Matembenuzidwe Abaibulo a mu Afirika
Matembenuzidwe oyambirira a Baibulo lathunthu m’chinenero cha mu Afirika anachitidwa mu Igupto. Pokhala odziŵika monga matembenuzidwe a Coptic, akukhulupiriridwa kukhala a m’zaka za zana lachitatu kapena lachinayi C.E. Pafupifupi zaka mazana atatu pambuyo pake, Baibulo linatembenuzidwira m’Chiitiopiya.
Zinenero zosalembedwa mazana ambiri zolankhulidwa kumwera kwa Aitiopiya ndi Sahara zinafunikira kuyembekezera kufika kwa amishonale m’zaka za zana la 19. Mu 1857 masinthidwe aakulu anachitika pamene Robert Moffat anatsiriza matembenuzidwe Abaibulo m’Chitswana, chinenero cha kumwera kwa Afirika. Iye analisindikizanso m’tizigawotizigawo pamakina apamanja. Limeneli linali Baibulo lathunthu loyamba kusindikizidwa mu Afirika ndipo linalinso matembenuzidwe athunthu oyamba kutembenuzidwira m’chinenero chimene poyamba chinali chosalembedwa cha mu Afirika. Mokondweretsa, Moffat anagwiritsira ntchito dzina la Mulungu lakuti Yehova m’matembenuzidwe ake. M’matembenuzidwe a 1872 ofalitsidwa ndi British and Foreign Bible Society, dzina lakuti Yehova likugwiritsiridwa ntchito m’mawu aakulu okambidwa ndi Yesu monga momwe alembedwera pa Mateyu 4:10 ndi Marko 12:29, 30.
Podzafika mu 1990 Baibulo lonse lathunthu linali litatembenuzidwira m’zinenero 119 za mu Afirika, pamene mbali zake zikumapezeka m’zowonjezereka 434.