Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 11/1 tsamba 21-22
  • Munthu Wophunzira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Munthu Wophunzira
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mbadwa ya ku Tariso
  • Nzika ya Roma
  • Lingaliro Loyenera
  • Mutha Kupeza Madalitso a Ufumu
    Nsanja ya Olonda—2001
  • “Mvetserani Mawu Anga Odziteteza”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
  • Paulo Anateteza Uthenga Wabwino kwa Akuluakulu a Boma
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Kusunga Maphunziro Pamalo Ake
    Galamukani!—1994
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 11/1 tsamba 21-22

Munthu Wophunzira

“PENYANI maitanidwe anu, abale, kuti saitanidwa ambiri anzeru, monga mwa thupi; ambiri amphamvu, mfulu zambiri, iyayi.” (1 Akorinto 1:26) Monga momwe mawuŵa akusonyezera, kufuna nzeru zakudziko zakuya ndi malo apamwamba kuli kwangozi. Zinthu zoterozo zikhoza kutsekereza kulandira mbiri yabwino kwa munthu.​—Miyambo 16:5; Marko 10:25.

Komabe, m’tsiku la Paulo ena amene anali anzeru mwakuthupi analandiradi chowonadi, ndipo mmodzi wa iwo anali Paulo weniweniyo. Monga munthu wophunzira kwambiri ndipo mwachiwonekere wochokera kubanja lapamwamba, Paulo anali mlaliki wachangu. Motero iye anasonyeza kuti anthu okhupuka m’dziko lino akhoza kutumikira Yehova ngati ali ndi mtima wowongoka. Akhoza ngakhale kugwiritsira ntchito maluso awo muutumiki wa Yehova.​—Luka 16:9.

Mbadwa ya ku Tariso

Paulo anabadwira m’Tariso, “mudzi womveka,” monga momwe iye anautchera pambuyo pake. (Machitidwe 21:39) Mwinamwake ndikumeneko kumene anadziŵira zinenero​—makamaka chidziŵitso cha Chigiriki​—chimene chinali chothandiza kwambiri m’ntchito yake yaumishonale. Moyo m’Tariso uyenera kuti unadziŵitsa Paulo osati mikhalidwe ya Ayuda yokha komanso miyambo ya Akunja, chidziŵitso chimene anagwiritsira ntchito m’zaka zapambuyo pake monga mtumwi kwa amitundu. Anadziŵa kufotokoza chowonadi mwanjira imene iwo anakhoza kumvetsetsa. (1 Akorinto 9:21) Mwachitsanzo, talingalirani nkhani yake kwa nzika za ku Atene yopezeka m’chaputala 17 cha Machitidwe. Kumeneko, mwaluso anagwiritsira ntchito maumboni a Chipembedzo cha Atene ndipo ngakhale kugwira mawu ina ya ndakatulo zawo m’nkhani yake yopereka chowonadi.

Nzika ya Roma

Paulo anali ndi mwaŵi wina wakudziko. Iye anali nzika ya Roma, ndipo anagwiritsira ntchito unzika umenewunso kupititsa patsogolo mbiri yabwino. Pamene anali m’Filipi, iye ndi anzake anamenyedwa ndi kuponyedwa m’ndende popanda kuzengedwa mlandu. Unali mlandu kuchitira nzika ya Roma zimenezi, ndipo pamene Paulo anadziŵitsa zimenezi kwa akuluakulu, anamlola kukhalabe ndi kutumikira mpingowo asanachoke kupita kugawo lake lotsatira.​—Machitidwe 16:37-40.

Pambuyo pake, pamene anakawonekera pankhope pa Kazembe Festo, Paulo anagwiritsira ntchito mwaŵi wa kukhala kwake nzika ya Roma kuchitira apilo mlandu wake kwa Kaisala. Motero, anachita chodzikanira cha mbiri yabwino pamaso pa wolamulira wamkulu koposa mu Ufumu wa Roma.​—Machitidwe 25:11, 12; Afilipi 1:7.

Paulo anaphunzitsidwa ntchito mwanjira yopindulitsa imene pambuyo pake inadzakhaladi yothandiza. Anaphunzitsidwa kusoka mahema, mwachiwonekere ndi atate wake. Chifukwa cha zimenezi, anakhoza kudzichirikiza yekha muuminisitala pamene ndalama zinamchepera. (Machitidwe 18:1-3) Analandiranso maphunziro ochuluka achipembedzo. Analeredwa monga “Mfarisi, mwana wa Afarisi.” (Machitidwe 23:6) Ndithudi, iye anaphunzira pamapazi a Gamaliyeli, mmodzi wa aphunzitsi Achiyuda otchuka kwambiri. (Machitidwe 22:3) Maphunziro oterowo, mwinamwake oyerekezeredwa ndi maphunziro abwino akuyunivesite alerolino, amapereka lingaliro lakuti banja lake linali lapamwamba ndithu.

Lingaliro Loyenera

Chiyambi cha Paulo ndi kuphunzitsidwa kwake kunamuikira mwaŵi wa mtsogolo mwabwino m’Chiyuda. Akapambana kwambiri. Komabe, pamene anakhulupirira kuti Yesu anali Mesiya, zonulirapo za Paulo zinasintha. Polembera Afilipi, anafotokoza zina za mwaŵi wake wakale wakudziko nati: “Zonse zimene zinandipindulira, zomwezo ndinaziyesa chitayiko chifukwa cha Kristu. Komatu zenizeninso ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiro cha Kristu Yesu Ambuye wanga.”​—Afilipi 3:7, 8.

Munthu wophunzira ameneyu sanayang’ane kumbuyo kukhumbira zimene akanachita ndi maphunziro ake akudziko; kapena sanagwiritsire ntchito “kuŵerengetsa kwake” kuti awopseze ena. (Machitidwe 26:24; 1 Akorinto 2:1-4) Mmalomwake, pokhulupirira Yehova Mulungu kotheratu, iye anati kusonya ku ziyembekezo zake zakale zachipambano: “Poiŵaladi zam’mbuyo, ndi kutambalitsira zam’tsogolo, ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo ya maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 3:13, 14) Paulo anawona zinthu zauzimu kukhala zopindulitsa.

Komabe, Paulo anagwiritsira ntchito zimene anaphunzira kalezo muutumiki wa Yehova. Pamene anati za Ayuda, “ndiwachitira iwo umboni kuti ali ndi changu cha kwa Mulungu,” ananena malinga ndi chidziŵitso cha zochitika kwa iye. (Aroma 10:2) Monga Mfarisi wokangalika, iye ndithudi anali ndi changu cha kwa Mulungu ndi Malemba. Pamene Paulo anakhala Mkristu, changu chake chinakhwimitsidwa ndi chidziŵitso cholongosoka, ndipo anatha kugwiritsira ntchito maphunziro ake akale pacholinga chabwino. Mwachitsanzo, m’bukhu la Ahebri, anagwiritsira ntchito chidziŵitso chake chachikulucho cha mbiri ya Aisrayeli ndi kulambira kwa m’kachisi kusonyeza kupambana kwa dongosolo Lachikristu.

Ena lerolino amene ali anzeru m’njira yakuthupi amalabadiranso mbiri yabwino. Anthu a maphunziro osiyanasiyana, kuphatikizapo akatswiri ndi azintchito zosiyanasiyana, alandira chowonadi ndi kugwiritsira ntchito maphunziro awo akale muutumiki wa Yehova. Komabe, mosasamala kanthu ndi mtundu wa maphunziro awo, Akristu samaleka kuwona mfundo yakuti ziyeneretso zofunikira koposa ndizo zauzimu. Izi ndizo “zinthu zofunika koposa” chifukwa chakuti zikhoza kutitsogolera ku moyo wosatha.​—Afilipi 1:10, NW.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena