Chisangalalo Chimene Kutumikira Yehova Kwandibweretsera
MONGA MOMWE YASIMBIDWIRA NDI GEORGE BRUMLEY
Ndinangotha kumene kuphunzitsa zakukonza mawailesi kwa kalasi ya achichepere ophunzira zaupolisi a Wolamulira Haile Selassie pamene mmodzi wa amenewa anandiuza mtseri kuti iye anadziŵa kuti ndinali mmishonale wa Mboni za Yehova. “Kodi mungaphunzire nane Baibulo?” iye anapempha motenthedwa maganizo.
POPEZA ntchito yathu panthaŵiyo inali yoletsedwa mu Ethiopia, ndikanachotsedwa m’dzikolo, monga momwe Mboni zina zinachitidwira, ngati olamulira akanamva za ine. Sindinadziŵe ngati wophunzirayo anali wowona mtima kapena ngati anali mzondi wa boma wotumidwa kudzandikola. Monga mutu wabanja wokhala ndi ana achichepere atatu akulera, lingaliro lakutaikiridwa ndi ntchito yanga ndi kukakamizidwa kuchoka m’dzikolo ndi kusiya mabwenzi amene ndinawakonda linandichititsa mantha.
‘Koma,’ inu mungafunse, ‘kodi munthu wa ku Amereka wokhala ndi banja lakulichirikiza anakonda bwanji kudzakhala kumpoto chakumwera kwa Afirika, kutali ndi kwawo ndi achibale?’ Tandilolani ndifotokoze.
Kukulira mu United States
M’ma 1920, pamene ndinali pa sukulu ya pulaimale, atate analembetsa sabuskripishoni ya magazini a Nsanja ya Olonda ndi kugula mabuku a Studies in the Scriptures. Atate anakonda kwambiri kuŵerenga ndipo anaŵerenga mabukuŵa mwachidwi. Iwo anali munthu woseketsa ndi wanjerengo, monga momwe anachitira njerengo ndi alendo amene anawaitana pa Masande. Atate anali ndi bukhu lalikulu lokongola lachikuto cha chikopa lolembedwa zilembo za golidi zakuti “Bukhu Lopatulika” patsogolo ndi pamsana pa bukhulo. Iwo ankayamba kukambitsirana mwakunena kuti, “Eya lero nla Sande. Kodi mungatiŵerengere mavesi angapo?”
Nthaŵi zonse mlendo ankavomereza, koma pamene anatsegula bukhulo masambawo anali osalembapo kanthu! Ndithudi, munthuyo anali kudabwa. Pamenepo atate ankanena kuti ‘alaliki sadziŵa chirichonse ponena za Baibulo,’ ndiyeno ankatenga kope ndi kuŵerenga Genesis 2:7. Pamenepo, polongosola kulengedwa kwa munthu woyamba, Baibulo limati: “Munthuyo nakhala wamoyo.”—Genesis 2:7, King James Version.
Atate ankafotokoza kuti munthu alibe moyo koma kuti ndiye moyowo, kuti mphotho yauchimo ndiyo imfa, ndi kuti pamene munthu afa, iye ngwakufadi, wosazindikira kanthu kalikonse. (Mlaliki 9:5, 10; Ezekieli 18:4; Aroma 6:23) Ngakhale pamene ndinali wosakhoza kuŵerenga bwino, ndinali nditaloŵeza pamtima Genesis 2:7. Zimenezi ndizo zikumbukiro zoyambirira zimene ndiri nazo zachisangalalo chenicheni chakudziŵa chowonadi cha Baibulo ndi kuchigaŵana ndi ena.
Popeza kuti panthaŵiyo tinali kulandira Nsanja ya Olonda pa nyumba pathu, banja lonse linayamba kusangalalira chakudya chauzimu chimenechi. Agogo anga kwa amayi anali kukhala nafe, ndipo anadzakhala wofalitsa woyamba wa mbiri yabwino m’banja lathu. Kunalibe mpingo ku Carbondale, Illinois, kumene tinali kukhala, koma tinali kuchita misonkhano ya mwamwaŵi. Mayi anali kutengera ana asanufe kumbali ina ya tawuniyo kumene akazi ena okalamba anachititsa phunziro la Nsanja ya Olonda. Tinayambanso kukhala ndi phande mu uminisitala wakumunda.
Kuchokera ku Ntchito Yokonza Mawailesi kumka Kundende
Ndinakwatira mu 1937 pamene ndinali wa zaka 17 zokha. Ndinayesa kupeza zotithandiza mwakukonza mawailesi ndi kuphunzitsa luso limeneli. Pambuyo pakubadwa kwa ana aŵiri, Peggy ndi Hank, ukwati wanga unatha. Chisudzulocho chinali kaamba ka cholakwa changa; sindinali kukhala ndi moyo monga Mkristu. Chenicheni chakuti sindinalere ana anga okulirapo aŵiriwo chakhala chondiŵaŵitsa mtima moyo wanga wonse.
Nkhondo Yadziko II inafika ndipo inandipeza ndikulingalira zinthu zambiri. Magulu a asilikali ankhondo anandilonjeza mwaŵi wa ntchito ya ukaputeni wankhondo ndi kuphunzitsa wailesi kwa olembedwa usilikali, koma nkhaŵa yanga ya zimene Yehova analingalira ponena za nkhondo inandichititsa kuyamba kupemphera tsiku lirilonse. Sabuskripishoni yanga ya Nsanja ya Olonda inali itatha, ndipo Lucille Haworth analandira chidziŵitso chakuti ikutha ndipo anandichezera. Perry Haworth, amene anali atate a Lucille, ndipo ambiri a banja lake lalikulu anali Mboni kuyambira m’ma 1930. Lucille ndi ine tinakondana, ndipo tinakwatirana mu December 1943.
Mu 1944, ndinabatizidwa ndipo ndinagwirizana ndi mkazi wanga mu uminisitala wanthaŵi yonse monga mpainiya. Posapita nthaŵi, ndinaitanidwa nditalembedwa kale mu utumiki wankhondo koma ndinakana. Monga chotulukapo, ndinalandira chiweruzo chakukhala m’ndende yokhaulitsira ya boma kwa zaka zitatu mu El Reno, Oklahoma. Chinali chisangalalo kuvutikira Yehova. M’mawa uliwonse pamene ndinadzuka ndikuzindikira kumene ndinali ndi chifukwa chake, ndinamva chikhutiro chachikulu ndipo ndinayamika Yehova. Pambuyo pa nkhondo awo a ife amene anali a zaka zoposa 25 zakubadwa anayamba kusiyidwa osalondedwa. Ndinamasulidwa m’February 1946.
Uminisitala Wanthaŵi Yonse
Pamene ndinagwirizananso ndi Lucille, anali kuchita upainiya mu tawuni yaing’ono ya Wagoner, Oklahoma. Tinalibe galimoto, chotero tinayenda pansi kulikonse, tikumayenda pansi tawuni yonseyo. Pambuyo pake tinasamukira ku Wewoka, Oklahoma. Posapita nthaŵi, ndinapeza ntchito pa nyumba ya wailesi yapafupi ndi kuyamba kugwira ntchito youlutsa. Kugwira ntchito maola asanu ndi limodzi pa tsiku ndi kufitsa maola aupainiya sikunali kosavuta, koma tinakondwera ndi mwaŵi umene tinali nawo wakutumikira Yehova. Tinakhoza kugula galimoto lakale panthaŵi imene tinkakonzekera msonkhano waukulu ku Los Angeles mu 1947. Kumeneko tinayamba kulingalira za kufunsira mwaŵi wopita ku Sukulu ya Baibulo ya Gileadi ya Watchtower kukaphunzira umishonale.
Tinazindikira kuti limeneli likakhala sitepi lalikulu, ndipo sitinafune kufulumira kupanga chosankha chakuchoka ku United States. Ndinali kuderabe nkhaŵa za kutaikiridwa ndi ana anga, chotero kachiŵirinso ndinayesa kuti ndiwapeze mwalamulo. Chifukwa cha njira yanga yamoyo yakaleyo ndi mbiri yakukhala nditaloŵapo m’ndende, kunali kosaphula kanthu. Chifukwa chake tinasankha kuyesa kukhala amishonale. Tinaitanidwa ku kalasi la chi 12 la Gileadi.
Tinamaliza maphunziro ku sukuluyo mu 1949, koma poyamba tinagaŵiridwa kuchezetsa mipingo mu Tennessee. Pambuyo pa zaka zitatu m’ntchito yoyendayenda mu United States, tinalandira kalata yochokera ku ofesi ya pulezidenti wa Watch Tower Society akumapempha ngati tikakonda kukaphunzitsa pasukulu mu Ethiopia pambali pa ntchito yolalikira. Chimodzi cha zofunika za bomalo chinali chakuti amishonale aphunzitse pasukulu. Tinalola, ndipo m’chilimwe cha 1952, tinanyamuka kupita ku Ethiopia.
Pamene tinafika ku Ethiopia, tinaphunzitsa makalasi a sukulu ya pulaimale m’mawa ndi kuchititsa makalasi aulere a Baibulo masana. Posapita nthaŵi, ambiri anayamba kufika pa maphunziro a Baibulo amene tinali kuchititsa omwe kaŵirikaŵiri tinali kuphunzitsa Baibulo kwa maola atatu kapena anayi tsiku lirilonse. Ophunzira ena anali apolisi; ena anali aphunzitsi kapena adikoni pamasukulu amishoni ndi masukulu a Orthodox mu Ethiopia. Nthaŵi zina m’kalasi lophunzira Baibulo lirilonse munali kupezeka anthu 20 kapena kuposapo! Ambiri a ophunzirawo anasiya chipembedzo chonyenga nayamba kutumikira Yehova. Tinali osangalala kwambiri. Kachiŵirinso, pamene ndinadzuka m’mamawa uliwonse, ndinapereka zithokozo kwa Yehova.
Ukholo ndi Kulalikira Mkati mwa Chiletso
Mu 1954 tinazindikira kuti tinali kudzakhala makolo, chotero tinafunikira kupanga chosankha kuti kaya tikabwerera ku United States kapena kukhalabe m’Ethiopia. Ndithudi, kukhalabe m’menemo, kukadalira pa kupeza kwanga ntchito yakuthupi. Ndinapeza ntchito monga injiniya panyumba ya mphepo, kuyang’anira nyumba ya wailesi ya Wolamulira Haile Selassie. Chotero tinakhalabe.
Pa September 8, 1954, mwana wathu wamkazi Judith anabadwa. Ndinaganiza kuti ntchito yanga inali yotetezereka chifukwa chakugwirira ntchito Wolamulirayo, koma pambuyo pa zaka ziŵiri ndinachotsedwa ntchito imeneyo. Komabe, pasanapite mwezi umodzi, ndinalembedwa ntchito ndi Dipatimenti ya Apolisi—ndi malipiro okwererapo ndithu—yophunzitsa kalasi la anyamata kukonza mawailesi otchedwa two-way radio. Mkati mwa zaka zitatu zotsatira, ana athu amuna Philip ndi Leslie anabadwa.
Panthaŵiyi, ufulu wathu wakukhala ndi phande m’ntchito yolalikira unali kusintha. Tchalitchi cha Orthodox cha ku Ethiopia chinali chitanyengerera boma kuti lithamangitse amishonale onse a Mboni za Yehova. Molangizidwa ndi Sosaite, ndinasintha chiphaso changa cha ntchito yaumishonale kukhala cha ntchito wamba. Ntchito yathu yaumishonale inaletsedwa, ndipo tinafunikira kukhala aluso ndi ochenjera. Misonkhano yonse yampingo inapitirizabe, koma tinakumana m’timagulu taphunziro tating’ono.
Apolisi anafufuza nyumba zosiyanasiyana za okaikiridwa kukhala Mboni. Komabe, mosadziŵa iwo, kaputeni wa polisi amene anali mlambiri wa Yehova ankatiuza nthaŵi zonse pamene ziukiro zinalinganizidwa. Chifukwa chake, palibe mabukhu amene analandidwa m’zaka zimenezo. Tinali kuchita phunziro lathu la Nsanja ya Olonda pa Sande mwakupita ku makantini akumphepete kwa tawuni kumene kunali magome ochitira pikiniki odyera panja.
Munali mkati mwa nthaŵiyi, pamene ndinali kuphunzitsa wailesi kwa ophunzira achichepere apolisi, pamene wophunzira yemwe ndatchula kuchiyambi kwa nkhani ino anandipempha phunziro la Baibulo. Ndinalingalira kuti anali wowona mtima, chotero tinayamba. Pambuyo pa maphunziro aŵiri okha, wophunzira wachiŵiri anadza naye, ndiyeno wachitatu. Ndinawachenjeza kusauza aliyense kuti anali kuphunzira nane, ndipo sanatero konse.
Mu 1958 Msonkhano wa Mitundu Yonse wa Chifuniro cha Mulungu unachitidwa m’Yankee Stadium ndi Polo Grounds m’New York. Panthaŵiyi, Peggy ndi Hank, limodzi ndi ziŵalo zina za banja langa lalikululo anali atakhala Mboni zokangalika. Ndinali wokondwera chotani nanga kukhala wokhoza kufikapo! Sindinangosangalala ndi kugwirizananso ndi ana anga okulirapo aŵiriwo ndi ziŵalo zina za banja komanso ndinachita chidwi kuwona khamu lalikulu la anthu oposa nusu ya miliyoni atasonkhana pa tsiku lomaliza la msonkhano waukuluwo!
Chaka chotsatira pulezidenti wa Sosaite, Nathan H. Knorr, anadzatichezera ku Ethiopia. Iye anapereka malingaliro abwino kwambiri ochitira ntchito m’mikhalidwe yoletsedwa ndipo analinso wokondwera ndi banja lathu ndi mmene tinali kuchitira mwauzimu. Ndinafotokoza kuti tinali kuphunzitsa ana kupemphera. Ndinapempha ngati akakonda kumva Judith akupemphera. Iye analola, pambuyo pake anauza Judith kuti: “Wachitadi bwino kwambiri, Judith.” Ndiyeno panthaŵi ya chakudya ndinapempha Mbale Knorr kutiperekera pemphero, ndipo pamene anamaliza, Judith anati: “Mwachitadi bwino kwambiri, Mbale Knorr!”
Kulera Ana Athu mu United States
Kontrakiti yanga ndi Dipatimenti ya Polisi inatha mu 1959. Tinafuna kukhalabe, koma boma silinavomereze kontrakiti yatsopano iriyonse. Chotero tikapita kuti? Ndinayesa kuti ndipite kumaiko ena kumene kusoŵa kunali kwakukulu kaamba ka abale koma zinalephereka. Mwachisoni pang’ono, tinabwerera ku United States. Titafika kumeneko, tinasangalala kugwirizananso ndi banja; ndipo ana anga asanu onsewo anazoloŵerana ndipo anakondana pamenepo. Akhala ogwirizana chiyambire panthaŵiyo.
Tinakhazikika mu Wichita, Kansas, kumene ndinapeza ntchito monga injiniya panyumba ya mphepo ndi kuulutsa nyimbo. Lucille tsopano anali kuchita ntchito za panyumba, ndipo ana anapita ku sukulu yoyandikana ndi nyumba yathu. Ndinachititsa phunziro la Nsanja ya Olonda la banja madzulo aliwonse a Lolemba, nthaŵi zonse ndikumalichititsa kukhala lamoyo ndi lokondweretsa. Nthaŵi zonse tinafufuza kuwona ngati kunali mavuto kusukulu.
Pamene mwana aliyense analembetsa mu Sukulu Yautumiki Wateokratiki, kuphunzira kumeneku kunawathandiza pamaphunziro awo akusukulu. Tinawaphunzitsa kuyambira paubwana mu utumiki wakumunda. Anaphunzira kugaŵira mabukhu ofotokoza Baibulo pamakomo, ndipo anapita nafe ku maphunziro a Baibulo apanyumba.
Tinayesanso kuphunzitsa anawo zinthu zazikulu zokhudza moyo, tikumafotokoza kuti aliyense wa iwo sakakhoza nthaŵi zonse kukhala ndi zimene wina anali nazo. Mwachitsanzo, sinthaŵi zonse kuti mphatso imodzi ikhoza kukwanira onse. “Ngati mbale wanu kapena mlongo alandira chidole,” tinali kuwauza motero, “ndipo iwe ulibe, kodi kuli koyenera kudandaula?” Ndithudi, panthaŵi zina, ana enawo analandira kanthu kena, chotero palibe amene ananyalanyazidwa. Nthaŵi zonse tinawakonda iwo onse, mosayanja mmodzi kuposa ena aŵiriwo.
Nthaŵi zina ana ena anali kuloledwa kuchita zinthu zimene ana athu sanaloledwe kuchita. Kaŵirikaŵiri ndinamva kuti, “ujeni amaloledwa kuchita ichi, kodi ife tilekeranji?” Ndinayesa kufotokoza, koma nthaŵi zina yankho linali kungokhala lakuti, “Inu simuli m’banja limenelo; muli m’banja la a Brumley. Tiri ndi malamulo osiyana.”
Kutumikira m’Peru
Kuyambira pamene ndinabwera kuchokera ku Ethiopia, Lucille ndi ine tinali kulakalaka kukhala ndi phande m’ntchito yaumishonale kachiŵirinso. Potsirizira pake, mu 1972, mwaŵi unadza wopita ku Peru, ku South America. Panalibe malo abwino kwambiri ofanana nawo olererako ana athu mkati mwa zaka zawo za 13-19. Mayanjano amene anasangalala nawo ndi amishonale, apainiya apadera, ndi ena amene anadzatumikira ku Peru anawathandiza kudziwonera okha chikondwerero chimene chimakhala ndi awo amene amathanga afuna mowona mtima zabwino za Ufumu. Philip anatcha mayanjano akewo kukhala chitsenderezo cha atsamwali chabwino.
Pambuyo pakanthaŵi mabwenzi akale aku Kansas anamva chipambano chimene tinali nacho mu uminisitala wa Ufumu, ndipo anadzagwirizana nafe m’Peru. Ndinalinganiza nyumba yathu monga nyumba ya amishonale. Aliyense anali ndi ntchito zapanyumba zogaŵiridwa kotero kuti onse akakhala ndi nthaŵi yakusangalala ndi uminisitala wakumunda. Tinali kukambitsirana lemba la Baibulo pa gome m’mamawa uliwonse. Inali nthaŵi yachimwemwe kwambiri kwa tonsefe. Kachiŵirinso, pamene ndinadzuka m’mamawa uliwonse ndi kuzindikira kumene ndinali ndi chifukwa chake, ndinapereka mwakachetechete zithokozo zochokera pansi pa mtima kwa Yehova.
M’kupita kwanthaŵi Judith anakwatiwa ndipo anabwerera ku States chifukwa mwamunayo sanapeze chiphaso chakuti akhalebe. Pambuyo pa zaka zitatu zautumiki waupaniya wapadera, Philip analemba kalata yofunsira mwaŵi wa utumiki wa pa Beteli ku Brooklyn, New York, ndipo anavomerezedwa. Potsirizira pake, Leslie nayenso anabwerera ku United States. Iwo anachoka mwachisoni ndipo, kaŵirikaŵiri atiuza kuti kupita nawo ku Peru kunali chinthu chabwino koposa chimene tinawachitira.
Pamene mkhalidwe wa chuma m’Peru unaipirapo, tinazindikira kuti nafenso tikafunikira kuchoka. Titabwerera ku Wichita mu 1978, tinapeza kagulu ka Mboni zolankhula Chispanya. Zinatipempha kukhala nazo ndi kuzithandiza, ndipo tinasangalala kutero. Mpingo unapangidwa, ndipo mwamsanga unafikira kukhala wokondeka kwa ife mofanana ndi imene tinatumikira papitapo.
Ecuador Atikodola
Mosasamala kanthu za nthenda ya sitiroko imene inandipuwalitsa pang’ono, ndinayembekezera molakalaka kuti Lucille ndi ine tikatumikire m’dziko lina. Mu 1984 woyang’anira woyendayenda anatiuza za chiwonjezeko mu Ecuador ndi kupereŵera kwa akulu Achikristu kumeneko. Ndinanena kuti sindikatha kuchita zambiri muutumiki wakumunda chifukwa chakupunduka kwanga, koma iye anandiuza motsimikiza kuti ngakhale wa zaka 65 zakubadwa wopunduka pang’ono akhoza kukhala mkulu wothandiza.
Atachoka sitinagone usiku wonsewo, tikumalankhula zakuthekera kwa kupita ku Ecuador. Lucille anali ndi chikhumbo chachikulu cha kupita chofanana ndi changa. Chotero tinatsatsa kabizinesi kathu kakupha tizilombo ndipo tinakagulitsa pambuyo pa masabata aŵiri. Tinagulitsa nyumba yathu m’masiku khumi okha. Chotero, m’masiku athu aukalamba, tinapezanso chisangalalo chathu chachikulu koposa, utumiki waumishonale m’dziko lachilendo.
Tinakakhala ku Quito, ndipo utumiki wakumunda unali wokondweretsa, tsiku lirilonse tikumakhala ndi chokumana nacho chatsopano kapena chochitika. Komano, mu 1987 ndinapimidwa ndi kupezedwa ndi kansa m’thumbo; ndinafunikira opaleshoni yamwamsanga. Tinabwerera ku Wichita kukachitidwa opaleshoni, imene inachitika bwino. Tinabwereranso ku Quito koma pambuyo pazaka ziŵiri zokha pamene ndinapezekanso ndi kansa, tinabwerera kukakhaliratu ku States. Tinakakhala ku North Carolina, kumene tsopano tiri.
Moyo Wolemera, Wofupa
Thanzi langa mtsogolomu nlosatsimikizirika. Ndinatopangidwa opaleshoni yoboola pamimba kutulutsa thumbo mu 1989. Ngakhale nditero, ndikutumikirabe monga mkulu ndipo ndikuchititsa maphunziro angapo a Baibulo kwa anthu amene amafika panyumba panga. M’kupita kwa zaka, tathandiza mazana a anthu mwa kufesa, kuthirira, kapena kulimirira mbewu za chowonadi. Chimenechi ndicho chisangalalo chimene sichimafwifwa konse, mosasamala kanthu kuti chabwerezedwa nthaŵi zingati.
Kuwonjezera pa izi, ndakhala ndi chisangalalo chachikulu kuwona ana anga onse akutumikira Yehova. Peggy watsagana ndi mwamuna wake Paul Moske kwa zaka 30, m’ntchito yoyendayenda mu United States. Philip ndi mkazi wake, Elizabeth, limodzi ndi Judith, anapitiriza muutumiki wapadera mu New York. Hank ndi Leslie ndi anzawo amuukwati ndi Mboni zokangalika, ndipo azichimwene anga ndi azichemwali pamodzi ndi mabanja awo, kuphatikizapo achibale ena oposa 80, onsewo akutumikira Yehova. Ndipo Lucille wakhala mkazi Wachikristu wachitsanzo chabwino kwapafupifupi zaka 50 zaukwati. M’zaka zaposachedwapa wachita mosaŵiringula ntchito zambiri zosakondweretsa kundithandiza kuti ndisamalire thupi langa lonyonyotsokali.
Ndithudi, moyo wanga wakhala wachisangalalo. Wakhala wachimwemwe kwambiri kuposa zimene mawu anganene. Kutumikira Yehova nkosangalatsa kwambiri kwakuti chiri chikhumbo changa chochokera pansi pa mtima kumlambira kosatha padziko lino lapansi. Ndimakumbukira nthaŵi zonse Salmo 59:16, limene limati: “Koma ine, ndidzaimbira mphamvu yanu; inde ndidzaimbitsa chifundo chanu m’mamawa: Pakuti inu mwakhala msanje wanga, ndi pothaŵirapo ine tsiku la nsautso yanga.”
[Chithunzi patsamba 23]
George Brumley ndi Wolamulira wa Ethiopia Haile Selassie
[Chithunzi patsamba 25]
George Brumley ndi mkazi wake, Lucille