Yehova Sayenera Kuimbidwa Mlandu
“Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuwopa Iye. Popeza adzi ŵa mapangidwe athu; Akumbukira kuti ife ndife fumbi.”—SALMO 103:13, 14.
1, 2. Kodi Abrahamu anali yani, ndipo ndimotani mmene Loti mwana wa mphwake anadzakhalira mumzinda woipa wa Sodomu?
YEHOVA sindiye ali ndi mlandu wa mavuto amene tingakumane nawo chifukwa cha zolakwa zathu. Pamfundoyi, talingalirani zimene zinachitika pafupifupi zaka 3,900 zapitazo. Bwenzi la Mulungu Abrahamu (Abramu) ndi Loti mwana wa mphwake anakhupuka kwambiri. (Yakobo 2:3) Kwenikweni, chuma chawo ndi zifuyo zinali zochuluka kwambiri kwakuti “dziko silinathe kuwakwanira iwo.” Ndiponso, panabuka mkangano pakati pa abusa a amuna aŵiriwo. (Genesis 13:5-7) Kodi nchiyani chikanachitidwa?
2 Kuti athetse mkanganowo, Abrahamu anapereka lingaliro lakuti apatukane, ndipo analola Loti kukhala woyamba kusankha malo. Ngakhale kuti Abrahamu ndiye anali mwamuna wachikulirepo ndipo kukadakhala koyenera kuti mwana wamphwakeyo amlole kutenga malo abwino koposa, Loti anasankha chigawo chabwino koposa—chigawo chonsecho chamadzi ochuluka cha Kumunsi kwa Yordano. Mawonekedwe akunja anali onyenga, chifukwa chakuti pafupipo panali mizinda yoluluzika ya Sodomu ndi Gomora. Mkupita kwanthaŵi, Loti ndi banja lake anasamukira m’Sodomu, ndipo zimenezi zinawaika m’vuto lauzimu. Ndiponso, iwo anatengedwa monga akapolo pamene Mfumu Kedorelaomere ndi anzake anagonjetsa wolamulira wa Sodomu. Abrahamu ndi amuna ake anawalanditsa, koma Loti ndi banja lake anabwerera ku Sodomu.—Genesis 13:8-13; 14:4-16.
3, 4. Kodi nchiyani chinachitika kwa Loti ndi ziwalo za banja lake pamene Mulungu anawononga Sodomu ndi Gomora?
3 Chifukwa cha kululuzika m’zakugonana ndi kunyonyotsoka kwa Sodomu ndi Gomora, Yehova anasankha kuwononga mizindayo. Iye mwachifundo anatumiza angelo aŵiri amene anatsogolera Loti, mkazi wake, ndi ana awo aŵiri aakazi kutuluka m’Sodomu. Sanayenera kuyang’ana kumbuyo, koma mkazi wa Loti anatero, mwinamwake akukhumbira zinthu zakuthupi zimene anasiya kumbuyo. Pamenepo, anasandulika mwala wa mchere.—Genesis 19:1-26.
4 Loti ndi ana ake aakazi anataikiridwa kwambiri chotani nanga! Atsikanawo anasiya amuna amene anali kudzawakwatira. Loti tsopano analibe mkazi ndi chuma chakuthupi. Kwenikweni, mkupita kwanthaŵi anasauka kufikira pakukhala m’phanga ndi ana ake aakaziwo. (Genesis 19:30-38) Chimene chidawoneka kukhala chabwino kwa iye chinadzakhala chosiyana kotheratu. Ngakhale kuti mwachiwonekere anali atachita zolakwa zazikulu, pambuyo pake anadzatchedwa “Loti wolungamayo.” (2 Petro 2:7, 8) Ndipo ndithudi Yehova Mulungu sanayenera kupatsidwa mlandu wa zolakwa za Loti.
‘Zolakwa—Angazidziŵe Ndani?’
5. Kodi Davide anamva bwanji ponena za zolakwa ndi kudzikuza?
5 Pokhala opanda ungwiro ndi ochimwa, tonsefe timalakwa. (Aroma 5:12; Yakobo 3:2) Mofanana ndi Loti, tinganyengedwe ndi mawonekedwe akunja ndi kulingalira molakwa. Chifukwa chake, wamasalmo Davide anachonderera kuti: ‘Zolakwa angazidziŵe ndani? Mundimasule kwa zolakwa zobisika. Ndiponso muletse kapolo wanu pazodzitama; zisachite ufumu pa ine: pamenepo ndidzakhala wangwiro, ndi wosachimwa cholakwa chachikulu.’ (Salmo 19:12, 13) Davide anadziŵa kuti angakhale anachita machimo amene sanawazindikire. Motero, anapempha kukhululukidwa machimo amene angakhale obisika kwa iye. Pamene anachita cholakwa chachikulu chifukwa chakuti thupi lake linamkakamiza kuyenda m’njira yolakwa, anakhumba kwambiri chithandizo cha Yehova. Anafuna kuti Mulungu amletse machitidwe akudzikuza. Davide sanafune kuti kudzitamandira kukhale mkhalidwe waukulu wa kaimidwe kake kamaganizo. Mmalomwake, anakhumba kukhala wodzipereka kotheratu kwa Yehova Mulungu ndi mtima wonse.
6. Kodi ndichitonthozo chotani chimene chingapezedwe pa Salmo 103:10-14?
6 Monga atumiki odzipereka a Yehova amakono, nafenso tiri opanda ungwiro motero timalakwa. Mwachitsanzo, mofanana ndi Loti, tingasankhe malo okhala osayenera. Mwinamwake tingalekerere mwaŵi wakufutukula utumiki wathu wopatulika kwa Mulungu. Ngakhale kuti Yehova amawona zolakwa zotero, amadziŵa amene ali ndi mtima wokhoterera pachilungamo. Ngakhale ngati tichita cholakwa chachikulu koma tilapa, Yehova amapereka chikhululukiro ndi chithandizo napitiriza kutiwona monga anthu owopa Mulungu. “Sanatichitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu,” anatero Davide. “Pakuti monga m’mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, Motero chifundo chake chikulira iwo akumuwopa iye. Monga kummaŵa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu. Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuwopa iye. Popeza adziŵa mapangidwe athu; Akumbukira kuti ife ndife fumbi.” (Salmo 103:10-14) Atate wathu wakumwamba wachifundo angathenso kutikhozetsa kuwongolera cholakwa chathu kapena angatipatse mwaŵi wina wakuwonjezera utumiki wathu wopatulika, kuchitamando chake.
Kulakwa kwa Kuimba Mlandu Mulungu
7. Kodi nchifukwa ninji timakumana ndi mavuto?
7 Pamene zinthu zilakwika, ndichibadwa chaumunthu kuimba mlandu munthu wina kapena chinthu china pachimene chachitika. Ena amaimba mlandu ngakhale Mulungu. Koma Yehova samadzetsa mavuto oterowo pa anthu. Iye amachita zinthu zabwino, osati zoipa. Eya, “iye amakwezera dzuŵa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama”! (Mateyu 5:45) Chifukwa chachikulu chimene timakhalira ndi mavuto nchakuti tikukhala m’dziko limene likuyendetsedwa pamalamulo adyera lokhala m’mphamvu ya Satana mdyerekezi.—1 Yohane 5:19.
8. Kodi Adamu anachitanji pamene zinthu sizinamuyendere bwino?
8 Kuimba mlandu Yehova Mulungu wa mavuto amene zolakwa zathu zimadzetsa paife kuli kopanda nzeru ndi kwangozi. Kuteroko kukhoza kutitayitsa ngakhale moyo wathu weniweniwo. Munthu woyamba, Adamu, anayenera kuthokoza Mulungu pazinthu zonse zabwino zimene analandira. Inde, Adamu anayenera kukhala woyamikira kwambiri chifukwa cha moyo weniweniwo ndi madalitso amene anasangalala nawo m’mudzi wonga paki, munda wa Edene. (Genesis 2:7-9) Kodi Adamu anachitanji pamene zinthu sizinayende bwino chifukwa chakusamvera kwake Yehova ndi kudya chipatso choletsedwacho? Adamu anadandaula kwa Mulungu kuti: “Mkazi amene munandipatsa ine kuti akhale ndi ine, ameneyo anandipatsa ine za mtengo, ndipo ndinadya.” (Genesis 2:15-17; 3:1-12) Ndithudi, sitiyenera kuimba mlandu Yehova, monga momwe Adamu anachitira.
9. (a) Ngati tikumana ndi zovuta chifukwa cha machitidwe athu opanda nzeru, kodi tingapeze kuti chitonthozo? (b) Malinga ndi Miyambo 19:3, kodi ena amachitanji pamene adzidzetsera okha mavuto?
9 Ngati tikumana ndi zovuta chifukwa cha machitidwe anthu opanda nzeru, tikhoza kutonthozedwa ndi chidziŵitso chakuti Yehova amazindikira bwinopo zofooka zathu kutiposa ndipo adzatiwonjola m’vuto lathu ngati tidzipereka kotheratu kwa iye. Tiyenera kuyamikira chithandizo chaumulungu chimene tilandira, ndi kusaimba mlandu konse Mulungu pamasoka ndi zovuta zimene timadzetsa pa ife eni. Mwambi wanzeru umati pamfundoyi: “Utsiru wa munthu ukhotetsa njira yake; Mtima wake udandaula pa Yehova.” (Miyambo 19:3) Matembenuzidwe ena amati: “Anthu ena amadziwononga okha ndi machitidwe awo opusa kenaka nkuimba mlandu AMBUYE.” (Today’s English Version) Matembenuzidwe enanso amati: “Umbuli wa munthu umaipitsa mikhalidwe yake ndipo amakwiyira Yehova.”—Byington.
10. Kodi ndimotani mmene kupusa kwa Adamu ‘kunawonongera njira yake’?
10 Mogwirizana ndi lingaliro la mwambi umenewu, Adamu anachita mwadyera ndipo kuganiza kwake kopusako ‘kunaluluza njira yake.’ Mtima wake unafulatira Yehova Mulungu, ndipo anatenga njira yakeyake yadyera, yodzigangira. Eya, Adamu anakhala munthu wosayamikira konse kotero kuti anaimba mlandu Mlengi wake ndipo motero anadzikhalitsa mdani kwa Wam’mwambamwamba! Tchimo la Adamu linawonongetsa moyo wake ndi wa banja lake. Muli chenjezo lotani nanga m’zimenezi! Awo okhoterera pakuimba mlandu Yehova chifukwa cha mikhalidwe yoipa angachite bwino kudzifunsa kuti: Kodi ndimapereka thamo kwa Mulungu pazinthu zabwino zimene ndimasangalala nazo? Kodi ndiri woyamikira kuti ndiri ndi moyo monga mmodzi wa zolengedwa zake? Kodi kungakhale kwakuti zolakwa za ine mwini ndizo zandibweretsera mavuto? Kodi ndiri woyenerera chiyanjo cha Yehova kapena chithandizo chifukwa cha kulondola chitsogozo chake, monga momwe chaperekedwera m’Mawu ake ouziridwa, Baibulo?
Upandu Ngakhale kwa Atumiki a Mulungu
11. Ponena za Mulungu, kodi atsogoleri achipembedzo Achiyuda a m’zaka za zana loyamba anali ndi liwongo la chiyani?
11 Atsogoleri achipembedzo Achiyuda a m’zaka za zana loyamba C.E. anadzinenera kukhala otumikira Mulungu koma ananyalanyaza mawu ake a chowonadi ndi kudalira pa luntha lawo. (Mateyu 15:8, 9) Chifukwa chakuti Yesu Kristu anavumbula malingaliro awo olakwa, anamupha. Pambuyo pake, anasonyeza udani waukulu kwa ophunzira ake. (Machitidwe 7:54-60) Njira ya amunawo inali yopotoka kwambiri kotero kuti anakwiyira ngakhale Yehova iye mwiniyo.—Yerekezerani ndi Machitidwe 5:34, 38, 39.
12. Kodi nchitsanzo chotani chimene chimasonyeza kuti ngakhale anthu ena ogwirizana ndi mpingo Wachikristu amayesa kuimba Yehova mlandu wa mavuto awo?
12 Ngakhale anthu ena mumpingo Wachikristu akhala ndi maganizo aupandu oterowo, akumayesa kupatsa mlandu Mulungu wa mavuto amene amakumana nawo. Mwachitsanzo, akulu oikidwa a mpingo wina anakuwona kukhala kofunika kupereka uphungu Wamalemba wachikondi koma wamphamvu kwa mkazi wachichepere wokwatiwa kumchenjeza za mayanjano ake ndi mwamuna wakudziko. Pakukambitsirana kwina, iye anaimba mlandu Mulungu kuti sanamthandize kulaka chiyeso chimene mayanjano ake ndi mwamunayo anadzetsa pa iye. Iye ananenadi kuti anakwiyira Mulungu kwambiri! Kukambitsirana Kwamalemba ndi zoyesayesa zobwerezabwereza zakumthandiza sizinaphule kanthu, ndipo njira yamkhalidwe woipa pambuyo pake inamchotsetsa mumpingo Wachikristu.
13. Kodi nkupeŵeranji mzimu wakudandaula?
13 Mzimu wakudandaula ukhoza kuchititsa munthu kuimba mlandu Yehova. “Anthu osapembedza” amene anakwaŵira mtseri kuloŵa mumpingo wa m’zaka za zana loyamba anali ndi mzimu woipa woterowo, ndipo unaphatikizapo mitundu ina ya kulingalira koipitsidwa mwauzimu. Monga momwe wophunzira Yuda ananenera, amuna ameneŵa anali “akusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa, nakaniza Mfumu wayekha, ndi Ambuye wathu, Yesu Kristu.” Yuda anatinso: “Amenewo ndiwo odandaula, oderera, akuyenda monga mwa zilakolako zawo.” (Yuda 3, 4, 16) Atumiki okhulupirika a Yehova mwanzeru adzapemphera kuti akhale nawo mzimu wakuyamikira, osati kaimidwe kamaganizo kodandaula kamene pomalizira pake kangawakwiyitse kufikira pakutaya chikhulupiriro mwa Mulungu ndi kuwononga unansi wawo ndi iye.
14. Kodi ndimotani mmene munthu angachitire ngati akhumudwitsidwa ndi Mkristu mnzake, koma kodi nchifukwa ninji imeneyi sindiyo njira yoyenera?
14 Mungalingalire kuti zimenezi sizingakuchitikireni. Komabe, zinthu zimene zimalakwika chifukwa cha zolakwa zathu kapena za ena zingatichititse kuimba mlandu Mulungu. Mwachitsanzo, munthu angakhumudwe ndi zimene wokhulupirira mnzake anganene kapena kuchita. Ndiyeno wokhumudwayo—mwinamwake amene watumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri—anganene kuti: ‘Malinga ngati munthu uja ali mumpingowu, sindidzafika pamisonkhano.’ Munthuyo angakwiye kwambiri kotero kuti angati mumtima mwake: ‘Ngati zinthu zotere zipitirizabe, sindifuna kukhala chiwalo cha mpingowu.’ Koma kodi Mkristu ayenera kukhala ndi kaimidwe ka maganizo koteroko? Ngati walakwiridwa ndi munthu wina wopanda ungwiro, kodi nkukwiyiranji ndi mpingo wonse wa anthu ovomerezedwa ndi Mulungu ndi amene akumtumikira mokhulupirika? Kodi nchifukwa ninji munthu aliyense amene wadzipatulira kwa Yehova angaleke kuchita chifuniro chaumulungu ndipo mwakutero akumakwiyiranso Mulungu? Kodi nkwanzeru yanji kulola munthu kapena zochitika kuwononga unansi wabwino wa munthuwe ndi Yehova? Ndithudi, kukakhala kupanda nzeru ndi kuchimwa kuleka kulambira Yehova Mulungu pachifukwa chirichonse.—Yakobo 4:17.
15, 16. Kodi Diotrefe anali ndi liwongo lachiyani, koma kodi Gayo anadzisungira motani?
15 Tayerekezerani kuti munali mumpingo umodzimodzi ndi Mkristu wachikondi Gayo. Iye anali ‘kuchita ntchito yokhulupirika’ m’kukhala wochereza kwa olambira anzake odzacheza—ndipotu alendo amene sankawadziŵa nkomwe! Koma mwachiwonekere, mumpingo umodzimodziwo munali mwamuna wonyada Diotrefe. Iye sanalandire chirichonse ndi ulemu chochokera kwa Yohane, mmodzi wa atumwi a Yesu Kristu. Kwenikweni, Diotrefe anali kunena mawu opanda pake ponena za Yohane. Mtumwiyo anati: “Izi sizimkwanira [Diotrefe], salandira abale iye yekha, ndipo ofuna kuwalandira awaletsa, nawataya kunja powatulutsa mumpingo.”—3 Yohane 1, 5-10.
16 Pamene Yohane akafika kumpingo, anafuna kudzakumbutsa zimene Diotrefe anali kuchita. Panthaŵiyi, kodi Gayo ndi Akristu ena ochereza alendo mumpingowo anachita motani? Palibe umboni Wamalemba wosonyeza kuti aliyense wa iwo anati: ‘Malinga ngati Diotrefe ali mumpingowu, sindifuna kukhala chiwalo chake. Simudzandiwonanso pamisonkhano.’ Mosakaikira, Gayo ndi ena ofanana naye anaima nji. Sanalole chirichonse kuwaleketsa kuchita chifuniro cha Mulungu, ndipo kwenikweni iwo sanakwiyire Yehova. Sanatero konse, ndipo sanagonjere kumisampha yamachenjera ya Satana Mdyerekezi, amene akanasangalala ngati iwo akanaleka kukhulupirika kwawo kwa Yehova ndi kumuimba mlandu.—Aefeso 6:10-18.
Musamkwiyire Konse Yehova!
17. Kodi tiyenera kuchita motani ngati munthu atilakwira kapena mkhalidwe sutikondweretsa?
17 Ngakhale ngati munthu wina mumpingo akhumudwitsa mtumiki wa Mulungu kapena ngati mkhalidwe sumsangalatsa, amene amakwiyayo akakhala akuwononga njira ya iye mwini ngati aleka kuyanjana ndi anthu a Yehova. Munthu woteroyo sakakhala akugwiritsira ntchito moyenera mphamvu yake yakulingalira. (Ahebri 5:14) Chotero khalani otsimikiza mtima kuyang’anizana ndi zovuta zonse monga wosunga umphumphu. Sungani kukhulupirika kwanu kwa Yehova Mulungu, Yesu Kristu, ndi mpingo Wachikristu. (Ahebri 10:24, 25) Chowonadi chimene chimatsogolera ku moyo wamuyaya sichingapezedwe kwina kulikonse.
18. Ngakhale kuti sinthaŵi zonse pamene timamvetsetsa zochita zaumulungu, kodi tingakhale otsimikizira za chiyani ponena za Yehova Mulungu?
18 Kumbukiraninso, Yehova samayesa konse aliyense ndi zinthu zoipa. (Yakobo 1:13) Mulungu, amene ndiye chikondi chenichenicho, amachita zabwino, makamaka kwa awo omkonda. (1 Yohane 4:8) Ngakhale kuti sinthaŵi zonse pamene timamvetsetsa zochita za Mulungu, tingakhale achidaliro kuti Yehova Mulungu sadzalephera konse kuchita zimene ziri zabwino koposa kwa atumiki ake. Monga momwe Petro ananenera kuti: “Potero dzichepetseni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu, kuti panthaŵi yake akakukwezeni; ndi kutaya pa iye nkhaŵa yanu yonse, pakuti iye asamalira inu.” (1 Petro 5:6, 7) Inde, Yehova amasamaladi anthu ake.—Salmo 94:14.
19, 20. Kodi tiyenera kuchita motani, ngakhale kuti nthaŵi zina ziyeso zathu zimatipsinja maganizo?
19 Chotero, musalole chirichonse kapena aliyense kukupunthwitsani. Monga momwe wamasalmo ananenera bwino lomwe kuti, “akukonda chilamulo chanu [Yehova Mulungu] ali nawo mtendere wambiri; Ndipo alibe chokhumudwitsa.” (Salmo 119:165) Tonsefe timakumana ndi ziyeso, ndipo nthaŵi zina zimenezo zingatipsinje maganizo mwanjira ina ndi kutiswa mtima. Koma musalole mkwiyo kukula mumtima mwanu, makamaka kukwiyira Yehova. (Miyambo 4:23) Mwachithandizo chake ndi maziko a Malemba, thetsani mavutowo amene mungathe ndipo pirirani amene apitirizabe.—Mateyu 18:15-17; Aefeso 4:26, 27.
20 Musalole konse mkwiyo wanu kukupangitsani kuchita zinthu mwanjira yopusa ndipo motero mukumaipitsa njira yanu. Lankhulani ndi kuchita mwanjira imene idzakondweretsa mtima wa Mulungu. (Miyambo 27:11) Itanirani pa Yehova mwapemphero la mtima wonse, mukumadziŵa kuti iye amakusamalanidi monga mmodzi wa atumiki ake ndipo adzakupatsani chidziŵitso chofunikira kuti mukhalebe panjira yanu ya ku moyo ndi anthu ake. (Miyambo 3:5, 6) Koposa zonse, musakwiyire Mulungu. Pamene zinthu zilakwika, nthaŵi zonse kumbukirani kuti Yehova sindiye ali ndi mlandu.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi Loti analakwa chiyani, koma kodi ndimotani mmene Mulungu anamuwonera?
◻ Kodi Davide anamva motani pazolakwa ndi kudzikuza?
◻ Pamene zinthu siziyenda bwino, kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuimba mlandu Mulungu?
◻ Kodi nchiyani chimene chidzatithandiza kupeŵa kukwiyira Yehova?
[Chithunzi patsamba 15]
Pamene anali kulekana ndi Abrahamu, Loti anasankha malo okhala osayenera