Mesiya—Kodi Ndiye Chiyembekezo Chenicheni?
Anadzitcha Mose. Komabe, dzina lake lenileni linaiŵalika m’mbiri. Mzaka za zana lachisanu C.E., anayendayenda pa chisumbu chonse cha Krete, akumakhutiritsa Ayuda kuti iye anali mesiya amene anali kudikirira. Anawauza kuti mwamsanga chitsenderezo chawo, ukapolo wawo ndi undende zikatha. Iwo anakhulupirira. Pamene tsiku lawo la chimasuko linadza, Ayudayo anatsatira “Mose” ku malo okwera oyang’anizana ndi Nyanja ya Mediterranean. Anawauza kuti iwo anayenera kudziponyera m’nyanja ndipo idzagawanikana akuwona. Ambiri anamvera, akumadziponya m’nyanja imene siinagaŵanikane. Ochuluka kwambiri anamira; ena anapulumutsidwa ndi amalinyero ndi asodzi. Komabe, Mose sanapezeke kulikonse. Mesiya ameneyo anapita.
KODI mesiya nchiyani? Mawu akuti “mpulumutsi,” “muwomboli,” ndi “mtsogoleri” angakumbukiridwe. Anthu ambiri amaganiza kuti mesiya ndimunthu amene amasonkhezera za chiyembekezo ndi kudzipereka mwa atsitiri ake, akumawalonjeza kuwatsogolera kuchoka ku chitsenderezo kumka ku ufulu. Popeza kuti mbiri ya anthu iri kwakukulukulu ya chitsenderezo, nkosadabwitsa kuti amesiya ambiri oterowo anawonekera mkati mwa zaka mazana ambiri. (Yerekezerani ndi Mlaliki 8:9.) Koma mofanana ndi wodzitcha yekha Mose wa ku Krete, amesiya ameneŵa kaŵirikaŵiri atsogolera owatsatira kukugwiritsidwa mwala ndi kungozi m’malo mwa chimasuko.
“Uyu ndiye Mfumu Mesiya!” Umo ndi mmene rabi wokwezedwayo Akiba ben Joseph analonjerera Simeon Bar Kokhba m’chaka cha 132 C.E. Bar Kokhba anali munthu wamphamvu amene anatsogolera gulu lamphamvu la asilikali. Potsirizira pake, anaganiza motero Ayuda ambiri, anafika munthu wakudzachotsa chitsenderezo chawo cha nthaŵi yaitali ku Ulamuliro Wadziko wa Aroma. Bar Kokhba analephera; kulephera kwake kunawonongetsa miyoyo ya anthu ake zikwi mazana ambiri.
M’zaka za zana la 12, mesiya wina Myuda anatulukira, panthaŵi ino mu Yemen. Pamene mlowa mmalo, kapena mtsogoleri, anamfunsa kaamba ka chizindikiro cha umesiya wake, mesiyayu ananena kuti mtsogoleriyo amdule mutu kuti chiukiriro chake chamwamsanga chikhale chizindikiro. Mtsogoleriyo anavomereza zimenezo—ndipo kumeneko kunali kutha kwa mesiya wa ku Yemen. M’zaka za zana limodzimodzilo, mwamuna wotchedwa David Alroy anauza Ayuda mu Middle East kukonzekera kuwuluka naye pa mapiko a angelo kubwerera ku Dziko Lopatulika. Ambiri anakhulupirira kuti anali mesiya. Ayuda aku Baghdad anayembekezera moleza mtima pa madenga a nyumba zawo, pamene pansipo mbala zinafunkha zinthu zawo iwo osadziŵa.
Sabbatai Zevi anatulukira mu zaka za zana la 17 kuchokera ku Smurna. Analengeza za umesiya wake kwa Ayuda mu Yuropu yense. Akristu nawonso, anamvera iye. Zevi analonjeza chimasuko kwa otsatira ake—mwachiwonekere akumawalola kuchita machimo modzifunira. Otsatira ake apafupi anachita madzoma amadyerero, kuvina maliseche, chisembwere, ndi kugonana kwa pachibale, kenako nkumadzilanga okha mwakukwapulana, kukunkhulika m’chipale chofeŵa ali maliseche, ndi mwakudzifochera kufikira m’khosi ali maliseche m’nthaka yozizira. Pamene anapita ku Turkey, Zevi anagwidwa ndi kuuzidwa kuti ayenera kutembenuka ndi kukhala Msilamu apo phuluzi akaphedwa. Anatembenuka. Otsatira ake ambiri anakhwethemuka. Komabe, kwa zaka mazana aŵiri zotsatira, Zevi anatchedwabe Mesiya ndi anthu ena.
Chikristu Chadziko nachonso chatulutsa amesiya ake. M’zaka za zana la 12, mwamuna wotchedwa Tanchelm anapanga gulu lankhondo la atsatiri ake ndi kulamulira tauni la Antwerp. Mesiyayu anadzitcha mulungu; anagulitsa ngakhale madzi ake osambamo kwa atsatiri ake kuti amwe monga chizindikiro chakudzipatulira! Mesiya wina “Wachikristu” anali Thomas Müntzer wa ku Jeremani wa m’zaka za zana la 16. Iye anatsogolera chipanduko chogalukira boma, akumauza otsatira ake kuti inali nkhondo ya Armagedo. Analonjeza kuti akaŵakha zipolopolo za mfuti za adaniwo m’malaya ake. Koma mmalomwake, anthu ake anapululutsidwa, ndipo Müntzer iye mwiniyo anadulidwa mutu. Amesiya ambiri oterowo anauka m’Chikristu Chadziko mkati mwa zaka mazana ambiri.
Zipembedzo zinanso zakhala ndi amesiya awo. Asilamu amasonya kwa Mahdi, kapena wotsogozedwa, amene adzatsogolera kuloŵa m’nyengo ya chilungamo. M’Chihindu, ena anena kuti ali milungu yosiyanasiyana imene inauka. Ndipo, monga momwe The New Encyclopædia Britannica imanenera, “ngakhale chipembedzo chosakhulupirira mesiya monga Chibuddha chapereka chiyembekezo, pakati pa magulu a Mahāyāna, mwa Buddha wamtsogolo wotchedwa Maitreya amene adzatsika kuchokera kumalo ake akumwamba ndi kudzatengera okhulupirika ku paradaiso.”
Amesiya a m’Zaka za Zana la 20
M’zaka za zana lathu lino, kufunika kwa mesiya weniweni kwakhala kofunikira mwamsanga kuposa ndi kalelonse; pamenepo, sikodabwitsa kuti ambiri adzipatsa dzinalo. M’Congo wa m’Afirika m’ma 1920, ’30, ndi ’40, Simon Kimbangu ndi womloŵa malo wake Andre “Jesus” Matswa anabukitsidwa monga amesiya. Iwo anafa, koma otsatira awo akuwayembekezerabe kubweranso ndi kuyambitsa zaka chikwi za m’Afirika.
Zaka za zana lino zawonanso kubuka kwa “timagulu tachipembedzo tamatsenga opezera katundu wamakono” mu New Guinea ndi Melanesia. Ziŵalo zawo zimayembekezera sitima yapamadzi kapena ndege kufika, yoyendetsedwa ndi amuna achingelezi onga mesiya amene adzawachititsa kukhupuka ndi kubweretsa nyengo ya chimwemwe ndipo ngakhale akufa adzauka.
Maiko otsungula nawonso akhala ndi amesiya awo. Ena ali atsogoleri achipembedzo, monga ngati Sun Myung Moon, wodzinenera kukhala woloŵa malo wa Yesu Kristu amene akufuna kuyeretsa dziko kupyolera mwa banja logwirizana la omtsatira. Atsogoleri andale zadziko ayesanso kutenga malo aumesiya, Adolf Hitler nkukhala chitsanzo chowopsa koposa ndi zonena zake za Ulamuliro Wake wa Zaka Chikwi zaulemerero.
Nthanthi ndi magulu andale zadziko apezanso malo aumesiya. Mwachitsanzo, The Encyclopedia Americana imanena kuti nthanthi yandale ya Marxizimu-Leninizimu iri ndi zikhulupiriro zaumesiya. Ndipo gulu la Mitundu Yogwirizana, lobukitsidwa kwambiri kukhala chiyembekezo chokha cha mtendere wadziko, ikuwonekera kwa ambiri kukhala mloŵa malo wa mesiya.
Kodi Nchiyembekezo Chenicheni?
Kupenda kwachidule kumeneku kumasonyeza poyera kuti mbiri ya magulu aumesiya kwakukulukulu yakhala mbiri yachinyengo, ya ziyembekezo zosweka ndi maloto chabe. Pamenepa, nzosadabwitsa kuti anthu ambiri lerolino amakhulupirira kuti chiyembekezo cha mesiya changokhala chochititsa munthu kukhala ndi mkhalidwe wabwino.
Komabe, tisanakaniretu chiyembekezo cha mesiya, choyamba tiyenera kudziŵa kumene chimachokera. Kwenikweni, “mesiya” ndiliwu la m’Baibulo. Liwu Lachihebri ndilo ma·shiʹach, kapena “wodzozedwa.” M’nthaŵi zosimbidwa m’Baibulo, mafumu ndi ansembe nthaŵi zina anaikidwa pamalo awo mwa dzoma lakudzoza, pamene mafuta onunkhira anatsiridwa pamutu. Chifukwa chake liwulo ma·shiʹach molondola linagwiritsiridwa ntchito pa iwo. Panalinso anthu amene anadzozedwa, kapena kuikidwa pamalo apadera, koma popanda dzoma lakudzoza. Mose amatchedwa “Kristu,” kapena “wodzozedwa,” pa Ahebri 11:24-26, chifukwa chakuti anasankhidwa monga mneneri ndi woimira wa Mulungu.
Kumasulira kwa mesiya kumeneku monga “wodzozedwa” kumapatula amesiya a m’Baibulo kwa amesiya onyenga amene takambitsiranawo. Amesiya a m’Baibulo sanadziike okha; ndipo sanasankhidwe ndi gulu la owatsatira owachirikiza. Iyayi, kuikidwa kwawo kunachokera kumwamba, kwa Yehova Mulungu iyemwiniyo.
Pamene Baibulo limalankhula za amesiya ambiri, limakweza mmodzi pamwamba pa ena onsewo. (Salmo 45:7) Mesiya ameneyu ndiye maziko a ulosi wa Baibulo, mfungulo ya kukwaniritsidwa kwa malonjezo a m’Baibulo ambiri ochititsa chidwi. Ndipo Mesiya ameneyu akhozadi kuthetsa mavuto amene tikuyang’anizana nawo lerolino.
Mpulumutsi wa Mtundu wa Anthu
Mesiya wa mu Baibulo amachita ndi mavuto a mtundu wa anthu mwakuyamba ndi magwero ake. Pamene makolo athu oyamba, Adamu ndi Hava, anapandukira Mlengi posonkhezeredwa ndi cholengedwa chauzimu chopanduka Satana, kwenikweni anali kudzitengera okha mphamvu yakulamulira. Anafuna kukhala osankha chabwino ndi choipa. Mwakutero anapambuka pakulamulira kwachikondi ndi kotetezera kwa Yehova, ndi kuloŵetsa banja la anthu m’chipolowe ndi tsoka lakudzilamulira, kupanda ungwiro, ndi imfa.—Aroma 5:12.
Pamenepa, nchikondi chotani nanga kuti panthaŵi yatsoka imeneyo m’mbiri ya anthu, mpamene Yehova Mulungu anapereka chiyembekezo choŵala kwa mtundu wa anthu. Popereka chiweruzo kwa apandu aumunthuwo, Mulungu ananeneratu kuti mbadwa zawo zikakhala ndi momboli. Wotchedwa “mbewu,” Mpulumutsi ameneyu akadza kudzawongolera chimene Satana anawononga m’Edene; Mbewuyo ikazunzunda “njokayo,” Satana, kumutu, kumfafaniza ndi kusakhalaponso.—Genesis 3:14, 15.
Kuchokera m’nthaŵi zamakedzana, Ayuda anawona ulosiwu kukhala Waumesiya. Matembenuzidwe angapo otchedwa Targum, amene ndiwo kutembenuzidwanso Kwachiyuda kwa Malemba Opatulika ogwiritsiridwa ntchito mofala m’zaka za zana loyamba akakwaniritsidwa “m’tsiku la Mfumu Mesiya.”
Chotero, mposadabwitsa kuti kuyambira pachiyambi penipenipo, anthu achikhulupiriro anasangalala ndi lonjezo limeneli la Mbeyu yobwerayo, kapena Mpulumutsi. Tangolingalirani za mmene Abrahamu anamverera pamene Yehova anamuuza kuti Mbewuyo ikabwera kudzera mwa mzera wake wobadwira, ndi kuti mwa mbewu imeneyo “mitundu yonse yapadziko lapansi”—osati mbadwa zake zokha—“idzadalitsidwa.”—Genesis 22:17, 18.
Mesiyayo ndi Boma
Maulosi apambuyo pake anadzagwirizanitsa ulosi umenewu ndi chiyembekezo cha boma labwino. Pa Genesis 49:10, Yuda mdzukulu wa mdzukulu wa Abrahamu anauzidwa kuti: “Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.” Momvekera bwino, “Silo” ameneyu anali kudzalamulira—ndipo akalamulira osati Ayuda okha komanso ‘anthu onse.’ (Yerekezerani ndi Danieli 7:13, 14.) Ayuda amakedzana anadziŵa Silo ameneyu kukhala Mesiya; kwenikweni, Matembenuzidwe ena Achiyuda anangotchula “Mesiya” mmalo mwa “Silo” kapena “mfumu Mesiya.”
Pamene kuunika kwa maulosi ouziridwa kunapitiriza kuŵala, zambiri zinavumbulidwa ponena za ulamuliro wa Mesiya ameneyu. (Miyambo 4:18) Pa 2 Samuel 7:12-16, Mfumu Davide, mbadwa ya Yuda, anauzidwa kuti Mbewuyo ikafika kudzera mumzera wake. Ndiponso, Mbewu imeneyi inali kudzakhala Mfumu yapadera. Mpando wake wachifumu, kapena ulamuliro wake, ukakhala kunthaŵi zonse! Yesaya 9:6, 7 amachirikiza mfundoyi kuti: “Kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro [“boma,” King James Version] udzakhala pa pheŵa lake, . . . za kuwonjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pampando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kumkabe nthaŵi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.”
Kodi mungayerekezere boma lotero? Wolamulira wachiweruzo cholungama, wachilungamo amene akhazikitsa mtendere ndi amene akulamulira kosatha. Nzosiyana chotani nanga ndi zipambano za m’mbiri za amesiya onama! Mesiya wa Baibulo ndiye wolamulira wa dziko lonse wokhala ndi mphamvu zonse ndi ulamuliro wofunikira kusintha mikhalidwe yadziko, ngwosiyaniranatu ndi atsogoleri onyenga ndi odzikhazikitsa okha.
Chiyembekezo chimenechi nchofunika kwambiri m’nthaŵi zathu zovuta zino. Mtundu wa anthu sunakhalepo m’kusoŵa kwakukulu kwa chiyembekezo mofanana ndi lerolino. Komabe, popeza kuti nkosavuta kugwera m’ziyembekezo zonyenga, nkofunika kwambiri kuti aliyense wa ife apende mosamalitsa funso ili: Kodi Yesu Mnazarayo analidi Mesiya wonenedweratuyo monga momwe ambiri amakhulupiririra? Nkhani yotsatira idzayankha funsolo.
[Bokosi patsamba 6]
Mesiya m’Brooklyn?
Posachedwapa, zilengezo zomamatiza, zikwangwani, ndi nyali za zizindikiro m’Israyeli zinalengeza “Kukonzekera kufika kwa Mesiya.” Mkupiti wolengeza umenewu wodya ndalama zokwanira $US400,000 unalinganizidwa ndi Alubavitcha, mpatuko wa Ayuda Achihasidi. Pali chikhulupiriro chofala pakati pa gululo lokhala ndi ziŵalo 250,000 chakuti rabi wawo wamkulu, Menachem Mendel Schneerson wa ku Brooklyn, New York, ndiye Mesiyayo. Chifukwa ninji? Schneerson samaphunzitsa kuti Mesiya adzabwera mumbadwo uno. Ndipo malinga nkunena kwa magazini a Newsweek, akuluakulu Achilubavitcha amaumirira kunena kuti rabiyo wazaka 90 sadzamwalira Mesiya asanafike. Kwa zana mazana ambiri kagulu kampatukoko kaphunzitsa kuti mbadwo uliwonse umatulutsa munthu amene amayenerera kukhala Mesiya. Schneerson akuwonekera kukhala munthuyo kwa otsatira ake, ndipo sanaike aliyense monga womloŵa m’malo. Chikhalirechobe, Ayuda ochuluka samamvomereza monga Mesiya, inatero Newsweek. Malinga nkunena kwa nyuzipepala ya Newsday, rabi mnzake wotsutsana naye wazaka 96 wotchedwa Eliezer Schach, wamutcha “mesiya wonyenga.”
[Chithunzi patsamba 7]
Chikhulupiriro chakuti Mose wa ku Krete anali mesiya chinataitsa miyoyo ya ambiri