Mtanda—Kodi Ndiwo Chizindikiro cha Chikristu?
KWA zaka mazana ambiri anthu ambirimbiri avomereza mtanda monga chizindikiro cha Chikristu. Koma kodi uwo ulidi? Ambiri amene akhulupirira motero mowona mtima akudabwa kwambiri kumva kuti mtanda suli wolekezera konse m’Chikristu Chadziko. Mmalo mwake, wagwiritsidwa ntchito kwambiri m’zipembedzo zosakhala Zachikristu padziko lonse lapansi.
Mwachitsanzo, kuchiyambiyambi kwa ma 1500, pamene Hernán Cortés ndi gulu lake lankhondo “Lachikristu” anakonzekera kuukira Ulamuliro wa Aztec, ananyamula mbendera zimene zinalengeza kuti: “Tiyeni titsatire chizindikiro cha Mtanda Wopatulika m’chikhulupiriro chowona, chifukwa chakuti mwachizindikiro chimenechi tidzapambana.” Iwo ayenera kukhala atadabwa kupeza kuti adani awo achikunjawo analemekeza mtanda wosasiyana ndi wa iwo eni. Bukhu lakuti Great Religions of the World limati: “Cortés ndi otsatira ake anaipidwa ndi nsembe za anthu zofukizidwa ndi Aztecs ndi zimene zinawonekera kukhala zizindikiro zofanizira Chikristu za usatana: . . . kulemekeza zizindikiro zonga mtanda za milungu yamphepo ndi yamvula.”
Nkhani yamkonzi m’nyuzipepala ya La Nación, wolemba José Alberto Furque akutchula kuti m’theka lachiŵiri la zaka za zana la 18, panali “kutsutsana kopsetsana mtima ndi kochititsa nthumanzi pakati pa akatswiri achiyambi cha anthu ndi mafuko awo ndi akatswiri ofukula za m’mabwinja ponena za magwero ndi tanthauzo la zizindikiro za mtanda” zimene anali kupeza m’mbali yaikulu ya Central ndi South America. Mwachiwonekere ena anali ofunitsitsa kutetezera kudziŵika kwa mtanda kukhala chizindikiro cholekezera ku “Chikristu” chabe kotero kuti anapeka nthanthi yakuti mwanjira ina yake nzika za America zinali zitalalikidwa kale ulendo wopanga mbiri wa Columbus usanachitike! Lingaliro losatsimikizirika limeneli linakanidwa monga lopanda maziko.
M’kupita kwanthaŵi, zotulukiridwa zina m’nkhaniyi zinachititsa mkangano wonse wotero kutha. Furque akuti: “m’bukhu lofalitsidwa mu 1893 ndi Smithsonian Institution, kunatsimikiziridwa kuti mtanda unali kulemekezedwa kale . . . kalekale nzika zoyambirira za ku Yuropu zisanafike mu North America, zimene zikutsimikizira nthanthiyo . . . yakuti chizindikiro chotero chinalimo m’zitaganya zonse monga mbali yakulambira makolo molemekeza mphamvu zimene zinayambitsa moyo.”
Baibulo limasonyeza kuti Yesu sanaphedwere konse pa mtanda wodziŵikawo, koma mmalo mwake, pa mtengo wamba, kapena stau·rosʹ. Liwu Lachigiriki limeneli, limene limawonekera pa Mateyu 27:40, kwakukulukulu limatanthauza nsanamira wamba yowongoka kapena nsichi, monga yogwiritsidwa ntchito pomanga maziko. Chifukwa chake, mtanda sunaimire konse Chikristu chowona. Yesu Kristu anasonyeza chisonyezero chenicheni, kapena “chizindikiro,” cha Chikristu chowona pamene anauza otsatira ake kuti: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.”—Yohane 13:35.