatsutsira mayesero a Satana. Mdyerekeziyo anayesa kuchititsa Yesu kugwiritsira ntchito mphamvu Yake yopatsidwa ndi Mulungu kudzipindulitsa Yekha, kukhutiritsa zosoŵa Zake zakuthupi, ndi kupeza thamo ndi kutchuka kwakudziko. Yesu anadziŵa bwino lomwe kuti mapindu adyera oterowo akapezedwa kokha pamtengo wokwera kwambiri​—kutaikiridwa ndi chiyanjo cha Mulungu​—mtengo wokwera kwambiri koposa umene anali wokonzekera kulipira, popeza kuti anawona unansi wake wabwino ndi Atate wake kukhala wamtengo wapatali kuposa china chirichonse. Ndicho chifukwa chake anakana kwa mtu wagalu zopereka za Satana, mosazengereza konse.​—Mateyu 4:1-10.

Monga otsatira a Kristu, nafenso timafuna kukhala ndi lingaliro limodzimodzilo lozindikira zinthu zopidulitsa monga Ambuye wathu. M’dongosolo lino lazinthu lolamuliridwa ndi Satana, pali zinthu zambiri zimene zingawonekere kukhala zodzetsa mapindu abwino koma zimene zingakhaledi zowononga unansi wathu ndi Mulungu. Zinthu zotero zonga kufunafuna kukwezedwa pantchito, kulondola maphunziro apamwamba, kupititsa patsogolo malo a munthuwe, kupalana chibwenzi ndi wosakhulupirira, kapena kudziloŵetsa m’malonda osawona mtima zikhoza kutitaitsa chikhulupiriro ndi chiyanjo cha Yehova mosavuta. Tiyenera kuŵerengera mtengo mosamalitsa pamene tiyang’anizana ndi mayesero oterowo.

Nzeru Yeniyeni Ndiyo Chitetezo

Zaka zingapo zapitazo, mwamuna wachichepere Wachikristu mumzinda waukulu ku Far East anapeza mwaŵi wakupita kudziko lakutali kukapititsa patsogolo maphunziro ake. Ngakhale kuti anali kale ndi maphunziro adziko abwino ndi ntchito yamalipiro apamwamba, sanakhutire nazo; anafuna kutukula mkhalidwe wake m’moyo. Akristu anzake anayesa kukambitsirana naye mfundo Zamalemba zimene tangozilingalirazo, koma sanalabadire ndipo anapitiriza ndi makonzedwewo. Ngakhale kuti poyamba anayesa kusunga chikhulupiriro chake, mkupita kwa nthaŵi anataya chiyamikiro chake cha chowonadi cha Baibulo, ndipo anayamba kukaikira. Pambuyo pa chaka chimodzi kapena chapompo, anataya kotheratu chikhulupiriro chake nadzinenera kukhala wokaikira kukhalako kwa Mulungu. Zowona, kupeza digiri lapamwamba la maphunziro akudziko kunampatsa chikhutiro chakutichakuti. Koma chifukwa cha ulemerero wakanthaŵi, ndimtengo waukulu chotani nanga umene anaulipira​—kusweka kwa chikhulupiriro chake ndi upandu wakutaya moyo wamuyaya!​—1 Timoteo 1:19.

Kumbali ina, awo amene samalola chirichonse kudodometsa unansi wawo ndi Mulungu apeza madalitso ochuluka kwa Yehova.

Chitsanzo ndicho mwamuna wachichepere amene anali ndi bizinesi yakulemba mapulani a zipinda za mkati mumzinda wotchulidwa kalewo. Pambuyo pa miyezi ingapo yokha atayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, anapeza mwaŵi woika pachiyeso​—kuchita ntchito yakukonzanso nyumba yopereka malipiro okwanira US$30,000. Komabe, ikaloŵetsamo kuswa malamulo aboma akumanga ndi malangizo oletsa kumanga nyumba zosaloledwa ndi lamulo. Popeza anaphunzira kuti Akristu ayenera kukhala omvera malamulo, anazindikira kuti kutenga ntchitoyo kukamtaitsa chiyanjo cha Mulungu. (Aroma 13:1, 2) Atapenda nkhaniyo mosamalitsa, anakana ntchitoyo. Ndi chotulukapo chotani? Kachitidwe kachikhulupiriro kameneka kanakhaladi posinthira kupita patsogolo kwake kwauzimu. M’chaka chimenecho, anapita patsogolo mpaka kudzipatulira ndi ubatizo. Anagulitsa bizinesi yake ndi kuloŵa ntchito imene inampatsa nthaŵi yowonjezereka yakuchita zinthu zauzimu. Tsopano akutumikira Yehova mosangalala ndi mwachangu.

Amuna achichepere onse aŵiriwa anaŵerengera mtengo. Kodi chosiyana chinali chiyani pazosankha zawo? Nzeru yaumulungu! Motani? Nzeru ndiyo luso lakugwiritsira ntchito chidziŵitso mwanjira imene kaŵirikaŵiri imabweretsa mapindu okhalitsa, ndipo nzeru yaumulungu imatanthauza kugwiritsira ntchito chidziŵitso mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu kaamba ka ife. Ngakhale kuti amuna achichepere aŵiriwo anali nacho chidziŵitso cha Baibulo, kuchigwiritsira ntchito kwawo kunawatsogolera ku zotulukapo zosiyana. Bukhu la Miyambo limati: “Pakuti nzeru idzaloŵa m’mtima mwako, Moyo wako udzakondwera ndi kudziŵa, Kulingalira kudzakudikira, Kuzindikira kudzakuchinjiriza; Kukupulumutsa ku njira yoipa, Kwa anthu onena zokhota.”​—Miyambo 2:10-12.

Mawu a Mulungu, Baibulo, ali magwero a nzeru yeniyeni kumene mungatembenukire nthaŵi zonse kaamba ka chitsogozo pamene mufunikira kupanga zosankha zofunika kwambiri. Mmalo mwakukhala wanzeru za nokha, labadirani uphungu wakuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, Osachirikizika pa luntha lako; Umlemekeze m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola mayendedwe ake.” (Miyambo 3:5, 6) Tiyenera kukhala odzichepetsa ndi ofunitsitsa kuphunzitsidwa, tikumapeŵa mzimu wadziko wodzigangira ndi waukhutu kumve umene wafalikira kwambiri lerolino.

Inde, sitingapeŵe kututa zimene tinafesa, ndipo kulidi koyenera ndi kolondola kusenza zotulukapo za zigamulo ndi zosankha zimene timapanga. (Agalatiya 6:7, 8) Chotero ŵerengerani mtengo musanachite chirichonse. Musalole chirichonse chowonekera kukhala mwaŵi kukuwonongerani mkhalidwe wanu wauzimu kapena unansi wanu ndi Yehova Mulungu. Pemphererani nzeru ndi kulingalira kwabwino kuti mupange zosankha zolondola, popeza kuti zosankha zimene muzipanga tsopano zingatanthauze moyo kapena imfa​—kosatha!​—Yerekezerani ndi Deuteronomo 30:19, 20.

[Zithunzi patsamba 28]

Kodi iye akaika ntchito zauzimu patsogolo m’moyo kapena ntchito yakudziko?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena