Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 12/15 tsamba 8-13
  • Yehova, Wochita Zinthu Zodabwitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova, Wochita Zinthu Zodabwitsa
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Wozunzika koma Wokhulupirika
  • Kuzoloŵerana ndi Yehova
  • Ubwino wa Yehova
  • Ntchito Zosayerekezereka za Yehova
  • Ukulu wa Yehova
  • Kuyenda ndi Mtima Umodzi
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Yehova Amafunikira Chitamando Chosatha
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Yehova Ndiye Chitsanzo Chachikulu Pankhani Yosonyeza Ubwino
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Chikondi Chokhulupirika cha Yehova N’chachikulu
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 12/15 tsamba 8-13

Yehova, Wochita Zinthu Zodabwitsa

‘Inu ndinu wamkulu ndi wakuchita zodabwitsa; inu ndinu Mulungu, nokhanu.’​—SALMO 86:10.

1, 2. (a) Kodi zotulukira za anthu zayambukira motani dziko? (b) Kodi nkuti kumene tingapeze chiyembekezo cha zinthu zabwinopo?

ANTHU amakono angadzitamandire kuti zimene atulukira nzodabwitsa​—ziwiya za magetsi, njira zakulankhulana ndi anthu amene ali kutali, vidiyo, galimoto, ulendo wapandege, ndi luso lazopangapanga la makompyuta. Zimenezi zasanduliza dziko kukhala chitaganya chimodzi. Komatu nchitaganya chotani nanga! Mmalo mwa mtendere, kulemera, ndi kukhala ndi zochuluka kwa aliyense, anthu akanthidwa ndi nkhondo zambanda, upandu, uchigaŵenga, kuipitsidwa kwa mpweya, nthenda, ndi umphaŵi. Ndipo zida za nyukliya zofalikira padziko lonse, ngakhale kuti zachepetsedwa m’chiwerengero, zikakhozabe kuwononga mtundu wa anthu, Amalonda a imfa, amene amapanga zida zankhondo, akupitirizabe kuyendetsa mabizinesi aakulu padziko lapansi. Olemera akuwonjezera kulemerako, ndipo osauka akusauka mowonjezereka. Kodi pali munthu amene angapeze njira yothetsera zimenezi?

2 Inde! Pakuti pali Munthu wina amene akutsimikizira chilanditso, ‘wapamwamba kwambiri kuposa wapamwambayo,’ Yehova Mulungu. (Mlaliki 5:8) Iye anauzira kulembedwa kwa masalmo, amene amapereka chitonthozo chachikulu ndi uphungu wanzeru m’nthaŵi za nsautso. Pakati pawo pali Salmo 86, limene liri ndi mawu apamwamba achidule akuti: “Pemphero la Davide.” Liri pemphero limene mungalipange kukhala la inu mwini.

Wozunzika koma Wokhulupirika

3. M’nthaŵi zino, kodi ndichitsanzo cholimbikitsa chotani chimene Davide akutipatsa?

3 Davide analemba salmo limeneli pamene anali kuzunzika. Ife lerolino, amene tikukhala ndi moyo mkati mwa “masiku otsiriza” adongosolo la Satana, ‘nthaŵi zowaŵitsa zovuta kuchita nazo’ zimenezi, tikukumana ndi ziyeso zofanana. (2 Timoteo 3:1; wonaninso Mateyu 24:9-13.) Mofanana nafe, Davide anavutika ndi nkhaŵa ndi chitsenderezo chifukwa cha mavuto omuyambukira. Koma iye sanalole konse mayeso amenewo kufooketsa chidaliro chake chakukhulupirira Mlengi wake. Iye anachonderera kuti: “Tcherani khutu lanu Yehova, mundiyankhe; pakuti ine ndine wozunzika ndi waumphaŵi. Sungani moyo wanga pakuti ine ndine wokondedwa wanu; Inu Mulungu wanga, pulumutsani mtumiki wanu wokhulupirira Inu.”​—Salmo 86:1, 2.

4. Kodi tiyenera kusonyeza motani chidaliro chathu?

4 Tingakhale achidaliro, monga momwe Davide analiri, kuti “Mulungu wa chitonthozo chonse,” Yehova, adzatchera khutu lake kudziko lino lapansi ndi kumvetsera mapemphero athu odzichepetsa. (2 Akorinto 1:3, 4) Tiri ndi chidaliro chotheratu mwa Mulungu wathu, tingathe kutsatira uphungu wa Davide wakuti: “Umsenze Yehova nkhaŵa zako, ndipo iye adzakugwiriziza: nthaŵi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.”​—Salmo 55:22.

Kuzoloŵerana ndi Yehova

5. (a) Kodi ndimotani mmene matembenuzidwe ena osamalitsa akonzera zophophonya za alembi Achiyuda? (b) Kodi ndim’njira yotani imene Salmo la 85 ndi la 86 limalemekezera Yehova? (Wonani mawu amtsinde.)

5 M’Salmo lachi 86, Davide akugwiritsira ntchito mawu akuti “O Yehova” (NW) nthaŵi 11. Pemphero la Davide nlosonyeza khama chotani nanga ndipo kuzoloŵerana kwake ndi Yehova nkokulira chotani nanga! Pambuyo pake, kuzoloŵerana kotero kogwiritsira ntchito dzina la Mulungu kunafikira kukhala konyansa kwa alembi Achiyuda, makamaka Asoferimu. Iwo anakulitsa kuchita mantha kokhulupirira malaulo kwakugwiritsira ntchito molakwa dzinalo. Monyalanyaza chenicheni chakuti munthu analengedwa m’chifanizo cha Mulungu, iwo sanafune kupereka kwa Mulungu mikhalidwe imenenso anthu amasonyeza. Chotero, m’malo 7 mwa 11 m’mene dzina la Mulungu limawonekera m’lemba Lachihebri la salmo limodzi limeneli, iwo analembamo dzina laulemu lakuti ʼAdho-naiʹ (Ambuye) mmalo mwa dzinalo YHWH (Yehova). Tiyenera kukhala oyamikira kuti New World Translation of the Holy Scriptures, kudzanso matembenuzidwe ena angapo osamalitsa, abwezeretsa dzina la Mulungu pamalo ake oyenerera m’Mawu a Mulungu. Monga chotulukapo, unansi wathu ndi Yehova ukugogomezeredwa monga momwe uyenera kukhalira.a

6. Kodi ndim’njira zotani m’zimene tingasonyeze kuti dzina la Yehova nlamtengo wapatali kwa ife?

6 Pemphero la Davide likupitirizabe kuti: “Ndisonyezeni chiyanjo, O Yehova, pakuti tsiku lonse ndiitana kwa inu. Kondweretsani moyo wamtumiki wanu, pakuti kwa inu, O Yehova, nditukulira moyo wanga weniweniwo.” (Salmo 86:3, 4, NW) Tawonani kuti Davide anapitirizabe kuitanira pa Yehova “tsiku lonse.” Ndithudi, iye anapemphera kaŵirikaŵiri usiku wonse, monga pamene anali wothaŵa m’chipululu. (Salmo 63:6, 7) Mofananamo lerolino, Mboni zina pamene zithupsidwa kugwiriridwa chigololo kapena kuukira kwina kwaupandu zimafuula kwa Yehova. Panthaŵi zina izo zadabwitsidwa ndi zotulukapo zokondweretsa.b Dzina la Yehova nla mtengo wapatali kwa ife, monga momwe linaliri kwa “Yesu Kristu, mwana wa Davide,” pamene anali padziko lapansi. Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kupempherera kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova nadziŵikitsa kwa iwo chimene dzinalo linaimira.​—Mateyu 1:1; 6:9; Yohane 17:6, 25, 26.

7. Kodi ndizitsanzo zotani zimene tiri nazo zakutsitsimula kwa Yehova moyo weniweni wa atumiki ake, ndipo tiyenera kulabadira motani?

7 Davide anatukulira moyo wake wathunthu kumwamba, kwa Yehova. Iye akutilimbikitsa kuchita mofananamo, akumanena pa Salmo 37:5 kuti: “Pereka njira yako kwa Yehova; khulupiriranso Iye, adzachichita.” Chotero pempho lathu kwa Yehova lakuti iye apangitse mtima wathu kukondwera silidzakhala losayankhidwa. Atumiki osunga umphumphu ambiri a Yehova akupitirizabe kupeza chisangalalo mu utumiki wake​—mosasamala kanthu za zovuta, zizunzo, ndi utenda. Abale athu m’zigawo zokanthidwa ndi nkhondo mu Afirika, monga Angola, Liberia, Mozambique, ndi Zaire, apitirizabe kuika utumiki wa Yehova pachiyambi m’miyoyo yawo.c Iye wawachititsadi kusangalala m’kututa zambirimbiri kwauzimu. Monga momwe iwo apiririra, ifenso tiyenera kutero. (Aroma 5:3-5) Ndipo pamene tipirira, tikupatsidwa chitsimikizo chakuti: ‘Masomphenya alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumirira potsirizira pake . . . Sadzazengereza.’ (Habakuku 2:3) Ndichiyembekezo chotheratu ndi chidaliro mwa Yehova, nafenso tipitirizetu ‘kulindirira kufikira mapeto.’

Ubwino wa Yehova

8. Kodi ndikuzoloŵerana kotani kumene tingakhale nako ndi Yehova, ndipo kodi iye wasonyeza motani ubwino wake?

8 Davide akupereka pemphero lina lochonderera kuti: “Inu, O Yehova, ndinu wabwino ndi wokhululuka msanga; ndi wachifundo chochuluka kwa onse oitanira pa inu. Tcherani khutu, O Yehova, kupemphero langa; ndipo mvetserani mawu a mapembedzero anga. M’tsiku la nsautso yanga ndidzaitana pa inu, pakuti mudzandiyankha.” (Salmo 86:5-7, NW) “O Yehova”​—mobwerezabwereza tikuchita chidwi chotani nanga ndi mawu osonyeza kuzoloŵerana amenewa! Ndiko kuzoloŵerana kumene kungakulitsidwe mosalekeza kupyolera mwa pemphero. Davide anapemphera panyengo ina kuti: “Musakumbukire zolakwa zaubwana wanga kapena zopikisana nanu: mundikumbukire monga mwachifundo chanu, chifukwa chaubwino wanu, Yehova.” (Salmo 25:7) Yehova ndiye chitsanzo chenicheni chaubwino​—m’kupereka dipo la Yesu, m’kusonyeza chifundo kwa ochimwa olapa, ndi m’kusonyeza kukoma mtima kwachikondi kwa Mboni zake zokhulupirika ndi zoyamikira.​—Salmo 100:3-5; Malaki 3:10.

9. Kodi nchitsimikiziro chotani chimene ochimwa olapa ayenera kulingalira mwamphamvu?

9 Kodi tiyenera kudera nkhaŵa zophophonya zapitazo? Ngati ife tsopano tiri kulambulira mapazi athu njira zowongoka, timalimbikitsidwa pamene tikumbukira chitsimikiziro cha mtumwi Petro kwa olapawo chakuti “nyengo za kutsitsimutsa” zidzadza kuchokera kwa Yehova. (Machitidwe 3:19) Tiyeni tiyandikire kwa Yehova m’pemphero kupyolera mwa Wopereka Dipo wathu, Yesu, amene mwachikondi anati: “Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine; chifukwa ndiri wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.” Pamene Mboni zokhulupirika zipemphera kwa Yehova lerolino m’dzina lokondedwa la Yesu, izo zimapezadi mpumulo.​—Mateyu 11:28, 29; Yohane 15:16.

10. Kodi ndiulemu wotani umene bukhu la Masalmo limapereka pa kukoma mtima kwachikondi kwa Yehova?

10 Bukhu la Masalmo limatchula ‘kukoma mtima kwa chikondi’ kwa Yehova nthaŵi zoposa zana. Kukoma mtima kwachikondi kotero nkochulukadi! M’mavesi ake anayi oyamba, Salmo 118 limapempha atumiki a Mulungu kuyamika Yehova, likumabwereza nthaŵi zinayi kuti “pakuti chifundo chake chachikondi chiri kunthaŵi zosadziŵika, (NW).” Salmo la 136 limagogomezera mkhalidwe wabwino koposawo wa ‘kukoma mtima kwake kwachikondi’ nthaŵi 26. Mulimonse mmene tingachimwire​—ndipo monga momwe Yakobo 3:2 akunenera, “timakhumudwa tonse pazinthu zambiri”​—tikhaletu okonzekera kufunafuna chikhululukiro cha Yehova, tiri ndi chidaliro cha chifundo chake ndi kukoma mtima kwachikondi. Kukoma mtima kwake kwachikondi ndiko chisonyezero chachikondi chake chokhulupirika kwa ife. Ngati ife tipitirizabe mokhulupirika kuchita chifuniro chake, iye adzasonyeza chikondi chake chokhulupirika mwakutilimbikitsa kuti tigonjetse chiyeso chirichonse.​—1 Akorinto 10:13.

11. Kodi ndimotani mmene chochita cha akulu chingathandizire kuchotsa malingaliro aliwongo?

11 Pangakhale nthaŵi pamene ife tingakhumudwitsidwe ndi ena. Kuchitiridwa nkhanza mwamaganizo kapena mwakuthupi paubwana kwachititsa ena kukhala ndi malingaliro aliwongo kapena kulankhula mawu osayenera. Mkhole wotero ungaitanire pa Yehova, ndi chidaliro chakuti iye adzayankha. (Salmo 55:16, 17) Mkulu wachifundo angasonyeze chikondwerero mwakuthandiza munthu wotero kuzindikira chenicheni chakuti sichinali chifukwa cha mkholewo. Pambuyo pake, kulankhula naye mwaubwenzi pafoni kochitidwa nthaŵi ndi nthaŵi ndi mkuluyo kungathandize munthuyo kufikira pamene adzakhoza ‘kusenza chothodwetsacho.’​—Agalatiya 6:2, 5.

12. Kodi ndimotani mmene nsautso zaŵirikizira, koma kodi tingazingojetse motani?

12 Pali mikhalidwe ina yambiri yomvetsa chisoni imene anthu a Yehova afunikira kulimbana nayo lerolino. Kuyambira pa Nkhondo Yadziko I mu 1914, masoka aakulu anayamba kukantha dziko lino lapansi. Monga momwe kunanenedweratu ndi Yesu, chimenecho chinali ‘chiyambi cha zoŵawa za nsautso.’ Nsautso zaŵirikiza pamene taloŵa kwambiri mu ‘mapeto a dongosolo la zinthu.’ (Mateyu 24:3, 8) “Kanthaŵi” ka Mdyerekezi kakufika pogomera mapeto ake enieni. (Chivumbulutso 12:12) “Monga mkango wobuma” umene ukufunafuna mkhole, Mdani wamkulu ameneyu akugwiritsira ntchito machenjera opezeka alionse kutilekanitsa ndi gulu lankhosa la Mulungu ndi kutiwononga. (1 Petro 5:8) Koma iye sadzapambana! Pakuti, mofanana ndi Davide, ife tikuika chidaliro chathu chonse mwa Mulungu wathu mmodzi, Yehova.

13. Kodi ndimotani mmene makolo ndi ana awo angapindulire ndi ubwino wa Yehova?

13 Mosakaikira, Davide anakhomereza mu mtima wa mwana wake Solomo kufunika kwa kudalira pa ubwino wa Yehova. Chotero, Solomo anakhoza kulangiza mwana wake kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; Umlemekeze m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola mayendedwe ako. Usadziyese wekha wanzeru; Wopa Yehova, nupatuke pa zoipa.” (Miyambo 3:5-7) Mofananamo makolo lerolino ayenera kuphunzitsa ana awo mmene angapempherere modalira Yehova ndi mmene angagonjetsere ziukiro zokakala za dzikoli​—monga chitsenderezo cha a msinkhu wofanana ku sukulu ndi ziyeso zakuchita chisembwere. Kukhalira moyo chowonadi limodzi ndi ana anu tsiku lirilonse kungathe kukhomereza pa mitima yawo yachichepereyo chikondi chowona cha pa Yehova ndi kudalira pa iye mwapemphero.​—Deuteronomo 6:4-9; 11:18, 19.

Ntchito Zosayerekezereka za Yehova

14, 15. Kodi nziti zimene ziri zina za ntchito zosayerekezereka za Yehova?

14 Mwachikhutiro chonse Davide akuti: “Palibe wofanana nanu pakati pa milungu, O Yehova, ndiponso palibe ntchito zirizonse zofanana ndi zanu.” (Salmo 86:8, NW) Ntchito za Yehova nzazikulu kwambiri, nzaulemerero kwambiri, nzapamwambamwamba, kuposa mmene munthu aliyense angayerekezere. Monga momwe chasonyezedwera pang’ono ndi sayansi yamakono, chilengedwe chonse cholengedwacho​—ukulu wake, kugwirizana kwake, ulemerero wake​—chatsimikizira kukhala chothetsa malovu kwambiri kuposa chinthu chirichonse chimene Davide anazindikira. Chikhalirechobe, ngakhale iyeyo anasonkhezeredwa kunena kuti: “Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo liwonetsa ntchito ya manja ake.”​—Salmo 19:1.

15 Ndiponso, ntchito za Yehova zalinganizidwa modabwitsa, m’njira imene anakhazikitsira ndi kukonzekeretsera dziko lapansi, kukhala ndi usana ndi usiku, nyengo, nthaŵi yakufesa ndi yakututa, ndi zokondweretsa zambirimbiri zodzasangalatsa anthu mtsogolo. Ndipo ife tiri opangidwa modabwitsa chotani nanga ndi kukonzekeretsedwa, kotero kuti tiri okhoza kusangalala ndi ntchito za Yehova zimene zatizinga!​—Genesis 2:7-9; 8:22; Salmo 139:14.

16. Kodi nchiti chimene chiri chisonyezero chachikulu koposa cha ubwino wa Yehova, chikumatsogolera kuntchito zinanso ziti zosayerekezereka?

16 Pambuyo pakusamvera Mulungu kochitidwa ndi makolo athu oyamba, kukumayambitsa nsautso zimene zakantha dziko lapansi kufikira lerolino, Yehova mwachikondi chake anachita ntchito yodabwitsa m’kutumiza Mwana wake ku dziko lapansi kukalengeza Ufumu wa Mulungu ndi kufa monga dipo la anthu. Ndicho chodabwitsa cha zonsezo! Pamenepo Yehova anaukitsa Kristu kukhala Mfumu inzake yosankhidwa. (Mateyu 20:28; Machitidwe 2:32, 34) Kuchokera mwa anthu okhulupirika Mulungu wasankhanso “chilengedwe chatsopano” cha amene adzalamulira ndi Kristu mokoma mtima monga “kumwamba kwatsopano” pa chimangidwe cha “dziko latsopano” chimene chidzaphatikizapo anthu mabiliyoni ambiri oukitsidwa. (2 Akorinto 5:17; Chivumbulutso 21:1, 5-7; 1 Akorinto 15:22-26) Chotero ntchito za Yehova zidzapita patsogolo kufikira pachimake chaulemerero! Ndithudi, tingathe kudzuma kuti: “O Yehova, . . . ubwino wanu ngwochuluka chotani nanga, umene mwasungira okuopani!”​—Salmo 31:17-19, NW.

17. Ponena za ntchito za Yehova, kodi ndimotani mmene Salmo 86:9 tsopano likukwaniritsidwira?

17 Ntchito zamakono za Yehova zimaphatikizapo zimene Davide akufotokoza pa Salmo 86:9 (NW) kuti: “Amitundu onse amene mudawalenga adzadza nadzagwada pamaso panu, O Yehova, nadzalemekeza dzina lanu.” Pambuyo pakuitana kuchokera pakati pa anthu otsala achilengedwe chake chatsopano, “akagulu kankhosa” oloŵa nyumba Aufumu, Yehova wasonkhanitsa kuchokera pakati pa “mitundu yonse” “khamu lalikulu” la “nkhosa zina,” mamiliyoni ambiri amenenso amasonyeza chikhulupiriro m’mwazi wokhetsedwa wa Yesu. Amenewa iye wawapanga kukhala gulu lamphamvu, chimangidwe chokha chapadziko lonse cha okonda mtendere padziko lapansi lerolino. Powona zimenezi, makamu akumwamba akuweramira Yehova, nalengeza kuti: “Thamo ndi ulemerero, ndi nzeru, ndi chiyamiko, ndi ulemu, ndi chilimbiko, ndi mphamvu zikhale kwa Mulungu wathu kufikira nthaŵi za nthaŵi.” Nalonso khamu lalikulu likulemekeza dzina la Yehova, likumamtumikira “usana ndi usiku,” liri ndi chiyembekezo chakupulumuka mapeto adziko lino ndi kukhala ndi moyo kosatha pa paradaiso wadziko lapansi.​—Luka 12:32; Chivumbulutso 7:9-17; Yohane 10:16.

Ukulu wa Yehova

18. Kodi ndimotani mmene Yehova wasonyezera kuti iye ali ‘Mulungu yekha’?

18 Kenako Davide akusumika maganizo pa Umulungu wa Yehova akumati: ‘Inu ndinu wamkulu ndi wakuchita zodabwitsa; Inu ndinu Mulungu, nokhanu.’ (Salmo 86:10) Kuyambira kalekale, Yehova wakhala akusonyeza kuti, ndithudi iye ali, ‘Mulungu yekha.’ Anali Farao wa Igupto wankhalweyo amene mwamwano anapereka chitokoso kwa Mose kuti: “Yehova ndani, kuti ndimvere mawu ake ndi kulola Israyeli apite? Sindimdziŵa Yehova.” Koma mwamsanga anadziŵa mmene Yehova aliri wamkulu! Mulungu wamphamvuyonse anachititsa manyazi milungu ya Igupto ndi ansembe ochita matsenga mwakutumiza miliri yowononga, akumanyonga ana aamuna achisamba a Igupto ndi kupululutsa Farao ndi magulu ake ankhondo okwezekawo m’Nyanja Yofiira. Ndithudi, palibe wofanana ndi Yehova pakati pa milungu!​—Eksodo 5:2; 15:11, 12.

19, 20. (a) Kodi ndiliti pamene nyimbo ya pa Chivumbulutso 15:3, 4 idzafika pachimake chakuimbidwa kwake? (b) Kodi ndimotani mmene ngakhale tsopano tingakhalire ndi phande m’ntchito ya Yehova?

19 Monga Mulungu yekha, Yehova wapitiriza kuchita zinthu zodabwitsa kukonzekerera kuwombola olambira ake omvera kwa Igupto wamakono​—dziko la Satana. Iye wachititsa ziweruzo zake kulengezedwa padziko lonse lapansi monga umboni kudzera mu mkupiti wakulalikira waukulu kuposa ina yonse m’mbiri, chotero kukwaniritsa ulosi wa Yesu pa Mateyu 24:14. Mwamsanga, “mapeto” ayenera kudza, pamene Yehova adzasonyeza ukulu wake pamlingo wosayerekezereka mwakusesa kuipa konse padziko lapansi. (Salmo 145:20) Pamenepo Nyimbo ya Mose ndi nyimbo ya Mwanawankhosa idzafika pachimake yakuti: “Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, [Yehova, NW] Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zowona, Mfumu inu ya nthaŵi zosatha. Ndani adzakhala wosawopa ndi wosalemekeza dzina lanu [Yehova, NW]? Chifukwa Inu nokha muli woyera.”​—Chivumbulutso 15:3, 4.

20 Ponena za ife, tikhaletu achangu m’kulankhula kwa ena za zifuno zaulemerero wa Mulungu zimenezi. (Yerekezerani ndi Machitidwe 2:11.) Yehova adzapitirizabe kuchita zinthu zazikulu ndi zodabwitsa m’tsiku lathu ndipo adzatero kufikira mtsogolomo, monga momwe nkhani yathu yotsatira idzafotokozera.

[Mawu a M’munsi]

a Ndemanga yoperekedwa ya Baibulo mu 1874 ikugwira mawu Andrew A. Bonar kukhala akunena kuti: “Panali zambiri, zambirimbiri, za umunthu wapadera wa Mulungu, ulemelero wa dzina lake, zimene zinavumbulutsidwa chakumapeto kwa Salmo lomalizira [la 85]. Zimenezi zingakhale chifukwa chake likutsatiridwa ndi linalo, ‘Pemphero la Davide,’ pafupifupi lodzalanso mofanana ndi umunthu wa Yehova. Mfundo yaikulu ya Salmo [la 86] limeneli ndiyo dzina la Yehova.”

b Wonani tsamba 28 la kope la Awake! ya June 22, 1984, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

c Kuti mupeze maumboni, wonani tchati cha “Lipoti la Chaka Chautumiki cha 1992 la Mboni za Yehova Padziko Lonse Lapansi,” chimene chidzakhala m’kope la January 1, 1993, la Nsanja ya Olonda.

Kodi Mukukumbukira?

◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupanga pemphero la Salmo 86 kukhala lathulathu?

◻ Kodi tingazoloŵerane motani ndi Yehova?

◻ Kodi Yehova amasonyeza motani ubwino wake kwa ife?

◻ Kodi nziti zimene ziri zina za ntchito zosayerekezereka za Yehova?

◻ Kodi Yehova ali ‘Mulungu yekha’ motani ponena za ukulu?

[Chithunzi patsamba 10]

Mu “dziko lapansi latsopano” lirinkudza, ntchito zodabwitsa za Yehova zidzapereka umboni wa ulemerero ndi ubwino wake

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena