Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 8/15 tsamba 30
  • Kodi Mumakumbukira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumakumbukira?
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Nkhani Yofanana
  • Kanani Zoyerekezera Zaudziko, Londolani Zenizeni Zaufumu
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Khoka ndi Nsomba Zimatanthauzanji kwa Inu?
    Nsanja ya Olonda—1992
  • ‘Opatsidwa’ Ali Mphatso ya Yehova
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Adzapulumuka Ndani “Nthaŵi ya Nsautso”?
    Nsanja ya Olonda—1992
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 8/15 tsamba 30

Kodi Mumakumbukira?

Kodi mwayamikira kuŵerenga makope aposachedwa a Nsanja ya Olonda? Eya, tiyeni tiwone ngati mungathe kuyankha mafunso otsatirapoŵa:

▫ Kodi nchiyani kwenikweni chimene chinachitiridwa chithunzithunzi bwino lomwe ndi mwaŵi wantchito wowonjezeredwa umene unaperekedwa kwa Anetini ndi ana aamuna a akapolo a Solomo atabwerera kuchokera kuundende wa ku Babulo?

Lerolino, pamene otsalira a Israyeli wauzimu padziko lapansi akucheperachepera, nkhosa zina zikuwonjezereka. Ena a nkhosa zina ameneŵa, mofanana ndi Anetini ndi ana aamuna a akapolo a Solomo, tsopano agaŵiridwa mathayo olemera moyang’aniridwa ndi otsalira. (Yesaya 61:5)​—4/15, tsamba 16-17.

▫ Kodi mneneri Zefaniya anatanthauzanji pamene anati: “Kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova”? (Zefaniya 2:2, 3)

Kuti aliyense atetezeredwe mkati mwa “chisautso chachikulu” chikudzacho, sikhani yakuti ukapulumutsidwa kamodzi, ndiko kuti wapulumutsidwa kunthaŵi yonse. (Mateyu 24:13, 21, NW) Kubisidwa patsikulo kudzadalira pa kupitiriza kwa munthu kuchita zinthu zitatu: Iye ayenera kufunafuna Yehova, kufunafuna chilungamo, ndi kufunafuna chifatso.​—5/1, tsamba 15-16.

▫ Kodi Mikaeli ‘akuimirira’ m’lingaliro lotani mu “nthaŵi ya chimaliziro”? (Danieli 12:1, 4)

Chiyambire pakukhazikitsidwa kwake monga Mfumu mu 1914, Mikaeli wakhala ‘ataimirira’ kaamba ka anthu a Yehova. Koma posachedwa Mikaeli ‘adzaimirira’ m’lingaliro lapadera kwambiri​—monga Mtumiki wa Yehova kuchotsa kuipa konse padziko lapansi ndipo monga Woombola anthu a Yehova.​—5/1, tsamba 17.

▫ Kodi chimwemwe chowona chimadalira pachiyani?

Chimwemwe chowona chimadalira pa unansi wathu wamtengo wapatali ndi Yehova, chivomerezo chake, ndi dalitso lake. (Miyambo 10:22) Chotero, chimwemwe chenicheni sichingapezedwe popanda kumvera Yehova ndi kudzigonjetsera mwachisangalalo ku chifuniro chake. (Luka 11:28)​—5/15, tsamba 16, 19.

▫ Pamene Yesu anachita zozizwitsa zake za kuchiritsa, kodi chikhulupiriro chinafunika kwa munthu amene anachiritsidwayo?

Mlingo wakutiwakuti wa chikhulupiriro unali wofunika kwa anthu ambiri kuti adze kwa Yesu kudzachiritsidwa. (Mateyu 8:13) Komabe, panalibe kufunikira kwa kulengeza chikhulupiriro kuti Yesu achite zozizwitsa zake, monga ngati pamene anachiritsa munthu wina wopunduka amene sanadziŵe kuti Yesu anali yani. (Yohane 5:5-13) Yesu anabwezeretsa ngakhale khutu lodulidwa la mtumiki wa mkulu wansembe wina, amene anali pakati pa adani a Yesu. (Luka 22:50, 51) Zozizwitsa zimenezi zinachitidwa ndi mphamvu ya mzimu woyera wa Mulungu, osati chifukwa cha chikhulupiriro cha munthu wodwalayo.​—6/1, tsamba 3.

▫ Kodi nchiyani chimene chikuimiriridwa ndi “khoka” lonenedwa m’fanizo la Yesu pa Mateyu 13:47-50?

“Khoka” limaimira chipangizo chapadziko lapansi chimene chimadzinenera kukhala mpingo wa Mulungu ndi chimene chimasonkhanitsa “nsomba.” Chaphatikizapo ponse paŵiri Chikristu Chadziko ndi mpingo wa Akristu odzozedwa, otsiriziraŵa akumapitirizabe kusonkhanitsa ‘nsomba zabwino,’ motsogozedwa ndi angelo, mogwirizana ndi Mateyu 13:49.​—6/15, tsamba 20.

▫ Kodi ndiati amene ali ena a malamulo a khalidwe labwino amene oweruza mu Israyeli anafunikira kugwiritsira ntchito posamalira mathayo awo?

Chiweruzo cholungama kwa olemera ndi osauka omwe, kusachita tsankho kosamalitsa, ndi kusalandira ziphuphu. (Levitiko 19:15; Deuteronomo 16:19)​—7/1, tsamba 13.

▫ Kodi akulu ayenera kuyesa kupeza chiyani poweruza mlandu?

Cholinga chimodzi ndicho cha kupeza zenizeni za mlanduwo, akumachita zimenezi mwachikondi. Pamene zimenezi zadziŵika, akuluwo ayenera kuchita zirizonse zimene zikufunika kutetezera mpingo ndi kuuchititsa kukhalabe ndi miyezo yapamwamba ya Yehova ndi kayendedwe katawatawa ka mzimu wa Mulungu. Kuweruzako kuyeneranso kupulumutsa, ngati nkotheka, wochimwa wokhala paupanduyo. (Yerekezerani ndi Luka 15:8-10.)​—7/1, tsamba 18-19.

▫ Kodi nchifukwa ninji zoyerekezera zogwirizana ndi kugonana kosaloledwa ziri zaupandu?

Polingalira mawu a Yesu pa Mateyu 5:27, 28, awo onse amene amadziphatikizabe m’zoyerekezera za kugonana kosaloledwa ngaliwongo la kuchita chigololo m’mitima yawo. Ndipo pali upandu weniweni wakuti zoyerekezera zotero zingatsogolere munthu kuchisembwere.​—7/15, tsamba 15.

▫ Kodi ndim’njira zotani zimene Yehova angatithandizire kulingalira mayesero athu moyenerera ndipo motero kuwapirira?

Tingakumbukire malemba onenedwa ndi okhulupirira anzathu kapena onenedwa mkati mwa phunziro la Baibulo. Zochitika zolamuliridwa ndi chitsogozo cha Mulungu zingatithandize kuwona chochita. Angelo angakhale ndi phande m’kutitsogoza, kapena mwina tingalandire chitsogozo kupyolera mwa mzimu woyera. (Ahebri 1:14)​—7/15, tsamba 21.

▫ Kodi Msonkhano wa ku Nicaea mu 325 C.E. unayambitsa kapena kutsimikizira chiphunzitso cha Utatu?

Ayi, Msonkhano wa ku Nicaea unachititsa kokha kufanana kwa Mwana ndi Atate kukhala “munthu mmodzi.” Lingaliro lakuti Atate, Mwana, ndi mzimu woyera anali Mulungu wowona​—anthu atatu mwa Mulungu mmodzi​—silinayambidwe ndi msonkhanowo kapena Abambo Atchalitchi.​—8/1, tsamba 20.

▫ Kodi Yobu ndiye yekha amene anali munthu wokhulupirika kwa Yehova mkati mwa nyengo imene anakhala ndi moyo? (Yobu 1:8)

Ayi, bukhu la Yobu lenilenilo limasonyeza kuti Elihu anali wovomerezedwa ndi Mulungu. Ndiponso, mkati mwa nthaŵi imene Yobu anakhalako, kunali Aisrayeli ambiri okhala mu Igupto, ndipo palibe chifukwa choganizirira kuti anthu onsewa anali opanda chikhulupiriro ndi osavomerezedwa ndi Mulungu.​—8/1, tsamba 31.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena